Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 35

Pitilizani “Kulimbikitsana”

Pitilizani “Kulimbikitsana”

“Pitilizani kutonthozana ndi kulimbikitsana.” —1 ATES. 5:11.

NYIMBO 90 Tilimbikitsane Wina na Mnzake

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Malinga na 1 Atesalonika 5:11, ni nchito iti imene tonsefe timagwila?

 KODI mpingo wanu unamangapo Nyumba ya Ufumu kapena kuikonzanso? Ngati n’conco, simuiŵala nthawi yoyamba imene munasonkhana m’Nyumba ya Ufumu imeneyo. Munamuyamikila kwambili Yehova. N’kutheka kuti munagwetsa misozi yacisangalalo cifukwa cokondwela, moti munalephela kuimba bwino nyimbo yotsegulila. Nyumba zathu za Ufumu zomangidwa bwino zimabweletsa citamando kwa Yehova. Koma pali nchito yomanga ya mtundu wina imene imabweletsa citamando cacikulu kwa Mulungu. Nchito imeneyo ni yofunika ngako kuposa yomanga zimango zenizeni. Imaphatikizapo kulimbikitsa anthu amene amabwela ku malo olambilila amenewo. Pa 1 Atesalonika 5:11 (ŵelengani), imene ni lemba la mutu wa nkhani ino, mtumwi Paulo anagwilitsa nchito mawu akuti “kulimbikitsana.” Mawuwa angatanthauzenso kumanga.

2. Kodi tikambilane ciyani m’nkhani ino?

2 Mtumwi Paulo ni citsanzo cabwino kwambili ca munthu amene anali kudziŵa bwino kulimbikitsa Akhristu anzake. Iye anali kutelo cifukwa cowacitila cifundo. M’nkhani ino, tikambilane mmene anathandizila abale na alongo ake (1) kupilila mayeso, (2) kukhala mwamtendele na ena, komanso (3) kulimbikitsa cikhulupililo cawo mwa Yehova. Tiyeni tione mmene tingatengele citsanzo cake kuti tizilimbikitsa abale na alongo athu masiku ano.—1 Akor. 11:1.

PAULO ANATHANDIZA ABALE NA ALONGO AKE KUPILILA MAYESO

3. Kodi Paulo anali na kapenyedwe kabwino kotani?

3 Paulo anali kuwakonda kwambili abale ake. Popeza iye anakumanapo na mavuto, anali kuonetsa cifundo cacikulu kwa Akhristu anzake akakumana na mavuto. Pa nthawi ina, Paulo ndalama zinam’thela. Conco anagwila nchito kuti apeze zosoŵa zake zakuthupi, komanso za amene anali naye. (Mac. 20:34) Iye anali wopanga mahema. Atafika ku Korinto, poyamba anali kugwila nchito yopanga mahema pamodzi na Akula na Purisikila. Koma “sabata lililonse” anali kulalikila Ayuda na Agiriki. Ndiyeno pamene Sila na Timoteyo anafika, “Paulo anatanganidwa kwambili ndi nchito yolalikila mawu a Mulungu.” (Mac. 18:2-5) Iye sanaiŵale kuti colinga cake cacikulu pa umoyo wake cinali kutumikila Yehova. Cifukwa cakuti anali kugwila nchito yolalikila mokangalika, iye anatha kulimbikitsa abale na alongo ake. Anawakumbutsa kuti sayenela kulola mavuto a pa umoyo, komanso kufuna-funa zosoŵa za banja kuwapangitsa kunyalanyaza “zinthu zofunika kwambili”—mbali zonse zokhudza kulambila Yehova.—Afil. 1:10.

