Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 30

Muziyamikila Malo Anu M’banja la Yehova

Muziyamikila Malo Anu M’banja la Yehova

“Munamucepetsa pang’ono poyelekeza ndi angelo, kenako munamuveka ulemelelo ndi ulemu monga cisoti cacifumu.” —SAL. 8:5, mawu amunsi.

NYIMBO 123 Gonjelani Dongosolo la Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Tikaganizila za cilengedwe conse ca Yehova, kodi tingafunse funso lotani?

TIKAGANIZILA za cilengedwe conse ca Yehova, tingamve monga anamvelela wamasalimo Davide. Popemphela kwa Yehova iye anafunsa kuti: “Ndikayang’ana kumwamba, nchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi zimene munapanga, ndimaganiza kuti: Munthu ndani kuti muzimuganizila, ndipo mwana wa munthu wocokela kufumbi ndani kuti muzimusamalila?” (Sal. 8:3, 4) Mofanana na Davide, ifenso tikadziyelekezela na cilengedwe conse, tiona kuti ndife aang’ono kwambili. Komabe, n’zolimbikitsa kudziŵa kuti Yehova amasamala za ife. Monga tionele m’nkhani ino, Yehova anali kusamalila anthu oyamba, Adamu na Hava, ndipo anawatenga kukhala ziwalo za banja lake.

2. Kodi colinga ca Yehova kwa ana ake oyamba padziko lapansi cinali ciani?

2 Adamu na Hava, anali ana oyamba a Yehova padziko lapansi, ndipo iye anali Tate wawo wacikondi. Monga ana ake, anafuna kuti iwo azigwila nchito. Conco, Mulungu anaŵauza kuti: “Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anile.” (Gen. 1:28) Iwo anafunikila kukhala na ŵana, komanso kusamalila malo awo okhala. Ngati Adamu na Hava akanacita zinthu mogwilizana na colinga ca Yehova, iwo pamodzi na mbadwa zawo akanakhalabe m’banja la Mulungu kwamuyaya.

3. N’cifukwa ciani tingakambe kuti Adamu na Hava anapatsidwa malo olemekezeka m’banja la Yehova?

3 Adamu na Hava anali na malo olemekezeka m’banja la Yehova. Ponena za mmene Yehova analengela munthu, pa Salimo 8:5 komanso mawu amunsi, Davide anati: “Munamucepetsa pang’ono poyelekeza ndi angelo, kenako munamuveka ulemelelo ndi ulemu monga cisoti cacifumu.” N’zoona kuti anthu sanapatsidwe mphamvu, nzelu, komanso maluso, olingana na angelo. (Sal. 103:20) Ngakhale n’telo, anthu ni ‘ocepako pang’ono’ powayelekezela na angelo amphamvu. Izi n’zocititsa cidwi kwambili! Yehova anapatsa makolo athu ciyambi cabwino ngako.

4. N’ciani cinacitikila Adamu na Hava cifukwa cosamvela Yehova? Nanga tikambilane ciani m’nkhani ino?

 4 Koma n’zacisoni kuti Adamu na Hava, anataya malo awo m’banja la Yehova. Izi zinabweletsa mavuto aakulu kwa mbadwa zake, monga tionele m’nkhani ino. Koma colinga ca Yehova sicinasinthe. Iye afuna kuti anthu omvela akakhale ana ake kwamuyaya. Coyamba, tiyeni tikambilane mmene Yehova waonetsela kuti amatilemekeza. Kenaka, tikambilane zimene tingacite pali pano poonetsa kuti tifuna kukakhala m’banja la Mulungu. Cothela, tidzaona madalitso amene ana a Yehova a padziko lapansi adzasangalala nawo kwamuyaya.

