Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 34

Na Imwe Muli na Malo mu Mpingo wa Yehova!

Na Imwe Muli na Malo mu Mpingo wa Yehova!

“Mofanana ndi thupi lomwe ndi limodzi koma lili ndi ziwalo zambili, ndipo ziwalo zonse za thupi, ngakhale ndi zambili, zimapanga thupi limodzi, ndi mmenenso Khristu alili.”—1 AKOR. 12:12.

NYIMBO 101 Tisunge Umodzi Wathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi ni mwayi wanji umene tili nawo?

NI MWAYI waukulu cotani nanga kukhala ciwalo ca mpingo wa Yehova! Tili m’paradaiso wauzimu wa anthu amtendele komanso acimwemwe. Kodi muli na malo otani mu mpingo?

2. Kodi ni fanizo lotani limene mtumwi Paulo anaseŵenzetsa m’makalata ake angapo ouzilidwa?

2 Ponena za malo amene tili nawo mu mpingo, tingaphunzile zambili pa fanizo limene mtumwi Paulo anaseŵenzetsa m’makalata ake angapo ouzilidwa. Mu iliyonse ya makalatawo, Paulo anayelekezela mpingo na thupi la munthu. Anayelekezelanso ofalitsa mu mpingo na ziwalo za thupi.—Aroma 12:4-8; 1 Akor. 12:12-27; Aef. 4:16.

3. Ni maphunzilo atatu ati amene tikambilane m’nkhani ino?

3 M’nkhani ino, tikambilana maphunzilo atatu ofunika amene tingatengepo pa fanizo la Paulo. Coyamba, tidzaona kuti aliyense wa ife ali na malo * mu mpingo wa Yehova. Caciŵili, tikambilane zimene tingacite ngati zimativuta kuona malo athu mu mpingo. Ndipo cacitatu, tione cifukwa cake tiyenela kukangalika pocita mbali yathu mu mpingo.

ALIYENSE WA IFE ALI NA MBALI YOCITA MU MPINGO WA YEHOVA

4. Kodi Aroma 12:4, 5 itiphunzitsa ciani?

4 Phunzilo loyamba limene tingatengepo pa fanizo la Paulo, n’lakuti aliyense wa ife amacita mbali yofunika m’banja la Yehova. Paulo anayamba fanizo lake pokamba kuti: “Monga tilili ndi ziwalo zambili m’thupi limodzi, koma ziwalozo sizigwila nchito yofanana, momwemonso ifeyo, ngakhale kuti ndife ambili, tili thupi limodzi mwa Khristu, ndipo aliyense payekha ndi ciwalo ca mnzake.” (Aroma 12:4, 5) Kodi mfundo ya Paulo inali iti? Inali yakuti aliyense wa ife ali na mbali yake mu mpingo, ndipo aliyense ni wofunika.

Timacita mbali zosiyana mu mpingo, koma aliyense wa ife ni wofunika (Onani ndime 5-12) *

5. Kodi Yehova wapeleka “mphatso” zotani mu mpingo?

5 Mukaganizila za amene ali na malo mu mpingo, maganizo anu angathamangile kwa abale amene amatsogolela. (1 Ates. 5:12; Aheb. 13:17) N’zoona kuti mwa Khristu, Yehova wapeleka “mphatso za amuna” mu mpingo wake. (Aef. 4:8) “Mphatso za amuna” zimenezi ziphatikizapo a m’Bungwe Lolamulila, abale othandizila Bungwe Lolamulila, a m’Komiti ya Nthambi, oyang’anila madela, alangizi a masukulu, akulu mu mpingo, komanso atumiki othandiza. Abale onsewa amaikidwa na mzimu woyela kuti asamalile nkhosa za Yehova zamtengo wapatali, na kulimbikitsa mpingo.—1 Pet. 5:2, 3.