4. Kodi Paulo na Timoteyo anawathandiza bwanji okhulupilila anzawo kupilila cizunzo?

4 Mpingo utangokhazikitsidwa ku Tesalonika, Akhristu atsopano anatsutsidwa kwambili. Pamene gulu la anthu aciwawa linalephela kupeza Paulo na Sila, anthuwo “anakokela abale ena kwa olamulila a mzindawo.” Ndipo anafuula kuti: “Anthu onsewa akucita zotsutsana ndi malamulo a Kaisara.” (Mac. 17:6, 7) Ganizilani cabe mantha amene Akhristu atsopanowo anakhala nawo ataona kuti anthu a mu mzindawo awaukila. Iwo akanabwelela m’mbuyo potumikila Yehova. Koma Paulo sanafune kuti zimenezo ziwacitikile. Ngakhale kuti iye na Sila anacoka mu mzindawo, anaonetsetsa kuti mpingo watsopanowo ukusamalidwa bwino. Paulo anakumbutsa Atesalonika kuti: “Tinatumiza Timoteyo m’bale wathu. . . , kuti adzakulimbitseni ndi kukutonthozani pa cikhulupililo canu, kuti pasapezeke wina wopatutsidwa ndi masautso amenewa.” (1 Ates. 3:2, 3) N’kutheka kuti Timoteyo anakumanapo na cizunzo mu mzinda wa Lusitara umene anali kukhala. Anaona mmene Paulo analimbikitsila abale kumeneko. Timoteyo ataona mmene Yehova anathandizila Akhristu a ku Lusitara, anatsimikizila abale na alongo atsopanowo kuti zinthu zidzakhala bwino.—Mac. 14:8, 19-22; Aheb. 12:2.

5. Kodi m’bale Bryant anapindula motani na thandizo la mkulu wina?

5 Kodi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake m’njila ina iti? Paulo na Baranaba atabwela ku Lusitara, Ikoniyo, na ku Antiokeya, “anawaikila akulu mumpingo uliwonse.” (Mac. 14:21-23) Mosakayikila, akulu amenewo analimbikitsa kwambili mpingo, monga mmene akulu masiku ano amacitila. Onani zimene m’bale wina dzina lake Bryant anakamba. Anati: “N’tafika zaka 15, atate anacoka panyumba, ndipo amayi anacotsedwa mu mpingo. N’namva monga nakanidwa, ndipo n’nakhwethemuka.” N’ciyani cinam’thandiza Bryant kupilila panthawi yovutayo? Mwini wake anati: “Mkulu wina dzina lake Tony anali kukamba nane pa misonkhano komanso panthawi zina. Ananifotokozela zitsanzo za anthu amene anakumanapo na mayeso koma anali acimwemwe. Anaŵelenga nane Salimo 27:10, ndipo nthawi zambili anali kukamba za Hezekiya, amene anatumikila Mulungu mokhulupilika olo kuti atate ake sanali citsanzo cabwino.” Kodi Bryant anapindula motani na thandizo la mkuluyo? Iye anati: “Cifukwa ca cilimbikitso ca m’bale Tony, m’kupita kwanthawi n’nayamba kucita utumiki wa nthawi zonse.” Inu akulu, muzikhala maso kuti muthandize anthu amene, monga Bryant, angafunike “mawu abwino” olimbikitsa.—Miy. 12:25.

6. Kodi Paulo anaseŵenzetsa bwanji zitsanzo za anthu akale kuti alimbikitse abale na alongo?

6 Paulo anakumbutsa Akhristu anzake kuti na mphamvu za Yehova, “mtambo wa mboni waukulu” unapilila mavuto. (Aheb. 12:1) Paulo anadziŵa kuti zitsanzo za anthu akale amene anapilila mavuto osiyana-siyana, zidzalimbikitsa abale na alongowo, komanso kuwathandiza kuika maganizo awo pa “mzinda wa Mulungu wamoyo.” (Aheb. 12:22) N’cimodzimodzinso masiku ano. Tonsefe timalimbikitsidwa tikamaŵelenga mmene Yehova anathandizila Gidiyoni, Baraki, Davide, Samueli, na ena ambili. (Aheb. 11:32-35) Nazonso zitsanzo zamakono za anthu okhulupilika zimatilimbikitsa. Ku likulu lathu, nthawi zambili amalandila makalata ocokela kwa abale na alongo, amene cikhulupililo cawo calimbilako pambuyo poŵelenga nkhani za atumiki a Yehova okhulupilika amakono.

