NKHANI YOPHUNZILA 35
Khalanibe Oleza Mtima
“Valani . . . kuleza mtima.”—AKOL. 3:12.
NYIMBO 114 “Khalani Oleza Mtima”
ZIMENE TIKAMBILANE a
1. N’cifukwa ciyani timawayamikila anthu oleza mtima?
TONSEFE timawayamikila anthu oleza mtima. Inde, timawalemekeza anthu amene amatha kuyembekezela popanda kukhumudwa. Timayamikilanso kuti anthu ena amatilezela mtima tikalakwitsa. Ndiponso timayamikila kuti amene anatiphunzitsa Baibo analeza nafe mtima pamene tinali kuvutikila kuphunzila mfundo za m’Baibo, kuzivomeleza, na kuzigwilitsa nchito. Coposa zonse, timayamikila kwambili kuti Yehova Mulungu amaleza nafe mtima.—Aroma 2:4.
2. Ni pa zocitika ziti pamene zingativute kukhala oleza mtima?
2 Ngakhale kuti timayamikila kuleza mtima kwa anthu ena, nthawi zina ife tomwe zingamativuke kukhala oleza mtima. Mwacitsanzo, kuleza mtima kungativute tikakhala pa mzele wautali kucipatala, maka-maka nthawi ikatithela yocitanso zinthu zina. Kapena tingalephele kuugwila mtima ena akatikhumudwitsa. Ndipo nthawi zina, cingakhale covuta kuyembekezela lonjezo la Yehova la dziko latsopano. Kodi mungakonde kukulitsa khalidwe la kuleza mtima? M’nkhani ino, tikambilane zimene kuleza mtima kumatanthauza, komanso cifukwa cake n’kofunika kwambili. Tikambilanenso cimene cingatithandize kukulitsa khalidwe limeneli.
KODI KULEZA MTIMA N’KUTANI?
3. Kodi munthu woleza mtima amatani anthu ena akamukhumudwitsa?
3 Tingakhale oleza mtima m’njila zinayi izi. Yoyamba, munthu woleza mtima sakwiya msanga. Amayesetsa kukhalabe wodekha, na kusabwezela anthu ena akamukhumudwitsa kapena akapanikizika maganizo. Mawu akuti “wosakwiya msanga” anaonekela koyamba m’Baibo pamene Yehova anadzifotokoza kuti ni “Mulungu wacifundo ndi wacisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi coonadi.”—Eks. 34:6.
4. Kodi munthu woleza mtima amatani pa nkhani yoyembekezela zinazake?
4 Yaciŵili, munthu woleza mtima amayembekezela modekha. Ngati cinthu sicinacitike panthawi imene anali kuciyembekezela, iye amakhalabe wodekha, ndipo sakhumudwa. (Mat. 18:26, 27) Pali mbali zambili zofuna kuti tiziyembekezela modekha. Mwacitsanzo, wina akamalankhula tiyenela kumvetsela modekha, mosam’dula mawu. (Yobu 36:2) Tingafunikilenso kuleza mtima pothandiza wophunzila wathu kumvetsa ziphunzitso za m’Baibo, kapena kuthetsa zizoloŵezi zoipa.
5. Ni njila ina iti imene tingaonetsele kuleza mtima?
5 Yacitatu, munthu woleza mtima sacita zinthu mwaphuma. N’zoona kuti zocitika zina zimafuna kucitapo kanthu mwamsanga. Komabe, munthu woleza mtima akamagwila nchito yofunika kwambili, saigwila mothamanga kuti aimalize mmangu-mmangu. M’malo mwake, amapatula nthawi yokwanila yolinganiza bwino mmene agwilile nchitoyo. Kenaka, amadekha poigwila.
