Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 31

“Sitikubwelela M’mbuyo”!

“Sitikubwelela M’mbuyo”!

“Conco sitikubwelela m’mbuyo.”—2 AKOR. 4:16.

NYIMBO 128 Pilila Mpaka Mapeto

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi Akhristu afunika kucita ciani kuti apitilize kuthamanga pa mpikisano wokalandila moyo mpaka ku mapeto?

AKHRISTU ali pa mpikisano wokalandila moyo. Kaya tangoyamba kumene mpikisanowu kapena takhala tikuthamanga kwa zaka, tifunika kupitilizabe kuthamanga mpaka ku mapeto. Malangizo amene mtumwi Paulo anapeleka kwa Akhristu a ku Filipi, angatilimbikitse kucita zimenezi. Pamene Akhristu a mu mpingowo analandila kalata ya Paulo, ena mwa iwo anali atatumikila Yehova kwa zaka zambili. Iwo anali kuthamanga mwakhama pa mpikisano wokalandila moyo. Koma Paulo anawalimbikitsa kuti ayenela kupitiliza kuthamanga mopilila. Iye anafuna kuti iwo apitilize kutengela citsanzo cake, mwa ‘kuyesetsa kucita zimenezi mpaka atapeza mphoto.’—Afil. 3:14.

2. N’cifukwa ciani malangizo amene Paulo anapeleka kwa Afilipi anali a pa nthawi yake?

2 Malangizo amene Paulo anapeleka kwa Afilipi anali a pa nthawi yake. Akhristu a mu mpingowo wa ku Filipi anakumana na cizunzo kungoyambila pamene mpingowo unakhazikitsidwa. Ca m’ma 50 C.E, Paulo anamva mawu m’masomphenya om’pempha kuti ‘awolokele ku Makedoniya.’ Conco, iye na Sila anapita ku Filipi kukalalikila uthenga wabwino. (Mac. 16:9) Kumeneko, anakumana na mayi wina dzina lake Lidiya. Pamene iye “anali kumvetsela, Yehova anatsegula kwambili mtima wake” kuti amvetsetse uthenga wabwino. (Mac. 16:14) Posakhalitsa, iye anabatizika pamodzi na a m’banja lake. Koma Satana sanangokhala phee n’kumaonelela. Nthawi yomweyo, anasonkhezela amuna a mu mzindawo kugwila Paulo na Sila n’kuwatengela kwa akuluakulu aboma, ndipo anali kuwaneneza mlandu wakuti ni anthu osokoneza mtendele. Zotulukapo zake zinali zakuti, Paulo na Sila anakwapulidwa, kuponyedwa m’ndende, ndipo pambuyo pake anauzidwa kuti acoke mu mzindawo. (Mac. 16:16-40) Kodi iwo anabwelela m’mbuyo? Kutalitali! Nanga bwanji za Akhristu a mu mpingo watsopanowo? Nawonso anapeleka citsanzo cabwino cifukwa anapilila. Mwacionekele, iwo analimbikitsidwa kwambili na citsanzo cabwino ca Paulo na Sila.

3. Kodi Paulo anazindikila ciani? Nanga tikambilane mafunso ati?

3 Paulo anali wotsimikiza mtima kuti sadzabwelela m’mbuyo. (2 Akor. 4:16) Iye anazindikila kuti, kuti athamange pa mpikisano wa moyo mpaka ku mapeto, anafunika kusumika maganizo ake pa mphoto. Kodi tingaphunzilepo ciani pa citsanzo cake? N’zitsanzo zamakono ziti za Akhristu okhulupilika, zimene zionetsa kuti tingathe kupilila olo tikumane na mavuto aakulu? Nanga ciyembekezo cathu ca kutsogolo cingatilimbikitse bwanji kusabwelela m’mbuyo?

KODI TINGAPHUNZILEPO CIANI PA CITSANZO CA PAULO?

4. Kodi Paulo anaonetsa bwanji kuti anali wokangalika olo kuti anali m’ndende?

4 Pamene analembela kalata Akhristu a ku Filipi, kodi Paulo anaonetsa bwanji kuti anali kutumikila mwakhama? Pa nthawiyo, iye anali pa ukaidi wosacoka pa nyumba ku Roma. Conco, analibe mwayi wocita zambili pa nchito yolalikila. Olo zinali conco, Paulo anali kulalikila mokangalika kwa anthu obwela kudzamuona, komanso anali kulembela makalata mipingo ya kutali. Masiku anonso, Akhristu ambili amene sacoka pa nyumba cifukwa ca ukalamba kapena matenda, amayesetsa kulalikila uthenga wabwino kwa anthu obwela kudzawaona. Iwo amalembanso makalata olimbikitsa kwa anthu amene sitingathe kuwalalikila mwacindunji.