PAULO ANAONETSA MMENE ABALE NA ALONGO ANGAKHALILE MWAMTENDELE NA ENA

7. Kodi tiphunzilapo ciyani pa uphungu wa Paulo wa pa Aroma 14:19-21?

7 Timalimbikitsa abale na alongo athu tikamakamba na kucita zinthu zolimbikitsa mtendele mu mpingo. Tisalole kuti kusemphana maganizo pa zinazake kutigaŵanitse. Ndipo tisamaumilile maganizo athu ngati palibe mfundo ya m’Malemba imene ingaphwanyidwe. Onani citsanzo ici. Mu mpingo wa ku Roma, munali Akhristu Aciyuda komanso amitundu ina. Cilamulo ca Mose citatha, alambili a Yehova analoledwa kudya cakudya ciliconse. (Maliko 7:19) Kucokela nthawiyo, Akhristu ena Aciyuda anamasuka n’kuyamba kudya zakudya zamitundu yosiyana-siyana. Koma ena sanatelo. Conco, mu mpingowo munakhala magaŵano cifukwa ca nkhani imeneyi. Paulo anaonetsa kufunika kosungitsa mtendele pamene anati: “Ndi bwino kusadya nyama kapena kusamwa vinyo kapena kusacita kalikonse kamene kamakhumudwitsa m’bale wako.” (Ŵelengani Aroma 14:19-21.) Paulo anathandiza Akhristu anzake kuona kuti kusamvana kumeneko kukanawononga mgwilizano wawo komanso wa mpingo. Iye analinso wokonzeka kusintha kacitidwe ka zinthu kuti apewe kukhumudwitsa ena. (1 Akor. 9:19-22) Nafenso tingalimbikitse ena na kusungitsa mtendele mwa kupewa kukangana pa nkhani zimene zangokhala makonda a munthu mwini.

8. Kodi Paulo anacita ciyani mu mpingo mutabuka nkhani imene ikanasokoneza mtendele?

8 Paulo anapeleka citsanzo cabwino cokhala mwamtendele na anthu a kaonedwe kosiyana pa nkhani zofunika kwambili. Mwacitsanzo, ena mu mpingo wa m’zaka za zana loyamba anaumilila mfundo yakuti anthu amitundu ina amene anakhala Akhristu adulidwe, mwina cifukwa coopa kutsutsidwa na Ayuda osakhala Akhristu. (Agal. 6:12) Paulo sanagwilizane nawo maganizo amenewo. Ndipo m’malo moumilila kuti anthu atsatile maganizo ake, modzicepetsa iye anakatula nkhaniyo kwa atumwi komanso akulu ku Yerusalemu. (Mac. 15:1, 2) Pamapeto pake, zimene anacitazo zinathandiza kuti Akhristuwo akhale acimwemwe, ndiponso kuti mu mpingo mukhale mtendele.—Mac. 15:30, 31.

9. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Paulo?

9 Pakabuka nkhani yaikulu, timalimbikitsa mtendele mwa kufuna-funa citsogozo ca awo amene Yehova waaika kuti asamalile mpingo. Nthawi zambili citsogozo cozikika pa Baibo cimapezeka m’zofalitsa zathu, komanso m’malangizo amene gulu la Mulungu limapeleka. Tikamaika mtima wathu pa kutsatila malangizowo m’malo moumilila maganizo athu, timathandiza kuti mu mpingo mukhale mtendele.

10. N’ciyani cina cimene Paulo anacita kuti alimbikitse mtendele mu mpingo?

10 Paulo analimbikitsa mtendele mwa kuchula makhalidwe abwino a abale na alongo ake, osati zimene sanali kucita bwino. Mwacitsanzo, kumapeto kwa kalata yake yopita kwa Aroma, iye anachula maina a anthu ambili. Anachulanso zabwino zimene ambili a iwo anali kucita. Tingatengele citsanzo ca Paulo mwa kumasuka kuchula makhalidwe abwino a abale na alongo athu. Tikatelo, timawathandiza kukhala okondana kwambili. Izi ndiye zimamangiliza mpingo m’cikondi.

11. Kodi mtendele tingaubwelezeletse bwanji pakabuka mkangano?

11 Nthawi zina, ngakhale Akhristu okhwima angasemphane maganizo kapena kukangana wina na mnzake. N’zimene zinacitika kwa Paulo na mnzake wapamtima Baranaba. Amuna aŵiliwa anakangana kwambili pa nkhani yakuti atenge Maliko pa ulendo wawo wotsatila wa umishonale. Panali “mkangano woopsa” pakati pawo moti anapatukana. (Mac. 15:37-39) Koma Paulo, Baranaba, na Maliko anakonzanso ubale wawo, kuonetsa kuti mtendele na mgwilizano mu mpingo unali wofunika kwambili. Pambuyo pake, Paulo anakamba zabwino za Baranaba na Maliko. (1 Akor. 9:6; Akol. 4:10) Nafenso tiyenela kuthetsa kusamvana kulikonse na ena mu mpingo, na kupitiliza kuona zabwino mwa iwo. Tikatelo, tidzalimbikitsa mtendele na mgwilizano.—Aef. 4:3.

