Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 34

‘Yendanibe M’coonadi’

‘Yendanibe M’coonadi’

‘Yendanibe m’coonadi.’—3 YOH. 4.

NYIMBO 111 Zifukwa Zokhalila Acimwemwe

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Kodi kukambilana za mmene tinaphunzilila “coonadi” kumatipindulila bwanji?

 “KODI munaphunzila bwanji coonadi?” Mosakayika konse, mwakhala mukuyankha funso limeneli maulendo ambili. Ili ni limodzi mwa mafunso amene timafunsa tikafuna kudziŵa zoculuka za Mkhristu mnzathu. Timakonda kumva mmene abale na alongo anadziŵila Yehova na kum’konda. Ndipo nafenso timakondwela kuwauzako cimene cinatikopa kuti tiyambe kukonda coonadi. (Aroma 1:11) Makambilano otelo amatikumbutsa kuti coonadi n’camtengo wapatali kwa ife. Cina, timakhala ofunitsitsa kwambili ‘kuyendabe m’coonadi,’ kapena kuti kukhala na umoyo umene umapangitsa Yehova kuti atiyanje na kutidalitsa.—3 Yoh. 4.

2. Kodi tikambilane ciyani m’nkhani ino?

2 M’nkhani ino, tikambilane zifukwa zina zimene zinatipangitsa kuyamba kukonda coonadi. Kenako, tikambilane mmene tingapitilizile kuonetsa kuti timaikonda mphatso yamtengo wapatali imeneyi. Kukambilana zimenezi kudzakulitsa ciyamikilo cathu pa Yehova potikokela m’coonadi. (Yoh. 6:44) Kudzakulitsanso cifuno cathu cophunzitsako ena coonadi ca m’Baibo.

CIFUKWA CAKE “COONADI” TIMACIKONDA

3. N’cifukwa cacikulu citi cimene timakondela coonadi?

3 Coonadi timacikonda pa zifukwa zambili. Koma cacikulu n’cakuti cimatiphunzitsa za Yehova Mulungu, amene ndiye Gwelo la coonadi. Kupitila m’Mawu ake Baibo, tinafika pom’dziŵa Mulungu monga wamphamvuzonse, amene analenga kumwamba na dziko lapansi. Komanso kuti iye ni Atate wathu wakumwamba amene amatisamalila mwacikondi. (1 Pet. 5:7) Tinafikanso podziŵa kuti Mulungu ni “wacifundo ndi wacisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi coonadi.” (Eks. 34:6) Yehova amakonda cilungamo. (Yes. 61:8) Ndiye cifukwa cake cimamuŵaŵa akamationa tikuvutika. Conco, iye ni wokonzeka kudzacotsapo mavuto onse panthawi yake yoikika. Inde, ni wofunitsitsa kudzatelo. (Yer. 29:11) N’zocititsa cidwi kwambili! M’pake kuti Yehova timam’konda kwambili.

Coonadi ca m’Baibo Cili Ngati . . . Nangula

Monga mmene nangula amathandizila boti kuti isamatengeke-tengeke na mafunde, naconso ciyembekezo cathu cozikika pa Baibo cimatithandiza kusasunthika tikakumana na mayeso. Coonadi ca m’Baibo cimatisonkhezelanso kuuzako ena za ciyembekezo cathu ca zam’tsogolo (Onani ndime 4-7)

4-5. N’cifukwa ciyani mtumwi Paulo anakamba kuti ciyembekezo cili monga nangula?

4 N’cifukwa cina citi cimene timakondela coonadi? Coonadi cimatipindulila m’njila zambili. Ganizilani citsanzo ici. Coonadi ca m’Baibo cimaphatikizapo ciyembekezo cathu ca zam’tsogolo. Pofotokoza kufunika kwa ciyembekezoco, mtumwi Paulo anati: “Ciyembekezo cimene tili nacoci cili ngati nangula wa miyoyo yathu ndipo n’cotsimikizika ndiponso cokhazikika.” (Aheb. 6:19) Monga mmene nangula amathandizila boti kuti isamatengeke-tengeke na mafunde, naconso ciyembekezo cathu cozikika pa Baibo cimatithandiza kusasunthika tikakumana na mayeso.

