Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 34

Phunzilani ku Maulosi a m’Baibo

Phunzilani ku Maulosi a m’Baibo

“Anthu ozindikila adzawamvetsetsa.”—DAN. 12:10.

NYIMBO 98 Malemba ni Ouzilidwa na Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. N’ciyani cingatithandize kuti tizisangalala poŵelenga maulosi a m’Baibo?

 M’BALE wina wacinyamata dzina lake Ben anati, “Nimakonda kuŵelenga maulosi.” Kodi inunso mumatelo? Kapena kodi mumaona kuti maulosi a m’Baibo ni ovuta kuwamvetsa? Nthawi zina mungaone kuti kuŵelenga maulosi n’kogwetsa ulesi. Komabe, mukadziŵa bwino cifukwa cimene Yehova anawaikilamo m’Mawu ake, mungayambe kuwakonda.

2. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

2 M’nkhani ino tifotokoze cifukwa cake tiyenela kuphunzila maulosi a m’Baibo, komanso mmene tingacitile zimenezo. Tikambilanenso maulosi aŵili a m’buku la Danieli kuti tione mmene tingapindulile pali pano tikawamvetsa.

N’CIFUKWA CIYANI TIYENELA KUPHUNZILA MAULOSI A M’BAIBO?

3. Kodi tiyenela kucita ciyani kuti tiwamvetse maulosi a m’Baibo?

3 Tiyenela kupempha thandizo kuti timvetse maulosi a m’Baibo. Nali fanizo. Yelekezani kuti mwapita ku malo acilendo, koma mnzanu amene mwapita naye amawadziŵa bwino malowo. Akudziŵa bwino pamene muli komanso kumene misewu ikupita. Mosakayika konse, mudzakondwela kwambili kuti mnzanuyo wakupelekezani. Inde, paja amati kuyenda aŵili si mantha! Mofananamo, Yehova akudziŵa bwino pomwe tafika na kumene tikupita. Conco, kuti timvetse maulosi a m’Baibo tiyenela kupempha thandizo la Yehova modzicepetsa.—Dan. 2:28; 2 Pet. 1:19, 20.

Kuŵelenga maulosi a m’Baibo kungatithandize kukonzekela zocitika zakutsogolo (Onani ndime 4)

4. N’cifukwa ciyani Yehova anaikamo maulosi m’Mawu ake? (Yeremiya 29:11) (Onaninso cithunzi.)

4 Molingana na kholo lililonse labwino, Yehova amafuna kuti ana ake akhale na tsogolo lacimwemwe. (Ŵelengani Yeremiya 29:11.) Koma mosiyana na makolo aumunthu, Yehova amakambilatu zakutsogolo, ndipo saphonyetsa ngakhale pang’ono. Iye anaikamo maulosi m’Baibo kuti tidziŵiletu pasadakhale zocitika zofunika kwambili. (Yes. 46:10) Cotelo, maulosi a m’Baibo ni mphatso zocokela kwa Atate wathu wakumwamba zoonetsa cikondi cake kwa ife. Koma mungakhale bwanji otsimikiza kuti zimene Baibo imanena zidzacitikadi?

5. Kodi acinyamata angaphunzile ciyani kwa m’bale Max?

5 Ku sukulu, acicepele athu amapezeka kuti ali pakati pa anthu osalemekeza Baibo kwenikweni, kapena sailemekeza n’komwe. Zokamba na zocita za anthuwo zingapangitse Mboni yacicepele kukhala na zikayiko. Onani cocitika ici ca m’bale Max. Iye anakamba kuti: “Nili wacicepele, n’nayamba kukayikila ngati zimene makolo anga anali kuniphunzitsa zinali za cipembedzo coona, komanso zakuti Baibo inauzilidwadi na Mulungu.” Kodi makolo ake anacita ciyani? M’baleyu ananena kuti: “Iwo anacita nane modekha, koma nidziŵa kuti anali na nkhawa.” Makolo a m’baleyo anayankha mafunso ake kucokela m’Baibo. Koma Max nayenso anacita mbali yake. Iye anati, “N’nali kuŵelenga maulosi a m’Baibo panekha, ndipo n’nali kuuzako acinyamata anzanga zimene n’nali kuphunzila.” Zotulukapo zake? M’baleyo anati: “Pambuyo pa zonsezi, n’natsimikiza kuti Baibo inauzilidwadi na Mulungu.”

