Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Zifooko Zanga Zaonetsa Mphamvu za Mulungu

Zifooko Zanga Zaonetsa Mphamvu za Mulungu

INE NA mkazi wanga titafika m’dziko la Colombia mu 1985, munali kucitika ciwawa coopsa. Boma inali kulimbana na magulu amphamvu ogulitsa amkolabongo m’mizinda, komanso asilikali oukila boma m’mapili. M’dela la Medellín, mmene pambuyo pake tinadzayamba kutumikila, munali magulu a acinyamata acifwamba onyamula zida. Anali kugulitsa amkolabongo, na kulipilitsa anthu ndalama kuti asawaphe. Anali kufika ngakhale pa kupha anthu cifukwa ca ndalama. Palibe ngakhale mmodzi amene anakhala na moyo kwa nthawi yaitali. Tinamva ngati tapita kumalo ena osati a pa dziko lapansi.

Kodi zinatheka bwanji kuti ife anthu wamba a ku Finland, dziko limene lili kumpoto kwambili kwa dziko la pansi, tipezeke ku South America? Ndipo kodi naphunzila ciyani m’zaka zonsezi?

NILI MWANA KU FINLAND

N’nabadwa mu 1955. Ndine wothela pa ana atatu aamuna. N’nakulila kum’mwela kwa dziko la Finland, pafupi na dela limene masiku ano limadziŵika kuti Vantaa.

Amayi anabatizika n’kukhala Mboni ya Yehova zaka zingapo ine nisanabadwe. Komabe, atate anali kucitsutsa kwambili coonadi, ndipo sanawalole amayi kuphunzila nafe, kapena kupita nafe ku misonkhano ya mpingo. Conco amayi anali kutiphunzitsa mfundo za coonadi zoyambilila za m’Baibo atate akacokapo.

N’naima zolimba kumbali ya Yehova nili na zaka 7

Kucokela nili mwana mpaka pano, nakhala nikuima zolimba kumbali ya Yehova. Mwa citsanzo, nili na zake 7, mphunzitsi wanga anakhumudwa nane zedi cifukwa n’nali kukana kudya cakudya cina cochedwa verilättyjä (makeke a ku Finland oikako magazi). Ananiyatsamitsa mwacikakamizo na dzanja limodzi atanyamula kekeyo kudzanja lina na foloko kuti aniike m’kamwa. Koma n’nakwanitsa kukankhila kumbali folokoyo ndipo inagwa pansi.

Nili na zaka 12, atate anamwalila. Conco, n’nayamba kupita kumisonkhano ya mpingo. Abale mu mpingo ananionetsa cikondi, ndipo izi zinanithandiza kupita patsogolo mwauzimu. N’nayamba kuŵelenga Baibo tsiku lililonse, komanso kuŵelenga zofalitsa zathu mwakhama. Zizoloŵezi zabwino zimenezi, zinanisonkhezela kubatizika nili na zaka 14, pa August 8, 1969.

Pasanapite nthawi yaitali n’tamaliza sukulu, n’nayamba upainiya wa nthawi zonse. Pambuyo pa milungu ingapo, n’napita kukatumikila kumalo osoŵa ku Pielavesi, dela lomwe lili capakati pa dziko la Finland.

Ku Pielavesi, n’kumene n’nakumana na Sirkka amene anakhala mkazi wanga wokondeka. N’nakopeka naye cifukwa ca kudzicepetsa kwake, komanso kukonda kwake zinthu zauzimu. Sanali kufuna kuchuka, kapena kufuna-funa umoyo wawofuwofu. Tonse aŵili tinali kufunitsitsa kutumikila Yehova mokwanila mmene tingathele, mosasamala kanthu za utumiki umene tingakhale nawo. Tinakwatilana pa March 23, 1974. M’malo mopita ku chuti ca okwatilana kumene, tinapita kukatumikila kudela la Karttula, kumene kunali kufunikila alaliki ambili a Ufumu.

Nyumba imene tinali kucita lendi mu mzinda wa Karttula ku Finland

YEHOVA ANATISAMALILA

Motoka imene mkulu wanga anatipatsa

Kungoyambila pomwe tinakwatilana, Yehova anationetsa kuti adzasamalila zofunikila zathu za kuthupi, tikaika Ufumu patsogolo. (Mat. 6:33) Mwa citsanzo, tili ku Karttula tinalibe motoka, tinali kugwilitsa nchito njinga. Koma m’nyengo yacisanu, kunali kuzizila koopsa. Kuti tikwanitse kulalikila gawo lalikulu la mpingowo, tinali kufunikila motoka. Koma tinalibe ndalama.

