Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 32

Muziyenda Modzicepetsa na Mulungu Wanu

Muziyenda Modzicepetsa na Mulungu Wanu

“Uziyenda modzicepetsa ndi Mulungu wako.”—MIKA 6:8.

NYIMBO 31 Uziyenda na Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi Davide anakamba ciani za kudzicepetsa kwa Yehova?

KODI n’koyenela kukamba kuti Yehova ni wodzicepetsa? Inde n’koyenela. Panthawi ina Davide anati: “Inu mudzandipatsa cishango canu ca cipulumutso, ndipo kudzicepetsa kwanu n’kumene kumandikweza.” (2 Sam. 22:36; Sal. 18:35) N’kutheka kuti Davide panthawiyi anali kuganizila za tsiku limene mneneli Samueli anabwela ku kunyumba kwawo kukadzoza mfumu ya Isiraeli ya m’tsogolo. Davide anali wamng’ono kwambili pa anyamata 8 a Jese, koma ndiye anasankhidwa na Yehova kuti aloŵe m’malo Mfumu Sauli.—1 Sam. 16:1, 10-13.

2. Tikambilana ciani m’nkhani ino?

2 N’zodziŵikilatu kuti Davide anali kuona Yehova monga mmene wamasalimo wina anali kumuonela. Ponena za Yehova, wamasalimoyo anati: “Iye amatsika m’munsi kuti aone kumwamba ndi dziko lapansi. Amadzutsa munthu wonyozeka kumucotsa m’fumbi. Amakweza munthu wosauka . . . kuti amukhazike pamodzi ndi anthu olemekezeka.” (Sal. 113:6-8) M’nkhani ino, coyamba tiona mfundo zina zofunika zimene tingaphunzile pa nkhani ya kudzicepetsa, mwa kukambilana mmene Yehova anaonetsela khalidweli pa zocitika zosiyana-siyana. Pambuyo pake tikambilananso zina zimene tingaphunzile pa nkhaniyi kwa mfumu Sauli, mneneli Danieli, komanso Yesu.

TINGAPHUNZILE CIANI PA CITSANZO CA YEHOVA CA KUDZICEPETSA?

3. Kodi Yehova amacita nafe zinthu motani? Nanga izi zionetsa ciani?

3 Njila imodzi imene Yehova amaonetsela kudzicepetsa ni mmene amacitila zinthu ndi anthu omwe ni opanda ungwilo. Iye watipatsa mwayi wom’lambila, ndipo kuposa pamenepo watipatsanso mwayi wokhala mabwenzi ake. (Sal. 25:14) Kuti zitheke kukhala naye paubwenzi, Yehova anapeleka mwana wake monga nsembe yotiwombola ku macimo athu. Ndithudi, Mulungu watisonyeza cifundo cacikulu!

4. Kodi Yehova anatipatsa ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

4 Onani njila ina imene Yehova waonetsela kudzicepetsa. Monga Mlengi, Yehova akanafuna sakanatilenga na ufulu wodzisankhila zocita mu umoyo. Koma anatilenga m’cifanizilo cake na kutipatsa ufulu wosankha. Iye amafuna kuti tizimutumikila mwakufuna kwathu cifukwa comukonda, komanso cifukwa cozindikila kuti kumumvela kumatipindulitsa. (Deut. 10:12; Yes. 48:17, 18) Ndife oyamikila kwambili kuti Yehova ni wodzicepetsa.