5. Malinga na mawu a Paulo pa Afilipi 3:12-14, kodi n’ciani cinam’thandiza kusumikabe maganizo ake pa mphoto?

5 Paulo sanalole zinthu zabwino kapena zoipa zimene anacita kumbuyoko kumuceutsa pa mpikisano wokalandila moyo. Iye anakamba kuti anafunika “kuiwala zinthu zakumbuyo” kuti ‘ayesetse kukapeza zakutsogolo,’ kapena kuti athamange pa mpikisano wa moyo mpaka ku mapeto. (Ŵelengani Afilipi 3:12-14.) Kodi n’zinthu zina ziti zimene zikanam’ceukitsa Paulo? Coyamba, iye asanakhale Mkhristu, anacita zinthu zambili zotamandika pakati pa Ayuda. Komabe, anaona zinthu zimenezo monga “mulu wa zinyalala.” (Afil. 3:3-8) Caciŵili, ngakhale kuti nthawi zina Paulo anali kudziimba mlandu cifukwa cozunza Akhristu, sanalole maganizo amenewo kumulepheletsa kutumikila Yehova. Komanso cacitatu, sanaganize kuti zimene anacita m’mbuyomo potumikila Yehova zinali zokwanila cakuti sanafunikenso kucita zambili. Paulo anacita zambili mu utumiki wake olo kuti anakumana na mavuto monga kumangidwa, kukwapulidwa, kuponyedwa miyala, ngalawa kumuswekela, kukhala wosadya komanso wosavala. (2 Akor. 11:23-27) Ngakhale kuti Paulo anacita zambili komanso anapilila mavuto ambili, anadziŵa kuti afunika kupitilizabe kutumikila Yehova mwakhama. Ni mmenenso ife tifunikila kucitila masiku ano.

6. Ni “zinthu zakumbuyo” zina ziti zimene tifunika kuiŵala?

6 Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Paulo pa nkhani ya “kuiwala zinthu zakumbuyo”? N’kutheka kuti mumadziimba mlandu cifukwa ca macimo amene munacita kumbuyoku. Ngati n’telo, bwanji osapatula nthawi yoŵelenga mosamala za nsembe ya dipo la Khristu? Kuŵelenga za nkhani yolimbikitsa imeneyi, kuisinkha-sinkha, na kuipemphelela, kudzakuthandizani kuleka kudziimba mlandu cifukwa ca macimo amene Yehova anakukhululukilani kale. Onani mfundo ina imene tingaphunzilepo pa citsanzo ca Paulo. Mwina munasiya nchito ya ndalama zambili pofuna kuika zinthu za Ufumu patsogolo. Ngati n’conco, mungaonetse kuti munaiŵala zinthu zakumbuyo mwa kupewa kulaka-lakanso zinthu zakuthupi zimene mukanakhala nazo. (Num. 11:4-6; Mlal. 7:10) “Zinthu zakumbuyo” zingaphatikizeponso zimene tinacita kumbuyoku potumikila Yehova kapena mayeselo amene tinapilila. N’zoona kuti kukumbukila mmene Yehova anatidalitsila na kuticilikiza kumbuyoku, kungatithandize kumuyandikila kwambili. Koma sitifunika kukhala okhutila na zimenezo, n’kumaona kuti zimene tinacita n’zokwanila.

Pa mpikisano wokalandila moyo, tifunika kusumika maganizo athu pa mphoto na kupewa zoceutsa (Onani ndime 7)

7. Malinga na 1 Akorinto 9:24-27, n’ciani cofunika kuti tipambane pa mpikisano wokalandila moyo? Fotokozani citsanzo.

7 Paulo anamvetsetsa malangizo a Yesu akuti tiyenela ‘kuyesetsa mwamphamvu’ kuloŵa pakhomo lopapatiza. (Luka 13:23, 24) Iye anadziŵa kuti mofanana na Khristu, anafunika kutumikila Yehova mwakhama kwa moyo wake wonse. Ndiye cifukwa cake anayelekezela umoyo wathu wacikhristu na mpikisano wothamanga. (Ŵelengani 1 Akorinto 9:24-27.) Munthu amene ali pa mpikisano wothamanga, amasumika maganizo ake onse pa kuyesetsa kuti akafike kothela, ndipo amapewa zoceutsa zilizonse. Mwacitsanzo, masiku ano, anthu ocita mpikisano wothamanga m’matauni, amathamanga m’misewu imene m’mbali mwake mumakhala malonda na zinthu zina zoceutsa. Kodi muganiza kuti munthu amene ali pa mpikisano wothamanga angapambane ngati ataima na kuyamba kuyang’ana malonda oyalidwa m’mbali mwa msewu? Iyai, n’zosatheka zimenezo! Pa mpikisano wokalandila moyo, nafenso tifunika kupewa zoceutsa. Ngati tisumika maganizo athu pa mphoto, komanso kutumikila Yehova mwakhama monga mmene Paulo anacitila, tidzalandila mphoto.

