Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 33

‘Anthu Okumvelani’ Adzapulumuka

‘Anthu Okumvelani’ Adzapulumuka

“Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umacita komanso zimene umaphunzitsa. Pitiliza kucita zimenezi, cifukwa ukatelo udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvela.”—1 TIM. 4:16.

NYIMBO 67 “Lalikila Mau”

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi tonsefe timafuna kuti abululu athu acite ciani?

MLONGO wina, dzina lake Pauline * anati: “Kungocokela pamene n’naphunzila coonadi, nakhala nikufunitsitsa kuti a m’banja langa onse nikakhale nawo m’Paradaiso. N’nali kufuna kuti maka-maka mwamuna wanga, Wayne, na mwana wathu wamwamuna ayambe kutumikila nane Yehova.” Kodi na imwe muli na acibululu amene sanayambe kutumikila Yehova? Ngati n’conco, ndiye kuti mofanana na mlongo Pauline, mumafuna kuti abululu anu ayambe kutumikila Yehova.

2. Ni mafunso ati amene tikambilane m’nkhani ino?

2 N’zoona kuti sitingakakamize abululu athu kulabadila uthenga wabwino. Komabe, tingawathandize kutsegula mtima na maganizo awo kuti alabadile uthenga wa m’Baibo. (2 Tim. 3:14, 15) N’cifukwa ciani tiyenela kuwalalikila abululu athu? N’cifukwa ciani tiyenela kucita nawo zinthu mowaganizila? Kodi tingawathandize bwanji kuyamba kukonda Yehova mmene ife timacitila? Nanga abale na alongo athu mu mpingo angatithandize bwanji?

N’CIFUKWA CIANI TIYENELA KUWALALIKILA ABULULU ATHU?

3. Mogwilizana na 2 Petulo 3:9, n’cifukwa ciani tiyenela kuwalalikila abululu athu?

3 Posacedwa, Yehova adzawononga dziko loipali. Ndipo anthu okhawo amene ali na ‘maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha’ ndiwo adzapulumuka. (Mac. 13:48) Timathela nthawi yoculuka na mphamvu zathu polalikila anthu osawadziŵa a m’dela lathu. Conco, m’pomveka kuti timafuna kuti nawonso abululu athu ayambe kutumikila Yehova limodzi nafe. Atate wathu wacikondi, Yehova, “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.”—Ŵelengani 2 Petulo 3:9.

4. N’ciani cosayenela cimene tingacite pamene tilalikila abululu athu?

4 Tifunika kukumbukila kuti pali njila yoyenela komanso yosayenela youzila ena uthenga wa cipulumutso. Mwacitsanzo, polalikila anthu amene sitiwadziŵa, timayesetsa kukamba nawo mokoma mtima kuti tisawakhumudwitse. Koma polalikila abululu athu, n’capafupi kukamba nawo mosawaganizila.

5. Kodi tiyenela kukumbukila ciani tikafuna kuuzako abululu athu coonadi?

5 Ambili a ife tikaganizila mmene tinakambila na abululu athu pa nthawi yoyamba imene tinawalalikila, timaona kuti sitinacite bwino. Timaona kuti tikanacita bwino kukamba nawo mokoma mtima. Mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti: “Nthawi zonse mawu anu azikhala acisomo, okoma ngati kuti mwawathila mcele, kuti mudziwe mmene mungayankhile wina aliyense.” (Akol. 4:5, 6) Ni bwino kukumbukila malangizo amenewa pamene tikamba na abululu athu. Apo ayi, zokamba zathu zingawakhumudwitse m’malo mowakopa kuti amvetsele uthenga wabwino.

TINGAWATHANDIZE BWANJI ABULULU ATHU?

Khalidwe lanu labwino lingapeleke umboni wamphamvu (Onani ndime 6-8) *

6-7. Fotokozani citsanzo coonetsa mmene Mkhristu angacitile zinthu mom’ganizila mwamuna kapena mkazi wake amene si Mboni.

6 Muzicita zinthu mowaganizila. Mlongo Pauline, amene tam’chula kuciyambi, anati: “Poyamba, n’nali kufuna kuti tizikamba nkhani zauzimu zokha-zokha na amuna anga. Sin’nali kukambako nawo nkhani zina.” Koma mwamuna wa mlongoyu sanali kudziŵa zambili za Baibo, ndiponso sanali kumvetsetsa zimene mkazi wake anali kukamba. Mwamunayo anali kuona kuti mkazi wake anali kungoganizila za cipembedzo cake basi. Ndipo anadela nkhawa poganiza kuti iye wayamba kugwilizana na kagulu koopsa kampatuko, komanso kuti akunamizidwa.