6. Kodi munthu woleza mtima amatani akakumana na mavuto?
6 Yacinayi, munthu woleza mtima amayesetsa kupilila mavuto popanda kudandaula. Munthu woleza mtima amakhalanso wopilila. N’zoona kuti sikulakwa kuuzako mnzathu moona mtima mmene tikumvela pa mavuto athu. Komabe, munthu woleza mtima samangokhalila kudandaula. Koma amaganizila madalitso amene ali nawo, ndipo amatumikilabe Yehova mwacimwemwe. (Akol. 1:) Monga Akhristu, tiyenela kukhala oleza mtima pambali zonsezi. Cifukwa? Tiyeni tioneko zifukwa zingapo. 11
CIFUKWA CAKE KULEZA MTIMA N’KOFUNIKA KWAMBILI
7. Malinga na Yakobo 5:7, 8, n’cifukwa ciyani kuleza mtima n’kofunika kwambili? (Onaninso cithunzi.)
7 Kuleza mtima n’kofunika kuti tikapulumuke. Mofanana na atumiki a Yehova okhulupilika akale, nafenso tiyenela kuyembekezela moleza mtima kuti Mulungu akwanilitse malonjezo ake. (Aheb. 6:11, 12) Baibo imatiyelekezela na mlimi. (Ŵelengani Yakobo 5:7, 8.) Mlimi amagwila nchito molimbika pobyala na kusamalila mbewu zake. Koma sadziŵa nthawi yeniyeni pamene mbewuzo zidzakula. Amangoyembekezela moleza mtima, ali na cikhulupililo cakuti adzakolola. Mofananamo, timakhala otangwanika na zinthu zauzimu ngakhale kuti ‘sitidziŵa tsiku limene Ambuye wathu adzabwela.’ (Mat. 24:42) Timayembekezelabe moleza mtima, tili na cidalilo cakuti Yehova adzakwanilitsa malonjezo ake onse pa nthawi yake. Tikapanda kukhala oleza mtima, tingatope na kuyamba kusiya coonadi. Cina, tingayambe kufuna-funa zinthu zotipatsa cimwemwe ca panthawi yomweyo. Koma tikakhala oleza mtima tidzapilila mpaka mapeto, ndipo tidzapulumuka.—Mika 7:7; Mat. 24:13.
8. Kodi kuleza mtima kumatithandiza bwanji pocita zinthu na anthu ena? (Akolose 3:12, 13)
8 Kuleza mtima kumatithandiza pocita zinthu na anthu ena. Kumatithandiza kumvetsela modekha ena akamalankhula. (Yak. 1:19) Kuleza mtima kumalimbikitsanso mtendele. Kumatiteteza kuti tisacite zinthu mopupuluma, na kukamba zinthu zosayenela tikapanikizika maganizo. Ndipo tikakhala oleza mtima, sitidzakwiya msanga wina akatikhumudwitsa. M’malo mobwezela, ‘tidzapitiliza kulolelana na kukhululukilana ndi mtima wonse.’—Ŵelengani Akolose 3:12, 13.
9. Kodi kuleza mtima kumatithandiza bwanji popanga zisankho? (Miyambo 21:5)
9 Kuleza mtima kungatithandizenso kupanga zisankho zabwino. M’malo modya mfulumila, tidzapatula nthawi yofufuza na kusanthula zisankhozo kuti tione zimene zili zabwino koposa. (Ŵelengani Miyambo 21:5.) Mwacitsanzo, tikamakufuna-funa nchito, tingafulumile kuvomela nchito iliyonse imene yapezeka, ngakhale kuti nchitoyo idzasokoneza kulambila kwathu Yehova. Komabe, tikakhala oleza mtima, tidzakhala pansi na kuganizila zinthu monga mayendedwe, maola ogwila nchito, komanso mmene idzakhudzila banja lathu na umoyo wathu wauzimu. Tikakhala oleza mtima, tidzapewa kupanga zisankho zoipa.