6. Malinga na 1 Atesalonika 2:6-8, kodi abale oikidwa na mzimu woyela amayesetsa kucita ciani?

6 Abale amaikidwa na mzimu woyela kuti asamalile maudindo osiyana-siyana. Ziwalo za thupi monga manja na miyendo, zimagwila nchito kuti thupi lonse lipindule. Mofananamo, nawonso abale oikidwa paudindo na mzimu woyela amagwila nchito mwakhama kuti apindulitse mpingo wonse. Iwo sadzifunila ulemelelo. M’malomwake, amayesetsa kulimbikitsa abale na alongo awo. (Ŵelengani 1 Atesalonika 2:6-8.) Timayamikila Yehova potipatsa amuna amenewa oyenelela mwauzimu, komanso osadzikonda.

7. Kodi ambili amene ali mu utumiki wanthawi zonse amalandila madalitso otani?

7 Ena mu mpingo angaikidwe kukhala amishonale, apainiya apadela, kapena apainiya a nthawi zonse. Ndipo kuzungulila dziko lonse, abale na alongo ambili atenga kulalikila na kupanga ophunzila kukhala nchito yawo. Mwa ici, iwo athandiza ambili kukhala ophunzila a Khristu Yesu. Ngakhale kuti alengezi a nthawi zonse amenewa amakhala na zocepa kuthupi, iwo alandila madalitso ambili ocokela kwa Yehova mu umoyo wawo. (Maliko 10:29, 30) Timawakonda kwambili abale na alongo amenewa, ndipo ndife okondwa kuti ni ziwalo za mpingo!

8. N’cifukwa ciani wofalitsa uthenga wabwino aliyense ni wofunika kwambili kwa Yehova?

8 Kodi abale apaudindo na atumiki a nthawi zonse, ndiwo okha ali na malo mu mpingo? Kutali-tali! Wofalitsa uthenga wabwino aliyense ni wofunika kwa Mulungu komanso ku mpingo. (Aroma 10:15; 1 Akor. 3:6-9) Ndipo cimodzi mwa zolinga zazikulu za mpingo ni kupanga ophunzila a Ambuye wathu Yesu Khristu. (Mat. 28:19, 20; 1 Tim. 2:4) Ofalitsa onse mu mpingo, obatizika na osabatizika, amaika patsogolo nchitoyi mu umoyo wawo.—Mat. 24:14.

9. N’cifukwa ciani tiyenela kuona alongo athu kukhala ofunika?

9 Yehova amalemekeza alongo poŵapatsa malo mu mpingo. Iye amaona akazi okwatiwa, amayi, akazi amasiye, komanso alongo osakwatiwa amene amam’tumikila mokhulupilika kuti ni ofunika. Malemba amachula akazi ambili amene anakondweletsa Mulungu. Iwo amachulidwa monga zitsanzo zabwino kwambili pa nzelu, cikhulupililo, cangu, kulimba mtima, kuwolowa manja, komanso pa nchito zabwino. (Luka 8:2, 3; Mac. 16:14, 15; Aroma 16:3, 6; Afil. 4:3; Aheb. 11:11, 31, 35) Ha! Ndife oyamikila cotani nanga kwa Yehova, kaamba ka akazi acikhristu amene tili nawo m’mipingo yathu—inde, akazi amene alinso na makhalidwe abwino!

10. N’cifukwa ciani tiyenela kuona okalamba athu kukhala ofunika?

10 Ndifenso odalitsika kukhala na okalamba ambili. Mipingo ina, ili na abale na alongo okalamba amene atumikila Yehova mokhulupilika moyo wawo wonse. Palinso okalamba ena amene mwina anaphunzila coonadi caposacedwa. Mulimonsemo, onsewa angamakumane na mavuto osiyana-siyana okhudza thanzi cifukwa ca ukalamba. Mavutowo angawalepheletse kucita zambili mu mpingo, komanso pa nchito yolalikila. Ngakhale n’conco, okalamba amenewa amacita zimene angathe pa nchito yolalikila, ndipo mwamphamvu zawo zocepazo, amacitabe khama pa kulimbikitsa na kuphunzitsa ena mocitila zinthu. Ndiponso timapindula na cidziŵitso cawo. Iwo ni okongoladi kwa Yehova, komanso kwa ife.—Miy. 16:31.