Yesu ali kumwamba. Pafupi na iye paimilila ena mwa olamulila anzake. Iwo pamodzi na Yesu akuyang’ana angelo miyanda-miyanda. Angelo ena akupita ku dziko lapansi kukacita nchito zawo. Onse amene ali pa cithunzici, Yehova anawagaŵila zocita (Onani ndime 5)

5. Kodi Yehova amatiphunzitsa bwanji kukhala odzicepetsa? (Onani cithunzi pacikuto.)

5 Yehova amatiphunzitsa kukhala odzicepetsa mwa zocita zake na ife anthu. Iye ni wanzelu kwambili kuposa aliyense m’cilengedwe conse. Ngakhale n’conco, ni wokonzeka kumvetsela maganizo a ena. Mwacitsanzo, Yehova anapatsa mwana wake mwayi wothandiza pa nchito yolenga zinthu zonse. (Miy. 8:27-30; Akol. 1:15, 16) Komanso ngakhale kuti Yehova ni wamphamvuzonse, amagaŵilako ena maudindo. Mwacitsanzo, anasankha Yesu kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Ndipo adzapatsa mwayi anthu 144 000 wolamulila pamodzi na Yesu. (Luka 12:32) Yehova anaphunzitsa Yesu kuti ayenelele kukhala Mfumu komanso Mkulu wa Ansembe. (Aheb. 5:8, 9) Amaphunzitsanso Akhristu amene adzalamulila pamodzi na Yesu, ndipo akaŵapatsa nchito sawayang’anila pa ciliconse cimene akucita pa nchitoyo, cifukwa amawadalila kuti adzacita zimene iye afuna.—Chiv. 5:10.

Timatengela citsanzo ca Yehova mwa kuphunzitsako ena nchito na kuwagaŵilako zocita (Onani ndime 6-7) *

6-7. Kodi mitu ya mabanja, akulu, komanso makolo angatengele bwanji citsanzo ca Yehova?

6 Ngati Atate wathu wakumwamba amene safunikila thandizo la wina aliyense amagaŵilako ena zocita, kuli bwanji ife? Mwacitsanzo, kodi ndinu mutu wa banja kapena mkulu mumpingo? Ngati n’conco, tengelani citsanzo ca Yehova mwa kugaŵilako ena zocita na kupewa kuwayang’anila pa ciliconse cimene akucita pa nchitoyo. Mukatengela citsanzo ca Yehova, nchito idzayenda komanso mudzathandiza ena kuphunzila nchitoyo. Kuwonjezela apo, mudzawathandiza kukhala na cidalilo pa nchitoyo. (Yes. 41:10) N’ciani cina cimene anthu amene ali paudindo angaphunzile kwa Yehova?

7 Baibo imaonetsa kuti Yehova amamvetsela maganizo a angelo. (1 Maf. 22:19-22) Makolo, kodi mungatengele bwanji citsanzo ca Yehova? Ngati m’poyenela, mungafunse ana anu kuti mudziŵe maganizo awo ponena za nchito inayake imene mufuna kugwila. Ngati malingalilo awo ali bwino, mungawagwilitsile nchito.

8. Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuleza mtima pocita zinthu na Abulahamu komanso Sara?

8 Njila ina imene Yehova amaonetsela kuti ni wodzicepetsa, ni mwa kukhala woleza mtima. Mwacitsanzo, iye amacita zinthu moleza mtima na atumiki ake ngati mwaulemu akayikila zosankha zake. Yehova atatsala pang’ono kuwononga mizinda ya Sodomu na Gomora, Abulahamu anadela nkhawa ndipo Yehova anamvetsela nkhawa zake. (Gen. 18:22-33) Komanso kumbukilani mmene Yehova anacitila zinthu na Sara, mkazi wa Abulahamu. Iye sanakhumudwe kapena kukwiya pamene Sara anaseka atamva lonjezo lake lakuti adzakhala na mwana mu ukalamba wake. (Gen. 18:10-14) Koma anakamba naye mwaulemu.