PAULO ANALIMBITSA CIKHULUPILILO CA ABALE NA ALONGO

12. Ni mavuto ena ati amene abale na alongo athu amakumana nawo?

12 Timalimbikitsa abale na alongo tikamalimbitsa cikhulupililo cawo mwa Yehova. Ena amasekedwa na acibale amene si Mboni, anzawo a kunchito, kapena a kusukulu. Ena akudwala matenda aakulu, kapena akuvutika kuti athetse maganizo odziimba mlandu. Ndipo ena amene anabatizika kale-kale, kwa nthawi yaitali akhala akuyembekezela mapeto a dongosolo lino. Mikhalidwe imeneyi ingaike cikhulupililo ca Akhristu masiku ano pa mayeso. Akhristu mu mpingo wa m’zaka za zana loyamba anakumana na mavuto ofanana na amenewa. Kodi Paulo anacita ciyani kuti alimbikitse abale na alongo amenewo?

Mofanana na mtumwi Paulo, kodi tingawalimbikitse bwanji ena (Onani ndime 13) b

13. Kodi Paulo anawathandiza bwanji aja amene anali kusekewa cifukwa ca zimene anali kukhulupilila?

13 Paulo anagwilitsa nchito Malemba polimbitsa cikhulupililo ca abale na alongo. Mwacitsanzo, Akhristu a Ciyuda mwina sanali kudziŵa zimene akanayankha acibale awo osakhulupilila amene anali kukamba kuti Ciyuda cinali copambana Cikhristu. Kalata imene Paulo analembela Aheberi mosakayikila inawalimbikitsa kwambili Akhristuwo. (Aheb. 1:5, 6; 2:2, 3; 9:24, 25) Iwo akanatha kuseŵenzetsa zimene iye analemba poyankha acibale awo amenewo. Masiku ano, tingathandize Akhristu anzathu amene amasekedwa, kuti aziseŵenzetsa zofalitsa zozikika pa Baibo pofotokoza za cikhulupililo cawo. Ngati acicepele athu amasekewa cifukwa cokhulupilila kuti zamoyo zinacita kulengedwa, tingawathandize kupeza mfundo zothandiza m’bulosha yakuti, Kodi Zamoyo Zinacita Kulengedwa? komanso yakuti Mmene Moyo Unayambira—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri. Mabulosha amenewa aonetsa cifukwa cake timakhulupilila kuti zamoyo zinacita kulengedwa.

Mofanana na mtumwi Paulo, kodi tingawalimbikitse bwanji ena (Onani ndime 14) c

14. Kodi Paulo anacitanso ciyani ngakhale kuti anali kutangwanika na nchito yolalikila na kuphunzitsa?

14 Paulo analimbikitsa abale na alongo kuonetsa cikondi mwa kucita “nchito zabwino.” (Aheb. 10:24) Iye anathandiza abale na alongo m’mawu komanso m’zocita. Mwacitsanzo, pamene Akhristu anzake anakumana na vuto la njala yadzaoneni, Paulo anathandizila kupeleka zinthu zofunikila kwa iwo. (Mac. 11:27-30) Ngakhale kuti iye anali kutangwanika na nchito yolalikila na kuphunzitsa, nthawi zonse anali kupeza mipata yothandizila osoŵa kuthupi. (Agal. 2:10) Mwa kutelo, iye analimbikitsa Akhristu anzakewo kukhala na cidalilo cakuti Yehova adzawasamalila. Masiku ano, tikamadzipeleka kugwilitsa nchito nthawi yathu, mphamvu zathu, komanso maluso athu kuti tithandize pakagwa tsoka, timalimbitsa cikhulupililo ca abale na alongo athu. Tingacitenso zimenezi mwa kucita copeleka pa nchito ya padziko lonse. Mwa njila zimenezi komanso zina, timathandiza abale na alongo athu kukhulupilila kuti Yehova sadzawasiya ngakhale pang’ono.

Mofanana na mtumwi Paulo, kodi tingawalimbikitse bwanji ena (Onani ndime 15-16) d

15-16. Kodi tingawalimbikitse bwanji amene cikhulupililo cawo cafooka?