11-12. Kodi mumalimbikitsidwa bwanji na acicepele mu mpingo mwanu?

11 Ganizilaninso za acicepele athu. Pamene akukula, amakumana na mavuto osiyana-siyana m’dzikoli lolamulidwa na Satana Mdyelekezi, komanso losonkhezeledwa na maganizo ake oipa. (1 Yoh. 5:19) Ngakhale n’telo, tonsefe timalimbikitsidwa poona acicepele athu akupeleka ndemanga pa misonkhano, kutengako mbali mu ulaliki, komanso kuteteza cikhulupililo cawo molimba mtima. Inde, na imwe acicepele muli na malo mu mpingo wa Yehova!—Sal. 8:2.

12 Komabe, pali abale na alongo athu ena amene amakayikila ngati alidi ofunika mu mpingo. Kodi n’ciani cingathandize aliyense wa ife kuona kuti ni wofunika mu mpingo? Tiyeni tione.

MUZIDZIONA KUTI NDIMWE WOFUNIKA MU MPINGO

13-14. N’ciani cingapangitse ena kudziona kuti ni osafunika mu mpingo?

13 Onani phunzilo laciŵili limene tingatengepo pa fanizo la Paulo. Iye anafotokoza vuto limene ambili ali nalo masiku ano. Iwo amakayikila ngati alidi ofunika mu mpingo. Paulo analemba kuti: “Ngati phazi linganene kuti: ‘Popeza sindine dzanja, sindili mbali ya thupi,’ cimeneco si cifukwa copangitsa phazi kusakhala mbali ya thupi. Ndipo ngati khutu linganene kuti: ‘Popeza sindine diso, sindili mbali ya thupi,’ cimeneco si cifukwa copangitsa khutu kusakhala mbali ya thupi.” (1 Akor. 12:15, 16) Kodi Paulo anafuna kumveketsa mfundo yanji pamenepa?

14 Ngati muyesa kudzilinganiza na ena mu mpingo, mudzayamba kudziona kuti ndinu wosafunika. Ena mu mpingo angakhale aphunzitsi aluso, adongosolo, kapena abusa aluso polimbikitsa ena. Mwina mumaona kuti imwe simungafike pa mlingo umenewo. Kumeneko kungakhale kudzicepetsa. (Afil. 2:3) Koma samalani. Ngati nthawi zonse mumadziyelekezela ndi ena amene ali na maluso kuposa imwe, mungakhumudwe na kulefuka. Mungafike poona kuti ndimwe osafunikila mu mpingo, monga taonela m’citsanzo ca Paulo. Kodi n’ciani cingakuthandizeni kuthetsa maganizo amenewo?

15. Malinga na 1 Akorinto 12:4-11, kodi tiyenela kukumbukila ciani pa mphatso zilizonse zimene tingakhale nazo?

15 Ganizilani mfundo iyi: Yehova anapeleka mphatso zozizwitsa za mzimu woyela kwa Akhristu ena a m’nthawi ya atumwi. Koma sikuti Akhristu onse analandila mphatso zofanana ayi. (Ŵelengani 1 Akorinto 12:4-11.) Yehova anawapatsa mphatso na maluso osiyana-siyana, koma aliyense wa iwo anali wofunika. Lelolino, sitilandila mphatso zozizwitsa za mzimu woyela. Ndipo monga zinalili kalelo, masiku anonso tingakhale na maluso osiyana-siyana, koma tonsefe ndife ofunika kwa Yehova.