7 Mlongo Pauline anafotokoza kuti ku madzulo komanso ku mapeto kwa wiki, anali kuthela nthawi yoculuka ali limodzi na abale na alongo ake auzimu ku misonkhano, mu ulaliki, na ku maceza. Iye anati: “Nthawi zina, amuna anga, a Wayne, akafika pa nyumba, anali kupeza kuti palibe anthu, ndipo anali kukhala wosungulumwa.” N’zosacita kufunsa kuti mwamuna wa mlongoyu anali kumuyewa mkazi wake na mwana wawo. Iye sanali kudziŵa kuti iwo anali kukhala ndi anthu otani. Ndipo anali kuona kuti mkazi wakeyo samuganizila, koma amaona anthu amenewo kukhala ofunika kuposa iye. Mwamunayo anaopseza mlongo Pauline kuti adzamusudzula. Kodi muganiza kuti mlongoyu akanacita ciani kuti aonetse kuti anali kum’ganizila mwamuna wake?

8. Malinga na 1 Petulo 3:1, 2, n’ciani cingawakhudze kwambili abululu athu?

8 Khalidwe lanu lizikucitilani umboni. Kaŵili-kaŵili, zimene timacita n’zimene zimakhudza kwambili abululu athu, kuposa zimene timakamba. (Ŵelengani 1 Petulo 3:1, 2.) M’kupita kwa nthawi, mlongo Pauline anazindikila mfundo imeneyi. Iye anati: “N’nali kudziŵa kuti amuna anga amatikonda, ndipo sanali kufunadi kunisudzula. Koma pamene ananiwopseza kuti adzanisudzula, n’nazindikila kuti nifunika kuyamba kucita zinthu mogwilizana na mfundo za Yehova. N’naona kuti nifunika kuonetsa citsanzo cabwino mwa zocita zanga, m’malo mokamba nawo kwambili zinthu zauzimu.” Mlongoyu analeka kuwakambitsa-kambitsa za Baibo amuna ake. M’malomwake, anayamba kukamba nawo nkhani zina. A Wayne anaona kuti mkazi wawo wayamba kucita nawo zinthu mowaganizila. Anaonanso kuti mwana wawo wayamba kuwalemekeza na kuwamvela kwambili. (Miy. 31:18, 27, 28) A Wayne ataona mmene Mawu a Mulungu anathandizila a m’banja lawo kusintha umunthu wawo, anayamba kucita cidwi na uthenga wa m’Baibo.—1 Akor. 7:12-14, 16.

9. N’cifukwa ciani tifunika kupitiliza kuthandiza abululu athu mwauzimu?

9 Pitilizani kuwathandiza abululu anu. Yehova ndiye citsanzo cabwino pa nkhani yothandiza anthu mwauzimu. “Mobwelezabweleza,” iye amapatsa anthu mwayi wolabadila uthenga wabwino kuti akapeze moyo. (2 Mbiri 36:15) Ndipo mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti apitilize kuthandiza anthu ena. Cifukwa ciani? Anamuuza kuti mwa kucita zimenezo, adzadzipulumutsa yekha komanso anthu omumvela. (1 Tim. 4:16) Popeza kuti timawakonda abululu athu, timafuna kuti nawonso adziŵe coonadi ca m’Mawu a Mulungu. Patapita nthawi, zokamba na zocita za mlongo Pauline zinathandiza kwambili a m’banja lake. Tsopano, iye ni wokondwa kutumikila Yehova pamodzi na mwamuna wake. Onse aŵili ni apainiya, ndipo a Wayne atumikila monga mkulu.

10. N’cifukwa ciani tiyenela kukhala oleza mtima?

10 Khalani oleza mtima. Tikayamba kutsatila mfundo za Mulungu, timasintha umoyo wathu komanso zimene timakhulupilila. Zingakhale zovuta kwa abululu athu kumvetsetsa cifukwa cake tapanga masinthidwe amenewa. Nthawi zambili, cinthu coyamba cimene amadabwa naco n’kuona kuti taleka kucita nawo zikondwelelo zacipembedzo, kapena kutengako mbali m’zandale. Ena mwa iwo angakhumudwe na zimenezi. (Mat. 10:35, 36) Koma sitiyenela kuleka kuwathandiza kumvetsetsa zimene timakhulupilila. Tikaleka, ndiye kuti tawaweluza kuti ni osayenelela kukapeza moyo wosatha. Koma Yehova sanatipatse udindo woweluza ena. Anapatsa Yesu udindo umenewu. (Yoh. 5:22) Tikakhala oleza mtima, m’kupita kwa nthawi abululu athu angayambe kumvetsela uthenga wathu.—Onani bokosi yakuti “ Phunzitsani mwa Kuseŵenzetsa Webusaiti Yathu.”