Mosayembekezela, mkulu wanga anabwela kudzationa. Anatipatsa motoka yake. Anali atalipila kale inshuwalansi. Tinali kungofunika kugulilamo mafuta. Conco, tinakhala na motoka imene tinali kufuna.

Yehova anatenga udindo wosamalila zosoŵa zathu za kuthupi. Tinali kungofunika kuika Ufumu patsogolo.

SUKULU YA GILIYADI

Tili pa sukulu ya apainiya mu 1978

Pomwe tinali ku Sukulu ya Apainiya mu 1978, m’bale Raimo Kuokkanen, a mmodzi wa alangizi athu anatilimbikitsa kufunsila Sukulu ya Giliyadi. Conco, tinayamba kuphunzila Cizungu na colinga cakuti tiyenelele sukulu imeneyi. Komabe, mu 1980 tisanafunsile sukuluyi tinaitanidwa kuti tikatumikile pa Beteli ya ku Finland. Pa nthawiyo, atumiki a pa Beteli sanali kuloledwa kufunsila Sukulu ya Giliyadi. Koma tinali kufuna kutumikila kumene Yehova aona kuti tingacite bwino, osati kumene ife tiona kuti tingacite bwino. Conco, tinapita kukatumikila ku Beteli. Ngakhale n’telo tinapitiliza kuphunzila Cizungu, kuti mwina tingadzakhale na mwayi wofunsila Sukulu ya Giliyadi.

Patapita zaka zingapo, Bungwe Lolamulila linalola kuti atumiki a pa Beteli nawonso azifunsila sukulu imeneyi. Nthawi yomweyo tinafunsila Sukulu ya Giliyadi, koma osati cifukwa cakuti sitinali kusangalala nawo utumiki wa pa Beteli, ayi. M’malo mwake, tinali kungofuna kudzipeleka kulikonse kumene kungafunikile thandizo ngati ndife oyenelela. Tinaitanidwa ku Giliyadi, ndipo tinacita nawo maphunzilo a kalasi ya namba 79 mu September 1985. Ndipo tinatumizidwa ku Colombia.

UTUMIKI WATHU WOYAMBA MONGA AMISHONALE

Utumiki wathu woyamba ku Colombia, unali wa pa Beteli. N’nali kuyesetsa kucita utumiki wanga mwakhama. Koma patapita caka cimodzi, n’naona kuti tiyenela kusintha utumiki. Iyi inali nthawi yanga yoyamba, komanso yokhayo imene n’napemphapo kusintha utumiki. Pambuyo pake tinatumizidwa monga amishonale a m’munda mu mzinda wa Neiva m’cigawo ca Huila.

Nthawi zonse nakhala ni kusangalala na nchito yolalikila. Nili ku Finland monga mpainiya wosakwatila, nthawi zina n’nali kulalikila kucoka m’mawa kwambili, mpaka m’madzulo kwambili. Titangokwatilana na Sirkka, tinalinso kulalikila kwa tsiku lonse. Tikapita kukalalikila ku magawo akutali, nthawi zina tinali kugona m’motoka yathu. Izi zinali kutithandiza kuti maŵa lake tilaŵilile ulaliki.

Titakhala amishonale a m’munda, tinakhalanso okangalika pa nchito yolalikila monga tinali kucitila poyamba. Mpingo wathu unakula, ndipo abale na alongo a ku Colombia anali acikondi, aulemu, komanso oyamikila.

MPHAMVU YA PEMPHELO

Pafupi na mzinda wa Neiva umene tinali kutumikilako, panali mizinda ina imene kunalibiletu Mboni. N’nali na nkhawa ya mmene uthenga wabwino ungafikile kumizinda imeneyi. Komabe, cifukwa ca asilikali oukila boma, madela amenewo anali oopsa kwa anthu amene sanali kukhala ku madelawo. Conco, n’nali kupemphela kuti munthu mmodzi wa ku madela amenewa akhale Mboni. N’nali kuganiza kuti munthuyo afunika kubwela ku Neiva kuti aphunzile coonadi. Conco, n’nali kupemphelanso kuti akabatizika, na kukula mwauzimu, akabwelele kwawo na kuyamba kulalikila kumeneko. Koma sin’nadziŵe kuti Yehova adzacitapo kanthu m’njila yabwino kuposa mmene n’nali kuganizila.