6. Kodi muyenela kutani mukakhala na zikayiko? Cifukwa ciyani?

6 Ngati mofanana na Max mwayamba kukayikila zakuti Baibo ilidi na coonadi, musadziimbe mlandu. Koma muyenela kucitapo kanthu. Cikayiko cili ngati nguwe. Popanda kucitapo kanthu, nguwe ingawononge zinthu zamtengo wapatali m’kupita kwa nthawi. Kuti muyambe kucotsa “nguwe” ku cikhulupililo canu, titelo kunena kwake, muyenela kudzifunsa kuti, ‘Kodi nimakhulupilila zimene Baibo imakamba zokhudza tsogolo?’ Ngati mumakayikila, muyenela kuŵelenga maulosi a m’Baibo amene anakwanilitsika kale. Mungacite motani zimenezi?

ZIMENE TINGACITE POŴELENGA MAULOSI A M’BAIBO

Kuti tizim’dalila Yehova monga anacitila Danieli, tiyenela kuŵelenga maulosi a m’Baibo modzicepetsa, kuwafufuza mokwana, tili na colinga cabwino (Onani ndime 7)

7. Kodi Danieli anatisiyila citsanzo cotani ca mmene tingaŵelengele maulosi? (Danieli 12:10) (Onaninso cithunzi)

7 Danieli anapeleka citsanzo cabwino ca moŵelengela maulosi. Anali kuŵelenga maulosi na colinga coyenela, comwe ndico kufuna kudziŵa coonadi. Danieli analinso wodzicepetsa. Anazindikila kuti Yehova amathandiza anthu ofuna kum’dziŵa bwino, ndiponso amatsatila miyeso yake yoyela mu umoyo wawo. (Dan. 2:27, 28; ŵelengani Danieli 12:10.) Danieli anaonetsa kuti anali wodzicepetsa podalila thandizo la Yehova. (Dan. 2:18) Cina, Danieli anali kufufuza mokwana. Anali kufufuza m’Malemba ouzilidwa amene analipo m’nthawi yake. (Yer. 25:11, 12; Dan. 9:2) Mungatengele bwanji citsanzo cake?

8. N’cifukwa ciyani ena amakana kukhulupilila kuti maulosi a m’Baibo amakwanilitsika? Nanga ife tiyenela kucita ciyani?

8 Santhulani zolinga zanu. Kodi colinga canu poŵelenga maulosi a m’Baibo ni kufunitsitsa kudziŵa coonadi? Ngati n’telo, Yehova adzakuthandizani. (Yoh. 4:23, 24; 14:16, 17) Koma ena amaŵelenga maulosi pa zifukwa zina. Ena amacita zimenezi kuti apeze maumboni akuti Baibo si louzilidwa na Mulungu. Potelo, amaona kuti ali na zifukwa zomveka zodziikila muyeso wawo-wawo wa cabwino na coipa, n’kuutsatila. Koma ife tiyenela kukhala na colinga cabwino. Cina, pali khalidwe lina lake lomwe lingatithandize kumvetsa maulosi a m’Baibo.

9. Ni khalidwe liti limafunikila kuti timvetse maulosi a m’Baibo? Fotokozani.

9 Khalani wodzicepetsa. Yehova analonjeza kuti anthu odzicepetsa adzawathandiza. (Yak. 4:6) Conco tiyenela kupempha thandizo lake kuti timvetse maulosi a m’Baibo. Tiyenelanso kuvomeleza kuti tifunikila thandizo la kapolo wokhulupilika, amene amagwilitsidwa nchito potipatsa cakudya cauzimu panthawi yake. (Luka 12:42) Yehova ni Mulungu wadongosolo. Conco, m’pomveka kuti amaseŵenzetsa njila imodzi yokha potithandiza kumvetsa coonadi ca m’Mawu ake.—1 Akor. 14:33; Aef. 4:4-6.

