Yohane M’batizi—Citsanzo Cabwino pa Nkhani ya Kukhalabe Wacimwemwe
KODI mumalaka-laka utumiki winawake wa mu mpingo, umene pali pano mulibe mwayi wokhala nawo? N’kutheka kuti mumalaka-laka udindo umene wina ali nawo. N’kuthekanso kuti mumalaka-laka utumiki umene munali nawo kumbuyoku. Koma cifukwa ca ukalamba, matenda, mavuto azacuma, kapena maudindo a m’banja, lomba simungakwanitsenso kucita utumiki umenewo. Kapenanso cifukwa ca kusintha kwa zinthu m’gulu la Mulungu, munasiya udindo umene munatumikilapo kwa nthawi yaitali. Mosasamala kanthu za cifukwa cimene munasiyila utumiki, mungayambe kuona kuti simucita zonse zimene mufuna potumikila Mulungu. Zinthu zikakhala conco, nthawi zina mungamakhale opanda cimwemwe. Ndiye funso n’lakuti, Tingacite ciani kuti tisamakhale okhumudwa nthawi zonse? Nanga n’ciani cingatithandize kukhalabe acimwemwe?
Tingaphunzile mfundo yofunika kwambili pa nkhani ya kukhalabe wacimwemwe mwa kuganizila citsanzo ca Yohane M’batizi. Iye anali na mwayi wocita utumiki wapadela. Koma mwacionekele, zina zimene zinacitika mu utumiki wake si zimene anali kuyembekezela. Iye ayenela kuti sanadziŵe zoti adzakhala m’ndende kwa nthawi yaitali kuposa imene anathela pa utumiki wake. Olo zinali conco, Yohane anakhalabe wacimwemwe pa nthawi yonse ya moyo wake. Kodi cinam’thandiza n’ciani? Nanga ife tingacite ciani kuti tikhalebe acimwemwe ngakhale pamene takumana na zofooketsa?
UTUMIKI WOKONDWELETSA WA YOHANE
Kumayambililo kwa 29 C.E., Yohane anayamba utumiki wake monga kalambulabwalo wa Mesiya. Iye anali kulalikila kuti: “Lapani, pakuti ufumu wakumwamba wayandikila.” (Mat. 3:2; Luka 1:12-17) Ambili analabadila uthenga wake. Makamu a anthu anabwela kucokela ku madela akutali kudzamvetsela uthenga wake, ndipo ambili analapa na kubatizika. Molimba mtima, Yohane M’batizi anacenjeza atsogoleli acipembedzo odzilungamitsawo kuti adzaweluzidwa ngati sadzasintha zocita zawo. (Mat. 3:5-12) Utumiki wake unafika pa cimake cakumapeto kwa 29 C.E, pa nthawi imene anabatiza Yesu. Kucokela pa nthawiyo, Yohane anayamba kutsogolela anthu kwa Yesu, Mesiya wolonjezedwa.—Yoh. 1:32-37.
Poganizila udindo wapadela wa Yohane, Yesu anakamba kuti: “Mwa onse obadwa kwa akazi, Mat. 11:11) N’zosakayikitsa kuti Yohane anakondwela na madalitso amene analandila. Mofanana na Yohane, Akhristu ambili alandila madalitso oculuka kucokela kwa Mulungu. Mwacitsanzo, ganizilani za m’bale Terry. Iye na mkazi wake, Sandra, akhala mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zoposa 50. M’bale Terry anakamba kuti: “N’nacitako mautumiki ambili okondweletsa. N’natumikilapo monga mpainiya, mtumiki wa pa Beteli, mpainiya wapadela, woyang’anila dela, woyang’anila cigawo, ndipo tsopano nikutumikilanso monga mpainiya wapadela.” Timakhala na cimwemwe tikalandila mwayi wa utumiki. Koma monga mmene tidzaphunzilila m’citsanzo ca Yohane, pamafunika khama kuti tipitilize kukhala acimwemwe zinthu zikasintha mu umoyo wathu.