9. Kodi makolo komanso akulu mumpingo angaphunzile ciani pa citsanzo ca Yehova ca kudzicepetsa?

9 Kodi imwe makolo na akulu mumpingo, mungaphunzilepo ciani pa citsanzo ca Yehova cimeneci? Kodi mumacita bwanji ngati anthu amene mumawayang’anila sanagwilizane na zosankha zanu? Kodi mumathamangila kuwadzudzula kapena mumayesetsa kumvetsetsa maganizo awo? Kukamba zoona, m’mipingo na m’mabanja zinthu zimayenda bwino kwambili komanso mumakhala cimwemwe ngati anthu amene ali na udindo amatengela citsanzo ca Yehova. Pofika pano, takambilana zimene tingaphunzile kwa Yehova pa nkhani ya kudzicepetsa. Tsopano tiyeni tione zimene tingaphunzile pa nkhaniyi kwa atumiki a Mulungu ochulidwa m’Baibo.

KODI TINGAPHUNZILE CIANI PA ZITSANZO ZA ANTHU ENA OCHULIDWA M’BAIBO?

10. Kodi Yehova amatiphunzitsa bwanji kupitila m’zitsanzo za ena?

10 Monga ‘Mlangizi wathu Wamkulu,’ Yehova anatipatsa zitsanzo za m’Baibo n’colinga cakuti tiphunzilepo kanthu. (Yes. 30:20, 21) Timaphunzila zambili mwa kusinkha-sinkha nkhani za m’Baibo za anthu amene anaonetsa makhalidwe abwino, kuphatikizapo khalidwe la kudzicepetsa. Timaphunzila zambili tikaŵelenga zitsanzo za anthu amene analephela kuonetsa makhalidwe abwino monga kudzicepetsa.—Sal. 37:37; 1 Akor. 10:11.

11. Kodi titengapo phunzilo lotani pa citsanzo coticenjeza ca Sauli?

11 Ganizilani zimene zinacitikila Mfumu Sauli. Poyamba iye anali mnyamata wodzicepetsa. Iye anadziŵa kuti panali zinthu zina zimene sakanakwanitsa kucita, ndipo anayopa kulandila udindo wokhala mfumu. (1 Sam. 9:21; 10:20-22) Koma m’kupita kwa nthawi, Sauli anayamba kudzikuza. Khalidwe la kudzikuza limeneli linaonekela atangokhala mfumu. Mwacitsanzo, pa nthawi ina iye analephela kuugwila mtima pamene anali kuyembekezela mneneli Samueli. M’malo modalila Yehova kuti adzateteza anthu ake, Sauli anapeleka nsembe yopseleza olo kuti sunali udindo wake kucita zimenezo. Zotulukapo zake zinali zakuti Yehova analeka kumuyanja Sauli, ndipo m’kupita kwa nthawi anam’kana kuti asakhale mfumu. (1 Sam. 13:8-14) Tingacite bwino kuphunzilapo kanthu pa citsanzo coticenjeza cimeneci mwa kupewa kucita zinthu modzikuza.

12. Kodi Danieli anaonetsa bwanji kudzicepetsa?

12 Mosiyana ndi citsanzo coipa ca Sauli, tsopano ganizilani citsanzo cabwino ca mneneli Danieli. Kwa moyo wake wonse, Danieli anali wodzicepetsa ndipo nthawi zonse anali kupempha Yehova kuti amutsogolele. Mwacitsanzo, pamene Yehova anamuseŵezetsa pomasulila maloto a Nebukadinezara, Danieli sanadzitame kuti anakwanitsa kucita zimenezo mwa nzelu zake. M’malomwake, anapeleka ulemelelo wonse kwa Yehova. (Dan. 2:26-28) Kodi tiphunzilapo ciani pamenepa? Ngati abale amatiyamikila cifukwa ca mmene timakambila nkhani kapena ngati zinthu zimatiyendela bwino mu ulaliki, tifunika kupeleka ulemelelo wonse kwa Yehova. Tifunika kuzindikila kuti popanda thandizo lake sitingakwanitse kucita zimenezi. (Afil. 4:13) Tikatelo, ndiye kuti tikutengela citsanzo cabwino ca Yesu. Motani?

