Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 33

Maso a Yehova Ali pa Anthu Ake

Maso a Yehova Ali pa Anthu Ake

“Diso la Yehova lili pa anthu amene amamuopa.” —SAL. 33:18.

NYIMBO 4 “Yehova ni M’busa Wanga”

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. N’cifukwa ciyani Yesu anapempha Yehova kuti awayang’anile otsatila ake?

 USIKU wakuti maŵa lake aphedwa, Yesu anapeleka pempho lapadela kwa Atate wake wakumwamba. Iye anapempha Yehova kuti ayang’anile otsatila ake. (Yoh. 17:15, 20) N’zoona kuti Yehova wakhala akuyang’anila anthu ake, kutanthauza kuti amawasamalila komanso amawateteza. Komabe, Yesu anadziŵa kuti otsatila ake adzatsutsidwa kwambili na Satana. Yesu anadziŵanso kuti iwo adzafunikila thandizo la Yehova kuti asagonje ku mayeso a Mdyelekezi.

2. Malinga na Salimo 33:18-20, n’cifukwa ciyani sitiyenela kuopa kukumana na mavuto?

2 M’dziko la Satanali, Akhristu oona amakumana na zopsinja zambili masiku ano. Timakumana na mavuto amene angatilefule, ngakhale kuyesa kukhulupilika kwathu kwa Yehova. Koma monga tionele m’nkhani ino, palibe cifukwa cocitila mantha. Maso a Yehova ali pa ife, akuona mavuto amene tikukumana nawo. Ndipo ni wokonzeka kutithandiza kuthana nawo. Tiyeni tsopano tikambilane zitsanzo ziŵili za m’Baibo, zoonetsa kuti “diso la Yehova lili pa anthu amene amamuopa.”—Ŵelengani Salimo 33:18-20.

TIKAMVA KUTI TILI TOKHA-TOKHA

3. Ni pa zocitika ziti pamene tingamve kuti tili tokha-tokha?

3 Ngakhale kuti tili m’banja lalikulu la olambila anzathu, nthawi zina tingamve kuti tili tokha. Mwacitsanzo, acicepele angamve kuti ali okha-okha pofotokozela anzawo a m’kalasi zimene amakhulupilila, kapena pamene asamukila mu mpingo wina watsopano. Ena a ife tingakhale na cisoni, kapena tingamavutike na maganizo olefula, poona kuti tifunika kulimbana na mavutowo tokha-tokha. Mwina tingaope kufotokozelako ena mmene tikumvela cifukwa coganiza kuti sadzatimvetsa. Ndipo nthawi zina, tingaone kuti palibe amasamala za ife. Kukhala na maganizo akuti tili tokha-tokha kungatipangitse kukhala na nkhawa, komanso kuona kuti palibe angatithandize. Yehova safuna kuti tizimva mwanjila imeneyi. N’cifukwa ciyani takamba conco?

4. N’cifukwa ciyani mneneli Eliya anakamba kuti: “Ndatsala ndekha-ndekha”?

4 Ganizilani citsanzo ca munthu wokhulupilika Eliya. Yezebeli anali atalumbila kuti adzamupha. Conco, iye anakhala umoyo wothaŵa-thaŵa kwa masiku 40 pofuna kupulumutsa moyo wake. (1 Maf. 19:1-9) Pamapeto pake, ali yekha-yekha m’phanga anauza Yehova kuti: “Ndatsala ndekha-ndekha [mneneli].” (1 Maf. 19:10) Komabe, m’dzikomo aneneli ena analimobe. Obadiya anali atapulumutsa aneneli 100 kuti Yezebeli asawaphe. (1 Maf. 18:7, 13) Ndiye n’cifukwa ciyani Eliya anamva kuti ali yekha-yekha? Kodi iye anaganiza kuti aneneli onse amene Obadiya anapulumutsa anali atamwalila? Kodi n’kutheka kuti iye anamva kuti ali yekha-yekha cifukwa cakuti panalibe anayamba kutumikila Yehova pambuyo pakuti Baala waonekela poyela kuti sindiye Mulungu woona pa Phili la Karimeli? Kodi anaona kuti panalibe anali kudziŵa kuti moyo wake unali paciswe? Kapena anaona kuti panalibe anali kusamala za iye? Baibo siifotokoza zambili za mmene Eliya anali kumvela. Koma cimene tidziŵa n’cakuti, Yehova anamvetsa cimene cinapangitsa Eliya kumva kuti ali yekha-yekha, ndipo anadziŵa mom’thandizila.

