Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 35

Lemekezani Wina Aliyense mu Mpingo

Lemekezani Wina Aliyense mu Mpingo

“Diso silingauze dzanja kuti: ‘Ndilibe nawe nchito,’ kapenanso, mutu sungauze mapazi kuti: ‘Ndilibe nanu nchito.’”—1 AKOR. 12:21.

NYIMBO 124 Tikhale Okhulupilika Nthawi Zonse

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi n’ciani cimene Yehova anacita kwa mtumiki wake aliyense?

MTUMIKI wa Mulungu aliyense, Yehova ndiye anamuitana mu mpingo wake. Ngakhale kuti timacita mbali zosiyana mu mpingo, tonsefe ndife ofunika ndipo timadalilana wina na mnzake. Mtumwi Paulo anatithandiza kumvetsetsa mfundo yofunika imeneyi. Motani?

2. Malinga na Aefeso 4:16, n’cifukwa ciani tifunikila kuona wina aliyense kukhala wofunika, ndiponso kuseŵenzela pamodzi?

2 Malinga na lemba limene pazikidwa nkhani ino, Paulo anagogomeza kuti palibe aliyense wa ife amene ayenela kuyang’ana mtumiki wa Yehova mnzake, n’kumati: “Ndilibe nawe nchito.” (1 Akor. 12:21) Kuti mu mpingo mukhale mtendele, tifunika kuona wina aliyense kukhala wofunika na kuseŵenzela pamodzi mogwilizana. (Ŵelengani Aefeso 4:16.) Ngati timagwilizana, aliyense adzaona kuti amakondedwa, ndipo mpingo udzakhala wolimba.

3. Kodi m’nkhani ino tikambilana ciani?

3 Kodi tingaonetse motani kuti timalemekeza Akhristu anzathu mu mpingo? M’nkhani ino, tikambilana mmene akulu angaonetsele ulemu kwa akulu anzawo. Cina, tikambilana mmene ife tonse tingaonetsele kuti timalemekeza abale na alongo athu amene sali pabanja. Ndipo cothela, tiphunzila mmene tingaonetsele kuti timalemekeza amene sakwanitsa kukamba bwino-bwino citundu cathu.

MUZILEMEKEZA AKULU ANZANU

4. Kodi pa Aroma 12:10 pali uphungu uti wa Paulo umene akulu ayenela kuutsatila?

4 Akulu onse mu mpingo amaikidwa na mzimu woyela wa Yehova. Koma aliyense wa iwo ali na mphatso komanso maluso osiyana. (1 Akor. 12:17, 18) Mwina ena anangoikidwa kumene pa udindo, ndipo ali na cidziŵitso cocepelako poyelekeza na akulu ena. Mwinanso ena sakwanitsa kucita zambili cifukwa ca ukalamba na matenda. Ngakhale n’conco, palibe mkulu aliyense amene ayenela kuyang’ana mkulu mnzake n’kumati, “Ndilibe nawe nchito.” M’malo mwake, mkulu aliyense ayenela kumvela uphungu wa Paulo wa pa Aroma 12:10.—Ŵelengani.

Akulu amaonetsa kuti amalemekeza akulu anzawo mwa kumvetselana mwachelu (Onani ndime 5-6)

5. Kodi akulu angaonetse bwanji kuti amalemekeza akulu anzawo? Nanga n’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kofunika?

5 Akulu amaonetsa kuti amalemekeza akulu anzawo mwa kumvetselana mosamala. Izi n’zofunika kwambili maka-maka akulu akakumana monga bungwe kuti akambilane nkhani zikulu-zikulu. Cifukwa ciani? Onani zimene Nsanja ya Mlonda ya cizungu ya October 1, 1988, inakamba. Inati: “Akulu azikumbukila kuti Khristu mwa mzimu woyela, angapangitse mkulu aliyense pa bungwe la akulu kutulutsa mfundo ya m’Baibo imene ingathandize pa nkhani imene akukambilana, kapena popanga cigamulo cofunika. (Mac. 15:6-15) Pa bungwe la akulu, palibe mkulu aliyense amene mzimu woyela umagwila nchito kwambili pa iye kuposa anzake.”

6. Kodi n’ciani cingathandize akulu kuseŵenzela pamodzi mogwilizana? Nanga zimenezi zingalimbikitse bwanji mpingo?

6 Mkulu amene amalemekeza akulu anzake amapewa kukhala woyamba nthawi zonse kulankhulapo pa miting’i ya akulu. Amapewanso kulankhulapo kwambili kuposa ena, ndipo saona kuti malingalilo ake nthawi zonse ndiwo oyenela. M’malomwake, amafotokoza malingalilo ake modzicepetsa. Amamvetselanso mwachelu ena akamapelekapo ndemanga zawo. Ndipo cofunika kwambili, iye amakhala wokonzeka kukambilana mfundo za m’Malemba, komanso kutsatila zitsogozo za “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mat. 24:45-47) Ngati akulu akambilana mwacikondi komanso mwaulemu, mzimu woyela wa Mulungu udzakhala pakati pawo, ndipo udzaŵathandiza kupanga zosankha zolimbikitsa mpingo.—Yak. 3:17, 18.

