Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 32

Cikondi Canu Cipitilize Kukula

Cikondi Canu Cipitilize Kukula

“Ine ndikupitiliza kupemphela kuti cikondi canu cipitilile kukula.”—AFIL. 1:9.

NYIMBO 106 Kukulitsa Mkhalidwe wa Cikondi

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’ndani anathandiza kukhazikitsa mpingo ku Filipi?

PAMENE mtumwi Paulo, Sila, Luka, na Timoteyo anafika mu mzinda wolamulidwa na Aroma wa Filipi, anapeza anthu ambili a cidwi na uthenga wa Ufumu. Abale anayi okangalika amenewa anathandiza kukhazikitsa mpingo mu mzindawo, moti ophunzila onse a kumeneku anayamba kusonkhana pamodzi, mwina ku nyumba kwa Lidiya, mlongo wokonda kuceleza alendo.—Mac. 16:40.

2. Kodi mpingowo unakumana na mavuto otani utangokhazikitsidwa?

2 Posakhalitsa, mpingo watsopanowo unayamba kukumana na mavuto. Satana anasonkhezela adani a coonadi kuyamba kutsutsa mwamphamvu nchito yolalikila imene Akhristu okhulupilika amenewo anali kucita. Paulo na Sila anagwidwa, kukwapulidwa na zikoti, komanso kuponyedwa m’ndende. Atawatulutsa m’ndendemo, anapita kukaona ophunzila atsopano na kukawalimbikitsa. Kenako, Paulo, Sila, na Timoteyo anacoka mu mzindawo, koma zioneka kuti Luka anatsala. Kodi Akhristu acatsopanowo anacita ciani? Mwa thandizo la Yehova, anapitiliza kutumikila Mulungu mokangalika. (Afil. 2:12) Conco, Paulo anali na cifukwa comveka cokhalila onyadila.

3. Malinga n’zimene Afilipi 1:9-11 imakamba, ni zinthu ziti zimene Paulo anapempha m’pemphelo lake?

3 Zaka pafupi-fupi 10 pambuyo pake, Paulo analembela kalata Akhristu a ku Filipi. Pamene tiŵelenga kalatayi, n’zosavuta kuona kuti Paulo anali kuwakonda kwambili abale ake. Iye analemba kuti: “Ndikufunitsitsa nditakuonani ndi cikondi cacikulu ngati cimene Khristu Yesu ali naco.” (Afil. 1:8) Iye analembanso kuti anali kuwapemphelela abalewo. Paulo anapempha Yehova kuti awathandize kukulitsa cikondi pakati pawo, kutsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ni ziti, kukhala opanda colakwa, kupewa kupunthwitsa ena, ndiponso kupitiliza kubala zipatso zolungama. N’zacidziŵikile kuti na ise masiku ano tingapindule kwambili na malangizo a Paulo ocokela pansi mtima amenewa. (Ŵelengani Afilipi 1:9-11.) M’nkhani ino, tikambilane malangizo amene iye analemba, na mmene tingawaseŵenzetsele.

CIKONDI CANU CIKULE

4. (a) Mogwilizana na 1 Yohane 4:9, 10, kodi Yehova anaonetsa bwanji cikondi cake kwa ife? (b) Kodi cikondi cathu pa Mulungu ciyenela kukhala cacikulu bwanji?

4 Yehova anaonetsa cikondi cake cacikulu kwa ife mwa kutumiza Mwana wake pa dziko lapansi kuti adzafe kaamba ka macimo athu. (Ŵelengani 1 Yohane 4:9, 10.) Cikondi codzimana ca Mulungu cimatilimbikitsa kum’konda. (Aroma 5:8) Kodi cikondi cathu pa Mulungu ciyenela kukhala cacikulu bwanji? Yesu anayankha funsoli pamene anauza Mfarisi kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” (Mat. 22:36, 37) Inde, timafuna kukonda Mulungu na mtima wathu wonse. Ndipo timafuna kuti cikondi cathu pa iye cizikulila-kulila. Paulo analangiza Afilipi kuti “cikondi [cawo] cipitilile kukula.” Kodi tingacite ciani kuti tikulitse cikondi cathu pa Mulungu?

