Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 33

Ciukililo Cimaonetsa kuti Mulungu ni Wacikondi, Wanzelu, Komanso Woleza Mtima

Ciukililo Cimaonetsa kuti Mulungu ni Wacikondi, Wanzelu, Komanso Woleza Mtima

“Kudzakhala kuuka.”—MAC. 24:15.

NYIMBO 151 Adzaitana

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’cifukwa ciani Yehova analenga zamoyo?

PANTHAWI ina, Yehova anali kukhala yekha. Koma sanali wosungulumwa, cifukwa iye ni wacikwane-kwane. Ndipo sadalila wina kuti akhale wosangalala. Olo n’telo, Yehova anafuna kuti ena akhale na moyo n’kumasangalala. Cifukwa ca cikondi cake, iye anayamba nchito yolenga.—Sal. 36:9; 1 Yoh. 4:19.

2. Kodi Yesu na angelo anamvela bwanji ataona zinthu zimene Yehova analenga?

2 Coyamba, Yehova analenga Mwana wake, Yesu. Ndiyeno kupitila mwa Mwana wake ameneyu, “zinthu zina zonse zinalengedwa,” kuphatikizapo angelo mamiliyoni ambili. (Akol. 1:16) Yesu anali kukondwela kwambili kuseŵenzela pamodzi na Atate wake. (Miy. 8:30) Nawonso angelo anali kukondwela. Iwo anali kuona pamene Yehova na Yesu Mmisili Waluso anali kulenga kumwamba na dziko lapansi. Kodi anaonetsa bwanji cisangalalo cawo? Baibo imakamba kuti dziko litalengedwa, iwo “anayamba kufuula ndi cisangalalo.” Ndipo mosakayikila anapitiliza kusangalala na zonse zimene Yehova analenga, maka-maka anthu. (Yobu 38:7; Miy. 8:31) Zolengedwa zonsezi zimaonetsa kuti Yehova ni wacikondi komanso wanzelu.—Sal. 104:24; Aroma 1:20.

3. Malinga na 1 Akorinto 15:21, 22, kodi nsembe ya dipo la Yesu imatipatsa mwayi wotani?

3 Colinga ca Yehova cinali cakuti anthu akhale na moyo wamuyaya m’dziko lokongola limene iye analenga. Koma pamene Adamu na Hava anapandukila Atate wawo wacikondi, ucimo na imfa zinaloŵa m’dziko. (Aroma 5:12) Kodi Yehova anacita ciani? Nthawi yomweyo, iye anakambilatu zimene adzacita kuti apulumutse mtundu wa anthu. (Gen. 3:15) Yehova anakonza zakuti adzapeleke dipo n’colinga cakuti ana a Adamu na Hava amasuke ku ucimo na imfa. Ndiyeno anapatsa munthu aliyense mwayi wosankha kumutumikila kuti akapeze moyo wosatha.—Yoh. 3:16; Aroma 6:23; ŵelengani 1 Akorinto 15:21, 22.

4. Tikambilana mafunso ati m’nkhani ino?

4 Lonjezo la Mulungu lakuti adzaukitsa akufa limatipangitsa kukhala na mafunso ambili. Mwacitsanzo, kodi ciukililo cidzacitika bwanji? Kodi okondedwa athu amene anamwalila tidzakwanitsa kuwadziŵa akadzaukitsidwa? Kodi ciukililo cidzatibweletsela cimwemwe m’njila zotani? Nanga kodi kusinkha-sinkha za ciukililo kungatithandize bwanji kuti tiziyamikila cikondi ca Yehova, nzelu, na kuleza mtima kwake? Tsopano tiyeni tikambilane mafunso amenewa.

MMENE CIUKILILO CIYENELA KUTI CIDZACITIKILA

5. N’cifukwa ciani tingakambe kuti anthu amene anafa adzaukitsidwa mwadongosolo komanso osati panthawi imodzi?

5 Yehova kupitila mwa Mwana wake, adzaukitsa anthu mamiliyoni ambili. Cioneka kuti akufawo sadzaukitsidwa panthawi imodzi. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa ngati onse adzaukitsidwa pa nthawi imodzi, mwina padziko lapansi pangadzakhale cipwilikiti. Koma Yehova sacita zinthu mopanda dongosolo. Iye adziŵa kuti dongosolo n’lofunika kuti anthu apitilize kukhala mwamtendele. (1 Akor. 14:33) Pamene Yehova Mulungu anali kukonza dziko lapansi pamodzi na Yesu, anacita zinthu mwanzelu komanso moleza mtima. Iye anakonza zinthu pang’ono-m’pang’ono pa dzikoli kuti likhale malo abwino okhalapo anthu. Nayenso Yesu adzacita zinthu mwanzelu komanso moleza mtima mu Ulamulilo wake wa Zaka 1, 000. Adzaonetsa makhalidwe amenewa pamene azikatsogolela anthu opulumuka Aramagedo pa nchito yokonza dziko lapansi kuti alandililemo anthu oukitsidwa.