10. Kodi muphunzilapo ciyani pa citsanzo ca mlongo Esther?

10 Fufuzani mokwana. Sankhani ulosi umene muli nawo cidwi ndipo ufufuzeni. N’zimene mlongo Esther anacita. Cidwi cake cinali pa maulosi amene anakambilatu za kubwela kwa Mesiya. Iye anati, “Nili na zaka 15 n’nayamba kufufuza maumboni otsimikizila kuti maulosiwo analembedwa nthawi ya Yesu isanafike.” Zimene anaŵelenga zokhudza mipukutu ya ku Nyanja Yakufa zinam’tsimikizila zimenezo. Iye ananena kuti, “Mipukutu ina inalembedwa nthawi ya Khristu isanafike. Conco maulosi a m’mipukutuyo anacokela kwa Mulungu.” Mlongo Esther anati, “Kuti nimvetse zimene niŵelenga n’nali kuziŵelenga kangapo.” Koma ni wokondwa kuti khama lake linamupindulila. Pambuyo poŵelenga maulosi osiyana-siyana mozama, iye anakamba kuti, “N’nali kudzionela nekha kuti zimene Baibo imanena n’zoonadi!”

11. Timapindula bwanji tikadzipezela umboni wotsimikizila kuti Baibo ni yoona?

11 Tikamaona maulosi ena a m’Mawu a Mulungu amene anakwanilitsika kale, timam’dalila kwathunthu Yehova komanso citsogozo cake. Kuwonjezela apo, maulosi a m’Baibo amatithandiza kuyembekezelabe zabwino kutsogolo, mosasamala kanthu za mavuto amene tikukumana nawo pali pano. Tiyeni tikambilane maulosi aŵili a m’buku la Danieli amene akukwanilitsika tsopano. Kuwamvetsetsa kungatithandize kupanga zisankho zanzelu.

KODI MAPAZI ACITSULO NA DONGO AMAKUKHUDZANI BWANJI?

12. Kodi mapazi ‘acitsulo cosakanizika ndi dongo lonyowa’ amaimila ciyani? (Danieli 2:41-43)

12 Ŵelengani Danieli 2:41-43. M’maloto a Mfumu Nebukadinezara amene Danieli anamasulila, mapazi a cifanizilo cimene mfumu inaona anali ‘acitsulo cosakanizika ndi dongo lonyowa’. Tikayelekezela ulosiwu na maulosi ena opezeka m’buku la Danieli komanso la Chivumbulutso, tiona kuti mapaziwa amaimila mgwilizano wa Britain na America, ulamulilo wamphamvu kwambili padziko lonse. Ponena za ulamulilo umenewu, Danieli anati “pa zinthu zina ufumuwo udzakhala wolimba koma pa zinthu zina udzakhala wosalimba.” N’ciyani cidzapangitsa ufumuwo kukhala wosalimba pa zinthu zina? Cifukwa n’cakuti anthu wamba, omwe amaimilidwa na dongo lonyowa amaulepheletsa kucita zinthu mwamphamvu ngati citsulo. b

13. Ni mfundo zoona ziti zomwe tingapeze tikamvetsa ulosiwu?

13 Zimene Danieli anafotokoza za cifanizilo ca m’maloto, maka-maka mapazi ake, zitiphunzitsa mfundo zoona zingapo zofunika kwambili. Mfundo yoyamba ni yakuti ulamulilo wa Britain na America waonetsa kuti ni wamphamvu pa mbali zina. Mwacitsanzo, ndiwo unacita mbali yaikulu pa kupambana nkhondo yoyamba ya padziko lonse na yaciŵili. Ngakhale n’telo, ulamulilo wamphamvu kwambili padziko lonse umenewu wafooketsedwa, ndipo udzapitiliza kutelo cifukwa ca mikangano pakati pa nzika zake. Mfundo yaciŵili ni yakuti mgwilizano wa Britain na America ndiwo ulamulilo wothela wamphamvu kwambili padziko lonse, umene udzakhalapo pomwe Ufumu wa Mulungu uzidzathetsa maufumu onse a anthu. Ngakhale kuti maiko ena angalimbane na ulamulilo wa Britain na America, maikowo sadzauloŵa m’malo. Tidziŵa izi cifukwa “mwala” womwe umaimila Ufumu wa Mulungu udzaphwanya mapazi a cifanizilo amene amaimila mgwilizano wa Britain na America.—Dan. 2:34, 35, 44, 45.