11-13. Kodi mwaphunzilapo ciani pa citsanzo ca Alice ca mmene anacitila zinthu na makolo ake?

11 Khalani okoma mtima, koma musasunthike. (Miy. 15:2) Ganizilani citsanzo ca Alice. Pa nthawi imene anaphunzila za Yehova, anali kukhala ku dziko lina. Makolo ake anali osakhulupilila Mulungu komanso okonda zandale. Atayamba kuphunzila, Alice anazindikila kuti afunika kufotokozela makolo ake mwamsanga zinthu zabwino zimene anali kuphunzila. Iye anati: “Ukazengeleza kuuzako a m’banja lako zimene wayamba kukhulupilila na kucita, pa nthawi imene ukawauze, iwo angakhumudwe kwambili.” Iye anali kulembela makolo ake makalata, pofuna kudziŵa maganizo awo pa ziphunzitso za m’Baibo. Anasankha nkhani zimene iwo akanacita nazo cidwi, monga ya cikondi. (1 Akor. 13:1-13) Iye anayamikila makolo ake cifukwa comulela bwino, ndipo anawatumizila mphatso. Akapita kukawaona, anali kuyesetsa kuthandiza amayi ake pa nchito za pa khomo. Poyamba, makolowo sanakondwele pamene Alice anawauza za cikhulupililo cake catsopano.

12 Pamene Alice anali ku nyumba kwa makolo ake, anapitilizabe kuŵelenga Baibo tsiku lililonse. Iye anati: “Kucita izi kunathandiza amayi kudziŵa kuti nimaona Baibo kukhala yofunika kwambili.” Pa nthawiyi, atate ake anayamba kuŵelenga Baibo n’colinga cakuti adziŵe cifukwa cake mwana wawo anali atasintha cikhulupililo cake. Cinanso, anafuna kuipeza zifukwa Baibo. Alice anati: “N’nawapatsa Baibo, ndipo n’nalembamo mfundo zocepa zogwila mtima.” Kodi panakhala zotulukapo zotani? Iwo sanapezemo zolakwika zilizonse m’Baibo. M’malomwake, zimene anaŵelengazo zinawafika pa mtima.

13 Tiyenela kukhala okoma mtima ndi osasunthika ngakhale pamene takumana na mayeselo. (1 Akor. 4:12b) Mwacitsanzo, Alice anali kutsutsidwa na amayi ake. Iye anati: “Pamene n’nabatizika, amayi ananinena kuti ndine ‘mwana woipa.’” Kodi Alice anacita ciani? Iye anati: “Sin’naleke kukamba nawo za cikhulupililo canga catsopano, koma mwaulemu n’nawafotokozela kuti nasankha kukhala Mboni ya Yehova, ndipo sinidzasintha maganizo anga. N’nawatsimikizila amayi kuti nimawakonda kwambili. Tonse tinalila, ndipo pambuyo pake ninawaphikila cakudya cokoma. Kucokela nthawiyo, amayi anayamba kuona kuti zimene n’nali kuphunzila m’Baibo zinali kunithandiza kukhala munthu wabwino.”

14. N’cifukwa ciani sitiyenela kugonja ngati ena atikakamiza kuleka kutumikila Yehova?

14 Timaona kulambila Yehova kukhala cinthu cofunika kwambili mu umoyo wathu. Koma zingatenge nthawi kuti abululu athu afike poimvetsetsa mfundo imeneyi. Mwacitsanzo, pamene Alice anaganiza zoyamba upainiya, m’malo mokacita maphunzilo kuti akaloŵe nchito imene makolo ake anali kufuna, amayi ake anakhumudwa kwambili mpaka analila. Koma Alice sanasinthe maganizo ake. Iye anati: “Ukagonja pa mbali imodzi, abululu ako amayambanso kukukakamiza kusintha maganizo pa mbali zina. Koma ngati ucita nawo zinthu mokoma mtima popanda kusintha maganizo ako, ena mwa iwo angamvetsele zimene uwauza.” Umu ni mmene zinakhalila kwa makolo ake. Onse lomba ni apainiya, ndipo atate ake ni mkulu.

KODI ABALE NA ALONGO MU MPINGO ANGATHANDIZE BWANJI?

