NKHANI YOPHUNZILA 17
NYIMBO 111 Zifukwa Zokhalila Acimwemwe
Musacokemo m’Paradaiso Wauzimu
“Kondwelani ndipo muzisangalala mpaka kalekale ndi zimene ndikulenga.”—YES. 65:18.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Mapindu amene timapeza m’paradaiso wauzimu na mmene tingakokele ena kuti aloŵemo.
1. Kodi paradaiso wauzimu n’ciyani? Ndipo tiyenela kukhala otsimikiza kucita ciyani?
PALI paradaiso winawake pa dziko lapansi masiku ano wodzala na anthu amene amacita zabwino. Anthu amene ali m’paradaiso ameneyu amafika m’mamiliyoni, ndipo amasangalala na mtendele weniweni. Iwo ni otsimikiza mtima kusacokamo, ndipo amafunanso kuti anthu ambili abwele kudzagwilizana nawo m’paradaiso wauzimu ameneyu! a
2. N’ciyani cocititsa cidwi na paradaiso wauzimu?
2 N’zocititsa cidwi kuti Yehova wapanga malo ophiphilitsa a bata m’dziko limene Satana walisandutsa kukhala la cidani, loipa, komanso loopsa. (1 Yoh. 5:19; Chiv. 12:12) Mulungu wathu wacikondi amadziŵa mmene dongosolo lino la zinthu limatikhudzila, ndipo amapeleka citetezo cimene timafunikila kuti tipitilize kukula mwauzimu. Mawu ake amafotokoza paradaiso wauzimu kuti ni “malo othawilapo,” komanso “dimba lothililidwa bwino.” (Yes. 4:6; 58:11) Cifukwa ca dalitso la Yehova, nzika za paradaiso ameneyu zimakhala na cimwemwe, ndipo n’zotetezeka m’masiku otsiliza ovuta ano.—Yes. 54:14; 2 Tim. 3:1.
3. Fotokozani kukwanilitsidwa koyamba kwa Yesaya caputala 65.
3 Kudzela mwa mneneli Yesaya, Yehova anafotokoza mmene zinthu zidzakhalile kwa anthu amene adzakhale m’paradaiso wauzimu. Mulungu anafotokoza zimenezi mu Yesaya caputala 65, ndipo mawuwo anakwanilitsidwa koyamba mu 537 B.C.E. Pa nthawiyo, Ayuda olapa anamasulidwa mu ukapolo ku Babulo, ndipo anabwelela ku dziko lawo. Yehova anadalitsa anthu ake, ndipo anawathandiza kukonza mzinda wowonongedwa wa Yerusalemu kuti ukhalenso wokongola. Anawathandizanso kubwezeletsa kacisi wake kuti akhalenso cimake ca kulambila koona.—Yes. 51:11; Zek. 8:3.
4. Kodi ulosi wa pa Yesaya 65 ukukwanilitsidwa bwanji masiku ano?
4 Kukwanilitsidwa kwaciŵili kwa ulosi wa Yesaya kunayamba mu 1919 C.E. pomwe alambili a Yehova amakono anamasulidwa ku ukapolo wa Babulo Wamkulu. Ndiyeno paradaiso wauzimu anayamba kukula kuzungulila dziko lonse lapansi. Alaliki a Ufumu okangalika anakhazikitsa mipingo ndipo anabala zipatso zauzimu. Amuna na akazi amene anali aciwawa komanso na makhalidwe aucinyama, anasintha n’kuvala “umunthu watsopano umene unalengedwa mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu.” (Aef. 4:24) N’zoona kuti madalitso amene Yesaya anakamba, adzakwanilitsidwa mwakuthupi m’dziko latsopano m’tsogolo. Koma ngakhale pali pano tikulandila madalitso oculuka m’paradaiso wauzimu. Tiyeni tione mmene paradaiso wauzimu ameneyu amatikhudzila, komanso cifukwa cake sitiyenela kucokamo.
