NKHANI YOPHUNZILA 36
Nyamulani Zofunikila Zokhazo, Tayani Zotsalazo
“Tiyeninso tivule [kapena kuti titaye] colemela ciliconse . . . Ndipo tithamange mopilila mpikisano umene atiikilawu.”—AHEB. 12:1.
NYIMBO 33 Tulila Yehova Nkhawa Zako
ZIMENE TIKAMBILANE a
1. Malinga na Aheberi 12:1, kodi tingacite ciyani kuti tikafike pa mzele womaliza pa mpikisano wokalandila moyo?
BAIBO imayelekezela umoyo wathu wacikhristu na mpikisano wothamanga. Othamanga amene adzafike pa mzele womaliza, adzawafupa na moyo wosatha. (2 Tim. 4:7, 8) Tiyenela kucita zonse zotheka kuti tisaleke kuthamanga, maka-maka pamene tatsala pang’ono kufika pa mzele womaliza. Mtumwi Paulo amene anafika pa mzele womaliza, anachula cimene cingatithandize kupambana mpikisanowu. Iye anatilangiza kuti “tivule [kapena titaye] colemela ciliconse . . . Ndipo tithamange mopilila mpikisano umene atiikilawu.”—Ŵelengani Aheberi 12:1.
2. Kodi ‘kuvula colemela ciliconse’ kumatanthauza ciyani?
2 Pamene mtumwi Paulo anati “tivule colemela ciliconse,” kodi anatanthauza kuti Mkhristu sayenela kunyamula kanthu? Ayi, mfundo yake si imeneyo. Iye anatanthauza kuti tiyenela kutaya colemela ciliconse cosafunikila. Zolemela zotelo zingatitopetse na kucepetsa liŵilo lathu. Kuti tipilile, tiyenela kuzindikila ciliconse cimene cingatilemetse, na kucitaya mwamsanga. Komabe, tiyenela kusamala kuti tisataye zinthu zofunikila kunyamula. Tikazitaya, sitingayenelele kuthamanga mpikisanowo. (2 Tim. 2:5) Nanga ni zinthu ziti zofunika kunyamula?
3. (a) Malinga n’kunena kwa Agalatiya 6:5, kodi tiyenela kunyamula ciyani? (b) Kodi tikambilane ciyani m’nkhani ino? Nanga n’cifukwa ciyani?
3 Ŵelengani Agalatiya 6:5. Paulo anachula zimene tiyenela kunyamula. Iye analemba kuti “aliyense ayenela kunyamula katundu wake.” Apa Paulo anali kunena za katundu wa udindo umene tonsefe tili nawo kwa Mulungu. Ndipo aliyense ayenela kudzinyamulila yekha katunduyo. M’nkhani ino, tikambilane wina wa “katundu” wofunika kunyamula, kenaka tiphunzile mmene tingamunyamulile. Tikambilanenso zolemela zosafunikila, na mmene tingazitayile. Aliyense payekha akanyamula zofunikila na kutaya zosafunikila, adzapambana mpikisano wokalandila moyo.
KATUNDU AMENE TIFUNIKILA KUNYAMULA
4. N’cifukwa ciyani lonjezo lomwe tinapanga podzipatulila si mtolo wolemetsa? (Onaninso cithunzi.)
4 Lonjezo lomwe tinapanga podzipatulila. Pamene tinadzipatulila kwa Yehova, tinalonjeza kuti tizim’lambila na kucita cifunilo cake. Tiyenela kulisunga lonjezolo. Kucita zimene tinalonjeza ni udindo waukulu, koma si mtolo wolemetsa ayi. Tikutelo cifukwa Yehova anatilenga kuti tizicita cifunilo cake. (Chiv. 4:11) Iye anatilenga m’cifanizilo cake, ndipo anaika mwa ife cikhumbo cofuna kum’dziŵa komanso kum’lambila. Mwa ici, timatha kumuyandikila na kusangalala pocita cifunilo cake. (Sal. 40:8) Kuwonjezela apo, tikamacita cifunilo ca Mulungu na kutsatila Mwana wake, ‘timatsitsimulidwa.’—Mat. 11:28-30.