MMENE YEHOVA WAONETSELA KUTI AMALEMEKEZA ANTHU

Kodi Yehova waonetsa motani kuti amatilemekeza? (Onani ndime 5-11) *

5. Tingaonetse bwanji kuti timamuyamikila Mulungu potilenga m’cifanizilo cake?

5 Yehova anatilemekeza potilenga m’cifanizilo cake. (Gen. 1:26, 27) Cifukwa cakuti tinalengedwa m’cifanizilo ca Mulungu, tingathe kukulitsa na kuonetsa makhalidwe abwino, monga cikondi, cifundo, kukhulupilika, komanso cilungamo. (Sal. 86:15; 145:17) Pamene tikulitsa makhalidwe amenewa, timalemekeza Yehova na kuonetsa kuti timamuyamikila. (1 Pet. 1:14-16) Tikamacita zinthu zokondweletsa Atate wathu wakumwamba, timakhala acimwemwe komanso okhutila. Popeza tili na makhalidwe amene Yehova ali nawo, tingathe kukhala mtundu wa anthu amene iye afuna m’banja lake.

6. Popanga dziko lapansi, kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti anawalemekeza anthu?

6 Yehova anatikonzela malo abwino okhalamo. Kale kwambili, Yehova asanalenge munthu woyamba, anapanga dziko lapansi kuti anthu azikhalamo. (Yobu 38:4-6; Yer. 10:12) Popeza Yehova ni woganizila ena komanso woolowa manja, anakonza zinthu zabwino zambili kuti tizikondwela nazo. (Sal. 104:14, 15, 24) Atayang’ana zinthu zimene anali kulenga, “anaona kuti zili bwino.” (Gen. 1:10, 12, 31) Iye analemekeza anthu poŵapatsa “mphamvu kuti alamulile” zinthu zonse zimene analenga padziko lapansi. (Sal. 8:6) Colinga ca Mulungu cinali cakuti anthu angwilo asamalile cilengedwe cake cokongola kwamuyaya. Kodi mumamuyamikila Yehova nthawi zonse pa colinga cake cabwino cimeneci?

7. Kodi Yoswa 24:15 imaonetsa motani kuti munthu ali na ufulu wodzisankhila zocita?

7 Yehova anatipatsa ufulu wodzisankhila zocita. Tili na ufulu wosankha zimene tifuna kucita mu umoyo wathu. (Ŵelengani Yoswa 24:15.) Mulungu wathu wacikondi amakondwela ngako tikasankha kum’tumikila. (Sal. 84:11; Miy. 27:11) Tingaseŵenzetse moyenelela ufulu wathu wodzisankhila zocita pa zocitika zosiyanasiyana. Ganizilani citsanzo ca Yesu.

8. Kodi Yesu anaseŵenzetsa bwanji ufulu wake wodzisankhila zocita?

8 Tingatengele citsanzo ca Yesu mwa kuika zofuna za ena patsogolo pa zofuna zathu. Tsiku lina pamene Yesu na ophunzila ake analema kwambili, anapita kumalo kwa okha kuti akapumuleko. Komabe, iwo sanapumule cifukwa khamu la anthu linawatsatila, ndipo linali lofunitsitsa kuphunzila kwa Yesu. Koma Yesu sanakhumudwe nawo. M’malomwake, iye anawamvelela cifundo. Ndiye kodi Yesu anacita ciani? “Anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambili.” (Maliko 6:30-34) Ngati titengela Yesu poseŵenzetsa nthawi na nyonga zathu pothandiza ena, timapeleka ulemelelo kwa Atate wathu wakumwamba. (Mat. 5:14-16) Cina, timaonetsa Yehova kuti tifuna kukhala m’banja lake.