MMENE ZINTHU ZILILI KWA A M’PARADAISO WAUZIMU
5. Malinga na lonjezo la pa Yesaya 65:13, ni madalitso otani amene timasangalala nawo m’paradaiso wauzimu?
5 Athanzi koma otsitsimulidwa. Ulosi wa Yesaya umaonetsa kusiyana kwa mmene umoyo ulili pakati pa anthu amene ali m’paradaiso wauzimu na amene salimo. (Ŵelengani Yesaya 65:13.) Yehova moolowa manja, amakhutilitsa zofunikila zauzimu za alambili ake. Watipatsa mzimu woyela, Mawu ake, komanso zofalitsa zozikika m’Baibo zimene timadya, kumwa na kusangalala nazo. (Yelekezelani na Chivumbulutso 22:17) Koma umu si mmene zilili kwa amene sali m’paradaiso wauzimu. Iwo ali na ‘njala . . . , ludzu . . . , ndipo amacita manyazi.’ Zosoŵa zawo zauzimu sizimakhutilitsidwa.—Amosi 8:11.
6. Kodi Yoweli 2:21-24 imatiphunzitsa mfundo yotani pa cakudya cauzimu cimene tili naco? Nanga cimatipindulila bwanji?
6 Mu ulosi wake, Yoweli anachula zinthu zofunikila pa umoyo monga mbewu, vinyo, komanso mafuta. Anachula zimenezi poonetsa kuti Yehova amapatsa anthu ake zinthu zofunikila kuphatikizapo cakudya cauzimu. (Yow. 2:21-24) Amacita zimenezi kupitila m’Baibo, m’zofalitsa zozikika m’Baibo, na webusaiti yathu. Amacitanso zimenezi kupyolela m’misonkhano ya mpingo, ya dela, komanso ya cigawo. Tingapindule na cakudya cauzimu cimeneci tsiku lililonse. Tikatelo timakhala athanzi, komanso timatsitsimulidwa kwambili.
7. N’ciyani cimatipatsa “cimwemwe mumtima”? (Yesaya 65:14)
7 Acimwemwe komanso okhutila. Anthu a Mulungu ‘amafuula mosangalala’ cifukwa mitima yawo ni yodzala na kuyamikila. (Ŵelengani Yesaya 65:14.) Timakhala na “cimwemwe mumtima” cifukwa ca mfundo zolimbikitsa za coonadi, malonjezo okhazika mtima pansi a m’Mawu a Mulungu, komanso ciyembekezo cotsimikizika cozikika mu nsembe ya dipo ya Khristu. Timakhala na cimwemwe cacikulu pokambilana zinthu zimenezi na alambili anzathu.—Sal. 34:8; 133:1-3.
8. Ni makhalidwe akulu-akulu ati amene amaonekela m’paradaiso wauzimu?
8 Cikondi komanso mgwilizano zomwe zili pakati pa anthu a Mulungu ndiwo makhalidwe aakulu m’paradaiso wauzimu. Makhalidwe amenewa amatipatsa cithunzi ca mmene umoyo udzakhalile m’dziko latsopano. Pa nthawiyo, atumiki a Yehova adzakhala okondana kwambili, komanso ogwilizana kuposa mmene zilili masiku ano. (Akol. 3:14) Mlongo wina anafotokoza zimene anaona nthawi yoyamba atakumana na anthu a Mulungu. Iye anati: “Sin’nakhalepo wacimwemwe ngakhale m’banja lathu. Nthawi yoyamba pamene n’naona cikondi ceniceni ni pakati pa Mboni za Yehova.” Aliyense amene afuna kukhala wacimwemwe, komanso wokhutila ayenela kuloŵa m’paradaiso wathu wauzimu. Mosasamala kanthu za mmene dziko limaonela mtumiki wa Yehova, iye ali na dzina lolemekezeka, kapena kuti mbili yabwino kwa Yehova, komanso ku banja lake la pa dziko lonse.—Yes. 65:15.