KUPILILA ZINTHU ZIMENE ZINGAFOOKETSE CIKHULUPILILO CATHU

8. N’zinthu zitatu ziti zofooketsa zimene tikambilane?

8 Lomba tiyeni tikambilane zinthu zitatu zimene zingatipangitse kubwelela m’mbuyo. Zinthu zake ni izi: Kuona kuti zimene tinali kuyembekezela zacedwa, kufooka kwa thanzi, komanso mayeselo osathelapo. Kuganizila mmene ena anapililila zinthu zofooketsa zimenezi kungatilimbikitse.—Afil. 3:17.

9. Kodi tingamvele bwanji ngati zimene tinali kuyembekezela sizinacitike?

9 Kuona kuti zimene tinali kuyembekezela zacedwa. Mwacibadwa, tonse timayembekezela mwacidwi zinthu zabwino zimene Yehova anatilonjeza. Mwacitsanzo, pa nthawi ina, mneneli Habakuku anakamba mawu oonetsa kuti anali kufunitsitsa kuti Yehova athetse zoipa zimene zinali kucitika mu Yuda. Ndipo Yehova anamuuza kuti apitilize ‘kuyembekezela.’ (Hab. 2:3) Komabe, ngati tiona kuti zimene tinali kuyembekezela zacedwa, cangu cathu cingazilale. Ndipo tingafike ngakhale potaya mtima. (Miy. 13:12) Zaconco n’zimene zinacitika kuciyambi kwa zaka za m’ma 1900. Pa nthawiyo, Akhristu ambili odzozedwa anali kukhulupilila kuti mu 1914 adzalandila mphoto yawo ya kumwamba. Koma zimenezo sizinacitike. Kodi anacita ciani ataona kuti zimene anali kuyembekezela zacedwa?

Zimene M’bale Royal na mkazi wake Pearl Spatz anali kuyembekezela sizinakwanilitsike mu 1914, koma iwo anapitiliza kutumikila Yehova mokhulupilika kwa zaka zambili (Onani ndime 10)

10. Kodi M’bale Spatz na mkazi wake anacita ciani ataona kuti zimene anali kuyembekezela sizinacitike?

10 Ganizilani citsanzo ca Akhristu aŵili okhulupilika amene sanalole zinthu zofooketsa zimenezo kuwabweza m’mbuyo. Woyamba ni M’bale Royal Spatz. Iye anabatizika mu 1908, ali na zaka 20. Iye anali kukhulupilila na mtima wonse kuti posapita nthawi adzalandila mphoto yake yakumwamba. Ndipo pamene anatomela mlongo Pearl mu 1911, m’baleyu anauza mlongoyo kuti: “Tonse tidziŵa zimene zidzacitika mu 1914. Conco, ni bwino kuti tikwatilane mwamsanga!” Kodi banja lacikhristu limeneli linabwelela m’mbuyo pa mpikisano wokalandila moyo cifukwa cakuti sanalandile mphoto yawo yakumwamba mu 1914? Iyai, cifukwa colinga cawo cacikulu cinali kucita cifunilo ca Mulungu mokhulupilika, osati kulandila mphoto. M’bale Royal na mkazi wake Pearl, anali otsimikiza mtima kuthamanga mopilila pa mpikisano wokalandila moyo. Ndipo n’zimenedi anacita. Anakhalabe acangu na okhulupilika kwa zaka zambili mpaka pamene anatsiliza utumiki wawo wa pa dziko lapansi. Mosakayikila, muyembekezela mwacidwi nthawi pamene Yehova adzayeletsa dzina lake, kukweza ucifumu wake, na kukwanilitsa malonjezo ake onse. Izi zidzacitika ndithu pa nthawi yoikika ya Yehova. Pamene tiyembekezela nthawiyo, tiyeni tipitilize kutumikila Yehova mokangalika. Ndipo tisafooke kapena kubwelela m’mbuyo cifukwa coona kuti zimene tinali kuyembekezela zacedwa.

Ngakhale kuti anali wokalamba, m’bale Arthur Secord (kumanzele) anali wofunitsitsa kucita zilizonse zimene angathe potumikila Yehova. (Onani ndime 11)

11-12. N’cifukwa ciani n’zotheka kutumikila Yehova mokhulupilika olo kuti tili na thanzi lofooka? Fotokozani citsanzo.