sanabadwepo wamkulu woposa Yohane M’batizi.” (KHALANIBE NA MTIMA WOYAMIKILA
Yohane M’batizi anakhalabe na cimwemwe cifukwa cakuti sanaleke kuyamikila mwayi wa utumiki umene anali nawo. Mwacitsanzo, ganizilani izi: Pambuyo pa ubatizo wa Yesu, utumiki wa Yohane unayamba kucepa, koma utumiki wa Yesu unali kuwonjezeleka. Ophunzila a Yohane anada nkhawa na zimenezi, moti anapita kwa iye nomuuza kuti: “Rabi, munthu amene munali naye kutsidya kwa Yorodano uja, . . . akubatiza ndipo anthu onse akupita kwa iye.” (Yoh. 3:26) Yohane anayankha kuti: “Iye amene ali ndi mkwatibwi ndiye mkwati. Koma mnzake wa mkwati, akaimilila ndi kumvetsela zimene akunena, amakhala n’cimwemwe coculuka cifukwa ca mawu a mkwatiyo. Conco cimwemwe canga casefukiladi.” (Yoh. 3:29) Yohane sanapikisane na Yesu. Komanso, sanaone utumiki wake kukhala wosafunika cifukwa ca utumiki wa Yesu, umene unali wofunika kwambili. M’malomwake, Yohane anakhalabe wacimwemwe, cifukwa coyamikila udindo wake wokhala “mnzake wa mkwati.”
Mtima woyamikila umene Yohane anali nawo unam’thandiza kukhalabe wacimwemwe, olo kuti anafunika kukhala wodzimana pa utumiki wake. Mwacitsanzo, Yohane anali Mnazili kucokela pamene anabadwa, ndipo sicinali cololeka kwa iye kumwa vinyo. (Luka 1:15) Pokamba za umoyo wa Yohane wodzimana kwambili, Yesu anati: “Yohane anabwela ndipo sanali kudya kapena kumwa.” Mosiyana na Yohane, Yesu na ophunzila ake sanali kukhala umoyo wodzimana kwambili. Anali kukhala monga anthu ena onse. (Mat. 11:18, 19) Cinanso, olo kuti Yohane sanaciteko cozizwitsa ciliconse, anali kudziŵa kuti ophunzila a Yesu, kuphatikizapo ena amene poyamba anali ophunzila ake, anapatsidwa mphamvu zocita zozizwitsa. (Mat. 10:1; Yoh. 10:41) Yohane sanadandaule na zimenezi. M’malomwake, anapitiliza kugwila modzipeleka nchito imene Yehova anam’patsa.
Na ife tikamayamikila utumiki wathu m’gulu la Yehova, tidzakhalabe acimwemwe. M’bale Terry, amene tam’tomola poyamba paja, anati, “N’nali kucita khama pa utumiki uliwonse umene napatsidwa.” Pokamba za umoyo wake mu utumiki wanthawi zonse, iye anati: “Nikaganizila zimene n’nacita, sinidandaula. Koma nimakhala wacimwemwe nthawi zonse.”
Cimene cingatithandize kuwonjezela cimwemwe cathu potumikila Mulungu ni kukumbukila cimene cili cofunika kwambili pa utumiki, kapena udindo uliwonse umene tingakhale nawo. Cofunika kwambili ni mwayi “wokhala anchito anzake a Mulungu.” (1 Akor. 3:9) Kuganizila za mwayi waukulu umene tili nawo wotumikila Mulungu, kudzatiteteza ku maganizo ofooketsa amene angatilande cimwemwe. Mwacitsanzo, tidzapewa kuyelekezela zimene timacita na zimene ena amacita potumikila Mulungu. Komanso, sitidzaona utumiki wathu monga wosanunkha kanthu, cifukwa couyelekezela na utumiki umene ena akucita.—Agal. 6:4.