9. Kodi Yesaya 65:16, 17 imalonjeza kuti n’ciyani cidzacitikila mavuto amene timakumana nawo?
9 Osatekeseka komanso odekha. Yesaya 65:14 imanena kuti anthu amene amasankha kukhalabe kunja kwa paradaiso wauzimu amalila “cifukwa copwetekedwa mtima [komanso] cifukwa cosweka mtima.” Nanga bwanji za zinthu zimene zapangitsa kuti anthu a Mulungu akumane na zoŵaŵa komanso zolefula? Zinthu zimenezi zidzaiŵalika kwa Mulungu ndipo zidzabisidwa kuti iye asazionenso. (Ŵelengani Yesaya 65:16, 17.) Yehova adzathetsa mavuto athu onse. Ndipo m’kupita kwa nthawi zinthu zimenezi zidzaiŵalika kothelatu.
10. N’cifukwa ciyani mumaona kuti ni dalitso kukhala m’gulu la Mulungu? (Onaninso cithunzi.)
10 Ngakhale masiku ano, timatsitsimulidwa pa misonkhano yathu ya Cikhristu cifukwa timakhala mwa bata ndipo timaiŵalako nkhawa za m’dziko loipali. Timathandizila kuti m’paradaiso wathu wauzimu mukhale bata tikamaonetsa zipatso zimene mzimu woyela umabala monga cikondi, cimwemwe, mtendele, kukoma mtima, komanso kufatsa. (Agal. 5:22, 23) Ni dalitso lalikulu zedi kukhala m’gulu la Mulungu! Awo amene akhalabe m’paradaiso wauzimu, adzaona kukwanilitsidwa kwathunthu kwa lonjezo la Mulungu la kupanga “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.”
11. Malinga na Yesaya 65:18, 19, kodi paradaiso wauzimu amene Yehova anapanga amatilimbikitsa kucita ciyani?
11 Oyamikila komanso okondwela. Yesaya anafotokoza zimene zimatipangitsa kukhala ‘okondwela komanso osangalala’ m’paradaiso wauzimu. Malo ophiphilitsa amenewa ni Yehova anawapanga. (Ŵelengani Yesaya 65:18, 19.) Ndiye cifukwa cake Yehova akutiseŵenzetsa kuti tithandize anthu kucoka m’mabungwe a dzikoli amene saphunzitsa coonadi kuti aloŵe m’paradaiso wauzimu wokongola ameneyu! Timasangalala na madalitso amene timakhala nawo cifukwa cokhala m’coonadi. Ndipo zimenezi zimatilimbikitsa kuuzako ena za madalitso amenewa.—Yer. 31:12.
12. Kodi malonjezo a pa Yesaya 65:20-24 amakupangitsani kumva bwanji? Ndipo cifukwa ciyani?
12 Cina, pokhala nzika za paradaiso wauzimu, timayamikila komanso kusangalala na ciyembekezo cimene tili naco. Ganizilani cabe zonse zimene tidzatha kuona, komanso kucita m’dziko latsopano! Baibo imalonjeza kuti: “Kumeneko sikudzakhalanso mwana wakhanda amene adzangokhala ndi moyo masiku ocepa okha, kapena munthu wacikulile amene sadzakwanitsa zaka zimene munthu amafunika kukhala ndi moyo.” ‘Tidzamanga nyumba n’kukhalamo ndipo tidzabyala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.’ Sitidzagwila “nchito mwakhama pacabe” cifukwa tidzakhala “anthu odalitsidwa ndi Yehova.” Iye watilonjeza moyo wotetezeka, wokhutilitsa, komanso wokhala na colinga. Ngakhale asanamuitane, iye adzadziŵa zofunikila za munthu aliyense ndipo adzakhutilitsa “zolakalaka za camoyo ciliconse.”—Yes. 65:20-24; Sal. 145:16.
