NKHANI YOPHUNZILA 34
NYIMBO 107 Cikondi ca Umulungu
Mmene Akulu Amaonetsela Cikondi na Cifundo Kwa Munthu Wocita Chimo
“Mulungu akukusonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu,. . . nʼcolinga coti ulape.”—AROMA 2:4.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Mmene akulu amathandizila anthu ocita chimo lalikulu mumpingo.
1. N’ciyani cimacitika munthu akacita chimo lalikulu?
M’NKHANI yapita tinakambilana mmene mtumwi Paulo anasamalila nkhani yokhudza munthu yemwe anacita chimo lalikulu mumpingo wa ku Korinto. Cifukwa munthu wocimwayo sanalape, anacotsedwa mumpingo. Koma monga mmene lemba la mfundo yaikulu ya nkhani ino ionetsela, Mulungu amatha kum’thandiza munthu amene wacita chimo lalikulu kuti alape. (Aroma 2:4) Kodi akulu angamuthandize bwanji amene wacita chimo lalikulu kuti alape?
2-3. Tiyenela kucita ciyani tikadziŵa kuti wolambila mnzathu wacita chimo lalikulu? Nanga n’cifukwa ciyani tiyenela kutelo?
2 Akulu akapanda kudziŵa kuti munthu anacita chimo, sangathe kum’thandiza kuti alape. Conco tikadziŵa kuti wokhulupilila mnzathu anacita chimo lalikulu limene lingacititse kuti acotsedwe mumpingo, kodi tiyenela kucita ciyani? Timulimbikitse kuti akapemphe thandizo kwa akulu.—Yes. 1:18; Mac 20:28; 1 Pet. 5:2.
3 Nanga bwanji ngati munthuyo safuna kukaonana nawo akulu? Zikakhala conco, ifeyo tifunika kupita kwa akulu kukawauza za nkhaniyo, kuti munthuyo alandile thandizo limene akufunikila. Kucita izi kudzaonetsa kuti timamukonda m’bale kapena mlongo wathu, cifukwa tidziŵa kuti akulu angamuthandize. Ngati munthuyo sangasinthe, ndiye kuti angaononge ubwenzi wake na Yehova. Ndipo ngati anthu ena amene si Mboni angadziŵe za nkhaniyo, zingaonongetse mbili ya mpingo. Conco, timalimba mtima na kupita kukauza akulu cifukwa timakonda Yehova komanso munthuyo.—Sal. 27:14.
MMENE AKULU AMATHANDIZILA MUNTHU WOCITA CHIMO LALIKULU
4. Kodi akulu amakhala na colinga citi pokakumana na munthu amene wacita chimo lalikulu?
4 Munthu mumpingo akacita chimo lalikulu, bungwe la akulu limasankha akulu atatu oyenelela kuti akakumane na munthuyo. a Abale amene asankhidwawo ayenela kukhala odzicepetsa pocita naye munthuyo. Ngakhale kuti colinga cawo ni kuthandiza wolakwayo kuti alape, iwo amadziŵa kuti sangakakamize munthu kusintha. (Deut. 30:19) Akulu amadziŵa kuti si munthu aliyense angalape monga anacitila Mfumu Davide. (2 Sam. 12:13) Anthu ena akacimwa, amakana kumvela malangizo a Yehova. (Gen. 4:6-8) Mulimonsemo, colinga ca akulu ni kuthandiza munthu amene wacita chimo kuti alape ngati n’zotheka. Kodi akulu amatsatila mfundo ziti pocita naye munthu amene wacita chimo lalikulu?
5. Kodi akulu amaonetsa makhalidwe ati pokumana na munthu amene wacita colakwa cacikulu? (2 Timoteyo 2:24-26) (Onaninso cithunzi.)
5 Akulu amaona munthu amene wacita chimo lalikulu monga nkhosa yamtengo wapatali imene yasocela. (Luka 15:4, 6) Pa cifukwa cimeneci, iwo akakumana na munthuyo, amapewa kucita naye mwaukali kapena mouma mtima. Akulu amapewanso kuganiza kuti kukumana na munthuyo ni mwambo cabe umene unakhazikitsidwa wofunika kuutsatila. M’malomwake, iwo amaonetsa makhalidwe ochulidwa pa 2 Timoteyo 2:24-26. (Ŵelengani.) Akulu amakhalabe odekha, ofatsa, komanso okoma mtima pamene akuyesetsa kumufika pamtima munthu wolakwayo.