16. Kodi tifunika kuseŵenzetsa uphungu uti wa mtumwi Paulo?

16 M’malo modziyelekezela na Akhristu ena, tifunika kuseŵenzetsa uphungu wouzilidwa wa mtumwi Paulo. Iye anati: “Aliyense payekha ayese nchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatelo adzakhala ndi cifukwa cosangalalila ndi nchito yake, osati modziyelekezela ndi munthu wina.”—Agal. 6:4.

17. Kodi tingapindule bwanji ngati titsatila uphungu wa Paulo?

17 Tikatsatila uphungu wouzilidwa wa Paulo na kupenda zimene timacita, tingayambe kuona kuti nafenso tili na mphatso na maluso athu. Mwacitsanzo, mkulu angakhale alibe mphatso yophunzitsa papulatifomu, koma angakhale waluso kwambili pa nchito yopanga ophunzila. Kapena angakhale wopanda dongosolo kweni-kweni kusiyana na akulu ena mu mpingo wake, koma angakhale m’busa wacikondi, ndipo ofalitsa amamasuka kum’fikila na kufunsila malangizo a m’Malemba. Kapenanso amadziŵika kuti ni woceleza. (Aheb. 13:2, 16) Ngati timatha kuona mphatso na maluso amene tili nawo, tidzakhala okhutila na zimene timacita pocilikiza mpingo. Ndipo sitidzacitila kaduka abale athu amene ali na mphatso zimene n’zosiyana na zathu.

18. Kodi tingakulitse bwanji maluso athu?

18 Kaya tikhale na malo otani mu mpingo, tonse tiyenela kuyesetsa kuwongolela utumiki wathu, na kukulitsa maluso athu. Potithandiza kucita zimenezi, Yehova amapeleka maphunzilo abwino kupitila m’gulu lake. Mwacitsanzo, pa misonkhano ya mkati mwa wiki timapatsidwa malangizo a mmene tingakhalile aluso mu utumiki wathu. Kodi timayesetsa kuseŵenzetsa malangizo amenewo?

19. Kodi mungacite ciani kuti mukwanilitse colinga coloŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu?

19 Maphunzilo ena abwino kwambili ni Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Amene amaloŵa sukuluyi ni abale na alongo amene ali mu utumiki wanthawi zonse, a zaka za pakati pa 23 na 65. Mwina mungaone kuti kwa imwe n’zosatheka kuloŵa sukulu imeneyi. Conco, m’malo moyang’ana pa zifukwa zimene zingakuletseni kuloŵa sukuluyi, bwanji osayang’ana pa zifukwa zimene mufuna kuloŵela sukuluyi? Ndiyeno pangani pulogilamu imene idzakuthandizani kukwanilitsa ziyenelezo za sukuluyi. Na thandizo la Yehova komanso khama lanu, zimene zinaoneka monga zosatheka poyamba, zingatheke.

SEŴENZETSANI MPHATSO ZANU PA KULIMBIKITSA MPINGO

20. Kodi tiphunzilapo ciani pa Aroma 12:6-8?

20 Phunzilo lacitatu limene tingatengepo pa fanizo la Paulo, lipezeka pa Aroma 12:6-8. (Ŵelengani.) Palembali, Paulo akuonetsanso kuti munthu aliyense mu mpingo ali na mphatso zake. Koma tsopano akugogomeza mfundo yakuti tiyenela kuseŵenzetsa mphatso zathuzo kulimbikitsila mpingo.

21-22. Kodi tingaphunzile ciani kwa m’bale Robert na Felice?