13. Kodi zimene Yesu anakamba pa Yohane 5:19, 30 zitiphunzitsa ciani pa nkhani ya kudzicepetsa?

13 Yesu anali kudalila Yehova olo kuti anali mwana wangwilo wa Mulungu. (Ŵelengani Yohane 5:19, 30.) Iye sanayese kulanda ulamulilo Atate wake wakumwamba. Afilipi 2:6 imakamba za Yesu kuti: “Kukhala wolingana ndi Mulungu sanakuganizilepo ngati cinthu coti angalande.” Pokhala mwana wogonjela, Yesu anali kudziŵa kuti panali zinthu zina zimene sakanakwanitsa kucita, ndipo anali kulemekeza ulamulilo wa Atate wake.

Yesu anali kuzindikila malile a udindo wake, ndipo sanacite zinthu zimene sunali udindo wake kucita (Onani ndime 14)

14. Kodi Yesu anayankha bwanji atapemphedwa kucita zinthu zimene sunali udindo wake?

14 Ganizilani mmene Yesu anayankhila pamene ophunzila ake Yakobo na Yohane, anabwela kwa iye pamodzi na amayi ŵawo, na kum’pempha cinacake cimene sunali udindo wake kuwapatsa. Mosazengeleza, Yesu anawayankha kuti Atate wake wakumwamba ndiwo okha ali na mphamvu yosankha amene adzakhala ku dzanja lake la manja na lamanzele mu Ufumu wa Mulungu. (Mat. 20:20-23) Apa Yesu anaonetsa kuti anali kuzindikila zinthu zimene sunali udindo wake kucita. Iye anali wodzicepetsa. Sanayese ngakhale pang’ono kucita zimene Yehova sanamulamule kucita. (Yoh. 12:49) Kodi tingatengele bwanji citsanzo cabwino cimeneci ca Yesu?

Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu ca kudzicepetsa? (Onani ndime 15-16) *

15-16. Kodi tingaseŵenzetse bwanji malangizo a pa 1 Akorinto 4:6?

15 Timatengela citsanzo ca Yesu ca kudzicepetsa mwa kutsatila malangizo a m’Baibo a pa 1 Akorinto 4:6. Lembali limati: “Musapitilile zinthu zolembedwa.” Conco ngati ena atipempha malangizo, tiyenela kupewa kuwakakamiza kutsatila maganizo athu kapena kungowayankha popanda kuganizilapo mosamala pa nkhaniyo. M’malomwake, tiyenela kuwaunikila malangizo a m’Baibo komanso a m’zofalitsa zathu. Tikatelo, tidzaonetsa kuti timazindikila zinthu zimene si udindo wathu kucita. Tidzaonetsanso kuti ndife odzicepetsa, ndipo timazindikila kuti ‘malamulo olungama’ a Mulungu Wamphamvuzonse ndiwo abwino kwambili kuposa maganizo athu.—Chiv. 15:3, 4.

16 Timaonetsa kudzicepetsa cifukwa timafuna kulemekeza Yehova. Koma palinso zifukwa zina. Tsopano tiona mmene kudzicepetsa kungatithandizile kuti tizikhala acimwemwe komanso mmene kungatithandizile kuti tizikhala bwino na ena.

KODI TIMAPINDULA BWANJI TIKAKHALA ODZICEPETSA?

17. N’cifukwa ciani anthu odzicepetsa nthawi zambili amakhala acimwemwe?

17 Anthu odzicepetsa nthawi zambili amakhala acimwemwe. N’cifukwa ciani zimakhala conco? Cifukwa anthu odzicepetsa amazindikila zimene sangakwanitse kucita, ndipo amayamikila thandizo iliyonse imene ena angaŵapatse. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitika pamene Yesu anacilitsa anthu 10 akhate. Pa anthu 10 amenewo, ni mmodzi yekha amene anabwelela kwa Yesu kukamuyamikila cifukwa comucilitsa matenda ake oopsawo. Munthu wodzicepetsa ameneyu anazindikila kuti payekha sakanatha kudzicilitsa. Conco anayamikila thandizo limene analandila, ndipo anatamanda Mulungu.—Luka 17:11-19.