11 Kufooka kwa thanzi. Munthu wothamanga pa mpikisano weni-weni, amafunika kukhala na mphamvu zambili. Koma ife siticita kufunikila mphamvu zambili kuti tikhale na cikhulupililo colimba kapena kuti titumikile Mulungu modzipeleka. Ndipo pali Akhristu ambili a thanzi lofooka amene amafunabe kucita zonse zimene angathe potumikila Yehova. (2 Akor. 4:16) Mwacitsanzo, pamene M’bale Arthur Secord anali na zaka 88, anali atatumikila pa Beteli kwa zaka 55. Pa nthawiyo, iye anali kudwala-dwala komanso anali wofooka. Tsiku lina, mlongo amene anali kumusamalila, amenenso ni nesi, anafika pafupi na bedi ya m’baleyo. Atamuyang’ana mwaubwenzi anati: “M’bale Secord, mwacita zambili potumikila Yehova.” Koma mtima wa M’bale Secord sunali pa zimene anacita kale. Iye anayang’ana mlongoyo, kumwetulila, na kukamba kuti: “N’zoonadi. Koma cofunika kwambili si zimene tinacita kumbuyoku. Cofunika kwambili ni zimene tikucita pali pano.”

12 Mwina mwatumikila Yehova kwa zaka zambili, koma lomba mumalephela kucita zoculuka cifukwa ca kufooka kwa thanzi. Ngati zili conco, musataye mtima. Dziŵani kuti Yehova amakumbukila zimene munacita kumbuyoku pom’tumikila mokhulupilika, ndiponso amayamikila. (Aheb. 6:10) Kumbukilaninso kuti cimene cimaonetsa kuti timakonda kwambili Yehova, si kuculuka kwa zimene timacita pom’tumikila. M’malomwake, timaonetsa cikondi na kudzipeleka kwathu kwa Yehova, mwa kukhalabe na cimwemwe komanso ciyembekezo, ndiponso kucita zonse zimene tingathe pom’tumikila. (Akol. 3:23) Yehova amadziŵa bwino zimene tingakwanitse, ndipo satiyembekezela kucita zimene sitingakwanitse.—Maliko 12:43, 44.

M’bale Anatoly na Lidiya Melnik, anapilila mokhulupilika olo kuti anakumana na mavuto ambili (Onani ndime 13)

13. Kodi citsanzo ca m’bale Melnik na mkazi wake cingatilimbikitse bwanji kupitiliza kutumikila Yehova, olo tikumana na mayeselo ambili?

13 Ziyeso zosathelapo. Atumiki ena a Yehova apilila mayeselo na cizunzo kwa zaka zambili. Mwacitsanzo, pamene m’bale Anatoly Melnik * anali na zaka 12 cabe, atate ake anawamanga, kuwaika m’ndende, na kuwathamangitsila ku Siberia, dela limene lili pa mtunda wa makilomita oposa 7,000 kucokela kwawo ku Moldova. Patapita caka cimodzi, Melnik, amayi ake, na agogo ake, nawonso anawathamangitsila ku Siberia. M’kupita kwa nthawi, iwo anayamba kusonkhana pa mudzi winawake. Kuti akafike kumeneko, anali kuyenda mtunda wa makilomita 30 m’dela lozizila koopsa. Patapita zaka, M’bale Melnik anamangidwa, ndipo anakhala m’ndende kwa zaka zitatu. Iye anasiya mkazi wake, Lidiya, na mwana wake wa caka cimodzi. Mosasamala kanthu za mavuto amenewa, M’bale Melnik na banja lake anapitilizabe kutumikila Yehova mokhulupilika. Tsopano, iye ali na zaka 82, ndipo akutumikila m’Komiti ya Nthambi ku Central Asia. Mofanana na M’bale Melnik na mkazi wake Lidiya, tifunika kucita zonse zimene tingathe potumikila Yehova, na kupitiliza kupilila mayeselo.—Agal. 6:9.

CIYEMBEKEZO CATHU CIMATILIMBIKITSA

14. Kodi Paulo anazindikila kuti anafunika kucita ciani kuti akalandile mphoto yake?

14 Paulo anali na cidalilo cakuti adzathamanga pa mpikisano wokalandila moyo mpaka ku mapeto, komanso kuti adzalandila mphoto. Monga Mkhristu wodzozedwa, anali na ciyembekezo cokalandila “mphoto ya ciitano ca Mulungu copita kumwamba.” Koma kuti akalandile mphoto imeneyo, Paulo anazindikila kuti anafunika kucita khama. (Afil. 3:14) Polembela Akhristu a ku Filipi, iye anaseŵenzetsa fanizo logwila mtima pofuna kuwathandiza kusumikabe maganizo awo pa mphoto.