5 Apa Paulo anali kufotokoza za ciyembekezo copita kumwamba ca Akhristu odzozedwa. Koma mawuwa amagwilanso nchito kwa Akhristu amene ali na ciyembekezo codzakhala na moyo kwamuyaya m’paradaiso padziko lapansi. (Yoh. 3:16) Kukamba zoona, kuphunzila za ciyembekezo ca moyo wosatha kwapangitsa umoyo wathu kukhala waphindu.

6-7. Kodi mlongo Yvonne wapindula bwanji pophunzila coonadi conena zam’tsogolo?

6 Ganizilani za mlongo wina dzina lake Yvonne. Iye sanakulile m’coonadi, ndipo ali mwana imfa anali kuiopa kwambili. Saiŵala mawu amene anaŵelengapo akuti: “Tsiku lina dziko lidzatha.” Iye anati: “Tsiku limenelo n’nakangiwa kugona usiku wonse. N’nali kungoganizila za tsogolo langa. N’nali kuganiza kuti: ‘Moyo uyenela kukhala na colinga. N’cifukwa ciani nili na moyo?’ N’nali kuopa imfa kwambili.”

7 Yvonne atakula n’kukhala mtsikana, anakumana na Mboni za Yehova. Iye anati: “N’nayamba kukhulupilila kuti n’zotheka ine kudzakhala na moyo wamuyaya m’paradaiso padziko lapansi.” Kodi kuphunzila coonadi kwam’pindulila motani mlongo wathu ameneyu? Mwini wake anati: “Masiku ano, sinilephelanso kugona usiku cifukwa coopa zam’tsogolo kapena imfa.” Monga mwaonela, coonadi n’cofunika ngako kwa Yvonne. Ndipo amasangalala kwambili kumauzako ena za ciyembekezo cake ca zam’tsogolo.—1 Tim. 4:16.

Coonadi ca m’Baibo Cili Ngati . . . Cuma

Kutumikila Yehova pali pano, komanso m’tsogolo mu Ufumu wa Mulungu, kuli ngati cuma. Kumaposa ciliconse cimene tingadzimane (Onani ndime 8-11)

8-9. (a) M’fanizo la Yesu, kodi munthu wina anaciona motani cuma cimene anapeza? (b) Kodi inu pacanu mumaciona motani coonadi?

8 Coonadi ca m’Baibo ciphatikizaponso uthenga wabwino wokamba za Ufumu wa Mulungu. Yesu anayelekezela coonadi cokamba za Ufumu na cuma cobisika. Pa Mateyu 13:44 Yesu anati: “Ufumu wakumwamba uli ngati cuma cobisika m’munda, cimene munthu anacipeza n’kucibisa. Cifukwa ca cimwemwe cimene anali naco, anapita kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo n’kukagula mundawo.” Pa lembali, munthuyu sanali kufuna-funa cuma ayi. Koma atacipeza, anadzimana zinthu zambili kuti akhale naco. Iye anacita kugulitsa zonse zimene anali nazo. Cifukwa ciyani? Cifukwa anaona kuti cumaco n’camtengo wapatali kuposa zonse zimene iye anagulitsa.

9 Kodi umu ni mmene inunso mamacionela coonadi? Mosakayika konse! Tidziŵa kuti palibe cingalingane na cimwemwe cimene timakhala naco cifukwa cotumikila Yehova pali pano, tili na ciyembekezo ca moyo wosatha mu Ufumu wa Mulungu. Kukhala pa ubale wolimba na Yehova n’kofunika kwambili kuposa ciliconse cimene tingadzimane. Ndipo timakondwela kucita ‘zomukondweletsa pa ciliconse.’—Akol. 1: 10.

10-11. N’ciyani cinasonkhezela m’bale Michael kusintha zinthu kwambili pa umoyo wake?