Papita nthawi, n’nayamba kuphunzila Baibo na mnyamata wina dzina lake Fernando González. Iye anali kukhala mu mzinda wa Algeciras. Uwu ni umodzi mwa mizinda kumene kunalibiletu Mboni. Fernando anali kuyenda makilomita opitilila 50 kubwela ku Neiva kudzagwila nchito. Anali kukonzekela mokwanila phunzilo lililonse. Ndipo pasanapite nthawi anayamba kupezeka pa misonkhano yonse ya mpingo. Kungoyambila pa zimene anaphunzila mu mlungu woyamba, Fernando anali kusonkhanitsa ena mwa anthu a m’dela lawo n’kuwaphunzitsa zimene waphunzila m’Baibo.

Nili na Fernando mu 1993

Fernando anabatizika mu January 1990, patangopita milungu 6 atayamba kuphunzila Baibo. Patapita nthawi, anayamba upainiya wa nthawi zonse. Cifukwa kunakhala Mboni imodzi ku mzinda wa Algeciras, zinakhala zotheka ofesi ya nthambi kutumiza apainiya apadela ku dela limeneli. Mu February 1992, mpingo unakhazikitsidwa m’delalo.

Kodi Fernando anali kulalikila m’dela lakwawo cabe? Ayi! Atakwatila, iye na mkazi wake anasamukila ku dela la San Vicente del Caguá, mzinda wina kumene kunalibe Mboni. Kumeneko, iwo anathandiza kukhazikitsa mpingo. Mu 2002, Fernando anaikidwa kukhala woyang’anila dela. Ndipo iye na mkazi wake Olga akutumikilabe m’dela mpaka pano.

Pa cocitika ici, n’naphunzilapo kufunika kochula mwacindunji zimene tifuna m’mapemphelo athu, zokhudza utumiki wathu. Yehova amacita zimene sitingakwanitse. Ndi iko komwe, nchitoyi ni yake, osati yathu.—Mat. 9:38.

YEHOVA AMATILIMBIKITSA NA KUTIPATSA MPHAMVU

Mu 1990 n’naikidwa kukhala woyang’anila dela. Dela lathu loyamba linali mu mzinda wa Bogotá, womwe ni likulu la Colombia. Tinali na nkhawa yakuti sitingakwanitse kucita utumiki umenewu. Ine na mkazi wanga ndife anthu wamba opanda maluso apadela alionse. Ndipo tinali tisanazoloŵele kukhala mu mzinda waukulu wokhalanso na anthu ambili. Komabe, Yehova anakwanilitsa lonjezo lake la pa Afilipi 2:13 yakuti: “Mulungu ndi amene amakulimbitsani. Amakupatsani mtima wofuna kucita zinthu zimene iye amakonda komanso mphamvu zocitila zinthuzo.”

Pambuyo pake, tinatumizidwa m’dela la Medellín, mzinda umene nachula kuciyambi. Anthu anali atazoloŵela ciwawa cimene cinali kucitika kumeneko, moti sizinalinso kuwacititsa mantha. Mwa citsanzo, tsiku lina nikutsogoza phunzilo m’nyumba ina, tinamva anthu akuwombelana mfuti pabwalo. N’nacita mantha moti n’natsala pang’ono kugwa pansi. Koma wophunzila wanga anapitiliza kuŵelenga ndime ali wodekha. Atatsiliza ananiuza kuti nimudikile pang’ono, ndipo anatuluka pabwalo. Patapita kanthawi, anabwelako na ana ake aŵili ndipo ananiuza kuti, “Pepani n’napita kukatenga ana angawa.”

Panalinso nthawi zina pamene miyoyo yathu inali kukhala pa ciopsezo. Nthawi ina, pamene tinali kucita ulaliki wa khomo na khomo, mkazi wanga anabwela akuthamanga kwa ine, ndipo anali kuoneka wa mantha kwambili. Ananiuza kuti munthu wina wamuwombela mfuti, koma waphonya. Izi zinanidetsa nkhawa kwambili. Koma pambuyo pake tinazindikila kuti munthuyo sanali kuwombela Sirkka. Koma anali kuwombela munthu wina amene anali kudutsa pafupi na Sirkka.

M’kupita kwa nthawi, tinaleka kucita nazo mantha za ciwawa zimenezi. Tinalimbikitsidwa na Mboni za kumeneko, zimene zinayang’anizanapo na mikhalidwe ngati imeneyi, komanso yoposa pamenepa. Tinali otsimikiza kuti ngati Yehova anawathandiza, nafenso adzatithandiza. Nthawi zonse tinali kutsatila malangizo ya akulu akumeneko, kucita zonse zotheka kuti tidziteteze, na kusiya zonse m’manja mwa Yehova.