5. Kodi tingakulitse bwanji cikondi cathu pa Mulungu?

5 Kuti tiyambe kukonda Mulungu, tifunika kumudziŵa. Baibo imati: “Munthu wopanda cikondi sadziwa Mulungu, cifukwa Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yoh. 4:8) Mtumwi Paulo anaonetsa kuti cikondi cathu pa Mulungu cimakula pamene tidziŵa coonadi ponena za iye, na kumvetsetsa mmene amaonela zinthu. (Afil. 1:9) Titayamba kuphunzila Baibo, tinayamba kum’konda Mulungu, olo kuti tinali tisanadziŵe zambili zokhudza makhalidwe ake abwino. Ndipo pamene tinapitiliza kuphunzila zambili za Yehova, cikondi cathu pa iye cinapitiliza kukula. Ndiye cifukwa cake timaona kuti kuŵelenga Baibo nthawi zonse na kusinkha-sinkha n’kofunika kwambili mu umoyo wathu.—Afil. 2:16.

6. Kodi pa 1 Yohane 4:11, 20, 21 tiphunzilapo ciani pa nkhani ya kukulitsa cikondi?

6 Kukumbukila cikondi cacikulu cimene Mulungu anationetsa, kumatilimbikitsa kukonda abale athu. (Ŵelengani 1 Yohane 4:11, 20, 21.) Mwina timaganiza kuti n’zosavuta kukonda abale na alongo athu. Tingakhale na maganizo amenewa cifukwa cakuti tonse timalambila Yehova, ndipo timayesetsa kutengela makhalidwe ake abwino. Kuwonjezela apo, tonse timatengela citsanzo ca Yesu, amene anafika mpaka potifela cifukwa cotikonda kwambili. Ngakhale n’conco, nthawi zina zingakhale zovuta kumvela lamulo lakuti tiyenela kukonda abale na alongo athu. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitika mu mpingo wa ku Filipi.

7. Tiphunzilapo ciani pa malangizo amene Paulo anapeleka kwa Eodiya na Suntuke?

7 Eodiya na Suntuke anali alongo okangalika, amene anatumikila “limodzi” na mtumwi Paulo. Koma zioneka kuti iwo analola kusiyana maganizo kusokoneza ubwenzi wawo. Conco, m’kalata imene Paulo analembela mpingo wawo, anachula maina awo mwacindunji, ndipo anawalangiza mosapita m’mbali kuti anayenela ‘kukhala amaganizo amodzi.’ (Afil. 4:2, 3) Paulo anaona kuti kunali kofunikila kupeleka malangizo ku mpingo wonse. Iye anati: “Muzicita zinthu zonse popanda kung’ung’udza ndi kutsutsana.” (Afil. 2:14) Mwacionekele, malangizo osapita m’mbali a Paulo anathandiza alongo okhulupilika amenewa, ndiponso mpingo wonse, kulimbitsa cikondi pakati pawo.

N’cifukwa ciani tifunika kupitiliza kuwaona moyenela abale athu? (Onani ndime 8) *

8. Kodi vuto lalikulu limene lingatilepheletse kukonda abale athu ni liti? Nanga tingalithetse bwanji?

8 Vuto limodzi lalikulu limene lingatilepheletse kukulitsa cikondi pa ena ni kukonda kusumika maganizo athu pa zophophonya zawo. Ili ndilo vuto limene Eodiya na Suntuke anali nalo. Koma tisaiŵale kuti tonse timalakwitsa zinthu zina tsiku lililonse. Ngati tiyang’ana kwambili pa zolakwa za ena, cikondi cathu pa iwo cimacepa. Mwacitsanzo, m’bale kapena mlongo akaiŵala kutithandiza kuyeletsa m’Nyumba ya Ufumu, tingakhumudwe. Ndipo tikayamba kuganizila zinthu zina zambili zimene Mkhristuyo analakwitsapo kumbuyoku, tingakhumudwe kwambili ndipo cikondi cathu pa iye cingacepe. Ngati zaconco zakucitikilani, mungacite bwino kukumbukila mfundo iyi: Yehova amaona zophophonya zathu komanso za Mkhristu mnzathuyo. Ngakhale n’telo, iye amatikonda tonse. Pa cifukwa ici, tifunika kutengela cikondi ca Yehova na kuyesetsa kuyang’ana pa makhalidwe abwino amene abale athu ali nawo. Ngati tiyesetsa kukonda abale athu, mgwilizano wathu na iwo umalimba.—Afil. 2:1, 2.