9. Kodi makolo ayenela kukumbukila ciani?

9 Yehova anapatsa anthu mphamvu zobeleka ana, komanso udindo wowaphunzitsa kukonda Yehova na kum’tumikila. Ngati ndimwe kholo, kodi mumayamikila mphatso yapadela imeneyi? Ngakhale kuti Yehova anapatsa angelo mphatso zambili zabwino, iwo sanapatsidwe mphatso yobeleka. Conco ngati ndinu kholo, muziyamikila udindo wapadela umenewu wolela ana. Munapatsidwa udindo wofunika kwambili, wolela ana “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4; Deut. 6:5-7; Sal. 127:3) Pofuna kuthandiza makolo, gulu la Mulungu lapeleka zida zophunzilila Baibo, monga mabuku, mavidiyo, nyimbo, komanso nkhani za pa webusaiti yathu. N’zoonekelatu kuti, Atate wathu wakumwamba na Mwana wake amakonda acicepele athu. (Luka 18:15-17) Ngati makolo amadalila Yehova, na kucita zonse zimene angathe posamalila ana awo amtengo wapatali, Yehova amakondwela. Makolo otelo amapatsa ana awo ciyembekezo codzakhala m’banja la Yehova kwamuyaya.

10-11. Kodi Yehova wapangitsa zinthu ziti kukhala zotheka cifukwa ca dipo?

10 Yehova anapeleka Mwana wake wokondekayo kuti tikakhalenso ziwalo za banja lake. Monga taonela  m’ndime 4, Adamu na Hava anataya malo awo m’banja la Yehova, anatayilanso ana awo. (Aroma 5:12) Adamu na Hava anacitila dala kusamvela Mulungu. Conco, panali poyeneladi kuŵacotsa m’banja la Mulungu. Nanga bwanji za ana awo? Yehova mwacikondi anakonza zakuti anthu omvela awatenge kukhala ana a m’banja lake. Iye anacita zimenezi kupitila mu nsembe ya dipo la Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Khristu. (Yoh. 3:16; Aroma 5:19) Cifukwa ca nsembe ya Yesu imeneyi, anthu okhulupilika okwana 144,000 amatengedwa kukhala ana a Mulungu.—Aroma 8:15-17; Chiv. 14:1.

11 Kuwonjezela apo, anthu okhulupilika mamiliyoni osaŵelengeka amacita cifunilo ca Mulungu. Iwo ali na ciyembekezo codzakhala ziwalo zacikwane-kwane m’banja la Mulungu, pambuyo pa mayeso othela kumapeto kwa zaka Cikwi. (Sal. 25:14; Aroma 8:20, 21) Pokhala na ciyembekezo cimeneci, iwo ngakhale pali pano amachulabe Yehova, Mlengi wawo, kuti “Atate.” (Mat. 6:9) Anthu amene adzaukitsidwe nawonso adzapatsidwa mwayi wophunzila zimene Yehova afuna kuti iwo azicita. Awo amene adzasankhe kumvela malangizo a Mulungu, pothela pake iwonso adzakhala m’banja lake.

12. Ni funso liti limene tifuna kupeza yankho lake?

12 Monga taonela, Yehova wacita zinthu zambili poonetsa kuti amalemekeza anthu. Iye watenga kale odzozedwa kukhala ana ake, komanso wapatsa a “khamu lalikulu” ciyembekezo codzakhala ana ake acikwane-kwane m’dziko latsopano. (Chiv. 7:9) Kodi tingacite ciani pali pano kuonetsa Yehova kuti tifuna kukhala ziwalo za banja lake mpaka muyaya?

ONETSANI YEHOVA KUTI MUFUNA KUKHALA M’BANJA LAKE

13. Kodi tingacite ciani kuti tikhale m’banja la Mulungu mpaka muyaya? (Maliko 12:30)

13 Onetsani kuti mumam’konda Yehova mwa kum’tumikila na mtima wonse. (Ŵelengani Maliko 12:30.) Pa mphatso zonse zimene Mulungu anatipatsa mwa cisomo cake, mphatso imene imaposa zonsezo, mwina ni mphatso ya kumulambila. Timaonetsa kuti timamukonda Yehova ngati ‘tisunga malamulo ake.’ (1 Yoh. 5:3) Moimilako Atate wake, Yesu anatilamula kupanga ophunzila na kuŵabatiza. (Mat. 28:19) Iye anatilamulanso kuti tizikondana. (Yoh. 13:35) Anthu omvela, Yehova amawalandila m’banja la alambili ake a padziko lonse.—Sal. 15:1, 2.