13. Kodi Yesaya 65:25 imawafotokoza motani masinthidwe amene anthu amapanga akayamba kutumikila Yehova?
13 Amtendele komanso otetezeka. Na thandizo la mzimu woyela, ambili amene kale anali aciwawa, ankhanza, komanso osaona mtima apanga masinthidwe aakulu pa umoyo wawo. (Ŵelengani Yesaya 65:25.) Acita zonse zotheka kuti asiye makhalidwe oipa amenewo. (Aroma 12:2; Aef. 4:22-24) Anthu a Mulungu akali opanda ungwilo, ndipo amalakwitsa zinthu. Ngakhale n’telo, Yehova wagwilizanitsa anthu a mitundu yosiyana-siyana m’gulu lacikondi komanso lamtendele. (Tito 2:11) Ici ni cozizwitsa cimene Mulungu wamphamvuyonse cabe ndiye angacicite!
14. Kodi Yesaya 65:25 inakwanilitsidwa bwanji kwa m’bale wina?
14 Kodi n’zothekadi anthu kusintha umunthu wawo? Ganizilani cocitika ici. Mnyamata wina anali kuikidwa m’ndende kaŵili-kaŵili ali na zaka 20. Iye anali waciwawa kwambili ndipo anali kucita zaciwelewele. Anamangidwapo cifukwa ca kuba galimoto, kuthyola nyumba za ena kuti abe, komanso cifukwa ca milandu ina ikulu-ikulu. Anali wokonzeka kumenyana na aliyense amene wam’puta. Atamvetsela coonadi ca m’Baibo kwa nthawi yoyamba na kuyamba kupezeka pa misonkhano, anakhutila kuti wadziŵa colinga ca moyo cimene ni kulambila Yehova m’paradaiso wauzimu. Atabatizika n’kukhala Mboni, nthawi zambili anali kuganizila mmene Yesaya 65:25 inakhalila yoona kwa iye. Iye anasintha kucoka pa kukhala ngati mkango, munthu waciwawa, n’kukhala ngati nkhosa, munthu wamtendele.
15. N’cifukwa ciyani timafuna kuitana ena kuti abwele m’paradaiso wauzimu? Nanga tingacite bwanji zimenezi?
15 Yesaya 65:13 imayamba na mawu akuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti.” Vesi 25 imamaliza na mawu akuti: “akutelo Yehova.” Mawu a Mulungu amakwanilitsika nthawi zonse. (Yes. 55:10, 11) Paradaiso wauzimu alipo, ndipo ni weniweni. Yehova anakhazikitsa gulu lapadela logwilizana la abale na alongo. Timapeza mtendele weniweni pakati pa anthu ake amenewa, ndipo timakhala otetezeka m’dzikoli la nkhanza. (Sal. 72:7) Ndiye cifukwa cake, timafuna kuthandiza anthu ambili mmene tingathele kuti agwilizane nafe pa ubale wathu wa Cikhristu. Tingacite zimenezi mwa kuika maganizo athu pa kupanga ophunzila.—Mat. 28:19, 20.
MMENE TINGAKOPELE ENA KUTI ABWELE M’PARADAISO WAUZIMU
16. Kodi anthu amakokedwela m’paradaiso wauzimu motani?
16 Aliyense wa ife ali na mbali imene afunika kucita pokongoletsa paradaiso wauzimu kuti azikopa anthu ena. Tingakwanilitse udindo umenewu mwa kutengela Yehova. Iye sakoka anthu mwa cikakamizo kuti aloŵe m’gulu lake. M’malo mwake, amawakokela kwa iye mwacikondi. (Yoh. 6:44; Yer. 31:3) Anthu a mitima yabwino amene aphunzila za makhalidwe abwino a Yehova, komanso umunthu wake wocititsa cidwi, amakokedwela kwa iye. Kodi ni motani mmene makhalidwe anthu abwino, komanso umunthu wathu zingakopele anthu kubwela m’paradaiso wauzimu?
