Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

ZIMENE MUNGACITE PA PHUNZILO LA INU MWINI

Anthu Auzimu Amapanga Zisankho Zanzelu

Anthu Auzimu Amapanga Zisankho Zanzelu

Ŵelengani Genesis 25:​29-34 kuti muone ngati Esau na Yakobo anapanga zisankho zanzelu.

Kumbani mozamilapo kuti mumvetse nkhani yonse. Kodi zinthu zinali bwanji izi zisanacitike? (Gen. 25:​20-28) Nanga n’ciyani cinacitika pambuyo pake?—Gen. 27:​1-46.

Kumbani mozamilapo kuti mumvetse mmene zinthu zinali kucitikila pa nthawiyo. Ni mwayi wapadela uti, komanso ni maudindo ati amene mwana woyamba kubadwa anali kukhala nawo?—Gen. 18:​18, 19; w10 5/1 13.

  • Kodi munthu anayenela kukhala woyamba kubadwa kuti akhale mu mzele wobadwila Mesiya? (w17.12 14-15)

Pezani maphunzilo amene alipo na kuwaseŵenzetsa. N’cifukwa ciyani Yakobo anaona mwayi wokhala woyamba kubadwa kuti ni wamtengo wapatali kuposa mmene Esau anauonela? (Aheb. 12:​16, 17; w03 10/15 28-29) Kodi Yehova anali kuwaona bwanji anthu aŵili a pacibale amenewa? Ndipo n’cifukwa ciyani? (Mal. 1:​2, 3) Kodi Esau akanawongolela pati kuti apange zisankho zanzelu?

  • Dzifunseni kuti, ‘Kodi ningaonetse bwanji kuti nimayamikila zinthu zauzimu m’zocita zanga mlungu uliwonse?’ Mwa citsanzo, ‘kodi nimapatula tsiku komanso nthawi yokwanila yocita kulambila kwa pabanja?’