MUZILEMEKEZA AKHRISTU AMENE SALI PABANJA

7. Kodi Yesu anali kuŵaona bwanji anthu amene sanali pabanja?

7 Mpingo umakhala na mabanja amene ali na ŵana komanso amene alibe ŵana. Komanso muli abale na alongo amene sali pabanja. Kodi iwo tiyenela kuŵaona motani? Onani mmene Yesu anali kuonela umbeta. Pa utumiki wake padziko lapansi, Yesu sanakwatilepo. Anakhala wosakwatila cakuti anaseŵenzetsa nthawi yake na mphamvu zake pocita utumiki wake. Yesu sanakhazikitse lamulo lakuti munthu afunika kukhala pabanja kapena kukhala mbeta. Komabe, iye anakamba kuti Akhristu ena angasankhe kukhala mbeta. (Mat. 19:11, 12) Yesu anali kulemekeza anthu amene sanali pabanja. Sanaone kuti anthuwo ni otsikilapo kapena osoŵekela mbali ina yake mu umoyo wawo.

8. Malinga na 1 Akorinto 7:7-9, kodi mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuganizila za ciani?

8 Mofanana ndi Yesu, mtumwi Paulo anacita utumiki wake ali mbeta. Paulo sanaphunzitsepo kuti Mkhristu akakwatila ndiye kuti walakwa. Iye anadziŵa kuti imeneyi ni nkhani yaumwini. Ngakhale n’telo, Paulo analimbikitsa Akhristu kuganizila ngati angathe kutumikila Yehova monga mbeta. (Ŵelengani 1 Akorinto 7:7-9.) Ndithudi Paulo sanali kuona Akhristu amene anali mbeta kukhala otsikilapo. Ndiye cifukwa cake anasankha Timoteyo, m’bale wosakwatila, kuti asamalile maudindo akulu-akulu. * (Afil. 2:19-22) Conco, kungakhale kulakwa kuganiza kuti m’bale ni woyenelela kapena ni wosayenelela, cabe cifukwa ali pabanja kapena sali pabanja.—1 Akor. 7:32-35, 38.

9. Kodi tingakambe ciani za cikwati na umbeta?

9 Yesu ngakhale Paulo sanaphunzitse zakuti Akhristu onse afunika kuloŵa m’banja kapena kukhala mbeta. Nanga tingakambe ciani za cikwati na umbeta? Nsanja ya Mlonda ya October 1, 2012, inakamba momveka bwino kuti: “Kunena zoona, zonsezi [cikwati na umbeta] ndi mphatso zocokela kwa Mulungu. . . . Yehova saona kuti kusakhala pabanja ni cinthu cocititsa manyazi kapena comvetsa cisoni.” Conco, tiyenela kulemekeza abale na alongo mu mpingo amene ni mbeta.

Pofuna kulemekeza abale na alongo amene ni mbeta, kodi tiyenela kupewa ciani? (Onani ndime 10)

10. Tingaonetse bwanji kuti timalemekeza abale na alongo athu amene ni mbeta?

10 Kodi tingaonetse bwanji kuti timalemekeza abale na alongo athu amene ni mbeta? Tifunika kukumbukila kuti Akhristu ena anacita kusankha okha kukhala mbeta. Ena amafuna kukhala pabanja, koma akalibe kupeza munthu woyenelela kumanga naye banja. Koma ena anataikilidwa wokondedwa wawo mu imfa. Mulimonsemo, kodi ena mu mpingo ayenela kumafunsa Akhristu amene ni mbeta cifukwa cake sali pabanja, kapena kudzipeleka kuti athandizile kupeza womanga naye banja? N’zoona kuti Akhristu ena amene ni mbeta angapemphe thandizo limenelo. Bwanji ngati munthu sanacite kupempha yekha, koma ife n’kufuna kugwapo kuti tithandize, kodi abale na alongo amene ni mbeta angamvele bwanji? (1 Ates. 4:11; 1 Tim. 5:13) Tiyeni timvele ndemanga za abale na alongo ena okhulupilika amene ni mbeta.

11-12. Kodi tiyenela kupewa kucita ciani kuti tisaŵalefule amene sali pabanja?