14. Tingaonetse bwanji kuti timakonda ena? (Mateyu 9:36-38; Aroma 12:10)

14 Onetsani cikondi kwa ena. Cikondi ndiye khalidwe lalikulu la Yehova. (1 Yoh. 4:8) Iye anationetsa cikondi tisanamudziŵe n’komwe. (1 Yoh. 4:9, 10) Timatengela citsanzo cake ngati tikonda ena. (Aef. 5:1) Njila yabwino koposa imene tingaonetsele kuti timakonda ena, ni kuwaphunzitsa za Yehova mapeto asanafike. (Ŵelengani Mateyu 9:36-38.) Tikatelo, timawapatsa ciyembekezo codzakhala m’banja la Mulungu. Pambuyo pakuti munthu wabatizika, tiyenela kupitiliza kum’konda na kumulemekeza. (1 Yoh. 4:20, 21) Kodi tingacite bwanji zimenezi? Tingatelo mwa kupewa kukayikila zolinga zake. Mwacitsanzo, ngati sitinamvetse cimene wacitila zina zake, tisamuganizile kuti wacita zimenezo na colinga cadyela. M’malo mwake, timuonetse ulemu m’bale wathu, na kumuonabe kukhala wotiposa.—Ŵelengani Aroma 12:10; Afil. 2:3.

15. Ndani amene tiyenela kucitila cifundo na kuwakomela mtima?

15 Muzicitila cifundo anthu onse na kuwakomela mtima. Ngati tifuna kukhala pakati pa anthu oyenelela kuchula Yehova kuti Atate kwamuyaya, tiziseŵenzetsa Mawu ake mu umoyo wathu. Mwacitsanzo, Yesu anatiphunzitsa kuti tizicitila cifundo anthu onse na kuwakomela mtima, ngakhale adani athu omwe. (Luka 6:32-36) Koma nthawi zina kucita zimenezi kumakhala kovuta. N’cifukwa cake, tiyenela kuganiza na kucita zinthu monga Yesu. Tikamayesetsa kucita zonse zotheka pomvela Yehova, komanso kutengela citsanzo ca Yesu, tidzaonetsa Atate wathu wa kumwamba kuti tifuna kukhala m’banja lake kwamuyaya.

16. Kodi tingateteze bwanji mbili yabwino ya banja la Yehova?

16 Tetezani mbili yabwino ya banja la Yehova. M’banja lakuthupi, n’zofala kwambili mwana wacicepele kutengela zocita za mkulu wake. Ngati mkulu wake amaseŵenzetsa mfundo za m’Baibo mu umoyo wake, amakhala citsanzo cabwino kwa mng’ono wake. Koma ngati mkulu wakeyo wayamba kucita zinthu zoipa, nayenso mng’ono wake angatengele citsanzo cake coipa. Ni mmenenso zilili m’banja la Yehova. Mkhristu amene anali wokhulupilika akayamba kukhala na maganizo ampatuko, kapena makhalidwe oipa, ena angatengele citsanzo cake coipa. Anthu amene amacita zimenezi, amaipitsa mbili ya banja la alambili a Yehova. (1 Ates. 4:3-8) Motelo, tiyenela kupewa kutengela zitsanzo zoipa, na kusalola ciliconse kuticotsa kwa Atate wathu wacikondi wakumwamba.