5. N’ciyani cingakuthandizeni kukwanilitsa zimene munalonjeza podzipatulila? (1 Yohane 5:3)
5 Kodi mungamunyamule motani katundu ameneyu? Zinthu ziŵili izi zingakuthandizeni. Coyamba, pitilizani kulimbikitsa cikondi canu pa Yehova. Mungacite zimenezi mwa kuganizila zabwino zimene wakucitilani, komanso madalitso amene wakusungilani. Cikondi canu pa Mulungu cikamakula, kudzakhala kwapafupi kumumvela. (Ŵelengani 1 Yohane 5:3.) Caciŵili, muzitengela Yesu. Iye anapambana pocita cifunilo ca Mulungu cifukwa anali kupempha thandizo kwa iye, komanso anakhazikitsa maganizo ake pa mphoto imene anali kudzalandila. (Aheb. 5:7; 12:2) Monga Yesu, muzipemphela kwa Yehova kuti akupatseni mphamvu. Cina, musaleke kuganizila za ciyembekezo ca moyo wosatha. Cikondi canu pa Mulungu cikamakula, komanso mukamatengela citsanzo ca Yesu, mudzakwanilitsa zomwe munalonjeza podzipatulila.
6. N’cifukwa ciyani tiyenela kusamalila maudindo athu m’banja? (Onaninso cithunzi.)
6 Maudindo athu m’banja. Pa mpikisano wathu wokalandila moyo, tizim’konda kwambili Yehova komanso Yesu kuposa mmene timakondela acibale athu. (Mat. 10:37) Koma izi sizitanthauza kuti tiyenela kunyanyala maudindo athu m’banja, poganiza kuti angatilepheletse kukondweletsa Mulungu na Khristu. Kuti Mulungu na Khristu atiyanje, tizikwanilitsa maudindo athu m’banja. (1 Tim. 5:4, 8) Tikatelo, tidzakhala acimwemwe. Yehova adziŵa kuti banja limakhala lacimwemwe ngati mwamuna na mkazi amakondana na kulemekezana, makolo amakonda ana awo na kuwaphunzitsa, komanso ngati ana amamvela makolo awo.—Aef. 5:33; 6:1, 4.
7. Kodi udindo wanu m’banja mungaukwanilitse motani?
7 Kodi mungamunyamule motani katundu ameneyu? Kaya udindo wanu ni wotani m’banja, muzidalila ulangizi wa m’Baibo. Musamacite zinthu motengela mmene mukumvela, cikhalidwe ca kwanuko, kapena zimene ochedwa alangizi a mabanja amanena. (Miy. 24: 3, 4) Muzifufuza m’zofalitsa zathu kuti mupeze malangizo othandiza a m’Baibo, na kuona mmene mungawagwilitsile nchito. Mwacitsanzo, nkhani zakuti “Mfundo Zothandiza Mabanja” zili na malangizo othandiza pa zovuta zimene okwatilana, makolo, komanso acinyamata amakumana nazo. b Conde, muziyesetsa kutsatila mfundo za m’Baibo ngakhale pamene ena m’banja sacita zimenezo. Mukatelo, banja lanu lidzapindula, ndipo Yehova adzakudalitsani.—1 Pet. 3:1, 2.