11 Woyang’anila dela wina amene ni mbeta, ndipo amacita bwino utumiki wake, amaona kuti umbeta uli na mapindu ambili. Ngakhale n’conco, iye anakamba kuti zingakhale zolefula ngati abale na alongo, amene m’kuona kwawo amafuna kuthandiza, akufunsa kuti: “N’cifukwa ciani simuli pabanja?” M’bale wina wotumikila pa ofesi yanthambi, amenenso ni mbeta, anakamba kuti: “Nthawi zina, abale na alongo amanipangitsa kuona monga anthu amene ni mbeta ni omvetsa cifundo. Ndipo zimenezi zingaonetse monga kuti umbeta si mphatso, koma tsoka.”

12 Mlongo wina wotumikila pa Beteli, amene ni mbeta, anati: “Ofalitsa ena amaganiza kuti anthu onse amene ni mbeta amakhala akufuna-funa munthu wokwatilana naye, ndipo maceza alionse amaŵaona kukhala mwayi wopezako munthu womanga naye banja. Panthawi ina, n’napita kukatumikila ku dela lina m’dziko lathu, ndipo n’nafika patsiku limene kunali msonkhano wa mpingo. Mlongo amene n’nafikila kunyumba kwake ananiuza kuti panali abale aŵili mu mpingowo, amene anali a msinkhu wanga. Ananitsimikizila kuti sakuyesa kunipezela mwamuna. Koma titangoloŵa m’Nyumba ya Ufumu, ananitengela kwa abale aŵili aja kuti nidziŵane nawo. Kukamba zoona, zinali zocititsa manyazi kwa ife atatu.”

13. Kodi ni zitsanzo ziti zimene zinalimbikitsa mlongo wina amene ni mbeta?

13 Mlongo winanso wotumikila pa Beteli, amene ni mbeta, anati: “Nimadziŵa apainiya ena amene akhala pa umbeta kwa zaka zambili, koma ni olimba mwauzimu, osumika maganizo pa utumiki, odzimana, okhutila na utumiki wawo, komanso othandiza kwambili mu mpingo. Iwo ni okhutila na umbeta wawo. Sadziona kuti ni oposa ena cifukwa cakuti sanakhalepo pabanja, kapena kuona kuti anamanidwa zinthu zina cabe cifukwa cakuti alibe mnzawo wa m’cikwati kapena ana.” Uwu ndiwo ubwino wokhala mu mpingo umene onse amalemekezana na kukondana. Palibe amene amakumvelela cisoni kapena kukucitila kaduka, kukunyalanyaza kapena kukukweza kwambili. Umangoona kuti amakukonda.

14. Tingaonetse bwanji kuti timalemekeza abale na alongo amene ni mbeta?

14 Abale na alongo athu amene ni mbeta amayamikila ngati tiwakonda cifukwa ca makhalidwe awo abwino, m’malo mowamvelela cifundo. Tiyenelanso kuŵayamikila pa kukhulupilika kwawo. Tikacita zimenezi, iwo sadzamvela monga tikuŵauza kuti: “Ndilibe nanu nchito.” (1 Akor. 12:21) M’malomwake, iwo adzaona kuti mpingo umaŵalemekeza na kuŵakonda.

MUZIWALEMEKEZA AMENE SAKWANITSA KUKAMBA BWINO-BWINO CITUNDU CANU

15. Ni masinthidwe ati amene abale na alongo ena anapanga kuti awonjezele utumiki wawo?

15 M’zaka zaposacedwa, ofalitsa ambili adziikila colinga cophunzila citundu cina kuti awonjezele utumiki wawo. Kuti acite zimenezi, iwo anafunika kusintha zinthu zina mu umoyo wawo. Abale na alongo amenewo, anasiya mpingo wa citundu cawo kuti akatumikile mu mpingo wa citundu cina umene ofalitsa Ufumu ni ocepa kwambili. (Mac. 16:9) Akhristu amenewo amadzipeleka mofunitsitsa kuti apititse patsogolo nchito ya Ufumu. Ngakhale kuti mwina zingawatengele zaka kuti adziŵe kukamba bwino citundu catsopano, iwo amathandiza mpingo m’njila zambili. Makhalidwe awo abwino komanso maluso awo zimalimbikitsa mpingo. Timaŵayamikila kwambili abale na alongo odzimana amenewo!

16. Kodi akulu ayenela kupenda abale pamaziko ati kuti ayenelele kutumikila monga akulu kapena atumiki othandiza?

16 Bungwe la akulu siliyenela kulephela kuyeneleza m’bale kukhala mkulu kapena mtumiki wothandiza cabe cifukwa sakwanitsa kukamba bwino citundu ca mpingo wawo. Akulu ayenela kuyang’ana pa ziyenelezo za m’Malemba, osati kudziŵa bwino citundu ca mpingowo.—1 Tim. 3:1-10, 12, 13; Tito 1:5-9.