“ZINTHU ZOFUNIKA KWAMBILI”

9. Kodi zina mwa “zinthu zofunika kwambili” zimene Paulo anachula m’kalata imene analembela Afilipi ni ziti?

9 Mouzilidwa na mzimu woyela, Paulo analangiza Akhristu a ku Filipi na ife tonse, kuti tiyenela ‘kutsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ni ziti.’ (Afil. 1:10) Zinthu zofunika kwambili zimenezi ziphatikizapo kuyeletsedwa kwa dzina la Yehova, kukwanilitsidwa kwa colinga cake, komanso mtendele na mgwilizano wa mu mpingo. (Mat. 6:9, 10; Yoh. 13:35) Ngati timaona zinthu zimenezi kukhala zofunika kwambili mu umoyo wathu, ndiye kuti timakonda Yehova.

10. N’ciani cimene tifunika kucita kuti Yehova azitiona kuti ndife opanda colakwa?

10 Paulo anakambanso kuti tifunika ‘kukhala opanda colakwa.’ Izi sizitanthauza kuti tifunika kukhala angwilo. Sitingathe kukhala osalakwa monga mmene Yehova Mulungu alili. Komabe, Yehova amationa kuti ndife opanda colakwa ngati ticita zonse zimene tingathe polimbitsa cikondi cathu, ndiponso ngati tiika patsogolo zinthu zofunika kwambili. Njila imodzi imene timaonetsela cikondi cathu ni mwa kuyesetsa kupewa kupunthwitsa ena.

11. N’cifukwa ciani tifunika kupewa kupunthwitsa ena?

11 Uphungu wakuti tifunika kupewa kupunthwitsa ena sitiyenela kuuona mopepuka. Kodi tingawapunthwitse bwanji anthu ena? Tingawapunthwitse mwa zosankha zathu pa zosangalatsa, zovala, ngakhale nchito. Zimene tingacite zingakhale kuti zilibe vuto. Koma bwanji ngati zimene ticitazo zikuvutitsa cikumbumtima ca wina, ndipo iye wapunthwa? Imeneyo ni nkhani yaikulu kwambili. Yesu anakamba kuti kwa munthu wopunthwitsa nkhosa ya Mulungu, cingam’khalileko bwino kum’mangilila cimwala cacikulu m’khosi mwake na kumuponya m’nyanja.—Mat. 18:6.

12. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca banja lina la apainiya?

12 Onani mmene m’bale wina na mkazi wake, amene ni apainiya, analabadilila cenjezo la Yesu limeneli. Mu mpingo umene anali kutumikila, munali m’bale wina na mkazi wake, amene anali acatsopano m’coonadi. Iwo anakulila m’mabanja oumitsa zinthu kwambili, cakuti zinthu zambili anali kuwaletsa kucita. Banja lacatsopano m’coonadi limenelo linali kukhulupilila kuti Akhristu sayenela kutamba mafilimu, ngakhale abwino-bwino. Iwo anakhumudwa kwambili atamvela kuti banja la apainiya lija linatamba filimu. Banja la apainiyalo litamvela zimenezi, linaleka kupita kukatamba mafilimu, mpaka pamene banja la Akhristu acatsopanowo linaphunzitsa zikumbumtima zawo kusiyanitsa bwino coyenela na cosayenela. (Aheb. 5:14) Mwa kucita izi, banja la apainiyalo linaonetsa kuti linali kukonda Akhristu acatsopanowo mwa zocita, osati m’mawu cabe.—Aroma 14:19-21; 1 Yoh. 3:18.