14. Kodi kumvetsa ulosi wonena za mapazi acitsulo na dongo kungatithandize bwanji kupanga zisankho zanzelu?

14 Kodi mumakhulupililadi kuti ulosi wa Danieli wonena za mapazi acitsulo na dongo ni woona? Ngati n’telo, zocita zanu pa umoyo zidzaonetsa zimenezo. Simudzaika maganizo anu pa kudziunjikila cuma m’dziko limene latsala pang’ono kuwonongedwa. (Luka 12:16-21; 1 Yoh. 2:15-17) Kumvetsa ulosiwu kudzakuthandizaninso kuona kufunika kwa nchito yolalikila na kuphunzitsa. (Mat. 6:33; 28:18-20) Pambuyo poŵelenga ulosiwu dzifunseni kuti, ‘Kodi zisankho zanga zimaonetsa kuti nimakhulupililadi kuti posacedwapa Ufumu wa Mulungu udzathetsa maboma onse a anthu?’

KODI “MFUMU YA KUMPOTO” NA “MFUMU YA KUM’MWELA” AMAKUKHUDZANI BWANJI?

15. Kodi “mfumu ya kum’mwela” na “mfumu ya kumpoto” amaimila ndani masiku ano? (Danieli 11:40)

15 Ŵelengani Danieli 11:40. Danieli caputala 11 imakamba za mafumu aŵili, kapena kuti maulamulilo a ndale, amene akulimbilana ulamulilo wa padziko lonse. Tikayelekezela ulosiwu na maulosi ena a m’Baibo, tipeza kuti “mfumu ya kumpoto” ni Russia na maiko ogwilizana naye, pamene “mfumu ya kum’mwela” ni Ulamulilo Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain na America. c

Tingalimbitse cikhulupililo cathu na kucepetsa nkhawa ngati tizindikila kuti kutsutsidwa na “mfumu ya kumpoto” komanso “mfumu ya kum’mwela,” kukukwanilitsa maulosi a m’Baibo (Onani ndime 16-18)

16. Kodi atumiki a Mulungu okhala m’dziko lolamulidwa na “mfumu ya kumpoto” amakumana na zopinga zotani?

16 Atumiki a Mulungu okhala m’dziko lolamulidwa na “mfumu ya kumpoto” akuzunzidwa na mfumu imeneyi. Mboni zina zamenyedwapo na kuponyedwa m’ndende kaamba ka cikhulupililo cawo. Zimene “mfumu ya kumpoto” ikucitazi sizikuwacititsa mantha abale athu, m’malo mwake, zikulimbitsa cikhulupililo cawo. Motani? Cifukwa abale athu akudziŵa kuti kuzunzidwa kwa anthu a Mulungu kukukwanilitsa ulosi wa Danieli. d (Dan. 11:41) Kudziŵa izi kungatithandize kukhalabe na ciyembekezo colimba komanso okhulupilika.

17. Kodi atumiki a Mulungu okhala m’dziko lolamulidwa na “mfumu ya kum’mwela” akumana na zopinga zotani?

17 M’zaka za kumbuyoku, “mfumu ya kum’mwela” nayonso yazunzapo anthu a Yehova. Mwacitsanzo, panthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse komanso yaciŵili, abale athu ambili anaponyedwa m’ndende komanso ana a Mboni anacotsedwa sukulu, cifukwa cokana kutengako mbali m’zandale. Koma m’zaka zaposacedwa, atumiki a Yehova okhala m’dziko lolamulidwa na mfumu ya kum’mwela, akumana na mayeso ambili ovuta kuwazindikila oyesa kukhulupilika kwawo. Mwacitsanzo, pa nthawi ya makampeni a masankho, Mkhristu angayesedwe kuti akhalile mbali cipani cinacake kapena wandale winawake. Ngakhale kuti sangavote, mumtima mwake angakhale ku mbali ina yake. Cotelo m’pofunika kwambili kusakhalila mbali m’zandale, m’zocita, komanso mmene tikumvela!—Yoh. 15:18, 19; 18:36.