15. Kodi Paulo anaseŵenzetsa bwanji fanizo la nzika polimbikitsa Afilipi kuti acite zonse zotheka kuti akalandile mphoto?

15 Paulo anakumbutsa Akhristu a ku Filipi kuti iwo anali nzika zakumwamba. (Afil. 3:20) N’cifukwa ciani iwo anafunika kukumbukila zimenezi? M’masiku amenewo, anthu anali kufunitsitsa kukhala nzika za Roma, cifukwa kukhala nzika ya Roma kunali na mapindu ena ake. * Koma Akhristu odzozedwa anali nzika za boma labwino kwambili, limene linali kudzawapindulitsa m’njila zambili. Kukhala nzika ya Roma kunali kosanunkha kanthu poyelekezela na kukhala nzika ya boma lakumwamba. Ndiye cifukwa cake Paulo analimbikitsa Afilipi kuti akhale na ‘makhalidwe oyenela uthenga wabwino wa Khristu.’ (Afil. 1:27) Masiku anonso, Akhristu odzozedwa amapeleka citsanzo cabwino mwa kupitiliza kucita zonse zotheka kuti akalandile mphoto yawo ya moyo wosatha kumwamba.

16. Kaya tili na ciyembekezo cokakhala na moyo kumwamba kapena pa dziko lapansi, kodi tifunika kupitiliza kucita ciani malinga na Afilipi 4:6, 7?

16 Kaya tili na ciyembekezo cokakhala na moyo wosatha kumwamba kapena m’paradaiso pa dziko lapansi, tifunika kupitiliza kucita zonse zimene tingathe kuti tikalandile mphotoyo. Mulimonse mmene zinthu zilili mu umoyo wathu, sitifunika kuyang’ana zinthu zakumbuyo, kapena kulola ciliconse kutilepheletsa kupita patsogolo potumikila Yehova. (Afil. 3:16) Mwina mumaona kuti malonjezo a Yehova akucedwa kukwanilitsidwa, kapenanso mphamvu zanu zikucepela-cepela cifukwa ca ukalamba. Mwinanso, mwakhala mukukumana na mavuto kapena cizunzo kwa zaka zambili. Mulimonsemo, “musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse.” Koma mwa pemphelo na pembedzelo zopempha zanu zizidziŵika kwa Mulungu, ndipo iye adzakupatsani mtendele wake umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.—Ŵelengani Afilipi 4:6, 7.

17. Tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

17 Munthu amene ali pa mpikisano wothamanga akatsala pang’ono kufika ku mapeto, amayesetsa kuthamanga mwamphamvu, ndipo amasumika maganizo ake onse pa kutsiliza mpikisanowo. Conco, pamene tili pafupi kutsiliza mpikisano wathu wokalandila moyo, tiyeni nafenso tipitilize kusumika maganizo athu pa kutsiliza mpikisanowu. Ndipo malinga na mmene zinthu zilili mu umoyo wathu, tiyeni tithamange mwamphamvu kuti tikalandile madalitso amene atikonzela. Kodi tingacite ciani kuti tipitilize kuthamanga moyenela? Nkhani yotsatila idzatithandiza kudziŵa zinthu zoyenela kuika patsogolo. Idzatithandizanso ‘kutsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ni ziti.’—Afil. 1:9, 10.

NYIMBO 79 Aphunzitseni Kucilimika

^ ndime 5 Zilibe kanthu kuti tatumikila Yehova kwa zaka zingati, tonse timafuna kupita patsogolo na kukula mwauzimu. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti asabwelele m’mbuyo. M’kalata imene iye analembela Afilipi, timapezamo malangizo olimbikitsa amene angatithandize kupilila pa mpikisano wokalandila moyo. M’nkhani ino, tikambilane mmene tingaseŵenzetsele malangizo ouzilidwa amenewo.

^ ndime 13 Ŵelengani nkhani yofotokoza mbili ya M’bale Melnik ya mutu wakuti, “Ndinaphunzitsidwa Kukonda Mulungu Kuyambira Ndili Mwana,” imene ili mu Galamukani ya November 8, 2004.

^ ndime 15 Popeza mzinda wa Filipi unali pansi pa ulamulilo wa Roma, anthu a mu mzindawo anali na maufulu ena amene nzika za Roma zinali nawo. Conco, fanizo la Paulo linali logwila mtima kwa Akhristu a kumeneko.