21 Ganizilani citsanzo ca m’bale wina amene timuchule kuti Robert. Pambuyo potumikila kudziko lina, iye anauzidwa kuti akatumikile pa Beteli ya m’dziko la kwawo. Abale anam’tsimikizila kuti kusinthidwa kwa utumiki wake sikunali cifukwa cakuti sanali kucita bwino. Ngakhale n’conco, iye anati: “Maganizo odziona kuti n’nali wolephela, n’nakhalabe nawo kwa miyezi yambili. Nthawi zina, n’nali kufuna kungoleka utumiki wa pa Beteli.” Kodi anapezanso bwanji cimwemwe? Mkulu mnzake anam’kumbutsa kuti utumiki uliwonse umene Yehova anatiphunzitsa kumbuyoku, unatikonzekeletsa kuti ticite bwino utumiki umene tili nawo palipano. M’bale Robert anaona kufunika koleka kuganizila zakumbuyo, na kusumika maganizo pa zimene angacite palipano.

22 M’bale Felice Episcopo nayenso anakumana na vuto lolinganako. Iye na mkazi wake atatsiliza maphunzilo a Giliyadi mu 1956, anakatumikila monga wadela ku Bolivia. Mu 1964, iwo anakhala na mwana. M’bale Felice anati: “Zinali zovuta kusiya utumiki wathu cifukwa tinali kuukonda kwambili. Tsopano, nikuona kuti n’nangotaya nthawi yanga kumadzimvela cisoni kwa pafupi-fupi caka cathunthu. Koma na thandizo la Yehova, n’nasintha kapenyedwe ka zinthu, na kuyamba kusamalila udindo wanga watsopano monga kholo.” Kodi zofanana na zimene zinacitika kwa m’bale Robert na Felice zinakucitikilamponi? Kodi mumalefulidwa cifukwa mulibenso mautumiki amene munali nawo kumbuyoku? Ngati zili conco, mungacite bwino kusintha kapenyedwe kanu na kusumika maganizo pa zimene mungacite palipano potumikila Yehova na abale anu. Mukatelo, mudzakhala wacimwemwe. Cina, kangalikani pa kuseŵenzetsa mphatso na maluso anu pa kuthandiza ena. Mudzapezadi cimwemwe pamene mulimbikitsa mpingo.

23. Kodi tiyenela kumapatula nthawi yocita ciani? Nanga tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

23 Aliyense wa ife ni wofunika kwa Yehova. Iye amafuna kuti tizidzimva kuti ndife ofunika m’banja lake. Tikamapatula nthawi yoganizila zimene tingacite kuti tilimbikitse abale na alongo athu, na kucitadi zimenezo, sitidzakhalanso na maganizo odziona kuti ndife osafunika mu mpingo! Nanga bwanji za mmene timaonela ena mu mpingo? Tingaonetse bwanji kuti timaŵaona kuti ni ofunika? M’nkhani yathu yokonkhapo, tidzakambilana nkhani yofunika imeneyi.

NYIMBO 24 Bwelani ku Phili la Yehova

^ ndime 5 Aliyense wa ife amafuna kuona kuti Yehova amamukonda. Koma nthawi zina, tingakayikile zakuti Yehova amatikonda. Nkhani ino, itithandiza kuona kuti aliyense wa ife ni wofunika mu mpingo.

^ ndime 3 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Malo amene tili nawo mu mpingo wa Yehova, atanthauza mbali imene timacita polimbikitsa mpingo. Ndipo malo amenewa sadalila mtundu, fuko, cuma, banja, miyambo, kapena maphunzilo amene tili nawo.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Zithunzi zitatuzo zionetsa zimene zimacitika msonkhano wa pa mpingo usanayambe, uli mkati, komanso ukatha. Cithunzi coyamba: Mkulu apatsa mlendo moni mwacimwemwe, m’bale wacinyamata akonza zolankhulila, ndiponso mlongo aceza na mlongo wokalamba. Caciŵili: Acikulile na acicepele omwe, akupeleka ndemanga pa Phunzilo la Nsanja ya Mlonda. Cacitatu: Okwatilana athandiza kuyeletsa mu Nyumba ya Ufumu. Mayi athandiza mwana wake kuika copeleka m’bokosi la zopeleka. M’bale wacinyamata asamalila mabuku, komanso m’bale alimbikitsa mlongo wokalamba.