Komabe, zocitika zina sizinali zoopsa mmene tinali kuziganizila. Tsiku lina pamene n’nali kulalikila pa nyumba ina, n’namva ngati azimayi aŵili akunyozana. Sin’nali kufuna kuonelela mkangano umenewo, koma mwini nyumba ananipempha kuti nipite naye pa khonde. Koma tinapeza kuti zomwe zinali kumveka ngati mkangano, sunali m’kangano wapakati pa anthu, koma zinali mbalame ziŵili zochedwa zinkhwe kapena kuti parrot, zimene zinali kuyeselela mawu a anthu apafupi.

MAUDINDO OWONJEZELA NA ZOVUTA ZAKE

Mu 1997, n’naikidwa kukhala mlangizi wa Sukulu Yophunzitsa Utumiki. b Nthawi zonse n’nali kusangalala kuloŵa masukulu aumulungu. Koma sin’naganizilepo kuti ningakhale na mwayi waukulu conci, wokhala mlangizi wa imodzi ya masukulu amenewa.

Pambuyo pake, n’natumikila monga woyang’anila cigawo. Makonzedwe amenewa atathetsedwa, n’nabwelela m’nchito ya dela. Nasangalala kutumikila monga mlangizi, komanso woyang’anila dela kwa zaka zoposa 30 tsopano. Mautumiki amenewa anibweletsela madalitso oculuka. Komabe, si nthawi zonse pamene zinthu zinali kuyenda bwino. Lekani nifotokoze.

Ndine munthu wolimba mtima. Izi zanithandiza kuthana na mikhalidwe yovuta mu umoyo wanga. Komabe, nthawi zina n’nali kucita zinthu mopupuluma pofuna kukonza zinthu mu mipingo. Pa nthawi ina, n’nadzudzulapo ena mwamphamvu kuti azikhala acikondi, komanso ololela pocita zinthu na ena. Koma mwa kutelo, n’nali kuonetsa kuti inenso nilibe makhalidwe amenewa.—Aroma 7:​21-23.

Nthawi zina zophophonya zanga zimanilefula kwambili. (Aroma 7:24) Pa nthawi ina n’nauzapo Yehova kuti zingakhale bwino n’tasiya utumiki wa umishonale na kubwelela kwathu ku Finland. Madzulo a tsikulo, n’napita ku msonkhano wa mpingo. Cilimbikitso cimene n’nalandila kumeneko, cinanithandiza kuona kuti niyenela kukhalabe mu utumiki wanga na kupitiliza kugwilila nchito pa zophophonya zanga. Mpaka pano, nimakhudzika na mmene Yehova anayankhila pemphelo langa. Kuwonjezela apo, nimayamikila kwambili kuona mmene Yehova ananithandizila mokoma mtima kugonjetsa zifooko zanga.

KUYANG’ANA KUTSOGOLO MWACIDALILO

Ine na mkazi wanga Sirkka ndife oyamikila kwambili kwa Yehova, potipatsa mwayi womutumikila mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zambili pa umoyo wathu. Niyamikilanso kwambili Yehova ponipatsa mkazi wacikondi komanso wokhulupilika amene nakhala naye kwa zaka zonsezi.

Posacedwa nikwanitsa zaka 70. Ndipo nizatula pansi utumiki wanga monga mlangizi, komanso woyang’anila dela. Komabe, sinidandaula nazo. Cifukwa ciyani? Cifukwa nimakhulupilila na mtima wonse kuti cofunika kwa mbili kwa Yehova na kum’tumikila modzicepetsa, komanso kum’tamanda na mtima wodzala na cikondi komanso ciyamikilo. (Mika 6:8; Maliko 12:​32-34) Kuti tikondweletse Yehova, sizidalila pa kukhala na utumiki wapadela ayi.

Nikayang’ana kumbuyo na kuganizila mautumiki amene nasangalala nawo, nimadziŵa kuti sin’nawalandile cifukwa cakuti n’nali woyenelela kwambili kuposa ena. Kapena cifukwa cakuti n’nali na luso lapadela. M’malo mwake, Yehova ananilola kucitako mautumiki amenewa cifukwa ca cisomo cake. Anatelo mosasamala kanthu za zifooko zanga. Nidziŵa kuti nakwanitsa kucitako mautumiki amenewa kokha na thandizo la Yehova. Mwa njila imeneyi, zifooko zanga zacititsa kuti mphamvu za Mulungu zionekele.—2 Akor. 12:9.

a Mbili ya m’bale Raimo Kuokkanen, inafotokozedwa mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 2006. Ndipo nkhaniyo ni ya mutu wakuti, “Ndife Otsimikiza Kutumikila Yehova.”

b Sukuluyi inaloŵedwa m’malo na Sukulu ya Alengezi a Ufumu.