6. Kodi akulu amakonzekeletsa bwanji mitima yawo asanakumane na munthu amene anacita colakwa cacikulu? (Aroma 2:4)
6 Akulu amakonzekeletsa mitima yawo. Akulu amayesetsa kutengela Yehova pocita naye munthu amene anacita chimo lalikulu. Iwo amacita zimenezi pokumbukila mawu a Paulo akuti: “Mulungu akukusonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu,. . . n’colinga coti ulape.” (Ŵelengani Aroma 2:4.) Akulu ayenela kukumbukila kuti iwo ni abusa amene ali pansi pa citsogozo ca Khristu. (Yes. 11:3, 4; Mat. 18:18-20) Asanakumane na munthuyo, a m’komiti ayenela kupempha Yehova kuti awathandize kukwanilitsa colinga cawo, comwe ni kuthandiza munthuyo kuti alape. Iwo amafufuza m’Malemba komanso m’zofalitsa zathu, ndiponso amapemphela kwa Yehova kuti awathandize kukhala ozindikila. Amaganizilanso zimene zinacititsa munthuyo kukhala na kaganizidwe kapena makhalidwe omwe anam’tsogolela ku chimolo.—Miy. 20:5.
7-8. Kodi akulu angatengele bwanji khalidwe la Yehova la kuleza mtima pokumana na munthu amene wacita colakwa cacikulu?
7 Akulu amatengela kuleza mtima kwa Yehova. Iwo amakumbukila mmene Yehova anacitila zinthu na anthu a kumbuyoku amene anacitapo macimo aakulu. Mwacitsanzo, iye anacita zinthu mokoma mtima na Kaini. Yehova anamucenjeza za zimene zingacitike ngati sangasinthe khalidwe lake, ndipo anamuuza kuti adzamudalitsa ngati angasinthe khalidwe lakelo. (Gen. 4:6, 7) Yehova anatuma mneneli Natani kukapeleka uphungu kwa Davide. Natani anaseŵenzetsa fanizo limene linafika pamtima mfumuyo na kum’thandiza kuti alape. (2 Sam. 12:1-7) Ndipo Yehova ‘anapitiliza kutumiza’ aneneli ake “mobwelezabweleza” kwa mtundu wosamvela wa Isiraeli. (Yer. 7:24, 25) Iye sanayembekezele kuti anthu ake alape kenako n’kuwathandiza. M’malomwake, iye anacitapo kanthu kuti awathandize ngakhale kuti anthuwo anali kumucimwila.
8 Akulu amatengela citsanzo ca Yehova pamene akuyesetsa kuthandiza munthu amene wacita chimo lalikulu. Monga yaonetsela 2 Timoteyo 4:2, akulu amacita zinthu “moleza mtima kwambili” na wokhulupilila mnzawo amene akusautsika cifukwa ca chimo limene anacita. Conco, nthawi zonse mkulu ayenela kucita zinthu modekha, komanso moleza mtima kuti athandize amene wacita chimo lalikulu kukhala na cifuno cocita zoyenela. Ngati mkulu angacite zinthu mokwiya kapena mokhumudwa, munthuyo sangamvetsele uphungu ndipo angakane kulapa.
9-10. Kodi akulu angathandize bwanji munthu amene anacita colakwa cacikulu kuzindikila zisankho zimene zinam’tsogolela kucita chimo?
9 Akulu amayesetsa kudziŵa zinthu zimene zinatsogolela munthuyo kuti acimwe. Mwacitsanzo, kodi n’ciyani cinafooketsa ubwenzi wake na Yehova? Kodi iye anasiya kuŵelenga Baibo mokhazikika kapenanso kupita mu utumiki? Kodi amapemphelabe kwa Yehova kaŵili-kaŵili? Kapena kodi mapemphelo ake anangokhala amwambo cabe? Kodi wakhala akulola maganizo olakwika kuzika mizu mwa iye? Kodi amakonda kuceza na ndani? Kodi amasankha mwanzelu zosangalatsa zimene amaonelela kapena kumvetsela? Kodi zisankho zimene anapanga pa nkhani zimenezi zinakhudza bwanji kaganizidwe kake komanso zikhumbo zake? Kodi iye akuzindikila mmene zisankho zake zaposacedwa na zocita zake zakhudzila Atate wake Yehova?
10 Mwa kufunsa mafunso othandiza amenewa kwa munthuyo, akulu angathandize munthuyo kuzindikila zimene zinacititsa kuti ubwenzi wake na Yehova ufooke. Ndipo mwina zimenezo n’zimene zinam’tsogolela kuti acite colakwa cimeneco. Akulu amacita zimenezi mokoma mtima, ndipo amapewa kumufunsa mafunso oloŵelela kwambili m’nkhani za munthu mwini. (Miy. 20:5) Kuwonjezela apo, iwo angaseŵenzetse mafanizo pothandiza munthuyo kuona na kuzindikila kulakwa kwake, monga mmene Natani anacitila kwa Davide. N’kutheka pa kukumana kwawo koyamba na munthuyo, iye angayambe kumva cisoni cifukwa ca zinthu zoipa zimene anacita, ndipo n’kutheka iye angalape.