10 Tonsefe tadzimana zinthu zambili kuti Yehova atiyanje. Ena analeka nchito zapamwamba m’dzikoli. Ndipo enanso anasiya kufuna-funa cuma kuti alemele. Palinso ena amene anasinthilatu umoyo wawo ataphunzila za Yehova. Izi n’zimene m’bale Michael anacita. Iye sanakulile m’coonadi. Ali mnyamata, anaphunzitsidwa maseŵela omenyana ochedwa karati. Iye anati: “N’nali kukonda kwambili kucita maseŵela olimbitsa thupi kuti nizioneka wamphamvu, ndipo nthawi zina n’nali kuona kuti palibe amene anganigonjetse.” Koma Michael atayamba kuphunzila Baibo, anadziŵa kuti Yehova sakondwela nazo zaciwawa. (Sal. 11:5) Ponena za banja limene linali kum’phunzitsa Baibo, Michael anati: “Iwo sananiuze kuti nisiye karati. M’malomwake, anali kungoniphunzitsa zimene Baibo imanena.”

11 Pamene Michael anali kuphunzila zambili za Yehova, m’pamenenso cikondi cake pa iye cinali kukulila-kulila. Iye anakhudzidwa kwambili kuona kuti Yehova amawacitila cifundo alambili ake. M’kupita kwanthawi, Michael anazindikila kuti ayenela kusintha umoyo wake. Iye anati: “N’naona kuti kunali kovuta kwambili kusiya karati. Koma n’nadziŵa kuti kucita zimenezi kusangalatsa Yehova. Conco, n’naona kuti kum’tumikila kunaposa ciliconse cimene ningadzimane.” M’bale Michael anaona kuti coonadi cimene anapeza n’camtengo wapatali. Ndiye cifukwa cake anasintha zinthu kwambili pa umoyo wake.—Yak. 1:25.

Coonadi ca m’Baibo Cili Ngati . . . Nyale

Nyale yoyaka bwino imatiunikila njila mu mdima. Mofananamo, Mawu a Mulungu amatiunikila njila m’dziko la Satana la mdimali (Onani ndime 12-13)

12-13. Kodi coonadi ca m’Baibo cam’thandiza bwanji Mayli?

12 Baibo imaonetsa kuti coonadi n’cofunika kwambili, moti imaciyelekezela na nyale younikila mu mdima. (Sal. 119:105; Aef. 5:8) Mlongo Mayli wa ku Azerbaijan, amayamikila ngako mmene Mawu a Mulungu am’thandizila. Iye anakulila m’banja la zipembedzo zosiyana. Atate ake anali Msilamu, koma amayi ake anali Myuda. Mlongoyu anati: “Ngakhale kuti sin’nali kutsutsa zakuti Mulungu aliko, panali nkhani zina zimene zinali kunizunguza mutu. N’nali kudzifunsa kuti, ‘N’cifukwa ciyani Mulungu analenga anthu? Nanga pali cilungamo canji kuti munthu amene akuvutika paumoyo wake akazunzikenso ku helo kwamuyaya?’ Popeza kuti anthu ambili amakamba kuti zinthu zonse zimene zimacitika ni cifunilo ca Mulungu, n’nali kudzifunsa kuti: ‘Kodi Mulungu amacititsa mavuto a anthu ndiyeno n’kumakondwela akaona kuti akuvutika?’”

13 Mayli anapitiliza kufuna-funa mayankho pa mafunso ake. M’kupita kwanthawi anayamba kuphunzila Baibo, ndipo anakhala Mboni ya Yehova. Iye anati: “Mfundo za coonadi ca m’Baibo zinasintha umoyo wanga kukhala wabwino. Mfundo zomveka komanso zodalilika za m’Mawu a Mulungu zinanithandiza kukhala na mtendele wa maganizo.” Mofanana na Mayli, tonsefe timatamanda Yehova “amene [anatiitana] kucoka mu mdima kuloŵa m’kuwala kwake kodabwitsa.”—1 Pet. 2:9.

14. Kodi tingacite ciyani kuti ticikonde kwambili coonadi? (Onani bokosi lakuti, “ Kuyelekezela Kwina.”)

14 Izi ni zina mwa zitsanzo zoonetsa phindu la coonadi. N’kutheka kuti inunso mwaganizilako zitsanzo zina. Pa phunzilo la inu mwini, bwanji osapezanso zifukwa zina zimene timacikondela coonadi? Tikamacikonda kwambili coonadi, timapezanso njila zoonetsela kuti timacikonda.