Anthu opulumuka Aramagedo adzaphunzitsa anthu oukitsidwa za Ufumu wa Yehova na malamulo ake (Onani ndime 6) *

6. Malinga na Machitidwe 24:15, kodi ena mwa anthu amene Yehova adzawaukitsa ni otani?

6 Koposa zonse, anthu amene adzapulumuka Aramagedo adzafunika kuphunzitsa anthu oukitsidwa za Ufumu wa Yehova na malamulo ake. Cifukwa ciani? Cifukwa ambili mwa oukitsidwawo adzakhala “osalungama.” (Ŵelengani Machitidwe 24:15.) Iwo adzafunika kusintha kwambili umoyo wawo kuti adzapindule na nsembe ya dipo la Khristu. Tangoganizilani nchito yaikulu imene idzakhalapo yophunzitsa coonadi anthu mamiliyoni ambili osadziŵa Yehova. Kodi munthu aliyense azikaphunzitsidwa payekha monga mmene timatsogozela maphunzilo a Baibo masiku ano? Kodi anthu amenewa adzaikidwa m’mipingo na kuphunzitsidwa kuti nawonso aziphunzitsako ena oukitsidwa? Palipano sitidziŵa. Koma cimene tidziŵa n’cakuti pofika kumapeto kwa Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1,000, “dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova.” (Yes. 11:9) Ndithudi, nthawi imeneyo tidzakhala na nchito yaikulu komanso yokondweletsa!

7. Tidziŵa bwanji kuti anthu a Yehova adzakhala acifundo pophunzitsa anthu oukitsidwa?

7 Mu Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1,000, anthu onse a Yehova adzafunika kusintha umoyo wawo kuti am’kondweletse. Conco iwo adzakhala acifundo pothandiza oukitsidwa kuthetsa zizoloŵezi zoipa na kuyamba kutsatila miyezo ya Yehova ya makhalidwe abwino. (1 Pet. 3:8) Mosakayikila, anthu oukitsidwawo adzakopeka ndi anthu a Yehova odzicepetsa amenenso adzakhala ‘akukonza cipulumutso cawo.’—Afil. 2:12.

KODI AMENE ADZAUKITSIDWA TIDZAKWANITSA KUWADZIŴA?

8. N’cifukwa ciani tingakambe kuti anthu amene adzalandila oukitsidwa adzakwanitsa kuwadziŵa okondedwa awo?

8 Pali zifukwa zingapo zimene tingakambile kuti anthu amene adzalandila oukitsidwa adzakwanitsa kuwadziŵa okondedwa awo. Mwacitsanzo, tikaganizila mmene Yehova anaukitsila anthu kale, cioneka kuti iye poukitsa anthu adzawapangila matupi atsopano olingana na amene anali nawo poyamba. Komanso azikakamba na kuganiza mmene anali kucitila atatsala pang’ono kumwalila. Kumbukilani kuti Yesu anayelekezela imfa na tulo. Ndiponso anayelekezela kuukitsa munthu kwa akufa na kumuutsa ku tulo. (Mat. 9:18, 24; Yoh. 11:11-13) Munthu akauka ku tulo, maonekedwe ake na mawu ake sizisintha. Komanso amakumbukila zimene anali kucita asanagone. Mwacitsanzo, ganizilani za Lazaro. Iye anali wakufa kwa masiku anayi, ndipo thupi lake linali litayamba kuwola. Koma Yesu atamuukitsa, azilongosi ake anamuzindikila nthawi yomweyo, ndipo mwacidziŵikile nayenso Lazaro anawakumbukila.—Yoh. 11:38-44; 12:1, 2.