SUMIKANI MAGANIZO ANU PA ZINTHU ZAUZIMU
Yohane ayenela kuti anali kudziŵa kuti utumiki wake udzakhala waufupi. Koma mwacionekele sanali kudziŵa kuti udzatha mwadzidzidzi. (Yoh. 3:30) Mu 30 C.E., miyezi 6 pambuyo pobatiza Yesu, Yohane anaponyedwa m’ndende na Mfumu Herode. Olo zinali conco, iye anapitiliza kucitila umboni. (Maliko 6:17-20) Kodi n’ciani cinam’thandiza kukhalabe wacimwemwe pa nthawi yovutayi? Anaikabe maganizo ake pa zinthu zauzimu.
Pamene Yohane anali m’ndende, anamvela za kupita patsogolo kwa utumiki wa Yesu. (Mat. 11:2; Luka 7:18) Iye anali kukhulupilila na mtima wonse kuti Yesu anali Mesiya. Koma ayenela kuti sanali kudziŵa mmene Yesu adzakwanilitsila zonse zimene Malemba anakamba ponena za Mesiya. Mwina anali kudzifunsa kuti, ‘Popeza Malemba amati Mesiya adzakhala mfumu, kodi n’kutheka kuti posacedwa Yesu adzayamba kulamulila? Kodi mwina izi zidzacititsa kuti nitulutsidwe m’ndende muno?’ Pofuna kumvetsetsa zimene Yesu adzacita, Yohane anatumiza aŵili mwa ophunzila ake kukafunsa Yesu kuti: “Kodi Mesiya amene tikumuyembekezela uja ndinu kapena tiyembekezele wina?” (Luka 7:19) Ophunzilawo atabwelako, Yohane ayenela kuti anamvetsela mwachelu pamene iwo anali kum’fotokozela kuti Yesu anacilitsa anthu mozizwitsa, na kuwauza kuti akauze Yohane kuti: “Akhungu akuona, olumala akuyenda, akhate akuyeletsedwa, ogontha akumva, akufa akuukitsidwa ndipo aumphawi akumva uthenga wabwino.”—Luka 7:20-22.
N’zosakayikitsa kuti Yohane analimbikitsidwa atamvela malipoti amenewa. Malipotiwa anaonetsa kuti Yesu anali kukwanilitsa maulosi okamba za Mesiya. Yesu ataonekela monga Mesiya, sanam’tulutse Yohane m’ndende. Olo zinali conco, Yohane anadziŵa kuti utumiki wake sunapite pacabe. Conco, olo kuti anali m’ndende, iye anali na cifukwa comveka cokhalila wacimwemwe.
Mofanana na Yohane, ngati tisumika maganizo athu pa zinthu zauzimu, tidzakwanitsa kupilila mwacimwemwe komanso moleza mtima. (Akol. 1:9-11) Motelo, tifunika kumaŵelenga Baibo na kusinkha-sinkha zimene taŵelenga. Kucita izi, kudzatithandiza kuona kuti utumiki wathu kwa Mulungu supita pacabe. (1 Akor. 15:58) Mlongo Sandra anati: “Kuŵelenga caputa cimodzi m’Baibo tsiku lililonse kwanithandiza kuyandikila Yehova. Kucita izi, kumanithandiza kuti nizisumika maganizo anga pa iye osati pa ine.” Tingacitenso bwino kuganizila za kupita patsogolo kwa nchito ya Ufumu. Tikatelo, tidzayamba kuganizila kwambili zimene Yehova akucita, m’malo moganizila kwambili za ife eni. Mlongo Sandra anakambanso kuti: “Mapulogilamu apamwezi a pa TV yathu amatithandiza kuyandikila kwambili gulu lathu. Amatithandizanso kukhalabe acimwemwe mu utumiki wathu.”
Mu utumiki wake waufupi, Yohane M’batizi analalikila na “mzimu ndi mphamvu ngati za Eliya.” Komanso mofanana na Eliya, Yohane “anali munthu monga ife tomwe.” (Luka 1:17; Yak. 5:17) Ngati titengela citsanzo cake, mwa kukhala oyamikila na kusumika maganizo athu pa zinthu zauzimu, nafenso tidzakhabe acimwemwe mu utumiki wathu, zivute zitani.