NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA August 2019

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya September 30-October 27, 2019.

“Sitikubwelela M’mbuyo”!

Kodi ciyembekezo cathu cingatithandize bwanji kuti tisabwelele m’mbuyo?

Cikondi Canu Cipitilize Kukula

Kalata yopita kwa Afilipi imatithandiza kudziŵa mmene tingakulitsile cikondi pakati pathu, olo pamene tikukumana na mavuto.

‘Anthu Okumvelani’ Adzapulumuka

Kodi tingawathandize bwanji abululu athu kuphunzila za Yehova?

Zimene Zingakuthandizeni Ngati Utumiki Wanu Watha

Zimakhala zovuta kwa abale na alongo ambili ngati utumiki wawo umene anali kuukonda kwambili watha. N’ciani cingawathandize kujaila umoyo watsopano?

Cikhulupililo—Khalidwe Limene Limatithandiza Kukhala Olimba Mwauzimu

Cikhulupililo n’camphamvu kwambili. Ngati tili na cikhulupililo, tingapilile mavuto aakulu okhala ngati phili.

Yohane M’batizi—Citsanzo Cabwino pa Nkhani ya Kukhalabe Wacimwemwe

Tingacite ciani kuti tikhalebe acimwemwe potumikila Mulungu, ngakhale pamene takumana na zofooketsa?