Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 14

NYIMBO 56 Khulupilila Coonadi Iwe Mwini

“Tiyesetse Mwakhama Kuti Tikhale Okhwima Mwauzimu”

“Tiyesetse Mwakhama Kuti Tikhale Okhwima Mwauzimu”

Tiyeni tiyesetse mwakhama kuti tikhale okhwima mwauzimu.”AHEB. 6:1.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Phunzilani mmene Mkhristu wokhwima kuuzimu amaganizila na kucita zinthu mogwilizana na cifunilo ca Mulungu, komanso popanga zisankho zanzelu.

1. Kodi Yehova amayembekezela ciyani kwa ife?

 N’ZOCITIKA zocepa cabe zimene zimabweletsa cimwemwe cacikulu kwa okwatilana kuposa kubadwa kwa mwana wawo. Komabe, ngakhale kuti makolo amam’konda ngako mwana wawo wakhanda, samafuna kuti akhalebe khanda mpaka kale-kale. Ndipo amada nkhawa kwambili akaona kuti mwana wawo sakukula. Mofananamo, Yehova amakondwela ngako tikatenga masitepe kuti tikhale otsatila a Yesu. Koma safuna kuti tikhalebe makanda kuuzimu. (1 Akor. 3:1) M’malo mwake, iye amatipempha kuti ‘tikhale anthu akulu-akulu’ kuuzimu.—1 Akor. 14:20.

2. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

2 Kodi kukhala Mkhristu wokhwima kuuzimu kumatanthauza ciyani? Kodi tiyenela kucita ciyani kuti tikhale Akhristu okhwima? Kodi cakudya cotafuna cimatithandiza motani kukula mwauzimu? Nanga n’cifukwa ciyani tiyenela kupewa kudzidalila? M’nkhani ino, tikambilane mayankho a mafunso amenewa.

KODI KUKHALA MKHRISTU WOKHWIMA KUMATANTHAUZA CIYANI?

3. Kodi kukhala Mkhristu wokhwima kumatanthauza ciyani?

3 M’Baibo, liwu la Cigiriki limene linamasulidwa kuti “akulu-akulu” lingatanthauzenso “wokhwima,” komanso “wofikapo.” a (1 Akor. 2:6) Timakhala akulu-akulu kapena kuti Akhristu okhwima kuuzimu tikamakula kucoka pa kukhala makanda kuuzimu n’kukhala amuna kapena akazi aakulu kuuzimu. Ngakhale titakula kuuzimu, tiyenela kupitilizabe kukula. (1 Tim. 4:15) Tonsefe, kuphatikizapo acicepele, tingakhale Akhristu okhwima. Koma n’ciyani cimaonetsa kuti munthu wakhala Mkhristu wokhwima?

4. Kodi Mkhristu wokhwima tingamudziŵe bwanji?

4 Mkhristu wokhwima ni munthu amene amatsatila miyeso yonse ya Mulungu, ndipo sasankhapo imene ingamukomele. N’zoona kuti pokhala wopanda ungwilo angalakwitse zina zake. Komabe, amaonetsa kuti amayendela mfundo za Mulungu mwa zimene amaganiza na zocita zake za tsiku na tsiku. Anavala umunthu watsopano, ndipo amayesetsa mwamphamvu kuti maganizo ake agwilizane na maganizo a Mulungu. (Aef. 4:​22-24) Anadziphunzitsa kupanga zisankho zozikika m’malamulo, komanso mfundo za Yehova. Conco, safunikila mndandanda wa malamulo omuuza zocita. Akapanga cisankho amayesetsa kutsatila zimene wasankhazo.—1 Akor. 9:​26, 27.

5. N’ciyani cingacitikile Mkhristu wosakhwima mwauzimu? (Aefeso 4:​14, 15)

5 Kumbali ina, Mkhristu amene amakhalabe khanda mwauzimu angatengeke mosavuta na “zinthu zacinyengo” komanso mabodza amene ampatuko amaphunzitsa mocenjela. b (Ŵelengani Aefeso 4:​14, 15.) Iye angamacitile ena nsanje, kubweletsa mikangano, kukhumudwa msanga, kapena kugonja akayesedwa.—1 Akor. 3:3.