Tikamva kuti tili tokha-tokha, ni mfundo yolimbikitsa iti imene tiphunzilapo poona mmene Yehova anathandizila Eliya? (Onani ndime 5-6))

5. Kodi Yehova anam’tsimikizila bwanji Eliya kuti sanali yekha?

5 Yehova anathandiza Eliya m’njila zosiyanasiyana. Anam’limbikitsa kuti alankhule. Kaŵili konse, iye anam’funsa kuti: “Ukufuna ciyani kuno”? (1 Maf. 19:9, 13) Nthawi zonse, Yehova anali kumvetsela pamene Eliya anali kufotokoza mmene anali kumvela. Yehova anayankha Eliya mwa kumuonetsa mphamvu zake komanso kuti aliko. Anam’tsimikizilanso kuti analipo ena ambili amene anali kutumikila Mulungu. (1 Maf. 19:11, 12, 18) Mosakayika, Eliya anatonthozedwa kwambili atakhutula za mumtima mwake kwa Yehova na kuona kuti wamuyankha. Yehova anapatsa Eliya mautumiki angapo ofunika kwambili. Anam’pempha kukadzoza Hazaeli kuti akhale mfumu ya Siriya, Yehu kuti akhale mfumu ya Isiraeli, komanso Elisa kuti akhale mneneli. (1 Maf. 19:15, 16) Mwa kum’patsa mautumiki amenewa, Yehova anathandiza Eliya kuti aike maganizo ake pa zinthu zolimbikitsa. Mulungu anam’patsanso bwenzi lapamtima, Elisa. Kodi mungacite ciyani kuti mulandile thandizo la Yehova mukamva kuti muli nokha-nokha?

6. Ni zinthu ziti zimene mungapemphe mukamva kuti muli nokha-nokha? (Salimo 62:8)

6 Yehova akukupemphani kuti muzipemphela kwa iye. Iye amaona mavuto amene mukukumana nawo, ndipo ni wokonzeka kumvetsela mapemphelo anu nthawi iliyonse. (1 Ates. 5:17) Iye amakondwela kumvetsela mapemphelo a alambili ake. (Miy. 15:8) Ni zinthu ziti zimene mungapemphe mukamva kuti muli nokha-nokha? Mukhutulileni za mumtima mwanu Yehova, monga mmene Eliya anacitila. (Ŵelengani Salimo 62:8.) Muuzeni nkhawa zanu na mmene mukumvela. Ndipo m’pempheni Yehova kuti akuthandizeni kuthana na nkhawa zanuzo. Mwacitsanzo, mukamva kuti muli nokha-nokha, ndipo mukucita mantha kulalikila ku sukulu, pemphani Yehova kuti akulimbitseni mtima kuti mukwanitse kulalikila. Munga’mpemphe ngakhale nzelu kuti mukwanitse kufotokoza mwaluso zimene mumakhulupilila. (Luka 21:14, 15) Mukamavutika na maganizo olefula, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuuzako Mkhristu wokhwima. Ndipo m’pempheni kuti athandize munthu amene mufuna kumuuzako vuto lanu kuti akumvetsetseni. Mukhutulileni za mumtima mwanu Yehova, onani mmene akuyankhila mapemphelo anu, ndipo labadilani thandizo la ena. Mukatelo, simudzamvanso kuti muli nokha-nokha.

