Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 31

Kodi Mudzayembekezela Yehova Moleza Mtima?

Kodi Mudzayembekezela Yehova Moleza Mtima?

“Ndidzayembekezela moleza mtima.”—MIKA 7:7.

NYIMBO 128 Pilila Mpaka Mapeto

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Kodi tikambilane ciani m’nkhani ino?

KODI mungamvele bwanji ngati katundu amene mufunitsitsa kulandila sanafike panthawi imene munali kuyembekezela? Mungakhumudwe, si conco kodi? Miyambo 13:12 imakamba mosapita m’mbali kuti: “Cinthu cimene unali kuyembekeza cikalepheleka, cimadwalitsa mtima.” Koma bwanji ngati mwadziŵa cifukwa cake katunduyo sanafike panthawi yake? Zikakhala conco, mumayembekezelabe moleza mtima.

2 M’nkhani ino, tikambilane mfundo zingapo za m’Baibo zimene zingatithandize ‘kuyembekezela moleza mtima.’ (Mika 7:7) Kenaka, tikambilane mbali ziŵili zimene zifuna kuti tiyembekezele Yehova moleza mtima kuti acitepo kanthu. Cotsilizila, tiona madalitso amene anthu oyembekezela pa Yehova adzapeza.

MFUNDO ZA M’BAIBO ZOTIPHUNZITSA KULEZA MTIMA

3. Kodi mfundo ya pa Miyambo 21:5 itiphunzitsa ciani?

3 Mfundo yoonetsa kufunika koleza mtima ili pa Miyambo 21:5. Pamati: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulila, koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.” N’kwanzelu kucita zinthu moleza mtima, ciliconse panthawi yake.

4. Ni mfundo yotani imene tipeza pa Miyambo 4:18?

4 Miyambo 4:18 imatiuza kuti, “njila ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kumene kumamka kuwonjezeleka mpaka tsiku litakhazikika.” Lembali, lionetsa bwino mmene Yehova amathandizila anthu ake kumvetsa colinga cake mwa pang’ono-pang’ono. Limagwilanso nchito poonetsa mmene Mkhristu amapitila patsogolo kuuzimu. Kukula mwauzimu safulumizitsa, kumatenga nthawi. Tiyenela kuŵelenga Mawu a Mulungu mwakhama na kuseŵenzetsa malangizo ake, komanso ocokela ku gulu lake. Tikatelo, pang’ono-m’pang’ono tidzayamba kukulitsa makhalidwe amene Khristu anali nawo. Kuwonjezela apo, cidziŵitso cathu ponena za Mulungu cidzawonjezeleka. Onani mmene Yesu anamveketsela mfundo imeneyi.

Monga mmene mbewu imakulila mwa pang’ono-pang’no, nayenso munthu amene wamvela na kulandila uthenga wa Ufumu amakula mwauzimu pang’ono-pang’ono (Onani ndime 5)

5. Kodi Yesu anafotokoza fanizo lanji poonetsa mmene kukula mwauzimu kumacitikila?

5 Yesu anafotokoza fanizo la kanjele kakang’ono, poonetsa mmene uthenga wa Ufumu umene timalalikila umakulila m’mitima ya anthu a maganizo abwino. Iye anati: “Mbewuzo zimamela ndi kukula. Koma mmene zimenezi zimacitikila, mwiniwakeyo [wobyala] sadziwa ayi. Pang’onopang’ono, payokha nthaka ija imabala zipatso. Coyamba mmela umabiliwila, kenako umatulutsa ngala, pamapeto pake maso okhwima a tiligu amaonekela m’ngalamo.” (Maliko 4:27, 28) Kodi Yesu anali kufuna kumveketsa mfundo yotani? Iye anali kufotokoza kuti monga mmene mbewu imakulila pang’ono-pang’ono, nayenso munthu amene walandila uthenga wa Ufumu amakula kuuzimu mwapang’ono-pang’ono. Mwacitsanzo, maphunzilo athu a Baibo akamayandikila Yehova, timatha kuona kuti iwo akupanga masinthidwe mu umoyo wawo. (Aef. 4:22-24) Koma tizikumbukila kuti Yehova ndiye amacititsa kanjele kakang’onoko kukula.—1 Akor. 3:7.

6-7. Kodi tiphunzilapo ciani tikaona mmene Yehova analengela dziko lapansi?

6 Pa zonse zimene amacita, Yehova moleza mtima amakhala na nthawi yokwanila kuti atsilize nchito yake. Amacita zimenezi kuti dzina lake lilemekezedwe, komanso kuti apindulitse anthu. Mwacitsanzo, ganizilani mmene Yehova mwapang’ono-pang’ono analengela dziko lapansi kuti anthu azikhalamo.