6. Kodi pali kufanana kotani pakati pa kukula mwauzimu na kukula mwakuthupi? (Onaninso cithunzi.)

6 Monga taonela kuciyambi, Malemba amayelekezela kukula kwauzimu na zimene zimacitika kuti munthu akule mwakuthupi. Mwana sadziŵa zambili. Conco, amafunika munthu wamkulu kumuteteza, komanso kumuyang’anila. Mayi angagwile dzanja mwana wake podutsa msewu. Pomwe mwanayo akusinkhuka, amayi ake angamamulole kudutsa yekha msewu. Koma angapitilize kumukumbutsa kuti aziyang’ana mbali zonse ziŵili asanadutse poopela ngozi. Mwanayo akakula angamapewe yekha ngozi za pa msewu zimenezi. Izi zionetsa kuti ana aang’ono amafunika thandizo la acikulile kuti apewe ngozi. Mofananamo, Akhristu osakhwima mwauzimu amafunika thandizo la Akhristu okhwima mwauzimu kuti apewe ngozi zauzimu, komanso kuti apange zisankho zanzelu. Mosiyana na zimenezi, Akhristu okhwima akafuna kupanga zisankho, amaseŵenzetsa mfundo za m’Baibo kuti adziŵe maganizo a Yehova na kuwatsatila.

Akhristu osakhwima ayenela kuphunzila kupanga zisankho zanzelu mwa kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo (Onani ndime 6)


7. Kodi Akhristu ofikapo mwauzimu amafunikila thandizo la ena?

7 Kodi izi zitanthauza kuti Mkhristu wokhwima safunikila thandizo la anthu ena? Ayi. Nthawi zina Akhristu okhwima nawonso angafunikile thandizo la anthu ena. Koma munthu wosakhwima amayembekezela ena kumuuza zocita, kapena kumupangila zisankho zimene iye mwini ayenela kupanga. Kumbali ina, Mkhristu wofikapo mwauzimu angapemphe nzelu kwa ena na kuona zokumana nazo za anthu ena na kudzipangila yekha cisankho podziŵa kuti Yehova amayembekezela aliyense “kunyamula katundu wake.”—Agal. 6:5.

8. Kodi Akhristu okhwima amasiyana motani?

8 Anthu okhwima mwakuthupi amasiyana m’maonekedwe. Mofananamo, nawonso Akhristu okhwima amasiyana m’makhalidwe awo. Angasiyane pa nzelu, kulimba mtima, kuwolowa manja, komanso mmene amaonetsela cifundo. Kuwonjezela apo, Akhristu okhwima angapange zisankho zosiyana pa nkhani imodzi, koma zovomelezeka mwa Malemba. Zimenezi zimacitika pa nkhani zimene zimafuna cikumbumtima. Kuzindikila zimenezi kumawathandiza kupewa kuweluzana pa nkhani zimene asiyana zisankho. M’malo mwake, iwo amaika maganizo awo pa zimene zingawathandize kuti akhalebe ogwilizana.—Aroma 14:10; 1 Akor. 1:10.

TINGATANI KUTI TIKHALE AKHRISTU OKHWIMA?

9. Kodi kukula mwauzimu kumacitika pakokha? Fotokozani.

9 Kukula mwakuthupi kumacitika mwacibadwa. Koma si mmene zimakhalila kuti munthu akhwime mwauzimu. Mwa citsanzo, abale na alongo ku Korinto analandila uthenga wabwino, anabatizika, analandila mzimu woyela, ndiponso anapindula na malangizo a Paulo. (Mac. 18:​8-11) Komabe, pambuyo pa zaka zambili cibatizikileni, ambili anakhalabe osakhwima. (1 Akor. 3:2) Kodi tingapewe bwanji zimenezi kuticitikila?