18. Kodi kudzicepetsa kumatithandiza bwanji kuti tizikhala bwino na ena? (Aroma 12:10)

18 Nthawi zambili anthu odzicepetsa amakhala bwino na ena ndiponso amapanga ubwenzi wolimba na ena. Cifukwa ciani? Cifukwa modzicepetsa amazindikila kuti anthu ena ali na makhalidwe abwino ndipo amayamba kuwadalila. Anthu odzicepetsa amakondwela ngati ena zinthu zikuwayendela bwino mu utumiki wawo ndipo sazengeleza kuwayamikila na kuwalemekeza.—Ŵelengani Aroma 12:10.

19. Fotokozani zifukwa zina zimene tiyenela kupewela khalidwe la kudzikuza?

19 Mosiyana ndi anthu odzicepetsa, anthu odzikuza cimawavuta kuyamikila ena, amafuna kuti iwo ndiwo azitamandidwa. Amakonda kudziyelekezela na ena komanso amalimbikitsa mzimu wa mpikisano. M’malo mophunzitsako ena nchito na kuwapatsa udindo, amagwila okha nchitoyo poganiza kuti ena sangaigwile bwino mmene iwo amafunila. Munthu wodzikuza amadziona wapamwamba kuposa ena, ndipo amacitila nsanje anthu amene amacita bwino kuposa iye. (Agal. 5:26) Nthawi zambili anthu otelo sapanga ubwenzi wolimba na ena. Tikazindikila kuti tiliko na vuto la kudzikuza, tiyenela kupemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima kuti atithandize kusintha maganizo athu, n’colinga cakuti khalidwe limeneli lisazike mizu mumtima mwathu.—Aroma 12:2.

20. N’cifukwa ciani tiyenela kukhala odzicepetsa?

20 Ndife oyamikila ngako kuti Yehova watipatsa citsanzo cabwino pa nkhani ya kudzicepetsa! Timaona kudzicepetsa kwake tikaganizila mmene amacitila zinthu na atumiki ake, ndipo timafuna kutengela citsanzo cake. Kuwonjezela apo, timafuna kutengela zitsanzo zabwino za anthu odzicepetsa ochulidwa m’Baibo, amene anali na mwayi woyenda na Mulungu. Tiyeni nthawi zonse tizipeleka ulemelelo kwa Yehova cifukwa iye ndiye woyenela kulandila ulemu na ulemelelo. (Chiv. 4: 11) Tikatelo, tidzakhala na mwayi woyenda na Atate wathu wakumwamba, amene amakonda anthu odzicepetsa.

NYIMBO 123 Gonjelani Dongosolo la Mulungu

^ ndime 5 Munthu wodzicepetsa amakhala wacifundo. Conco, m’pomveka kukamba kuti Yehova ni wodzicepetsa. M’nkhani ino, tikambilana zimene tingaphunzile kwa Yehova pa nkhani ya kudzicepetsa. Tikambilananso zina zimene tingaphunzile pa nkhani ya kudzicepetsa kwa Mfumu Sauli, mneneli Danieli, komanso Yesu..

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mkulu akuphunzitsa m’bale wacinyamata nchito yosamalila magawo a mpingo. M’kupita kwa nthawi, mkuluyo akumulola m’bale wacinyamatayo kugwila yekha nchitoyo popanda kumuyang’anila pa ciliconse cimene akucita.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo akufunsila malangizo kwa mkulu kuti adziŵe ngati n’koyenela kukapezeka pa cikwati cocitikila m’chechi. M’malo mofotokoza maganizo ake, mkuluyo akuonetsa mlongoyo mfundo za m’Baibo zimene angatsatile.