18. Kodi zimatikhudza bwanji tikamaona mkangano wapakati pa “mfumu ya kumpoto” na “mfumu ya kum’mwela”? (Onaninso cithunzi)

18 Anthu amene sakhulupilila maulosi a m’Baibo amakhala na nkhawa yaikulu kwambili akaona “mfumu ya kum’mwela” ‘ikukankhana’ na “mfumu ya kumpoto.” (Dan. 11:40) Mafumu aŵiliwa ali na zida zanyukiliya zamphamvu kwambili zomwe zingathe kufafaniza kamoyo kalikonse padzikoli. Koma ife tidziŵa kuti Yehova sadzalola zimenezo kucitika. (Yes. 45:18) Conco m’malo motibweletsela nkhawa, mkangano wapakati pa “mfumu ya kumpoto” na “mfumu ya kum’mwela” umalimbitsa cikhulupililo cathu. Mkanganowo umatitsimikizila kuti mapeto alidi pafupi.

PITILIZANI KUŴELENGA MAULOSI

19. Kodi tiyenela kuvomeleza mfundo iti yokhudza maulosi a m’Baibo?

19 Sitidziŵa kuti maulosi ena a m’Baibo adzakwanilitsika motani. Ngakhale mneneli Danieli, sanamvetse zonse zimene analemba. (Dan. 12:8, 9) Koma kusamvetsa mmene ulosi winawake udzakwanilitsikile sikutanthauza kuti ulosiwo sudzakwanilitsika. Sitipeneka konse kuti Yehova adzatiuza zoyenela kudziŵa pa nthawi yake, monga anacitila kumbuyoko.—Amosi 3:7.

20. Ni maulosi ati a m’Baibo ocititsa cidwi amene adzakwanilitsika posacedwa? Nanga tiyenela kupitiliza kucita ciyani?

20 Coyamba, padzakhala cilengezo ca “bata ndi mtendele.” (1 Ates. 5:3) Kenako, maulamulilo andale adzaukila cipembedzo conyenga na kucifafanizilatu. (Chiv. 17:16, 17) Pambuyo pake, maulamulilowo adzaukila anthu a Mulungu. (Ezek. 38:18, 19) Izi n’zimene zidzabutsa nkhondo yothela ya Aramagedo. (Chiv. 16:14, 16) Ndife otsimikiza kuti zonsezi zatsala pang’ono kucitika. Koma poyembekezela zimenezi, tisaleke kuonetsa ciyamikilo cathu kwa Atate wathu wakumwamba, mwa kuŵelenga maulosi a m’Baibo, komanso kuthandiza ena kucita cimodzimodzi.

NYIMBO 95 Kuwala Kuwonjezeleka

a Ngakhale zinthu zivute bwanji m’dzikoli, tili na cidalilo cakuti kutsogoloku zinthu zidzakhala bwino. Cidalilo cimeneco timacipeza pophunzila maulosi a m’Baibo. Nkhani ino ifotokoza cifukwa cake tiyenela kuŵelenga maulosi a m’Baibo. Tikambilanenso mwacidule maulosi aŵili olembedwa na Danieli, na kuona mmene aliyense wa ife angapindulile akawamvetsa.

b Onani nkhani yakuti “Yehova Waulula ‘Zimene Ziyenera Kuchitika Posachedwapa,’” mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2012, ndime 7-9.

c Onani nkhani yakuti “Kodi ‘Mfumu ya Kumpoto’ Ndani Masiku Ano?,” mu Nsanja ya Mlonda ya May 2020 masa 12-13 ndime 3-4.

d Onani nkhani yakuti “Kodi ‘Mfumu ya Kumpoto’ Ndani Masiku Ano?,” mu Nsanja ya Mlonda ya May 2020 ndime 7-9.