10. Kodi tiyenela kucita ciyani kuti tikhale okhwima mwauzimu? (Yuda 20)

10 Kuti tikhale okhwima, coyamba tiyenela kukulitsa cikhumbo cofuna kukhala Mkhristu wokhwima. Amene amafuna “kukhalabe osadziŵa zinthu” amasankha kukhalabe makanda, ndipo sapita patsogolo mwauzimu. (Miy. 1:22) Sitifuna kukhala ngati anthu aakulu mwakuthupi amene amapitiliza kudalila makolo awo kuwapangila zisankho. M’malo mwake, timasenza tokha udindo wodzidyetsa kuti tikule mwauzimu. (Ŵelengani Yuda 20.) Ngati mukuyesetsa kuti mukhale wokhwima, pemphelani kwa Yehova kuti akupatseni cikhumbo na mphamvu kuti mukwanitse kucita zimenezo.—Afil. 2:13.

11. Ni zinthu ziti zimene zingatithandize kufika pa ucikulile wauzimu? (Aefeso 4:11-13)

11 Yehova satiyembekezela kufika pa ucikulile wauzimu pa ife tokha. Amene amatumikila monga abusa komanso aphunzitsi mu mpingo wa Cikhristu, ni okonzeka kutithandiza. Iwo amatithandiza kufika “pa msinkhu wa munthu wamkulu” mwauzimu, “ngati mmene Khristu analili.” (Ŵelengani Aefeso 4:​11-13.) Yehova amapelekanso mzimu wake woyela potithandiza kuti tikhale na “maganizo a Khristu.” (1 Akor. 2:​14-16) Kuwonjezela apo, Mulungu anauzila anthu kulemba Mauthenga Abwino anayi, potionetsa mmene Yesu anali kuganizila komanso kucitila zinthu pamene anali kucita utumiki wake pa dziko lapansi. Mwa kutengela maganizo a Yesu na kacitidwe kake ka zinthu, tingakwanilitse colinga cathu cokhala Mkhristu wokhwima.

MMENE CAKUDYA COTAFUNA CIMATITHANDIZILA KUKULA KUUZIMU

12. Kodi “mfundo zoyambilila zokhudza Khristu” n’ciyani?

12 Kuti tifike pa ucikulile wauzimu tiyenela kucita zambili kuposa pa kuphunzila “mfundo zoyambilila zokhudza Khristu,” zomwe ni ziphunzitso zoyambilila za Cikhristu. Zitsanzo za ziphunzitso zoyambilila zimenezi ziphatikizapo kulapa, cikhulupililo, ubatizo, komanso ciukitso. (Aheb. 6:​1, 2) Izi ni zina mwa ziphunzitso zimene zimapanga maziko a Cikhristu. Pa cifukwa cimeneci, mtumwi Petulo anachula ziphunzitso zimenezi pophunzitsa khamu la anthu pa Pentekosite. (Mac. 2:​32-35, 38) Tiyenela kukhulupilila ziphunzitso zoyambilila zimenezi kuti tikhale ophunzila a Khristu. Mwa citsanzo, Paulo anacenjeza kuti aliyense wokana ciphunzitso ca ciukitso wakana ziphunzitso zonse za Cikhristu. (1 Akor. 15:​12-14) Komabe, sitiyenela kukhala okhutila podziŵa cabe ziphunzitso zoyambilila.

13. Kodi tingatani kuti tipindule na cakudya cotafuna cauzimu cochulidwa pa Aheberi 5:14? (Onaninso cithunzi.)

13 Mosiyana na ziphunzitso zoyambilila, cakudya cotafuna cauzimu cimaphatikizapo malamulo a Yehova, komanso mfundo zake. Izi zimatithandiza kumvetsa kaganizidwe ka Mulungu. Kuti tipindule na cakudya cimeneci, tiyenela kuŵelenga Mawu a Mulungu, kuwasinkhasinkha na kugwilitsa nchito zimene taŵelenga. Tikamacita zimenezi, timadziphunzitsa kupanga zisankho zokondweletsa Yehova. cŴelengani Aheberi 5:14.