17. Kodi tingakope bwanji anthu ena kubwela m’paradaiso wauzimu?
17 Njila imodzi imene tingakopele anthu ena kubwela m’paradaiso wauzimu ni mwa kucita zinthu mwacikondi komanso mokoma mtima na alambili anzathu. Timafuna kuti acatsopano akapezeka pa misonkhano yathu, azimva mmene anamvela osakhulupilila omwe anapezeka pa msonkhano ku mpingo wa ku Korinto. Iwo anati: “Zoonadi Mulungu ali pakati panu.” (1 Akor. 14:24, 25; Zek. 8:23) Conco, tiyenela kupitiliza kutsatila ulangizi wakuti: “Muzikhala mwamtendele pakati panu.”—1 Ates. 5:13.
18. N’ciyani cingakope anthu kuti abwele m’gulu lathu?
18 Nthawi zonse tiziyesetsa kuona abale na alongo athu mmene Yehova amawaonela. Tingacite zimenezi mwa kuika maganizo athu pa makhalidwe awo abwino, m’malo mwa zophophonya zawo zimene zidzatha. Tizithetsa kusamvana kulikonse kumene kungakhalepo pakati pathu mwacikondi. Tingatelo ngati titsatila ulangizi wakuti: “Muzikomelana mtima, muzisonyezana cifundo cacikulu komanso muzikhululukilana ndi mtima wonse.” (Aef. 4:32) Zotsatila zake n’zakuti, anthu amene amafuna kuwacitila zinthu mwanjila imeneyi adzakopeka na paradaiso wauzimu. b
MUSACOKEMO M’PARADAISO WAUZIMU
19. (a) Malinga na bokosi lakuti “ Anabwelela Pambuyo Potulukamo,” kodi ena anati ciyani atabwelela m’paradaiso wauzimu? (b) Kodi tiyenela kutsimikiza mtima kucita ciyani? (Onaninso cithunzi.)
19 Ni mwayi waukulu zedi kukhala m’paradaiso wauzimu! Paradaiso ameneyu wakongola kwambili kuposa kale. Ndipo anthu amene akulambila Yehova mmenemo akuculukila-culukila kuposa kale lonse. Tiyeni tipitilize kuyamikila mwayi umene tili nawo wokhala m’paradaiso amene Yehova anatipangila. Aliyense amene akufuna kukhala wotsitsimulidwa, wokhutila, wabata, komanso wotetezeka, ayenela kuloŵa m’paradaiso wauzimu ndipo sayenela kucokamo. Komabe, tiyenela kusamala kwambili cifukwa Satana akucita zonse zotheka kuti atiopseze kuti ticoke m’paradaiso ameneyu. (1 Pet. 5:8; Chiv. 12:9) Tisamulole kuti apambane. Tiyeni ticite khama kuteteza paradaiso wathu wauzimu kuti apitilize kukhala wokongola, woyela, komanso wa mtendele.
KODI MUNGAYENKHE BWANJI?
-
Kodi paradaiso wauzimu n’ciyani?
-
Ni madalitso ati amene timalandila m’paradaiso wauzimu?
-
Tingakope bwanji ena kuti aloŵe m’paradaiso wauzimu?
NYIMBO 144 Yang’ana pa Mphoto!
a KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Mawu akuti “paradaiso wauzimu” amaimila mtendele komanso mgwilizano umene timasangalala nawo polambila Yehova. M’paradaiso wauzimu ameneyu, timasangalala kukhala paubale wabwino na Yehova komanso na anthu ena.
b Onelelani vidiyo pa jw.org yakuti Kodi Ali Kuti Tsopano? Alena Žitníková: Mmene Maloto Anga Anathekela, kuti muone madalitso amene mlongoyu analandila cifukwa cokhala m’paradaiso wauzimu.
c MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Pomwe abale na alongo akusangalala na maceza m’Nyumba ya Ufumu, m’bale wina wadzipatula.