MMENE TIMAONETSELA KUTI TIMACIKONDA COONADI

15. Kodi tingaonetse bwanji kuti coonadi timacikonda?

15 Timaonetsa kuti coonadi timacikonda mwa kuŵelenga Baibo, na zofalitsa zozikika pa Baibo. Kaya takhala m’coonadi nthawi yoculuka motani, nthawi zonse pamakhala zambili zofunika kuphunzila. Magazini yoyamba ya Nsanja ya Mlonda inati: “Coonadi cili ngati duŵa laling’ono m’sanga, limene lili pakati pa viudzu vimene vatsala pang’ono kuliphimba. Kuti mulipeze, mufunika kusakila mwakhama. . . . Kuti mukhale nalo, mufunika kuŵelama na kulitenga. Musakhutile na duŵa limodzi cabe la coonadi. . . . Pitilizani kusakila ena ambili, musaleke.” Kuphunzila kumafuna khama, koma kumapindulitsa.

16. Kodi inu pacanu, ni njila iti yothandiza imene mumagwilitsa nchito poŵelenga na kuphunzila coonadi? (Miyambo 2:4-6)

16 Si tonse amene timakonda kuŵelenga na kuphunzila. Koma Yehova akutipempha kuti ‘tizifuna-funa’ coonadi na ‘kucifufuza’ kuti ticimvetsetse. (Ŵelengani Miyambo 2:4-6.) Tikamayesetsa mwakhama, tidzapindula. Ponena za kuŵelenga Baibo payekha, m’bale Corey anakamba kuti amafufuza vesi iliyonse payokha. Iye anati: “Nimaŵelenga mawu a m’munsi, mavesi ena ofotokoza mfundo yofanana na ya vesiyo, ndiponso kufufuza m’mabuku ena. . . . Nimadziŵa zambili cifukwa coŵelenga mwa njila imeneyi.” Kaya timagwilitsa nchito njila imeneyi kapena ina, timaonetsa kuti timayamikila coonadi pothelapo nthawi yociphunzila, komanso kuikilapo mtima.—Sal. 1:1-3.

17. Kodi kukhala m’coonadi kutanthauza ciyani? (Yakobo 1:25)

17 Tidziŵa kuti kungophunzila coonadi pakokha sikokwanila. Kuti tipindule kwambili, tiyenela kukhala m’coonadi. Kutanthauza kuti tiyenela kugwilitsa nchito zimene timaphunzila pa umoyo wathu. Tikatelo, coonadi cidzatibweletsela cimwemwe ceniceni. (Ŵelengani Yakobo 1:25.) Tingacite ciyani kuti tionetsetse kuti tikukhala m’coonadi? M’bale wina anakamba kuti tiyenela kudzifufuza kuti tione zimene timacita bwino, na zimene siticita bwino kuti tiwongolele. Mtumwi Paulo anati: “Mulimonse mmene tapitila patsogolo, tiyeni tipitilize kupita patsogolo mwa kuyenda moyenela m’njila yomweyo.”—Afilipi 3:16.

18. N’cifukwa ciyani timayesetsa ‘kuyendabe m’coonadi’?

18 Tangoganizilani mapindu amene timapeza tikamayesetsa ‘kuyendabe m’coonadi.’ Timakhala na umoyo wabwino, komanso timakondweletsa Yehova na okhulupilila anzathu. (Miy. 27:11; 3 Yoh. 4) Izi n’zifukwa zabwino zotipangitsa kukonda coonadi, na kugwilitsa nchito zimene timaphunzila.

NYIMBO 144 Yang’ana pa Mphoto

a Tikamati “coonadi,” nthawi zambili timatanthauza zimene timakhulupilila komanso umoyo wathu wacikhristu. Kaya ndife atsopano m’coonadi kapena aciyambakale, tingapindule kwambili mwa kuganizila cimene cinatipangitsa kuyamba kukonda coonadi. Tikatelo, tidzakhala ofunitsitsa kucita zokondweletsa Yehova.