8. Kodi zisankho zathu zingakhale na zotulukapo zotani?
8 Kuyankha mlandu pa zisankho zathu. Yehova anatipatsa ufulu wodzisankhila zocita. Ndipo amafuna kuti tizisangalala na zisankho zabwino zimene timapanga. Koma tikapanga zisankho zoipa, iye saticinjiliza ku zotulukapo zake. (Agal. 6:7, 8) Conco, tikapanga zisankho zolakwika, tikakamba mawu osayenela, kapena tikacita zinthu zosayenela, timakolola zimene tafesa. Malinga na zimene tacita, timakhala na cikumbumtima covutitsidwa. Komabe, kudziŵa kuti tidzayankha mlandu pa zisankho zathu kudzatilimbikitsa kulapa, kukonza zolakwazo, na kupewa kuzibwelezanso. Kucita izi kudzatithandiza kuthamangabe pa mpikisano wokalandila moyo.
9. Kodi muyenela kucita ciyani mukapanga cisankho colakwika? (Onaninso cithunzi.)
9 Kodi mungamunyamule motani katundu ameneyu? Ngati n’zosatheka kusintha cisankho colakwika, mungocivomeleza basi. Paja amati madzi akatayika saoleka. Musawononge nthawi na mphamvu zanu poyesa kudzilungamitsa, kudziimba mlandu, kapena kuimba mlandu anthu ena pa zisankho zolakwika zimene mungapange. M’malo mwake, vomelezani zolakwa zanu, ndipo yesetsani kucita zoyenela mmene mungathele. Mukadziimba mlandu pa colakwa canu, modzicepetsa muuzeni Yehova m’pemphelo, civomelezeni colakwaco, ndipo m’pempheni kuti akukhululukileni. (Sal. 25:11; 51:3, 4) Ngati pali ena amene anakhumudwa na colakwaco, apepeseni, ndipo ngati m’pofunikila pemphani thandizo kwa akulu. (Yak. 5:14, 15) Phunzilam’poni kanthu pa zolakwa zanu, ndipo onenetsani kuti musadzabwelezenso. Mukatelo, khalani wotsimikiza kuti Yehova adzakucitilani cifundo, na kupeleka thandizo lofunikila kwa inu.—Sal. 103:8-13.
ZOLEMELA ZIMENE TIYENELA KUTAYA
10. N’cifukwa ciyani kufuna kucita zimene sitingakwanitse ni colemetsa coyenela kutaya? (Agalatiya 6:4)
10 Kufuna kucita zimene sitingakwanitse. Tingangodzitopetsa tokha tikamafuna kucita zimene sitingakwanitse podziyelekezela na anthu ena. (Ŵelengani Agalatiya 6:4.) Tikamadziyelezela na anthu ena, tingayambe kucita nsanje komanso kupikisana nawo. (Agal. 5:26) Pofuna kucita zimene ena amacita, ngakhale kuti tikudziŵa bwino kuti ife sitingathe kucita zimenezo, tingangodzivulaza tokha. Ngati “cinthu cimene unali kuyembekeza cikalepheleka cimadwalitsa mtima,” kuli bwanji kufuna kucita zimene sitingakwanitse! (Miy. 13:12) Kucita zimenezo kungatiwonongele mphamvu zathu, na kucepetsa liŵilo lathu pa mpikisano wokalandila moyo.—Miy. 24:10.
11. N’ciyani cingakuthandizeni kupewa mtima wofuna kucita zimene simungakwanitse?
11 Kodi mungacitaye bwanji colemetsa cimeneci? Musakhale na mtima wofuna kucita zambili kuposa zimene Yehova amafuna kwa inu. Iye sayembekezela kuti mum’patse zimene simungakwanitse. (2 Akor. 8:12) Dziŵani kuti Yehova salinganiza utumiki wanu na utumiki wa anthu ena. (Mat. 25:20-23) Kukhulupilika kwanu, kupilila kwanu, na utumiki wanu umene mumaucita na mtima wonse, n’zamtengo wapatali kwa iye. Conco, modzicepetsa civomelezeni kuti msinkhu wanu, thanzi lanu, komanso mikhalidwe yanu, singakuloleni kucita zonse zimene mukufuna. Monga anacitila Barizilai, muzikanako mautumiki ena ngati cidzakhala covuta kuwakwanilitsa cifukwa ca msinkhu wanu kapena thanzi lanu. (2 Sam. 19:35, 36) Ndipo mofanana na Mose, landilani thandizo la ena, komanso gaŵilankoni ena zocita pakakhala pofunikila. (Eks. 18:21, 22) Kudzicepetsa kotelo kudzakuthandizani kupewa mtima wofuna kucita zimene simungakwanitse, kumene kungakutopetseni pa mpikisano wokalandila moyo.