7 Pofotokoza mmene Yehova analengela dziko lapansi, Baibo imakamba kuti iye “anaika miyezo yake, “maziko ake,” komanso “mwala wake wapakona.” (Yobu 38:5, 6) Iye anatenganso nthawi yoyang’ana zinthu zimene analenga. (Gen. 1:10, 12) Ganizilani mmene angelo anamvelela atayamba kuona zinthu zimene Yehova anali kulenga. Iwo ayenela kuti anakondwela ngako na zimenezi! Ndipo pa nthawi ina, iwo “anayamba kufuula ndi cisangalalo.” (Yobu 38:7) Kodi tiphunzilaponji pamenepa? Tiphunzilapo kuti Yehova anatenga zaka masauzande kuti atsilize kulenga zinthu zonse. Ndipo atayang’ana zonse zimene analenga mwaluso, iye anaona kuti “zinali zabwino kwambili.”—Gen. 1:31.

8. Tikambilana ciani tsopano?

8 Monga taonela pa zitsanzo zimene takambilana, tingapeze mfundo zambili m’Mawu a Mulungu, zimene zimationetsa kufunika kokhala oleza mtima. Tsopano, tiyeni tikambilane mbali ziŵili zofuna kuti tiziyembekezela pa Yehova moleza mtima.

NI PA ZOCITIKA ZITI PAMENE TIYENELA KUYEMBEKEZELA YEHOVA?

9. Ni pa cocitika citi pamene tiyenela kuyembekezela Yehova?

9 Tiyenela kuyembekezela kuti mapemphelo athu ayankhidwe. Tikapempha mphamvu zotithandiza kulimbana na ciyeso cina cake, kapena zotithandiza kugonjetsa cifooko cina cake, tingaone monga Yehova akutenga nthawi kuyankha pemphelo lathu. N’cifukwa ciani Yehova sayankha mapemphelo athu onse nthawi yomweyo?

10. N’cifukwa ciani kuleza mtima kuli kofunika pa nkhani ya kupemphela?

10 Yehova amamvetsela mwachelu mapemphelo athu. (Sal. 65:2) Iye amaona mapemphelo athu ocokela pansi pamtima monga umboni wakuti tili na cikhulupililo. (Aheb. 11:6) Yehova ali na cidwi coona ngati zocita zathu zigwilizana na mapemphelo athu, komanso ngati tikucita cifunilo cake. (1 Yoh. 3:22) Conco, tingafunike kukhala oleza mtima, na kucita zinthu mogwilizana na mapemphelo athu pamene tiyesetsa kuthetsa zizoloŵezi zoipa. Yesu anati mapemphelo athu ena sangayankhidwe mwamsanga. Iye anatilimbikitsa kuti: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitilizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulilani. Pakuti aliyense wopempha amalandila, aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzamutsegulila.” (Mat. 7:7, 8) Tikatsatila malangizo amenewa na ‘kulimbikila kupemphela,’ tingakhale na cidalilo cakuti Atate wathu wa kumwamba adzamvetsela na kuyankha mapemphelo athu.—Akol. 4:2.

Poyembekezela pa Yehova, timapitilizabe kupemphela kwa iye mwa cikhulupililo (Onani ndime 11) *

11. Kodi Aheberi 4:16 ingatithandize bwanji tikaona kuti mapemphelo athu sakuyankhidwa mwamsanga?

11 Olo kuti pangatenge nthawi kuti mapemphelo athu ayankhidwe, Yehova analonjeza kuti adzatiyankha “pa nthawi imene tikufunika thandizo.” (Ŵelengani Aheberi 4:16.) Ndiye cifukwa cake, sitiyenela kuimba Yehova mlandu ngati zimene tinali kuyembekezela, sizinacitike mwamsanga mmene tinali kuganizila. Mwacitsanzo, kwa zaka zambili anthu oculuka akhala akupemphela kuti Ufumu wa Mulungu uwononge dongosolo loipali. Ndipo izi n’zimene Yesu anatiuza kucita. (Mat. 6:10) Koma kungakhale kupusa munthu kutaya cikhulupililo cake mwa Mulungu, cabe cifukwa mapeto sanafike pa nthawi imene anthu anali kuganizila. (Hab. 2:3; Mat. 24:44) Conco, n’canzelu kupitiliza kuyembekezela pa Yehova, komanso kupemphela kwa iye mwa cikhulupililo. Mapeto adzafika pa nthawi yake yoikidwilatu, cifukwa Yehova anasankha kale ‘tsiku na ola’ pamene mapeto adzafika. Ndipo tsikulo lidzakhala nthawi yoyenelela kwa anthu onse.—Mat. 24:36; 2 Pet. 3:15.