13. Kodi tingapangitse bwanji munthu kugwela m’chimo?

13 Tingapunthwitsenso munthu mwa kum’sonkhezela kucita zinthu zimene zingamugwetsele m’chimo. Kodi izi zingacitike bwanji? Cabwino, tiyelekezele kuti pali wophunzila Baibo amene ali na vuto la ucakolwa. Pambuyo polimbana na vutoli kwa nthawi yaitali, iye wakwanitsa kuligonjetsa. Ndipo wazindikila kuti cofunika kuti vutoli lisakayambenso ni kupewelatu kumwa moŵa. Iye akupita patsogolo mofulumila, ndipo akubatizika. Patapita nthawi, tsiku lina m’bale akumuitanila ku phwando na kumupatsa moŵa, amvekele: “Ndiwe Mboni lomba. Uli na mzimu wa Yehova. Ndipo limodzi mwa makhalidwe amene mzimu woyela umabala ni kudziletsa. Conco, ngati ndiwe wodziletsa, ungathe kumwako pang’ono popanda vuto lililonse.” Kodi mwaona ngozi imene ingakhalepo ngati m’bale wacatsopanoyo atamvela malangizo olakwika amenewa?

14. Kodi misonkhano yathu imatithandiza bwanji kuseŵenzetsa malangizo a pa Afilipi 1:10?

14 Misonkhano yathu imatithandiza m’njila zambili kuseŵenzetsa malangizo a pa Afilipi 1:10. Coyamba, zimene timaphunzila pa misonkhano imeneyi zimatikumbutsa zinthu zimene Yehova amaona kuti n’zofunika kwambili. Caciŵili, timaphunzila mmene tingasewenzetsele malangizo amene timalandila, n’colinga cakuti tikhale opanda colakwa. Ndipo cacitatu, misonkhanoyi imatilimbikitsa “pa cikondi ndi nchito zabwino.” (Aheb. 10:24, 25) Abale athu akamatilimbikitsa, cikondi cathu pa iwo komanso pa Mulungu cimakulila-kulila. Ngati timakonda abale athu na Mulungu na mtima wonse, tidzayesetsa kupewa kuwapunthwitsa.

PITILIZANI KUDZAZIDWA NA “ZIPATSO ZOLUNGAMA”

15. Kodi ‘kudzazidwa ndi zipatso zolungama’ kutanthauza ciani?

15 Paulo anapemphelela Afilipi mocokela pansi pa mtima kuti ‘adzazidwe ndi zipatso zolungama.’ (Afil. 1:11) Mwacidziŵikile, “zipatso zolungama” zimenezi zinaphatikizapo cikondi cawo pa Yehova ndi anthu ake. Zinaphatikizaponso nchito youzako ena za ciyembekezo cawo cokondweletsa na cikhulupililo cawo mwa Yesu. Pa Afilipi 2:15, Paulo anaseŵenzetsa mawu ena ofanizila. Anakamba kuti Akhristu a ku Filipi anali ‘kuwala monga . . . zounikila m’dziko.’ Mawu amenewa ni ogwilizana na zimene Yesu anakamba, zakuti ophunzila ake ni “kuwala kwa dziko.” (Mat. 5:14-16) Cinanso, Yesu analamula otsatila ake kuti ayenela ‘kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzila’ ake. Anakambanso kuti iwo ‘adzakhala mboni zake mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.’ (Mat. 28:18-20; Mac. 1:8) Conco, timabala “zipatso zolungama” pamene tigwila mwakhama nchito yofunika kwambili imeneyi.

Pamene ali pa ukaidi wosacoka pa nyumba ku Roma, Paulo akulembela kalata Akhristu a mu mpingo wa ku Filipi. Paulo akuseŵenzetsanso mpata umenewu kulalikila kwa asilikali omulondela ndi anthu ena obwela kudzamuona. (Onani ndime 16)

16. Kodi Afilipi 1:12-14 ionetsa bwanji kuti tingawale monga zounikila ngakhale pamene zinthu zili zovuta mu umoyo wathu? (Onani cithunzi pa cikuto.)