12. Kodi tiyenela kudziimba mlandu pa zisankho zolakwika zimene anthu ena amapanga? Fotokozani.
12 Kudziimba mlandu pa zisankho zolakwika za anthu ena. Sitingasankhile anthu ena zocita kapena kuwateteza ku zotulukapo zoipa pa zisankho zawo. Mwacitsanzo, mwana pakhomo angasankhe kuleka kutumikila Yehova. Izi zingabweletse cisoni cacikulu kwa makolo. Paja amati nkhuyu zodya mwana zinapota amake. Ndipo makolo amene amadziimba mlandu pa cisankho coipa ca mwana wawo amasenza mtolo wolemetsa. Koma uwu si katundu amene Yehova amayembekezela makolo kunyamula.—Aroma 14:12.
13. Kodi kholo liyenela kucita ciyani mwana akapanga cisankho colakwika?
13 Kodi mungacitaye bwanji colemetsa cimeneci? Kumbukilani kuti Yehova anatipatsa ufulu wodzisankhila zocita. Iye amalola munthu aliyense kudzisankhila zocita. Izi ziphatikizapo kusankha kum’tumikila kapena ayi. Yehova amadziŵa kuti sindinu wangwilo. Amangofuna kuti mucite zimene mungathe. Ndipo mwana wanu ndiye adzayankha mlandu pa zisankho zake, osati inu. (Miy. 20:11) Ngakhale n’telo, mungamaganizile zimene munalakwitsapo m’mbuyomu monga kholo. Ngati n’conco, muuzeni Yehova mmene mukumvela, na kum’pempha kuti akukhululukileni. Iye adziŵa kuti n’zosatheka kusintha zimene munalakwitsapo m’mbuyomu. Pa nthawi imodzimodzi, sangakondwele ngati mwateteza mwana wanu kuti asakolole zimene anafesa. Ndipo dziŵani kuti ngati mwanayo angayesetse kubwelela kwa Yehova, iye ni wofunitsitsa kum’landila na manja aŵili.—Luka 15:18-20.
14. N’cifukwa ciyani kudziimba mlandu mopitilila malile n’colemetsa cofunika kucitaya?
14 Kudziimba mlandu mopitilila malile. Tikacimwa, m’pomveka kudziimba mlandu. Koma Yehova safuna kuti ticite kupitilila nako malile. Ni colemetsa cimene tiyenela kucitaya. Kodi tingadziŵe bwanji kuti timadziimba mlandu mopitilila malile? Tikaulula macimo athu, kulapa zenizeni, komanso kucita zonse zotheka kuti tisabwelezenso cimolo, tingakhale na cidalilo cakuti Yehova anatikhululukila. (Mac. 3:19) Tikatelo, iye safuna kuti tipitilize kudziimba mlandu cifukwa adziŵa kuti kungativulaze. (Sal. 31:10) Tikakhala na cisoni cacikulu, tingacoke pa mpikisano wathu wokalandila moyo.—2 Akor. 2:7.