Kodi mumayesa kupeza mipata yowonjezela utumiki wanu komanso yolalikila na ena? (Onani ndime 7)

7. Mwaphunzilapo ciyani pa citsanzo ca Mauricio?

7 Yehova wapatsa tonsefe nchito yabwino yakuti tiigwile. Mungakhale na cidalilo cakuti iye amaona na kuyamikila zonse zimene mumacita mu mpingo komanso mu ulaliki. (Sal. 110:3) Kodi kugwila nchito yolalikila mokangalika kungakuthandizeni bwanji mukamva kuti muli nokha-nokha? Onani citsanzo ici ca m’bale wacinyamata dzina lake Mauricio. b Pambuyo pakuti Mauricio wabatizidwa, mnzake wina wapamtima pan’gono-m’pang’ono anayamba kusiya coonadi. Mauricio anati: “N’taona kuti iye wasiya Yehova, n’nakhwethemuka. N’nayamba kukayikila ngati nidzasunga lumbilo langa la kudzipatulila kwa Yehova na kukhalabe m’banja lake. N’namva kuti nili nekha-nekha, ndipo n’naganiza kuti palibe angamvetse mmene n’nali kumvela.” Kodi n’ciyani cinam’thandiza Mauricio? Iye anati: “Kuwonjezela utumiki kunanithandiza kupewa kumangoganizila za ine mwini, komanso zinthu zolefula. Pamene n’nali kulalikila na ena n’nakhala wacimwemwe, ndipo sin’namvenso kuti nili nekha-nekha.” Ngakhale kuti sitingalalikile na okhulupilila anzathu pamaso-m’pamaso, timalimbikitsidwa tikamacita nawo zinthu monga ulaliki wa makalata komanso wa pafoni. N’ciyaninso cina cinamuthandiza Mauricio? Iye anati: “N’nali kukhalanso wotangwanika na mautumiki mu mpingo. N’nali kukonzekela bwino nkhani za m’sukulu na kuzikamba ku mpingo. Kucita izi kunanithandiza kuona kuti Yehova na anthu ena amaona kuti ndine wofunika.”

MAYESO AAKULU AKATILEFULA

8. Kodi mayeso aakulu angatikhudze bwanji?

8 M’masiku ano otsiliza, tidzakumana na mayeso aakulu. Komabe, mayeso amenewa angabwele panthawi yosayembekezeleka. Mwacitsanzo, tingakumane na mavuto azacuma, tingadwale matenda aakulu, kapena kutayikilidwa munthu amene timakonda mu imfa. Tikakumana na mavutowo, tingapanikizike maganizo komanso tingalefuke, makamaka ngati takumana nawo motsatizana, kapena ngati atigwela panthawi imodzi. Koma tisaiŵale kuti maso a Yehova ali pa ife. Ndipo na thandizo lake, tingayang’anizane na mavutowo molimba mtima.

9. Fotokozani ena mwa mayeso amene Yobu anakumana nawo.

9 Ganizilani mmene Yehova anathandizila munthu wokhulupilika Yobu. Iye anakumana na mayeso angapo othetsa nzelu m’kanthawi kocepa. M’tsiku limodzi cabe, Yobu analandila uthenga woipa komanso wozizilitsa m’nkhongono wakuti watayikilidwa ziŵeto zake, atumiki ake aphedwa, komanso coipa kwambili, ana ake okondedwa afa. (Yobu 1:13-19) Akali m’cisoni conseci, Yobu anadwala matenda oŵaŵa, thupi lake lonse lili zilonda zokha-zokha. (Yobu 2:7) Zinthu zinafika poipa kwambili cakuti Yobu anakamba kuti: “Moyo ndaukana, sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.”—Yobu 7:16.

Yehova pofuna kum’tsimikizila Yobu kuti amamusamalila mwacikondi, analankhula naye za mmene amasamalila zolengedwa zake (Onani ndime 10)

10. Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Yobu kupilila mayeso? (Onani cithunzi pacikuto.)