Kodi tingaphunzile ciani kwa Yosefe pa nkhani ya kuleza mtima? (Onani ndime 12-14)

12. Ni pa cocitika cotani maka-maka pamene kuleza mtima kungakhale kotivuta?

12 Tingafunike kuyembekezela moleza mtima kuti cilungamo cicitike. Anthu m’dzikoli amakonda kucitila nkhanza akazi kapena amuna, osiyana nawo mtundu, cikhalidwe, kapena dziko. Ena amacitilidwa nkhanza cifukwa cakuti ni olemala, kapena cifukwa codwala matenda okhudza maganizo. Atumiki a Yehova ambili akupilila zopanda cilungamo cifukwa ca cikhulupililo cawo. Akaticitila zopanda cilungamo mwa njila imeneyi, tiyenela kukumbukila mawu a Yesu akuti: “Amene adzapilile mpaka pa mapeto, ndiye amene adzapulumuke.” (Mat. 24:13) Koma bwanji ngati wina wacita colakwa cacikulu mu mpingo? Pambuyo pakuti akulu adziŵa za colakwaco, kodi mudzasiya nkhaniyo m’manja mwawo, na kuyembekezela moleza mtima kuti adzaisamalila motsatila malangizo a Yehova? Kodi akulu amacita ciani wina akacita colakwa?

13. Kodi Yehova amafuna kuti akulu aziweluza bwanji milandu?

13 Akulu akadziŵa kuti wina wacita colakwa cacikulu mu mpingo, amapempha “nzelu yocokela kumwamba” kuti athe kuona nkhaniyo mmene Yehova akuionela. (Yak. 3:17) Colinga cawo ni kufuna ‘kubweza wocimwa panjila yake yoipa,’ ngati n’kotheka. (Yak. 5:19, 20) Cina, iwo amayesetsa kucita zonse zotheka kuti ateteze mpingo na kutonthoza okhudzidwawo. (2 Akor. 1:3, 4) Asanayambe kuweluza mlandu wa colakwa cacikulu, coyamba akulu amaifufuza nkhaniyo, ndipo izi zimatenga nthawi. Ndiyeno mwa pemphelo komanso mosamala, iwo amapeleka uphungu wa m’Malemba kwa wolakwayo “pa mlingo woyenela.” (Yer. 30:11) Olo kuti akulu sagonekeza nkhani, iwo sapanga zigamulo mopupuluma. Akulu akamatsatila malangizo a Yehova poweluza mlandu, mpingo umapindula kwambili. Koma ngakhale pamene akulu atsatila bwino ndondomeko yoweluzila mlandu, munthu wolakwilidwayo amakhalabe wopwetekedwa mtima. Ngati izi zingacitike kwa inu, kodi mungatani kuti kukhumudwa kwanu kusapitilile malile?

14. Ni citsanzo citi ca m’Baibo cingakuthandizeni ngati Mkhristu mnzanu wakukhumudwitsani kwambili?

14 Kodi munthu wina, kapena Mkhristu mnzanu anakucitilamponi colakwa coŵaŵa kwambili? Mungapeze zitsanzo zabwino m’Mawu a Mulungu zimene zingakuthandize kuyembekezela Yehova kuti akonze zinthu. Mwacitsanzo, ngakhale kuti Yosefe anacitilidwa zopanda cilungamo na abale ake enieni, iye sanasunge cakukhosi. M’malo mwake, iye anasumika maganizo pa utumiki wake kwa Yehova, amene anamudalitsa kwambili cifukwa ca kupilila moleza mtima. (Gen. 39:21) M’kupita kwanthawi, Yosefe anakhululukila amene anamulakwila, ndipo Yehova anamudalitsa kwambili. (Gen. 45:5) Mofanana na Yosefe, nafenso tingatonthozedwe ngati tayandikila Yehova, na kuyembekezela kuti adzathetsa zopanda cilungamo zimene ena angaticitile.—Sal. 7:17; 73:28.