11. Kodi Yesu anacita nawo motani anthu ocimwa?
11 Akulu amayesetsa kutengela citsanzo ca Yesu. Pokambilana na Saulo wa ku Tarisi, Yesu woukitsidwayo, anamufunsa funso lomupangitsa kuganiza lakuti: “Saulo, Saulo, n’cifukwa ciyani ukundizunza?” Mwa kutelo, Yesu anathandiza Saulo kuzindikila kuti anali kucita zinthu zoipa. (Mac. 9:3-6) Ndipo ponena za “mayi uja Yezebeli,” Yesu anakamba kuti: “Ndamupatsa nthawi kuti alape.”—Chiv. 2:20, 21.
12-13. Kodi akulu angapatse bwanji nthawi munthu amene anacita chimo lalikulu kuti alape? (Onaninso cithunzi.)
12 Potengela citsanzo ca Yesu, akulu sakhala ofulumila kugamula kuti munthu wocita colakwayo sangalape. Ena angalape pa kukumana kwawo koyamba na komiti ya akulu. Koma ena angafunikile nthawi. Conco, akulu angalinganize kuti akumane na munthuyo maulendo angapo. N’kutheka kuti pambuyo pokumana naye koyamba, Mkhristu wolakwayo angayambe kuganizilapo mozama pa zimene anauzidwa. Angaonetse kudzicepetsa mwa kupempha Yehova kuti amukhululukile chimo lake. (Sal. 32:5; 38:18) Conco, pa kukumana kwawo kotsatila na munthuyo, n’kutheka kuti munthuyo angaonetse khalidwe losiyana na limene anaonetsa pa kukumana kwawo koyamba.
13 Kuti athandize munthuyo kulapa, akulu amamucitila cifundo komanso kumukomela mtima. Iwo amapemphela kwa Yehova kuti adalitse zoyesayesa zawo pothandiza Mkhristu wolakwayo kuzindikila kulakwa kwake na kum’thandiza kuti alape.—2 Tim. 2:25, 26.
14. N’ndani maka-maka amathandiza munthu wocimwa kulapa? Nanga n’cifukwa ciyani tikutelo?
14 Munthu wocimwa akalapa, zimakhala zokondweletsa zedi! (Luka 15:7, 10) Ngakhale kuti akulu amacita zonse zotheka kuti munthuyo alape, kodi ndani maka-maka amene amathandiza munthuyo kusintha? Kumbukilani zimene Paulo analemba ponena za anthu ocimwa. Iye anati: “Mwina Mulungu angawalole kulapa.” (2 Tim. 2:25) Conco Yehova, osati munthu wina aliyense, ndiye amathandiza Mkhristu wolakwayo kusintha kaganizidwe kake na kacitidwe kake ka zinthu. Paulo anafotokoza zinthu zabwino zimene zimacitika munthu akalapa. Iye anafotokoza kuti munthuyo amadziŵa coonadi molondola, nzelu zimamubwelela, ndipo amapulumuka mu msampha wa Mdyelekezi.—2 Tim. 2:26.
15. Kodi akulu angacite ciyani kuti apitilize kuthandiza wocimwa amene walapa?
15 Munthu amene anacita chimo akalapa, a m’komiti amapanga makonzedwe ocita maulendo aubusa kwa munthuyo. Amacita zimenezo pofuna kuti munthuyo apitilize kulandila thandizo lofunikila limene lingamuthandize kupewa misampha ya Satana, komansokomanso kuti apitilize kucita zoyenela. (Aheb. 12:12, 13) Komabe, akulu sauza ena mumpingo za chimo limene munthuyo anacita. Koma kodi mpingo uyenela kuuzidwa ciyani zokhudza nkhaniyo?
“UZIWADZUDZULA PAMASO PA ONSE”
16. Kodi Paulo anali kunena za ndani ponena mawu akuti “pamaso pa onse” pa 1 Timoteyo 5:20?
16 Ŵelengani 1 Timoteyo 5:20. Paulo analemba mawu amenewa pouza mkulu mnzake Timoteyo. Anacita zimenezo pomuuza mocitila nawo anthu amene ali na “cizolowezi cocita chimo.” Kodi Paulo anatanthauza kuti wocimwayo ayenela kudzudzulidwa pamaso pa mpingo wonse? Pokamba mawu akuti “pamaso pa onse,” iye sanatanthauze mpingo wonse ayi. M’malomwake, anali kunena za anthu ocepa amene angadziŵe za chimo limene munthuyo wacita. Anthuwo angaphatikizepo amene anamuona akucita chimolo, kapena amene munthuyo anawauzako za chimo limene anacita. Zikatelo, akulu ayenela kuuza anthuwo mseli kuti nkhaniyo inasamalidwa, komanso kuti wocimwayo anawongoleledwa.