MMENE TINGAKULITSILE KULEZA MTIMA
10. Kodi Mkhristu angakulitse bwanji kuleza mtima?
10 Muzipempela kuti mukulitse kuleza mtima. Kuleza mtima ni cipatso cimene mzimu woyela umabala. (Agal. 5:22, 23) Conco, tiyenela kupempha mzimu woyela wa Yehova kuti utithandize kukulitsa cipatso cimeneci. Kuleza mtima kwathu kukakhala pa mayeso, ‘tidzapemphabe’ mzimu woyela kuti utithandize kukhala oleza mtima. (Luka 11:9, 13) Tingapemphenso Yehova kuti atithandize kuona zinthu mmene iye amazionela. Pambuyo popemphela, tiyenela kuyesetsa kukhala oleza mtima tsiku lililonse. Tikamapemphela kwambili kuti tikhale oleza mtima, na kuyesetsa kukhala otelo, khalidweli lidzazika mizu mumtima mwathu. Ndipo lidzakhala umunthu wathu.
11-12. Kodi Yehova waonetsa bwanji kuleza mtima?
11 Muzisinkhasinkha zitsanzo za m’Baibo. M’Baibo muli zitsanzo zambili za anthu amene anali oleza mtima. Tikamasinkhasinkha zitsanzo zimenezo, tidzaphunzila mmene tingaonetsele kuleza mtima. Tisanakambilane zina mwa zitsanzozo, tiyeni coyamba tione citsanzo ca kuleza mtima cabwino koposa ca Yehova.
12 M’munda wa Edeni, Satana ananeneza Yehova na kuipitsa mbili yake ponena kuti si wacilungamo, komanso kuti ni Wolamulila wopanda cikondi. M’malo momuwononga nthawi yomweyo, Yehova analeza mtima na kudziletsa, podziŵa kuti padzatenga nthawi kuti anthu akhulupililedi kuti ulamulilo wake ndiwo wabwino koposa. Ndipo pomwe akuyembekezela kuti nkhaniyo ithe, iye wakhala akupilila cinenezo pa dzina lake. Kuwonjezela apo, Yehova wakhala akuyembezela moleza mtima kuti anthu ambili akhale na mwayi wokalandila moyo wosatha. (2 Pet. 3:9, 15) Cifukwa ca kuleza mtima kwake, anthu mamiliyoni afika pom’dziŵa. Tikamaika maganizo athu pa mapindu amene akhalapo cifukwa ca kuleza mtima kwa Yehova, cidzakhala cofeŵa kwa ife kuyembekezela nthawi imene adzabweletsa mapeto a dzikoli.
13. Kodi Yesu anaonetsa motani kuleza mtima potengela Atate wake? (Onaninso cithunzi.)
13 Yesu amatengela ndendende kuleza mtima kwa Atate wake, ndipo anaonetsa khalidwe limeneli ali pano padziko lapansi. Sicinali capafupi kwa iye nthawi zonse kukhala woleza mtima, maka-maka kwa alembi onyenga na Afarisi. (Yoh. 8:25-27) Koma mofanana na Atate wake, Yesu sanali kukwiya msanga. Iye sanabwezele pamene anthu anali kumunyoza. (1 Pet. 2:23) Anapilila moleza mtima mayeso popanda kudandaula. Ndiye cifukwa cake Baibo imatiuza kuti: “Ganizilani mozama za munthu amene anapilila malankhulidwe onyoza ngati amenewo a anthu ocimwa.” (Aheb. 12:2, 3) Mwa thandizo la Yehova, nafenso tingawapilile moleza mtima mayeso alionse amene angatipeze.