16 Kaya zinthu zili bwanji mu umoyo wathu, nafenso tingawale monga zounikila. Ndipo nthawi zina, zinthu zimene zingaoneke monga zopinga zotilepheletsa kulalikila uthenga wabwino, zingatipatse mwayi wolalikila. Mwacitsanzo, mtumwi Paulo anali pa ukaidi wosacoka pa nyumba ku Roma pamene analembela kalata Akhristu a ku Filipi. Koma izi sizinamulepheletse kulalikila kwa asilikali omulondela ndi kwa anthu obwela kudzamuona. Paulo analalikila mwakhama kwambili pa nthawi imene anali pa ukaidi, ndipo izi zinalimbikitsa abale kulankhula “mawu a Mulungu mopanda mantha.”—Ŵelengani Afilipi 1:12-14; 4:22.

Nthawi zonse, muziyesetsa kusakila mipata yolalikila mmene mungathele (Onani ndime 17) *

17. Fotokozani citsanzo camakono coonetsa mmene abale amabalila zipatso ngakhale m’nthawi zovuta.

17 Abale na alongo athu ambili aonetsa kulimba mtima monga mmene Paulo anacitila. Iwo ali m’maiko amene mulibe ufulu wolalikila poyela kapena ku nyumba na nyumba. Conco, amapeza njila zina zolengezela uthenga wabwino. (Mat. 10:16-20) M’dziko lina, limene abale alibe ufulu wolalikila poyela, woyang’anila dela wina analangiza ofalitsa kuti aliyense wa iwo azilalikila acibululu ake, maneba, anzake a ku sukulu, anzake a ku nchito, na mabwenzi ena. Anawauza kuti aziona amenewa monga “gawo” lawo. Pasanathe zaka ziŵili, ciŵelengelo ca mipingo m’dela limenelo cinakwela kwambili. N’kutheka kuti m’dziko limene tikhala muli ufulu wolalikila. Ngakhale n’conco, tingaphunzile mfundo yofunika pa citsanzo ca abale na alongo athu amenewa. Tiziyesetsa kulalikila mmene tingathele, tili na cikhulupililo cakuti Yehova adzatithandiza kupitiliza kugwila nchitoyi ngakhale m’nthawi zovuta.—Afil. 2:13.

18. Kodi tiyenela kuyesetsa kucita ciani?

18 Popeza tili m’nthawi yapadela, tiyenela kuyesetsa kutsatila malangizo ouzilidwa amene mtumwi Paulo analemba m’kalata yake yopita kwa Afilipi. Tifunika kutsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ni ziti, kukhala opanda colakwa, kupewa kupunthwitsa ena, ndiponso kubala zipatso zolungama. Tikatelo, cikondi cathu cidzapitiliza kukula, ndipo izi zidzapeleka ulemelelo kwa Atate wathu wacikondi, Yehova.

NYIMBO 17 ‘Nifuna’

^ ndime 5 Kuposa kale lonse, ino ndiyo nthawi yofunika kulimbitsa cikondi pa abale athu. Kalata youzilidwa imene Paulo analembela Afilipi ingatithandize kudziŵa mmene tingakulitsile cikondi pakati pathu, ngakhale m’nthawi zovuta.

^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pamene abale akuyeletsa m’Nyumba ya Ufumu, m’bale Johnson waleka kuseŵenza kuti akambe na m’bale wina komanso mwana wake. Izi zakhumudwitsa Willson, amene akuyeletsa. Mu mtima mwake, iye akuti, ‘Johnson naye wayambanso kuceza pa nchito m’malo moti aziseŵenza.’ Pambuyo pake, Willson akuona Johnson akuthandiza mlongo wacikulile mokoma mtima. Willson wacita cidwi na zimenezi, ndipo wakumbukila mfundo yakuti ni bwino kuyang’ana kwambili pa makhalidwe abwino a m’bale wakeyo.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’dziko limene Mboni zilibe ufulu wolalikila poyela, mosamala, m’bale akulalikila uthenga wa Ufumu kwa mnzake. Pamene m’baleyu ali ku nchito, akulalikilanso mnzake wogwila naye nchito pa nthawi yopumula.