15 Paulo sanaleke kulimbikitsa amene cikhulupililo cawo cinali cofooka. Anawaonetsa cifundo, ndipo anakamba nawo mwaubwenzi komanso molimbikitsa. (Aheb. 6:9; 10:39) Mwacitsanzo, polemba kalata yopita kwa Aheberi, iyenso anadziloŵetsamo pogwilitsa nchito mawu akuti “tiganizile mozama” komanso akuti “tisatengeke.” Izi zionetsa kuti nayenso anafunikila kuseŵenzetsa uphungu wake umenewo. (Aheb. 2:1, 3) Monga Paulo, sitileka kulimbikitsa anthu amene cikhulupililo cawo cafooka. Kucita izi kumaonetsa kuti timawakonda. Makambidwe athu aubwenzi angawalimbikitsenso kwambili.

16 Paulo anawatsimikizila abale na alongo ake kuti Yehova anali kudziŵa nchito zawo zabwino. (Aheb. 10:32-34) Nafenso tingacite cimodzimodzi pothandiza Mkhristu mnzathu amene cikhulupililo cake cafooka. Tingam’pemphe kuti atiuzeko cimene cinam’pangitsa kuti aphunzile coonadi. Kapena, tingam’limbikitse kuganizila zocitika pamene anaona kuti Yehova wam’thandiza. Tingatengele mwayi mpata umenewu kuti tim’tsimikizile kuti Yehova sanaiŵale nchito zake zoonetsa kuti amam’konda, komanso kuti sadzamusiya. (Aheb. 6:10; 13:5, 6) Makambilano otelo akhoza kulimbikitsa abale athu amenewo kuti apitilize kutumikila Mulungu.

“PITILIZANI KUTONTHOZANA”

17. Ni maluso ati amene tiyenela kupitiliza kuwakulitsa?

17 Monga mmene wogwila nchito ya mamangidwe amakulitsila maluso ake m’kupita kwa nthawi, nafenso tinganole maluso athu kuti tizilimbikitsa ena mogwila mtima. Tingawathandize kupeza mphamvu zotha kupilila mayeso mwa kuwauzako zitsanzo za anthu akale amene anapilila. Tingalimbikitsenso mtendele mu mpingo mwa kuchula zabwino zimene ena amacita, kusungitsa mtendele pakabuka nkhani imene ingausokoneze, komanso kubwezeletsa mtendele tikasemphana maganizo na ena. Cina, tingalimbitsebe cikhulupililo ca abale na alongo athu powauzako mfundo zofunika za coonadi ca m’Baibo, kuwathandiza pa zosoŵa zawo, ndiponso polimbikitsa aliyense amene wafooka mwauzimu.

18. Kodi mudzayesetsa kucita ciyani?

18 Abale na alongo amene amagwila nchito zomanga za gulu amakhala acimwemwe komanso okhutila. Nafenso timakhala acimwemwe komanso okhutila tikamalimbitsa cikhulupililo ca abale na alongo athu. Mosiyana na zimango zenizeni zimene zimawonongeka m’kupita kwa nthawi, zotulukapo za utumiki wathu wolimbikitsa ena zimakhala zabwino mpaka kale-kale. Conco tiyeni tiziyesetsa “kutonthozana ndi kulimbikitsana.”—1 Ates. 5:11.

NYIMBO 100 Alandileni na Manja Aŵili

a Umoyo m’dzikoli ni wovuta. Abale na alongo athu amakumana na mavuto osiyana-siyana. Tingakhale dalitso kwa iwo ngati timapeza mipata yakuti tiwalimbikitse. Kukambilana citsanzo mtumwi Paulo kutithandiza pa nkhani imeneyi.

b MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Tate akuonetsa mwana wake mmene angagwilitsile nchito mfundo za m’zofalitsa zathu kuti apewe kukondwelela Khrisimasi.

c MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Banja lapita kudela lina kukathandiza amene akhudzidwa na tsoka la zacilengedwe.

d MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Mkulu akulimbikitsa m’bale amene cikhulupililo cake cafooka. Akuonetsa m’baleyo mapikica a Sukulu ya Utumiki Waupainiya imene analoŵela pamodzi kumbuyoko. Mapikicawo am’kumbutsa nthawi pamene anali kusangalala na utumiki. M’baleyo wayamba kulakalaka cimwemwe cimene anali naco pamene anali kutumikila Yehova. Potsilizila pake, iye akuyambanso kucita zauzimu.