Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Satana wakhala akuipitsa dzina la Mulungu kucokela pa cipanduko ca mu Edeni

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Kodi nkhani yakuti “Dzina Lanu Liyeletsedwe” mu Nsanja ya Mlonda ya June 2020, inaunika motani kamvedwe kathu pa nkhani yokhudza dzina la Mulungu na ulamulilo wake?

M’nkhaniyo, tinaphunzila kuti pali nkhani imodzi yofunika kwambili, imene ni kuyeletsedwa kwa dzina lalikulu la Mulungu. Nkhaniyi ikhudza anthu onse komanso angelo. Nkhani ya ulamulilo wa Yehova ni yogwilizana na nkhani yaikulu ija, yomwe ni kuyeletsedwa kwa dzina la Mulungu. Mofananamo, nkhani ya kukhulupilika kwa anthu nayonso ili mbali ya nkhani yaikulu imeneyi.

N’cifukwa ciyani tsopano tikugogomeza kuti nkhani yaikuluyo yazikika pa dzina la Mulungu na kuyeletsedwa kwake? Tiyeni tikambilane zifukwa zitatu.

Yehova adzapangitsa dzina lake kulemekezedwa kwamuyaya

Coyamba, Satana anaipitsa dzina la Mulungu, kapena kuti mbili yake m’munda wa Edeni. Funso la macenjela la Satana linaonetsa kuti Yehova ni woipa, womana, ndiponso kuti amaikila anthu ake malamulo okhwima komanso opanda cilungamo. Ndiyeno iye anatsutsa mosapita m’mbali zimene Yehova anakamba, mwakutelo anati Mulungu ni wabodza. Iye anaipitsa dzina la Yehova. Conco, anakhala “Mdyerekezi,” kutanthauza “woneneza.” (Yoh. 8:44) Cifukwa cokhulupilila mabodza a Satana, Hava sanamvele Mulungu, ndipo apandukila ulamulilo wa Mulungu. (Gen. 3:1-6) Mpaka lelo, Satana amaipitsabe mbili ya Mulungu pofalitsa mabodza akuti Yehova si Mulungu wabwino. Amene amakhulupilila mabodzawo akhoza kulephela kumvela Mulungu. Koma kwa anthu a Mulungu, kuipitsa dzina lake loyela n’kusoŵelatu cilungamo. Ndipo kuipitsidwa kwa dzinalo, ndiwo muzu wa mavuto na zoipa zonse m’dzikoli.

Caciŵili, kaamba ka ubwino wa cilengedwe conse, Yehova ni wofunitsitsa kuyeletsa dzina lake, na kucotselatu citonzo pa dzinalo. Izi ndizo zofunika kwambili kwa iye. Ndiye cifukwa cake iye anati: “Ndidzayeletsa dzina langa lalikulu.” (Ezek. 36:23) Yesu nayenso anaonetsa bwino cimene atumiki onse a Yehova okhulupilika ayenela kuika patsogolo m’mapemphelo awo pamene anati: “Dzina lanu liyeletsedwe.” (Mat. 6:9) Ndipo mobweleza-bweleza, Baibo imagogomeza kufunika kokweza dzina la Mulungu. Onankoni zitsanzo izi: “M’patseni Yehova ulemelelo wa dzina lake.” (1 Mbiri 16:29; Sal. 96:8) “Imbani nyimbo zotamanda dzina lake.” (Sal. 66:2) “Ndipo ndidzalemekeza dzina lanu mpaka kale-kale.” (Sal. 86:12) Pa nthawi inayake, Yehova analankhula iye mwini kucokela kumwamba pamene Yesu anali pa kacisi ku Yerusalemu. Yesu atanena kuti “Atate lemekezani dzina lanu,” Yehova anayankha kuti: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.”—Yoh. 12:28. a