17. Kodi tiyenela kupewa kaganizidwe kotani? Nanga n’cifukwa ciani?

17 Dalilani Yehova m’malo modalila zinthu zakuthupi. Yehova anatilonjeza kuti adzatipatsa cakudya, zovala, komanso pogona, ngati tifunafuna ufumu coyamba na kutsatila miyezo yake yolungama. (Sal. 55:22; Mat. 6:33) Tikakhulupilila lonjezo limeneli, tidzapewa kuganiza kuti zinthu zakuthupi za m’dzikoli, n’zimene zingatibweletsele citetezo ceniceni na cimwemwe cosatha. Timadziŵa kuti tidzakhala na mtendele weniweni wa maganizo, kokha ngati ticita cifunilo ca Yehova. (Afil. 4:6, 7) Ngakhale tingakwanitse kugula zinthu zambili, tizionanso ngati nthawi tili nayo yozisamalila. Kodi n’kutheka kuti timakonda kwambili zinthu zimene tili nazo? Tizikumbukilanso kuti Mulungu anatipatsa zocita m’banja lake. Mwa ici, tisamalole zinthu zina kutitangwanitsa. Sitifuna olo pang’ono kukhala monga mnyamata uja amene anataya mwayi wotumikila Yehova, komanso mwayi wotengedwa kukhala mmodzi wa ana ake, cabe cifukwa cokondetsetsa zinthu zocepa zakuthupi zimene anali nazo.—Maliko 10:17-22.

ZIMENE ANA A YEHOVA ADZASANGALALA NAZO KWAMUYAYA

18. Ni mwayi waukulu uti, komanso madalitso, amene anthu omvela adzasangalala nawo kwamuyaya?

18 Anthu omvela adzasangalala na dalitso lalikulu, limene ni mwayi wokonda Yehova na kum’tumikila kwamuyaya! Awo amene ali na ciyembekezo codzakhala padziko lapansi, adzasangalala na nchito yosamalila dziko lapansi lokongola, limene Yehova analipanga kuti anthu azikhalamo. Posacedwa, dziko lapansi komanso zamoyo zonse, zidzakhalanso zatsopano mu Ufumu wa Mulungu. Yesu adzathetsa mavuto onse amene Adamu na Hava anabweletsa cifukwa cosankha kucoka m’banja la Mulungu. Cina, Yehova adzaukitsa anthu mamiliyoni, na kuwapatsa thanzi labwino, komanso moyo wosatha m’dziko lapansi limene adzalisandutse kukhala paradaiso. (Luka 23:42, 43) Pamene banja la Yehova la padziko lapansi lidzakhala langwilo, onse adzakhala na “ulemelelo ndi ulemu,” zimene Davide anakamba.—Sal. 8:5.

19. Kodi tiyenela kukumbukila ciani?

19 Ngati ndinu a “khamu lalikulu,” muli na ciyembekezo cabwino zedi. Mulungu amakukondani, ndipo afuna kuti mukhale ciwalo ca banja lake. Conco, citani zonse zotheka kuti mum’kondweletse. Tsiku lililonse, muzikumbukila malonjezo a Mulungu mu mtima mwanu. Muziyamikila mwayi umene muli nawo wolambila Atate wathu wakumwamba. Komanso, muziyamikila mwayi wanu wom’tamanda mpaka muyaya!

NYIMBO 107 Cikondi ca Umulungu

^ ndime 5 Kuti banja liyende bwino, aliyense m’banjamo ayenela kudziŵa udindo wake, komanso kulimbikitsa mgwilizano. Tate ayenela kutsogolela banjalo mwacikondi, mayi ayenela kucilikiza mwamuna wake, ndipo ana ayenela kumvela makolo awo. Ni mmenenso zilili m’banja la Yehova. Mulungu wathu ali nafe colinga, ndipo ngati ticita zinthu mogwilizana na colingaco, tidzakhala m’banja la alambili ake kwamuyaya.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Cifukwa colengedwa m’cifanizilo ca Mulungu, mwamuna na mkazi wake akutha kuonetsana cikondi na cifundo pakati pawo, komanso kwa ana awo. Banjali limam’konda Yehova. Iwo akuonetsa kuti amayamikila mphatso yobeleka ana, powaphunzitsa anawo kukonda Yehova na kum’tumikila. Makolo aseŵenzetsa vidiyo pofotokozela ana awo cifukwa cake Yehova anapeleka Yesu monga dipo. Akuŵaphunzitsanso kuti m’paradaiso akubwelayo, tidzasamalila dziko lapansi komanso zinyama kwamuyaya.