9. N’cifukwa ciani anthu amene anamwalila sadzaukitsidwa ali na maganizo na thupi langwilo?

9 Yehova analonjeza kuti mu ulamulilo wa Khristu, palibe aliyense amene adzakamba kuti: “Ndikudwala.” (Yes. 33:24; Aroma 6:7) Conco, akufa adzaukitsidwa na matupi athanzi. Koma sadzakhala angwilo nthawi yomweyo, cifukwa ngati angadzaukitsidwe ali na maganizo angwilo komanso thupi langwilo, mwina abululu awo sadzakwanitsa kuwazindikila. Cioneka kuti pang’ono-m’pang’ono anthu onse adzakhala angwilo mu Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1,000. Ulamulilo wa zaka 1,000 umenewu ukadzatha, m’pamene Yesu adzabwezela Ufumu kwa Atate wake. Panthawiyo Ufumu wa Mulungu udzakhala utatsiliza nchito yake kuphatikizapo kuthandiza anthu kukhala angwilo.—1 Akor. 15:24-28; Chiv. 20:1-3.

KODI CIUKILILO CIDZATIBWELETSELA CIMWEMWE M’NJILA ZOTANI?

10. Kodi mudzamvela bwanji pamene akufa adzaukitsidwa?

10 Ganizilani cabe mmene mudzamvelela pamene mudzalandila okondedwa anu amene anamwalila. Kodi mudzasekelela kwambili kapena mudzagwetsa misozi ya cisangalalo? Kodi mudzafuula mosangalala poimba nyimbo zotamanda Yehova? N’zodziŵikilatu kuti mudzam’konda kwambili Atate wanu wacikondi na Mwana wake cifukwa ca mphatso yabwino ngako imeneyi ya ciukililo.

11. Mogwilizana na mawu a Yesu pa Yohane 5:28, 29, kodi anthu omvela Mulungu adzakhala na mwayi wotani?

11 Tangoganizilani cisangalalo cimene anthu oukitsidwa adzakhala naco akadzavula umunthu wawo wakale na kuyamba kutsatila miyezo yolungama ya Mulungu. Anthu amene adzasintha umoyo wawo, adzakhala na mwayi wokhala na moyo wosatha m’Paradaiso. Koma anthu amene adzapandukila Mulungu, sadzaloledwa kusokoneza mtendele m’Paradaiso.—Yes. 65:20; ŵelengani Yohane 5:28, 29.

12. Kodi anthu onse padziko lapansi adzadalitsidwa bwanji na Yehova?

12 Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulila, anthu ake adzaona kukwanilitsidwa kwa mawu a pa Miyambo 10:22 akuti: “Madalitso a Yehova ndi amene amalemeletsa, ndipo sawonjezelapo ululu.” Popeza kuti mzimu wa Yehova udzakhala ukugwila nchito pa anthu ake, iwo adzalemela mwauzimu. Izi zitanthauza kuti adzatengela kwambili makhalidwe a Khristu, komanso pang’ono-m’pang’ono adzakhala angwilo. (Yoh. 13:15-17; Aef. 4:23, 24) Tsiku lililonse, thanzi lawo na makhalidwe awo zizikasintha kukhala zabwino kuposa poyamba. Udzakhala umoyo wokondweletsa ngako! (Yobu 33:25) Koma kodi kusinkha-sinkha za ciukililo kungatithandize bwanji pa nthawi ino?

MUZIYAMIKILA CIKONDI CA YEHOVA

13. Kulingana na Salimo 139:1-4, kodi kuukitsa akufa kumene Yehova adzacita kuonetsa bwanji kuti iye amatidziŵa bwino?

13 Monga takambila kale, Yehova poukitsa akufa, adzabwezeletsa maganizo awo na umunthu wawo, moti adzakhala mmene analili asanamwalile. Kodi zimenezi zionetsa ciani? Zionetsa kuti Yehova amakukondani kwambili ndipo amadziŵa bwino maganizo anu, zokamba, na zocita zanu. Amadziŵanso bwino mmene mumamvelela. Conco ngati mwamwalila, Yehova pokuukitsani adzakwanitsa kubwezeletsa maganizo anu na umunthu wanu wonse. Mfumu Davide anali kudziŵa kuti Yehova amatidziŵa bwino aliyense payekha. (Ŵelengani Salimo 139:1-4.) Kodi tiyenela kumvela bwanji poona kuti Yehova amatidziŵa bwino kwambili?