17. Ngati chimo lalikulu ladziŵika mumpingo kapena lidzadziŵika ndithu, kodi payenela kupelekedwa cilengezo cotani? Ndipo cifukwa ciyani?
17 Nthawi zina zimacitika kuti chimolo ladziŵika kwambili mumpingo kapena lidzadziŵika ndithu. Zikakhala conco, kudzudzula munthuyo “pamaso pa onse,” kumaphatikizapo mpingo wonse. Zikatelo, mkulu ayenela kupeleka cilengezo ku mpingo cakuti m’bale kapena mlongoyo anadzudzulidwa. N’cifukwa ciyani ayenela kucita zimenezi? Paulo anati: “Kuti ena onsewo akhale ndi mantha” na kupewa kugwela m’chimo.
18. Ngati munthu wobatizika wosakwanitsa zaka 18 wacita chimo lalikulu, kodi akulu ayenela kuisamalila motani nkhani yake? (Onaninso cithunzi.)
18 Kodi akulu ayenela kucita ciyani ngati wacicepele wobatizika yemwe sanakwanitse zaka 18 wacita colakwa cacikulu? Bungwe la akulu liyenela kusankha akulu aŵili kuti akaonane na wacicepeleyo pamodzi na makolo ake acikhristu. b Akuluwo ayenela kufunsa zimene makolowo acitapo kale pofuna kuthandiza mwanayo kusintha khalidwe lake na kulapa. Nthawi zina akuluwo angaone kuti mwanayo akumvela uphungu umene makolo ake akumupatsa, ndipo iye akuyesetsa kusintha khalidwe lake na kaganizidwe kake. Zikakhala conco, akuluwo angagamule kuti m’posafunikila kupanga komiti ya akulu yodzaonana na mwanayo na makolo ake. Akulu amadziŵa kuti Yehova wapeleka udindo kwa makolo wophunzitsa ana awo mwacikondi na kuwaongolela. (Deut. 6:6, 7; Miy. 6:20; 22:6; Aef. 6:2-4) Ndipo mwa apa na apo, akulu adzayamba kukambilana na makolo pofuna kutsimikizila kuti mwanayo akulandila thandizo limene akufunikila. Nanga akulu ayenela kucita ciyani ngati mwana wobatikizayo saleka kucita zoipa ndipo safuna kulapa? Zikatelo, komiti ya abale atatu iyenela kukumana naye pamodzi na makolo ake acikhristu.
“YEHOVA NDI WACIKONDI CACIKULU KOMANSO WACIFUNDO”
19. Kodi akulu amacita ciyani potengela citsanzo ca Yehova pokumana na munthu amene anacita chimo lalikulu?
19 Akulu amene amatumikila m’makomiti anapatsidwa udindo na Yehova wosungitsa ciyelo ca mpingo. (1 Akor. 5:7) Iwo amacita zonse zotheka kuti athandize munthu wolakwayo kuti alape ngati n’kotheka. Ndipo pamene akuthandiza munthuyo, akulu amakhala na cidalilo cakuti iye angasinthe. N’cifukwa ciyani amacita zimenezi? Amatelo pofuna kutengela Yehova yemwe “ndi wacikondi cacikulu komanso wacifundo.” (Yak. 5:11) Onani mmene mtumwi wacikalambile Yohane anaonetsela khalidwe lacikondi kwa abale na alongo ake. Iye analemba kuti: “Ana anga okondedwa, ndikukulembelani zinthu izi kuti musacite chimo. Komabe, wina akacita chimo, tili ndi wotithandiza wolungama, Yesu Khristu, amene ali ndi Atate.”—1 Yoh. 2:1.
20. Tidzakambilana ciyani m’nkhani yotsatila?
20 N’zacisoni kuti nthawi zina, Mkhristu amene wacita colakwa cacikulu amakana kulapa. Zikakhala telo, Mkhristuyo amacotsedwa mumpingo. Kodi akulu amasamalila bwanji nkhani za conco? Tidzakambilana zimenezi m’nkhani yomaliza ya mpambo uno wa nkhani.
NYIMBO 103 Abusa ni Mphatso za Amuna
a Kale, gulu limeneli linali kuchedwa komiti ya ciweluzo. Koma popeza kuti kuweluza ni mbali imodzi cabe ya nchito yawo, sitidzagwilitsanso nchito mawu amenewo. M’malomwake, tidzayamba kuwachula kuti komiti ya akulu.
b Mfundo imene tafotokoza yokhudza makolo, igwilanso nchito kwa omuyang’anila ovomelezeka mwalamulo, kapena ena omwe akumusamalila wacicepeleyo.