14. Kodi tingaphunzilenji pa kuleza mtima kwa Abulahamu? (Aheberi 6:15) (Onaninso cithunzi.)
14 Bwanji ngati mapeto amene tawayembekezela kwa nthawi yaitali sakufika? Tingayambe kuda nkhawa kuti mwina tidzamwalila mapetowo asanafike. N’ciyani cingatithandize kuyembekezelabe moleza mtima? Ganizilani citsanzo ca Abulahamu. Iye atafika zaka 75 wopanda mwana, Yehova anam’lonjeza kuti: “Ine ndidzatulutsa mtundu waukulu mwa iwe.” (Gen. 12:1-4) Kodi Abulahamu anaona kukwanilitsidwa kwa lonjezo limeneli? Osati kwathunthu. Atawoloka Mtsinje wa Firate, anayembekezela zaka 25 kuti mozizwitsa akhale na mwana Isaki. Ndipo anayembekezelanso zaka zina 60 kuti adzukulu ake Esau na Yakobo abadwe. (Ŵelengani Aheberi 6:15.) Koma Abulahamu sanaone mbadwa zake zikukhala mtundu waukulu na kulandila Dziko Lolonjezedwa. Ngakhale n’telo, munthu wokhulupilika ameneyu anali pa ubwenzi wolimba na Mlengi wake. (Yak. 2:23) Abulahamu akadzaukitsidwa, adzakondwela kwambili kudziŵa kuti cikhulupililo na kuleza mtima kwake zinabweletsa madalitso ku mtundu wonse wa anthu. (Gen. 22:18) Kodi tiphunzilapo ciyani? Si malonjezo onse a Yehova amene adzakwanilitsidwa ife tili moyo. Komabe, tikaleza mtima monga Abulahamu, tidzakhala otsimikiza kuti Yehova adzatifupa pali pano, komanso m’dziko latsopano tidzalandila madalitso oculuka.—Maliko 10:29, 30.
15. Kodi tingasankhe kuphunzila ciyani pa phunzilo la munthu mwini?
15 M’Baibo, muli zitsanzo zambili za anthu amene anali oleza mtima. (Yak. 5:10) Conco, mungadziikile colinga coŵelenga zitsanzo zimenezo pa phunzilo la inu mwini. b Mwacitsanzo, ngakhale kuti Davide anadzozedwa akali wacicepele kukhala mfumu yam’tsogolo ya Isiraeli, anayembekezela kwa zaka zambili kuti ayambe kulamulila. Nayenso Simiyoni komanso Anna anatumikila Yehova mokhulupilika poyembekezela Mesiya wolonjezedwayo. (Luka 2:25, 36-38) Mukamaŵelenga nkhani ngati zimenezi, muziyesa kupeza mayankho pa mafunso aya: N’ciyani cinathandiza munthu ameneyu kukhala woleza mtima? Kodi kuleza mtima kunam’pindulila motani? Nanga ningatengele bwanji citsanzo cake? Tingatengenso cenjezo pa zitsanzo za anthu amene sanali oleza mtima. (1 Sam. 13:8-14) Mungadzifunse kuti: ‘N’ciyani cinapangitsa kuti asakhale oleza mtima? Nanga anakumana na mavuto otani?’
16. Kodi kuleza mtima kuli na mapindu otani?
16 Mapindu a kuleza mtima. Tikakhala oleza mtima, timakhala acimwemwe komanso odekha. Izi zimathandiza kuti tikhale na thanzi labwinopo. Tikamalezela mtima anthu ena, timakhala nawo pa ubale wabwino. Mpingo umakhala wogwilizana kwambili. Ndipo wina akatikhumudwitsa, kusakwiya msanga kumatithandiza kupewa kuikulitsa nkhaniyo. (Sal. 37:8; Miy. 14:29) Koma coposa zonse, tikakhala oleza mtima, timatengela Atate wathu wakumwamba, ndipo timamuyandikila kwambili.
17. Kodi tiyenela kuyesetsa kucita ciyani?
17 Kuleza mtima ni khalidwe labwino zedi! Ngakhale kuti nthawi zina kuleza mtima kumavuta, Yehova angatithandize kukulitsa khalidwe limeneli. Ndipo pamene tikuyembekezela moleza mtima dziko latsopano, sitikayikila olo pang’ono kuti “diso la Yehova lili pa anthu amene amamuopa, amene amayembekezela kukoma mtima kwake kosatha.” (Sal. 33:18) Conde, tisaleke kuvala kuleza mtima.
NYIMBO 41 Mvelani Pemphelo Langa Conde
a M’dziko la Satanali, anthu si oleza mtima. Ngakhale n’telo, Baibo imatiuza kuti tivale kuleza mtima. Nkhani ino ifotokoza cifukwa cake khalidweli n’lofunika kwambili, komanso mmene tingalikulitsile.
b Kuti mupeze zitsanzo za m’Baibo pa nkhani ya kuleza mtima, onani buku ya Cizungu yakuti Watch Tower Publications Index, pa mutu wakuti “Patience.”