14. Kodi tiyenela kumvela bwanji poona kuti Yehova amatidziŵa bwino kwambili?

14 Popeza kuti Yehova amatidziŵa bwino, sitiyenela kukhala na nkhawa yakuti iye amangoyang’ana pa zofooka zathu. Cifukwa ciani? Kumbukilani kuti Yehova amatikonda kwambili. Iye amaona aliyense wa ife kukhala wamtengo wapatali. Amadziŵa bwino zonse zimene zimaticitikila pa umoyo komanso mmene zimatikhudzila. Kukamba zoona, zimenezi n’zolimbikitsa kwambili! Conco tisataye mtima poganiza kuti tili tekha. Pa mphindi iliyonse, tsiku lililonse, Yehova amakhala nafe pafupi kuti atithandize.—2 Mbiri 16:9.

MUZIYAMIKILA NZELU ZA YEHOVA

15. Kodi ciyembekezo cakuti akufa adzauka cimaonetsa bwanji nzelu za Yehova?

15 Kuopa imfa ni cida camphamvu. Anthu olamulidwa na Satana amaseŵenzetsa cida cimeneci pokakamiza anthu ena kucita zinthu zosakhulupilika kwa mabwenzi awo, kapena kucita zinthu zimene adziŵa kuti n’zoipa. Koma kwa ife cida cimeneci cilibe mphamvu. Cifukwa ciani? Cifukwa tidziŵa kuti ngati adani athu angatiphe, Yehova adzatiukitsa. (Chiv. 2:10) Tidziŵa kuti palibe ciliconse cimene angacite cimene cingatilekanitse na cikondi ca Yehova. (Aroma 8:35-39) Ndithudi, Yehova waonetsa nzelu zapadela potipatsa ciyembekezo cakuti akufa adzauka! Ciyembekezo cimeneci, cimatithandiza kuti tisamaope imfa ngati anthu amene ali kumbali ya Satana atiopseza kuti atipha tikakana kucita zinazake. Cimatithandizanso kukhala olimba mtima kuti tikhalebe okhulupilika kwa Yehova.

Kodi zosankha zathu zimaonetsa kuti timakhulupililadi lonjezo la Yehova lakuti adzatithandiza kupeza zosoŵa zathu zakuthupi? (Onani ndime 16) *

16. Ni mafunso ati amene muyenela kudzifunsa? Nanga mafunso amenewa angakuthandizeni bwanji kudziŵa kuti mumadaliladi Yehova?

16 Ngati adani a Yehova akuopsezani kuti akuphani, kodi mudzakhala na cidalilo cakuti Yehova adzakuukitsani? Kodi mungadziŵe bwanji kuti mudzakhala naco? Njila imodzi ni mwa kudzifunsa kuti, ‘Kodi zosankha zing’ono-zing’ono zimene nimapanga tsiku lililonse zimaonetsa kuti nimadaliladi Yehova?’ (Luka 16:10) Funso lina lingakhale lakuti, ‘Kodi mu umoyo wanga nimaonetsadi kuti nimakhulupilila lonjezo la Yehova lakuti adzanithandiza kupeza zosoŵa zanga zakuthupi ngati niika zinthu za Ufumu patsogolo? (Mat. 6:31-33) Ngati mwayankha kuti inde pa mafunso amenewa, ndiye kuti mumadalila Yehova, ndipo ndimwe okonzeka kulimbana na ciyeso ciliconse cimene mungakumane naco kutsogolo.—Miy. 3:5, 6.

MUZIYAMIKILA KULEZA MTIMA KWA YEHOVA

17. (a) Kodi nkhani ya ciukililo ionetsa bwanji kuti Yehova ni woleza mtima? (b) Kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila kuleza mtima kwa Yehova?

17 Yehova anaikilatu tsiku na nthawi pamene adzawononga dziko loipali. (Mat. 24:36) Iye ni woleza mtima, ndipo sadzawononga dzikoli nthawiyo ikalibe kukwana. Mulungu amalaka-laka kuukitsa akufa, koma akulezabe mtima. (Yobu 14:14, 15) Iye akuyembekezela nthawi yoyenela yakuti akaukitse akufa. (Yoh. 5:28) Tili na zifukwa zabwino zokhalila oyamikila kaamba ka kuleza mtima kwa Yehova. Tangoganizilani! Cifukwa ca kuleza mtima kwa Yehova, anthu ambili kuphatikizapo ife amene, takhala na mwayi wolapa macimo athu. (2 Pet. 3:9) Yehova amafuna kuti anthu ambili akhale na mwayi wokapeza moyo wosatha. Conco, tiyeni tizionetsa kuti timayamikila kuleza mtima kwake. Kodi tingaonetse bwanji kuyamikila? Mwa kuyesetsa kusakila anthu a ‘maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha,’ komanso kuwathandiza kuti ayambe kukonda Yehova na kum’tumikila. (Mac. 13:48) Tikatelo, tidzawathandiza kuti apindule na kuleza mtima kwa Yehova, monga mmene ife tapindulila.