15. N’ciani cinathandiza mlongo wina kupilila zopanda cilungamo moleza mtima?

15 Si zonse zopanda cilungamo zimene n’zoipa kwambili monga zinacitikila Yosefe. Ngakhale n’telo, tingakhumudwebe ngati ena aticitila zoipa mwa njila ina iliyonse. Tikakhumudwitsana na Mkhristu mnzathu, kapena munthu wosalambila Yehova, tidzapindula ngati tiseŵenzetsa mfundo za m’Baibo. (Afil. 2:3, 4) Ganizilani cocitika ici. Mlongo wina anakhumudwa kwambili atadziŵa kuti mnzake wa kunchito anali kum’kambila zoipa kwa ena. M’malo mothamangila kucitapo kanthu, mlongoyo anayamba wadekha na kuganizila citsanzo ca Yesu. Pamene Yesu ananenezedwa zacipongwe, sanabwezele cipongwe kwa ena. (1 Pet. 2:21, 23) Cifukwa ca citsanzo ca Yesu cimeneci, iye anangosankha zoiŵalako nkhaniyo. Pambuyo pake, iye anatulukila kuti mnzakeyo anali kudwala matenda aakulu, ndipo anali wopsinjika maganizo kwambili. Pamenepo, mlongoyo anaona kuti sicinali colinga ca mnzakeyo kukamba zimene anakambazo. Mlongoyo anakondwela kwambili kuti anapilila moleza mtima pa zopanda cilungamo zimenezo, cakuti anapeza mtendele wa maganizo.

16. N’ciani cingatilimbikitse tikamapilila zopanda cilungamo? (1 Petulo 3:12)

16 Ngati mukupilila zopanda cilungamo kapena zinthu zina, dziŵani kuti Yehova ali pafupi na “anthu a mtima wosweka.” (Sal. 34:18) Amakukondani cifukwa ca kuleza mtima kwanu, komanso pomutulila nkhawa zanu. (Sal. 55:22) Iye ni woweluza wa dziko lonse lapansi. Amaona zonse zimene zikucitika. (Ŵelengani 1 Petulo 3:12.) Ngati mukumana na mavuto amene simungawathetse, kodi mudzayembekezela Yehova moleza mtima?

MADALITSO OSATHA KWA OYEMBEKEZELA PA YEHOVA

17. Malinga na Yesaya 30:18, kodi Yehova watilonjeza ciani?

17 Posacedwa, Atate wathu wa kumwamba adzatidalitsa kudzela mu Ufumu wake. Yesaya 30:18 imati: “Yehova azidzayembekezela kuti akukomeleni mtima ndipo adzanyamuka kuti akucitileni cifundo, pakuti Yehova ndi Mulungu amene amaweluza mwacilungamo. Odala ndi anthu onse amene amamuyembekezela.” Onse oyembekezela pa Yehova, adzalandila madalitso pali pano komanso m’dziko latsopano limene likubwela.

18. Kodi tiyembekezela madalitso otani?

18 Anthu a Mulungu akakaloŵa m’dziko latsopano, sadzakhalanso na nkhawa, kapena mavuto amene amakumana nawo masiku ano. Zopanda cilungamo zidzatha, ndipo zopweteka sizidzakhalaponso. (Chiv. 21:4) Sitidzakhalanso na nkhawa ya kusapeza zimene tifunikila, cifukwa zidzakhalapo zoculuka. (Sal. 72:16; Yes. 54:13) Zidzakhala zokondweletsa zedi!

19. Kodi Yehova akutikonzekeletsa ciani pali pano?

19 Koma pali pano, Yehova akutikonzekeletsa umoyo watsopano pansi pa ulamulilo wake, potithandiza kugonjetsa zizoloŵezi zoipa na kukulitsa makhalidwe aumulungu. Musataye mtima, ndipo musalefuke. Umoyo wabwino uli patsogolo. Pamene tikuyembekezela tsogolo labwino, tiyeni tipitilize kuyembekezela Yehova moleza mtima pamene iye akutsiliza nchito yake!

NYIMBO 118 “Tiwonjezeleni Cikhulupililo”

^ ndime 5 Kodi munamvelapo munthu amene watumikila Yehova kwanthawi yaitali akukamba kuti, ‘Sin’naganizilepo kuti ningafike msinkhu uno mapeto asanacitike? Tonsefe timafuna kuti Yehova awononge dziko loipali, maka-maka m’nthawi zino zovuta. Komabe, tiyenela kukhala oleza mtima. M’nkhani ino, tikambilane mfundo za m’Baibo zimene zingatithandize kuyembekezela moleza mtima. Tikambilanenso mbali ziŵili zimene zifuna kuti tiyembekezele Yehova moleza mtima. Cotsilizila, tiona madalitso amene anthu oyembekezela pa Yehova adzapeza.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Kungoyambila ali mwana, mlongo wakhala akupemphela kwa Yehova. Ali mwana, makolo ake anamuphunzitsa mopemphelela. Ali wacitsikana anayamba upainiya, ndipo nthawi zonse anali kupempha Yehova kuti adalitse utumiki wake. Pambuyo pa zaka, mwamuna wake atadwala, akucondelela Yehova kuti amupatse mphamvu zofunikila kuti apilile ciyeso cimeneco. Lelo lino, monga mkazi wamasiye, iye akupitiliza kupemphela, ali na cidalilo cakuti Atate wake wakumwamba, adzayankha mapemphelo ake monga mmene akhala akucitila mu umoyo wake wonse.