Kodi mpingo ungawathandize bwanji abululu athu amene si Mboni? (Onani ndime 15-16) *

15. Malinga na Mateyu 5:14-16 komanso 1 Petulo 2:12, kodi ‘nchito zabwino’ za ena mu mpingo zingathandize bwanji abululu athu?

15 Yehova amakokela anthu kwa iye kupitila mu ‘nchito zabwino’ za abale na alongo mu mpingo. (Ŵelengani Mateyu 5:14-16; 1 Petulo 2:12.) Ngati mwamuna kapena mkazi wanu si Mboni ya Yehova, kodi anaonanapo na abale na alongo a mu mpingo wanu? Mlongo Pauline, amene tam’tomolapo kale m’nkhani ino, anaitanila abale na alongo ku nyumba kwawo, n’colinga cakuti amuna ake, a Wayne, awadziŵe. A Wayne anafotokoza mmene m’bale wina anawathandizila kudziŵa bwino Mboni za Yehova. Iwo anati: “Iye anapempha chuti ca tsiku limodzi ku nchito, n’colinga cakuti abwele kukatamba nane gemu ina yake. Mu mtima n’nati, ‘Ndiye kuti ni munthu wabwino-bwino.’”

16. N’cifukwa ciani abululu athu tiyenela kuwaitanila ku misonkhano?

16 Njila ina yabwino kwambili yothandizila abululu athu kuphunzila coonadi ni kuwaitanila ku misonkhano ya mpingo. (1 Akor. 14:24, 25) Msonkhano woyamba umene a Wayne anapezekapo unali wa Cikumbutso. Iwo anakwanitsa kupezekapo cifukwa unacitika madzulo atakomboka ku nchito, ndipo sunatenge nthawi yaitali. Iwo anati: “Sin’namvetsetse nkhani imene inakambidwa pa msonkhanowo, koma cimene cinanicititsa cidwi kwambili ni anthu. Ananilandila na manja aŵili na kunipatsa moni wotentha wa kumanja. N’naona kuti anali anthu abwino.” Pa nthawiyi, n’kuti m’bale wina na mkazi wake atayamba kale kucita zinthu mokoma mtima kwambili kwa mlongo Pauline. Anali kum’thandiza kusamalila mwana wake pa misonkhano na mu ulaliki. Conco, pamene a Wayne anaganiza zoyamba kuphunzila kuti adziŵe bwino zimene akazi awo anali kukhulupilila, anapempha mwamuna wa banja lija kuti ayambe kuphunzila nawo Baibo.

17. Kodi sitiyenela kudziimba mlandu pa nkhani iti? Nanga n’cifukwa ciani sitifunika kuleka kuthandiza abululu athu?

17 Timalaka-laka kuti abululu athu onse ayambe kutumikila nafe Yehova. Koma nthawi zina, olo titayesetsa bwanji kuwathandiza, sangabwele m’coonadi. Zikakhala conco, sitiyenela kudziimba mlandu cifukwa ni cosankha cawo. Ndi iko komwe, sitingakakamize munthu kukhulupilila zimene timaphunzila. Komabe, abululu athu angakhudzidwe kwambili akaona cimwemwe cimene tili naco potumikila Yehova. Conco, muziwapemphelela. Muzikamba nawo mowaganizila. Ndiponso musaleke kuwathandiza! (Mac. 20:20) Khalani na cikhulupililo cakuti Yehova adzadalitsa khama lanu. Ndipo ngati abululu anu asankha kukumvelani, adzapulumuka!

NYIMBO 57 Tilalikile kwa Anthu a Makhalidwe Onse

^ ndime 5 Tonse timafuna kuti abululu athu adziŵe Yehova. Koma iwo ali na ufulu wosankha kutumikila Yehova kapena ayi. M’nkhani ino, tikambilane zimene tingacite kuti cikhale cosavuta kwa abululu athu kumvetsela uthenga wathu.

^ ndime 1 Maina ena asinthidwa. M’nkhani ino, mawu akuti “abululu” kapena “acibululu” atanthauza abale athu amene si Mboni.

^ ndime 53 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale wacinyamata akuthandiza atate ake amene si Mboni kukonza motoka. Pa nthawi yoyenelela, iye akuwatambitsa vidiyo ya pa jw.org®.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo amvetsela mwachelu pamene mwamuna wake amene si Mboni, akufotokoza mmene nchito yayendela pa tsikulo. Pambuyo pake, akucita maseŵela ena ake pamodzi na banja lake.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo waitanila abale na alongo ku nyumba kwawo. Iwo akuyesetsa kum’dziŵa bwino mwamuna wake. Patapita nthawi, mwamunayo wapezeka ku Cikumbutso pamodzi na mkazi wake.