Cakudya cauzimu cotafuna cimatiphunzitsa mmene tingapangile zisankho zimene zimakondweletsa Yehova (Onani ndime 13) d


14. Kodi Paulo anawathandiza bwanji Akorinto kufika pa ucikulile wauzimu?

14 Akhristu osakhwima mwauzimu cimawavuta kupanga zisankho zoyenela pa nkhani zimene palibe lamulo la m’Baibo loikika. Ena amaganiza kuti angacite zilizonse zimene afuna ngati palibe lamulo la m’Baibo, pamene ena amapempha anzawo kuti awauze zocita. Mwa citsanzo, Akhristu a ku Korinto anapempha Paulo kuti awaikile lamulo lowauza kuti ayenela kudya nyama yopelekedwa nsembe ku mafano kapena ayi. Paulo anadziŵa kuti nkhani zina zimafuna munthu kuseŵenzetsa cikumbumtima cake. Anadziŵanso kuti munthu aliyense ali na “ufulu” wodzipangila zisankho. Conco, anafotokoza mfundo zothandiza munthu kupanga zisankho zimene zingamusiye na cikumbumtima coyela, koma pa nthawi imodzi-modzi zimene sizingapunthwitse ena. (1 Akor. 8:​4, 7-9) Mwa kutelo, Paulo anathandiza Akorinto kukula mwauzimu kuti azitha kugwilitsa nchito mphamvu zawo za kuzindikila m’malo modalila munthu wina kuti awauze zocita.

15. Kodi Paulo anawathandiza bwanji Akhristu Aciheberi kupita patsogolo mwauzimu?

15 Titengapo phunzilo lofunika kwambili pa zimene Paulo analembela Aheberi. Ena a iwo analeka kukula mwauzimu; ndipo anafika ngakhale ‘poyambanso kufuna mkaka osati cakudya cotafuna.’ (Aheb. 5:12) Iwo analephela kutsatila mfundo za coonadi zimene zinali kuvumbulidwa mwapang’ono-pang’ono kupitila mu mpingo. (Miy. 4:18) Mwa citsanzo, Akhristu ambili aciyuda anali kulimbikitsabe ena kutsatila Cilamulo ca Mose ngakhale kuti panali patapita zaka 30 pamene Cilamuloco cinathetsedwa pa maziko a nsembe ya Khristu. (Aroma 10:4; Tito 1:10) Kunena zoona, zaka 30 zimene zinapitapo zinali zokwanila kwa Akhristuwo kuti asinthe maganizo awo pa nkhani ya Cilamulo. Aliyense amene anaŵelengapo kalata youzilidwa ya mtumwi Paulo yopita kwa Aheberi angatsimikize kuti buku limeneli lili na cakudya cauzimu cotafuna. Cakudyaco n’cimene Akhristuwo anali kufunikila kuti alimbikitse cikhulupililo cawo cakuti kalambilidwe ka Cikhristu ni kopambana kuposa ka m’Cilamulo. Cakudyaco cinawathandizanso kukhala olimba mtima kuti apitilize kulalikila mosasamala kanthu za zitsutso zocokela kwa Ayuda anzawo.—Aheb. 10:​19-23.

PEWANI KUDZIDALILA

16. Kuwonjezela pa kupita patsogolo kuti tifike pa ucikulile, n’ciyaninso cina cimene tiyenela kucita?

16 Tonsefe tiyenela kuyesetsa kufika pa ucikulile wauzimu, komanso kucita zonse zotheka kuti tipitilize kukhala wacikulile kuuzimu. Izi zingatheke ngati tipewa kudzidalila. (1 Akor. 10:12) Tiyenela ‘kupitiliza kudziyesa’ kuti tione ngati tikupita patsogolo mwauzimu.—2 Akor. 13:5.