15. Tingacite ciyani kuti tisamadziimbe mlandu mopitilila malile? (1 Yohane 3:19, 20) (Onaninso cithunzi.)
15 Kodi mungacitaye bwanji colemetsa cimeneci? Mukayamba kudziimba mlandu mopitilila muyeso, muzikumbukila kuti Mulungu ‘amakhululukiladi.’ (Sal. 130:4) Iye akakhululukila anthu omwe alapa moona mtima, amawalonjeza kuti: “Macimo [anu] sindidzawakumbukilanso.” (Yer. 31:34) Izi zitanthauza kuti Yehova sadzakuimbani mlandu pa macimo anu akale. Conco, musamaone kuti zotsatilapo za macimo anu ni umboni wakuti iye sanakukhululukileni. Ndipo musadziimbe mlandu poona kuti macimo anu akumbuyo akukulepheletsani kucita zambili potumikila Mulungu. Yehova sakhalila kuganizila zolakwa zanu, inunso musamatelo.—Ŵelengani 1 Yohane 3:19, 20.
THAMANGANI M’NJILA YAKUTI MUKALANDILE MPHOTO
16. Monga othamanga pa mpikisano, kodi tiyenela kudziŵa ciyani?
16 Pamene tikuthamanga pa mpikisano umenewo, ‘tithamange m’njila yoti tikalandile mphoto.’ (1 Akor. 9:24) Tingatelo ngati tidziŵa kusiyanitsa zinthu zofunikila kunyamula, na zinthu zoyenela kutaya. M’nkhani ino, takambilana zinthu zingapo zofunika kunyamula, komanso zoyenela kutaya. Koma si zokhazo ayi. Yesu anakamba kuti ‘tingalemedwe na kudya kwambili, kumwa kwambili, komanso nkhawa za moyo.’ (Luka 21:34) Palinso malemba ena amene angakuthandizeni kuona zimene mungasintheko pothamanga pa mpikisano wokalandila moyo.
17. N’cifukwa ciyani ndife otsimikiza kuti tidzapambane pa mpikisano wokalandila moyo?
17 Ndife otsimikiza kuti tidzapambane pa mpikisano wokalandila moyo cifukwa Yehova adzatipatsa mphamvu zofunikila. (Yes. 40:29-31) Conco, musalefuke! Tengelani mtumwi Paulo amene anathamanga molimbika kuti akalandile mphoto imene inali patsogolo pake. (Afil. 3:13, 14) Palibe angakuthamangileni mpikisano umenewu. Koma mwa thandizo la Yehova mudzapambana! Iye adzakuthandizani kunyamula zofunikila, na kutaya zosafunikila. (Sal. 68:19) Yehova akakhala kumbali yanu, mudzakwanitsa kuthamanga mopilila mpikisanowo, na kupambana.
NYIMBO 65 Pita Patsogolo!
a Nkhani ino itithandiza mmene tingathamangile pa mpikisano wokalandila moyo. Pamene tikuthamanga, pali zofunikila kunyamula. Izi ziphatikizapo lonjezo limene tinapanga podzipatulila, maudindo a m’banja, komanso kuyankha mlandu pa zisankho zathu. Komabe, tiyenela kutaya zolemetsa zilizonse zimene zingacepetse liŵilo lathu. Kodi zolemelazo ziphatikizapo ciyani? Nkhani ino iyankha funso limeneli.
b Nkhani zakuti “Mfundo Zothandiza Mabanja” mungazipeze pa jw.org ku Chichewa. Mwacitsanzo, nkhani yakuti “Kodi Mungasonyezane Bwanji Ulemu?,” komanso yakuti “Kodi Mungasonyeze Bwanji Kuti Mumayamikila Zimene Mwamuna kapena Mkazi Wanu Amacita?” zingathandize okwatilana. Nkhani yakuti “Phunzitsani Ana Anu Kugwilitsa Nchito Foni Mosamala,” komanso yakuti “Zimene Mungacite Kuti Muzimasukilana Ndi Mwana Wanu,” zingathandize makolo. Ndipo acinyamata angapindule na nkhani yakuti “Kodi Mungatani Kuti Musamangotengela Zocita za Anzanu?,” komanso yakuti “Kodi Mungatani Ngati Mumasoŵa Woceza Naye?”