10 Maso a Yehova anali pa Yobu. Cifukwa cakuti Yehova anali kum’konda Yobu, anam’patsa zonse zofunikila kuti akwanitse kupilila mayesowo. Yehova analankhula na Yobu kuti am’kumbutse nzelu zake zakuya, na cikondi cake cacikulu pa zolengedwa zake. Iye anakamba pa nyama zambili zocititsa cidwi. (Yobu 38:1, 2; 39:9, 13, 19, 27; 40:15; 41:1, 2) Yehova anagwilitsanso nchito mnyamata wina wokhulupilika dzina lake Elihu kuti alimbikitse Yobu na kum’tonthoza. Elihu anam’tsimikizila kuti Yehova nthawi zonse amapeleka mphoto kwa alambili ake cifukwa ca kupilila kwawo. Cina, Yehova anasonkhezela Elihu kuti apeleke uphungu wacikondi kwa Yobu. Elihu anathandiza Yobu kusaganizila kwambili za iye mwini pom’kumbutsa kuti iye ni wocepa poyelekezela na Yehova, Mlengi wa cilengedwe conse. (Yobu 37:14) Yehova anapatsanso Yobu zocita. Anamuuza kuti apemphelele anzake atatu amene anali atacimwa. (Yobu 42:8-10) Kodi Yehova amatithandiza bwanji masiku ano tikakumana na mayeso aakulu?

11. Kodi Baibo imatitonthoza motani tikakumana na mayeso?

11 Yehova sakamba nafe mwacindunji monga anacitila kwa Yobu. Koma amakamba nafe kupitila m’Mawu ake Baibo. (Aroma 15:4) Iye amatitonthoza mwa kutipatsa ciyembekezo ca za kutsogolo. Ganizilani mfundo za m’Baibo zimene zingatitonthoze tikakumana na mayeso. M’Malemba, Yehova amatitsimikizila kuti palibe ciliconse—ngakhale mayeso aakulu— cimene ‘cingatilekanitse nai cikondi ca Mulungu.’ (Aroma 8:38, 39) Amatitsimikizilanso kuti “ali pafupi ndi onse oitanila pa iye” m’pemphelo. (Sal. 145:18) Yehova amatiuza kuti tikamudalila, tingapilile ciyeso ciliconse, ndipo tingakhale acimwemwe ngakhale kuti tikuvutika. (1 Akor. 10:13; Yak. 1:2, 12) Mawu a Mulungu amatikumbutsanso kuti mayeso amene timakumana nawo ni akanthawi komanso osakhalitsa tikawayelekezela na mphoto yamuyaya imene anatilonjeza. (2 Akor. 4:16-18) Yehova amatipatsa ciyembekezo cotsimikizika cakuti adzawononga Satana Mdyelekezi, amene ni gwelo la mayeso amene timakumana nawo, komanso anthu oipa amene ali kumbali yake. (Sal. 37:10) Kodi mwasungako pa mtima Malemba ena olimbikitsa kuti adzakuthandizeni kupilila mayeso kutsogoloku?

12. Kodi Yehova amafuna kuti ticite ciyani kuti tizipindula kwambili na Mawu ake?

12 Yehova amafuna kuti tizipatula nthawi yoŵelenga Baibo nthawi zonse na kusinkhasinkha zimene timaŵelengazo. Tikamagwilitsa nchito zimene timaphunzila, cikhulupililo cathu cimalimba, ndipo timamuyandikila kwambili Atate wathu wakumwamba. Mwa ici, timakwanitsa kupilila mayeso. Yehova amapelekanso mzimu wake woyela kwa aja amene amadalila Mawu ake. Ndipo mzimuwo umatipatsa “mphamvu yoposa yacibadwa” kuti tipilile mayeselo alionse.—2 Akor. 4:7-10.

13. Kodi cakudya cauzimu cimene “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” amatipatsa, cimatithandiza bwanji kupilila mayeso?

13 Na thandizo la Yehova, “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” amakonza nkhani, mavidiyo, na nyimbo zotithandiza kulimbitsa cikhulupililo cathu, na kukhalabe maso mwauzimu. (Mat. 24:45) Tiyenela kuseŵenzetsa bwino zonse zimene Yehova amatipatsa panthawi yake. Caposacedwa, mlongo wina wa ku America anaonetsa kuti amayamikila cakudya cauzimu cimeneci. Iye anati: “Pa zaka 40 zimene natumikila Yehova, cikhulupililo canga cayesedwapo mobweleza-bweleza.” Mlongoyu anakumana na mayeso aakulu. Ambuye ŵake ŵaamuna anaphedwa na dalaivala woledzela, makolo ake anadwala kwambili ndipo anamwalila, komanso iye anadwala khansa kaŵili konse. Kodi n’ciyani cinamuthandiza kupilila? Mwini wake anati: “Yehova wakhala akunisamalila nthawi zonse. Cakudya cauzimu cimene iye amatipatsa kupitila mwa kapolo wokhulupilika ndi wanzelu canithandiza kupilila. Pa cifukwa cimeneci, nikumva monga mmene Yobu anamvela. Iye anati: “Mpaka ine kumwalila, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.’”—Yobu 27:5.