17. Kodi kalata ya Paulo kwa Akolose, ionetsa motani kufunika kokhalabe wokhwima mwauzimu?

17 M’kalata imene Paulo analembela Akolose, anagogomeza kufunika kokhalabe wokhwima mwauzimu. Ngakhale kuti Akolose anali atakhala Akhristu okhwima, Paulo anawacenjeza kuti asagwele mu msampha wa kaganizidwe ka dziko. (Akol. 2:​6-10) Komanso Epafura, amene ayenela kuti anali kuwadziŵa bwino abale a mu mpingowo, anawapemphelela mosalekeza kuti ‘apitilize kukhala olimba mwauzimu’ kapena kuti okhwima. (Akol. 4:12) Mfundo yake ni yakuti onse aŵili, Paulo na Epafura, anadziŵa kuti kukhalabe wokhwima kumafuna kulimbikila, komanso thandizo la Mulungu. Iwo anali kufuna kuti Akolose akhalebe okhwima, kapena kuti afike pa ucikulile wauzimu mosasamala kanthu za mavuto amene anali kukumana nawo.

18. N’ciyani cingacitikile Mkhristu wokhwima ngati sanasamale? (Onaninso cithunzi.)

18 Paulo anacenjeza Aheberi kuti Mkhristu wokhwima angataye ciyanjo ca Mulungu ngati sanasamale. Mkhristu angakhale nkhutukumve pa malamulo a Mulungu, ndipo izi zingamulepheletse kulapa kuti Mulungu amukhululukile. N’zokondweletsa kuti Aheberi sanaipe kufika pamenepo. (Aheb. 6:​4-9) Nanga bwanji za amene amazilala kapena kucotsedwa mu mpingo masiku ano, koma kenako n’kulapa? Kulapa kwawo kumaonetsa kuti ni osiyana na anthu amene Paulo anachula. Akabwelela kwa Yehova, iwo amafunikila thandizo limene iye amapeleka. (Ezek. 34:​15, 16) Akulu angakonze zakuti Mboni ya cidziŵitso iwathandize kukonzanso ubale wawo na Mulungu.

Yehova amapatsa mphamvu anthu amene afunikila mphamvu mwauzimu (Onani ndime 18)


19. Kodi tiyenela kukhala na colinga cotani?

19 Ngati mukuyesetsa kukhala Mkhristu wokhwima, n’zotheka kukwanilitsa colinga canu. Pitilizani kudya cakudya cotafuna cauzimu, komanso kusintha maganizo anu kuti agwilizane na maganizo a Yehova. Ndipo ngati munafika kale pa ucikulile, pitilizani kucita zotheka kuti mukhalebe Mkhristu wokhwima.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi kukhala Mkhristu wokhwima kumatanthauza ciyani?

  • Tingacite ciyani kuti tikhale Akhristu okhwima?

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kupewa kudzidalila?

NYIMBO 65 Pita Patsogolo!

a M’Malemba a Ciheberi mulibe mawu akuti “wokhwima” komanso “wosakhwima,” koma muli mawu amene amapeleka lingalilo lofanana na mawu amenewa. Mwa citsanzo, buku la Miyambo limasiyanitsa mnyamata wosadziŵa zinthu na mnyamata wanzelu komanso wodziŵa zinthu.—Miy. 1:​4, 5.

b Onani nkhani yakuti “Samalani Kuti Musamapusitsike Ndi Nkhani Zabodza” pa mpambo wakuti “Nkhani Zina” pa jw.org mu Chichewa kapena mu JW Library.®

c Onani mbali yakuti “Zimene Mungacite pa Phunzilo la Inu mwini” mu kope ino ya magazini.

d MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale akuseŵenzetsa mfundo zimene waphunzila m’Mawu a Mulungu posankha zosangalatsa.