Cacitatu, Colinga ca Yehova n’cogwilizana na dzina lake, kapena kuti mbili yake. Ganizilani izi: Pambuyo pa mayeso othela kumapeto kwa Ulamulilo wa Khristu wa Zaka Cikwi, n’ciyani cidzatsatilapo? Kodi padzakhalabe maganizo osiyana pa nkhani yaikulu ija yokhudza kuyeletsedwa kwa dzina la Mulungu? Kuti tiyankhe funsoli, tikumbukile mbali ziŵili zija zogwilizana na nkhani yaikulu, zimene ni kukhulupilika kwa anthu komanso ulamulilo wa Yehova wa cilengedwe conse. Kodi anthu amene adzakhalabe okhulupilika adzafunika kupitiliza kuonetsa kukhulupilika kwawo? Ayi. Iwo adzakhala angwilo, komanso oti ayesedwa mofikapo. Ndipo adzakhala atalandila moyo wosatha. Kodi padzafunikilanso nthawi kuti angelo komanso anthu adziŵe kuti ulamulilo wa Yehova ndiwo wabwino koposa? Ayi. Pa nthawiyo, onse kumwamba na padziko lapansi adzakhala ogwilizana, komanso adzavomela kuti ulamulilo wa Yehova ndiwo wabwino koposa. Nanga bwanji za dzina la Mulungu?

Pa nthawiyo, onse adzakhala atadziŵa zoona ponena za Yehova, ndipo dzina lake lidzakhala litayeletsedwa kothelatu. Ngakhale n’telo, dzina la Mulungu lidzapitilizabe kukhala lofunika kwa atumiki ake onse okhulupilika—kumwamba na padziko lapansi. Zidzatelo cifukwa onse adzaona Yehova akupitiliza kucita zodabwitsa. Ganizilani izi: Cifukwa cakuti Yesu modzicepetsa adzabweza ulamulilo kwa Yehova, Mulungu adzakhala “zinthu zonse kwa aliyense.” (1 Akor. 15:28) Pambuyo pa izi, anthu padziko lapansi adzasangalala na “ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Ndipo Yehova adzakwanilitsa colinga cake cogwilizanitsa zolengedwa zake za kumwamba na za padziko lapansi, kuti zikhale banja limodzi logwilizana.—Aef. 1:10.

Zinthu zonsezi zikadzacitika, kodi banja la Yehova la kumwamba na padziko lapansi lidzamva bwanji? Kukamba zoona, tidzakhalabe na cikhumbo camphamvu cotamanda dzina lake labwino. Wamasalimo Davide anauzilidwa kulemba kuti: “Adalitsike Yehova Mulungu . . . Lidalitsike dzina lake laulemelelo mpaka kale-kale.” (Sal. 72:18, 19) Tsiku lililonse, tizikhala na zifukwa zatsopano zom’tamandila mpaka kale-kale.

Dzina lakuti Yehova liimila ciliconse cokhudza iye. Coposa zonse, dzina lake limatikumbutsa za cikondi cake. (1 Yoh. 4:8) Pa nthawiyo tizikumbukila kuti cikondi n’cimene cinasonkhezela Yehova kuti atilenge, kutipatsa dipo, komanso kutionetsa kuti ulamulilo wake ni wacilungamo. Komabe, tidzapitiliza kuona cikondi ca Yehova mpaka muyaya. Tidzalimbikitsidwa kumuyandikila monga Atate wathu, na kumuimbila nyimbo zotamanda dzina lake kwamuyaya.—Sal. 73:28.

a Baibo imaonetsanso kuti Yehova amacita zinthu “cifukwa ca dzina lake.” Mwacitsanzo, iye amatsogolela anthu ake, kuwathandiza, kuwapulumutsa, kuwakhululukila, komanso kuwasunga na moyo. Amacita zonsezi cifukwa ca dzina lake lalikulu, lakuti Yehova.—Sal. 23:3; 31:3; 79:9; 106:8; 143:11.