Kodi tingakhale bwanji dalitso kwa ena mumpingo mwathu? (Onani ndime 14)

14. Kodi Yehova amawaseŵenzetsa bwanji alambili anzathu kuti atithandize tikakumana na mayeso? (1 Atesalonika 4:9)

14 Yehova waphunzitsa anthu ake kuti azikondana na kutonthozana panthawi ya mavuto. (2 Akor. 1:3, 4; ŵelengani 1 Atesalonika 4:9.) Potengela citsanzo ca Elihu, abale na alongo athu amakhala okonzeka kutithandiza kuti tikhalebe okhulupilika pamene takumana na mavuto. (Mac. 14:22) Mwacitsanzo, ganizilani mmene mpingo unalimbikitsila Diane na kum’thandiza kukhalabe wolimba mwauzimu pamene mwamuna wake anadwala matenda aakulu. Iye anati: “Zinali zovuta. Koma m’miyezi yovutayo, n’naona dzanja la Yehova lamphamvu komanso lacikondi. Abale na alongo anagwapo kuti atithandize. Iwo anali kutiyendela, kutitumila mafoni, na kutikumbatila. Izi zinatithandiza kupilila. Popeza nilibe motoka, abale na alongo anali kunithandiza kuti nizipezeka ku misonkhano, komanso kupita mu ulaliki ngati ningathe.” Ni dalitso lalikulu kukhala m’banja lacikondi lauzimu limeneli.

TIMAYAMIKILA KUTI YEHOVA AMATISAMALILA MWACIKONDI

15. N’cifukwa ciyani ndife otsimikiza kuti n’zotheka kupilila mavuto?

15 Tonsefe tidzakumana na mayeso. Koma monga taphunzilila, mayesowo sitidzayang’anizana nawo patokha. Monga tate wacikondi, Yehova amatiyang’anila nthawi zonse. Iye ali nafe, ni wokonzeka kumva pempho lathu, komanso wofunitsitsa kutithandiza. (Yes. 43:2) Ndife otsimikiza kuti tingakwanitse kupilila mavuto, cifukwa iye watipatsa mowolowa manja zonse zofunikila zotithandiza kupilila. Watipatsa mwayi wa pemphelo, Baibo, cakudya cauzimu camwana alilenji, komanso abale na alongo acikondi amene amatithandiza tikakumana na mavuto.

16. Tingacite ciyani kuti tikhalebe m’cikondi ca Yehova?

16 Timayamikila kwambili kukhala na Atate wathu wakumwamba amene maso ake ali pa ife. “Mitima yathu imakondwela mwa iye.” (Sal. 33:21) Tingamuonetse Yehova kuti timayamikila cisamalilo cake cacikondi, mwa kuseŵenzetsa bwino zonse zimene amatipatsa kuti zitithandize. Tiyenelanso kucita mbali yathu kuti tikhalebe m’cikondi ca Mulungu. M’mawu ena, ngati tiyesetsabe kumvela Yehova, na kucita zoyenela pamaso pake, maso ake adzakhalabe pa ife mpaka kale-kale!—1 Pet. 3:12.

NYIMBO 30 Tate Wanga, Mulungu Wanga, Bwenzi Langa

a Timafunika thandizo la Yehova kuti tikwanitse kupilila mavuto amene timakumana. Nkhani ino itithandiza kuona kuti maso a Yehova alidi pa anthu ake. Iye amaona mavuto amene timakumana nawo aliyense payekha, ndipo amatipatsa zofunikila kuti tithane nawo mavutowo.

b Maina ena asinthidwa.