18. N’cifukwa ciani tiyenela kucita zinthu moleza mtima na ena?

18 Yehova adzapitiliza kuleza nafe mtima mpaka kumapeto kwa zaka 1,000 pamene tidzakhala angwilo. Iye ni wokonzeka kutikhululukila macimo mpaka nthawiyo pamene tidzakhala angwilo. Conco, tiyenela kutengela citsanzo cake mwa kuona makhalidwe abwino mwa ena na kuwalezela mtima. Mwacitsanzo, ganizilani citsanzo ca mlongo wina amene mwamuna wake analeka kusonkhana cifukwa covutika na nkhawa yaikulu. Mlongoyo anati: “Iyi inali nthawi yovuta kwambili kwa ine. Umoyo wa banja lathu unasintha mwadzidzidzi, ndipo zonse zimene tinali kufuna kucita zinasokonezekelatu.” Pa nthawi yovuta imeneyo, mkazi wacikondi ameneyu anapitiliza kupilila moleza mtima. Iye anadalila Yehova, ndipo nthawi zonse anali kum’thandiza mwamuna wake. Mofanana na Yehova, mlongoyu sanasumike maganizo pa vutolo, koma pa zabwino zimene mwamuna wake anali kucita. Iye anati: “Mwamuna wanga ali na makhalidwe abwino, ndipo akuyesetsa kuthetsa nkhawa yake pang’ono-pang’ono.” Zoonadi, n’kofunika kwambili kuti tizilezela mtima a m’banja lathu kapena abale na alongo mu mpingo, amene amayesetsa kugonjetsa mavuto amene akukumana nawo.

19. Kodi tiyenela kutsimikiza mtima kucita ciani?

19 Mulungu atalenga dziko lapansi, Yesu na angelo anakondwela kwambili. Koma ganizilaninso cimwemwe cimene iwo adzakhala naco akadzaona kuti dziko lapansi ladzala ndi anthu angwilo amene amakonda Yehova na kum’tumikila. Ganizilaninso cimwemwe cimene anthu okalamulila pamodzi na Khristu kumwamba adzakhala naco poona kuti mtundu wa anthu ukupindula na nchito yawo. (Chiv. 4:4, 9-11; 5:9, 10) Zidzakhala zosangalatsa kwambili kukhala m’dziko limene anthu azidzagwetsa misozi ya cisangalalo osati kulila cifukwa ca cisoni. M’dzikolo simudzakhala matenda, zopweteka, cisoni, na imfa. Mavuto onse adzathelatu. (Chiv. 21:4) Pamene tikuyembekezela nthawiyo, tiyeni titsimikize mtima kutengela citsanzo ca Atate wathu wacikondi, wanzelu, komanso woleza mtima. Tikatelo, tidzakhalabe acimwemwe olo tikumane na mavuto otani. (Yak. 1:2-4) Ndithudi, ndife oyamikila kwambili kaamba ka lonjezo la Yehova lakuti “kudzakhala kuuka”!—Mac. 24:15.

NYIMBO 141 Moyo ni Cozizwitsa

^ ndime 5 Yehova ni Tate wacikondi, wanzelu, komanso woleza mtima. Makhalidwe amenewa amaonekela bwino tikaganizila mmene analengela zinthu zonse, ndiponso lonjezo lake lakuti adzaukitsa akufa. M’nkhani ino, tikambilana ena mwa mafunso amene tingakhale nawo pankhani ya ciukililo. Tikambilananso mmene tingaonetsele kuti timayamikila cikondi ca Yehova, nzelu, na kuleza mtima kwake.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Munthu amene anamwalila zaka mahandiledi zapitazo, waukitsidwa mu Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1,000. M’bale amene anapulumuka pa Aramagedo akuphunzitsa munthu woukitsidwayo zimene afunika kucita kuti apindule na nsembe ya dipo la Khristu.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale akuuza abwana ake ku nchito kuti masiku ena mkati mwa wiki sazikwanitsa kugwila nchito ya ovataimu. Akuwafotokozela kuti pa masiku amenewo amacita zinthu zauzimu madzulo. Komabe, akuwauzanso kuti ngati pa masiku ena papezeka nchito inayake imene iye afunika kuicita mwamsanga, ni wokonzeka kuigwila nchitoyo pa ovataimu.