Cidziŵitso Kwa Oŵelenga
Kwa Oŵelenga
M’magazini ino ya Nsanja ya Mlonda, muli nkhani zokwanila 5 zimene n’zogwilizana:
M’nkhani yoyamba, tidzakambilana mmene Yehova amakondela anthu, komanso zimene wacita kuti atithandize kulimbana nawo ucimo na kum’kondweletsa.
M’nkhani yaciŵili, tidzaphunzila zimene munthu ayenela kucita kuti alape, komanso mmene Yehova wathandizila anthu kuti alape.
Nkhani yacitatu idzafotokoza zimene mpingo wa ku Korinto unalangizidwa kucita na munthu amene anacita chimo lalikulu koma wosalapa.
M’nkhani yacinayi, tidzaphunzila mmene akulu amathandizila amene anacita chimo lalikulu.
M’nkhani yothela tidzaphunzila zimene mpingo ungacite kuti upitilize kucita naye mwacikondi komanso cifundo munthu amene wacotsedwa mumpingo.