17. Kodi makolo amayang’anizana na mafunso ati akakukila kudziko lina?

17 Mabanja ena acikhristu amasamukila kumaiko ena cifukwa cothaŵa kwawo, kapena kukafuna nchito. Zikakhala conco, ana awo kusukulu amaphunzila citundu ca ku dzikolo. Makolo nawonso angafunikile kuphunzila citundu ca ku dzikolo kuti apeze nchito. Koma bwanji ngati m’delalo muli mpingo kapena kagulu ka citundu cawo? Kodi banjali liyenela kumasonkhana ku mpingo uti? Kodi angafunikile kupita ku mpingo wa citundu ca ku dzikolo kapena wa citundu cawo?

18. Malinga na Agalatiya 6:5, tingalemekeze bwanji cosankha ca mutu wa banja?

18 Mutu wa banja ufunika kusankha mpingo umene banja lake lizisonkhanako. Popeza iyi ni nkhani ya banja, iye afunika kupanga cosankha moganizila zimene zingapindulitse banja lake. (Ŵelengani Agalatiya 6:5.) Mulimonse mmene iye angasankhile, tiyenela kulemekeza cosankha cake na kulandila banjalo na manja aŵili mu mpingo wathu.—Aroma 15:7.

19. Kodi mitu ya mabanja ifunika kuganizila ciani mwa pemphelo?

19 Mabanja ena angakhale mu mpingo wa citundu cawo, koma mwina ana awo sacidziŵa bwino citunduco. Ngati mpingowo uli kudela limene anthu amakamba citundu ca ku dziko limene anasamukila, zingakhale zovuta kwa ana awo kumvetsela pa misonkhano na kupita patsogolo mwauzimu. Cifukwa ciani? Cifukwa ana angamapite kusukulu imene imaseŵenzetsa citundu ca ku dzikolo. Zikakhala conco, mitu ya mabanja ifunika kuganizilapo mwa pemphelo zimene angacite kuti athandize ana awo kuyandikila Yehova na gulu lake. Makolo angafunikile kuphunzitsa ana awo kuti acidziŵe bwino citundu cawo, kapena angafunikile kuganizila zokukila ku mpingo wa citundu cimene ana awo amamvetsa bwino. Zilizonse zimene mutu wa banja ungasankhe, mpingo umene asankha kupitako ufunika kuwalemekeza na kuwaona kuti ni ofunika.

Kodi tiyenela kuŵaona motani abale na alongo amene akuphunzila citundu catsopano? (Onani ndime 20)

20. Kodi tiyenela kuŵaona motani abale na alongo amene akuphunzila citundu catsopano?

20 Monga taonela, m’mipingo yambili muli abale na alongo amene akuyesetsa kuphunzila citundu catsopano pa zifukwa zosiyana-siyana. N’zoona kuti zingakhale zovuta kwa iwo kuti alankhule bwino-bwino. Koma ngati sitiyang’ana kwambili pa kalankhulidwe kawo, tidzaona cikondi cawo pa Yehova na mtima wawo wofunitsitsa kum’tumikila. Ndiyeno poona makhalidwe awo abwino amenewo, tidzawakonda na kuwalemekeza kwambili abale na alongo athu amenewo. Sitidzakamba kuti: “Ndilibe nanu nchito,” cabe cifukwa sakamba bwino-bwino citundu cathu.

NDIFE OFUNIKA KWAMBILI KWA YEHOVA

21-22. Ni mwayi waukulu uti umene tili nawo?

21 Yehova anatipatsa mwayi waukulu kwambili potiitana mu mpingo wake. Kaya ndife amuna, akazi, mbeta, okwatila, okwatiwa, acicepele, okalamba, kaya timadziŵa kukamba bwino citundu cina kapena ayi, tonsefe ndife ofunika kwambili kwa Yehova, komanso kwa wina na mnzake.—Aroma 12:4, 5; Akol. 3:10, 11.

22 Tiyeni tipitilize kuseŵenzetsa maphunzilo abwino amene tatengapo pa fanizo la Paulo la thupi la munthu. Pocita zimenezi, tidzafuna-funa mipata yolimbikitsila abale na alongo athu mu mpingo wa Yehova, na kuwalemekeza.

NYIMBO 90 Tilimbikitsane Wina na Mnzake

^ ndime 5 Anthu a Yehova amacokela ku zikhalidwe zosiyana-siyana, koma aliyense amacita mbali yake mu mpingo. Nkhani ino itithandiza kuona cifukwa cake n’kofunika kulemekeza wina aliyense mu mpingo.

^ ndime 8 Sitingakambe motsimikiza kuti Timoteyo sanakwatilepo.