Mfundo Yothandiza Pa Kuŵelenga Kwanu
Pezani Cuma ca Kuuzimu Cokhudza Yehova
Tikamaŵelenga Baibo, tingagwilitse nchito zida zosiyana-siyana kuti timvetsetse zimene tikuŵelengazo. Colinga cathu poŵelenga sikungowonjezela cidziŵitso ca m’Baibo ayi. Koma timafuna kupeza cuma cauzimu cokhudza makhalidwe a Yehova, kuti tikulitse cikondi cathu pa iye. Kuti ticite zimenezi, tizidzifunsa kuti, ‘Kodi nkhaniyi iniphunzitsa ciyani za Yehova?’
Mungafufuze umboni woonetsa mmene Yehova wakhala akuonetsela cikondi, nzelu, cilungamo, na mphamvu. Koma Yehova alinso na makhalidwe ena ambili osililika. N’kuti kumene tingapeze mfundo zambili zokhudza makhalidwe ake?
Onani m’ndandanda wa makhalidwe a Yehova oposa 50 m’buku la cizungu la kuti Watch Tower Publications Index. Pitani pa mutu wakuti “Jehovah.” Ndiyeno pitani kamutu kakuti “Qualities by Name.” Fufuzani makhalidwe amene agwilizana na nkhani ya m’Baibo imene mukuŵelengayo. (Ngati mulibe bukuli, gwilitsani nchito Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova. Pitani pa mutu wakuti “Yehova Mulungu.” Kenaka pitani pa kamutu kakuti “Makhalidwe a Yehova.”)