Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 31

NYIMBO 12 Mulungu Wamkulu, Yehova

Zimene Yehova Anacita Kuti Apulumutse Anthu ku Ucimo

Zimene Yehova Anacita Kuti Apulumutse Anthu ku Ucimo

“Mulungu anakonda kwambili dziko moti anapeleka mwana wake wobadwa yekha.”YOH. 3:16.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Mmene Yehova wakhala akutithandizila kulimbana na ucimo, komanso makonzedwe omwe iye walinganiza amene adzatithandiza kukapeza moyo wosatha komanso kukhala opanda ucimo.

1-2. (a) Kodi ucimo n’ciyani? Nanga tingaugonjetse bwanji? (Onaninso mbali yakuti “Kufotokozela Mawu Ena.”) (b) Tikambilane ciyani m’nkhani ino, komanso m’nkhani zina za mu Nsanja ya Mlonda ino? (Onaninso danga lakuti “Cidziŵitso Kwa Oŵelenga” m’magazini ino.)

 KODI mungakonde kudziŵa kuzama kwa cikondi cimene Yehova Mulungu ali naco pa inu? Mungapeze yankho la funso limeneli mwa kuphunzila zimene iye anacita kuti akupulumutseni ku ucimo na imfa. Ucimo a ni mdani woopsa amene simungathe kumugonjetsa pa inu nokha. Tonsefe timacimwa tsiku lililonse, ndipo timafa cifukwa ca ucimo. (Aroma 5:12) Koma pali nkhani yabwino. Na thandizo la Yehova, tingathe kugonjetsa ucimo, ndipo sitikukaika konse kuti tidzapambana!

2 Kwa zaka pafupifupi 6,000, Yehova Mulungu wakhala akuthandiza anthu kulimbana na ucimo. N’cifukwa ciyani amatelo? Cifukwa amatikonda. Iye wakhala akukonda anthu kucokela paciyambi. Conco waticitila zinthu zazikulu zimene zimatithandiza tikacimwa. Mulungu adziŵa kuti ucimo umabweletsa imfa. Iye safuna kuti tizifa, koma amafuna kuti tikhale na moyo kwamuyaya. (Aroma 6:23) Amafuna kuti inuyo mukakhale na moyo wosatha. M’nkhani ino, tikambilane mafunso atatu awa: (1) Kodi Yehova anapeleka ciyembekezo cotani kwa anthu ocimwa? (2) N’ciyani cimene anthu ocimwa ochulidwa m’Baibo anacita kuti akondweletse Mulungu? (3) Kodi Yesu anacita ciyani kuti apulumutse anthu ku ucimo na imfa?

KODI YEHOVA ANAPELEKA CIYEMBEKEZO COTANI KWA ANTHU OCIMWA?

3. N’ciyani cinacititsa kuti makolo athu acimwe?

3 Pomwe Yehova analenga mwamuna na mkazi woyamba, anali kufuna kuti akhale acimwemwe. Anawapatsa malo abwino okhala, mphatso ya ukwati, komanso nchito yokondweletsa. Anawauza kuti adzaze dziko lapansi na ana awo, komanso kuti apange dziko lonse lapansi kukhala paradaiso monga mmene munda wa Edeni unalili. Koma anawapatsa lamulo limodzi losavuta kutsatila. Iye anawacenjeza kuti ngati angaphwanye lamulo limenelo, komwe kunali kumupandukila mwadala, iwo adzafa. Tidziŵa zimene zinacitika. Mngelo wina woipa amene sanali kukonda Mulungu komanso anthu, anawanyengelela kuti aphwanye lamulo limene anapatsidwa. Adamu na Hava anacita zimene mngelo woipa uja amene ni Satana anali kufuna. Cifukwa colephela kukhulupilila Atate wawo wacikondi, iwo anacimwa. Monga tidziŵila, zimene Yehova ananena zinacitikadi. Cifukwa cakuti sanamvele, Adamu na Hava anayamba kuvutika kwa moyo wawo wonse. Anayamba kukalamba, ndipo pamapeto pake anafa.—Gen. 1:​28, 29; 2:​8, 9, 16-18; 3:​1-6, 17-19, 24; 5:5.

4. N’cifukwa ciyani Yehova amadana nawo ucimo? Ndipo n’cifukwa ciyani amatithandiza kulimbana nawo? (Aroma 8:​20, 21)

4 Yehova anaika nkhani yomvetsa cisoni imeneyi m’Baibo kuti itithandize. Imatithandiza kumvetsa cifukwa cake iye amadana kwambili na ucimo. Ucimo umatilekanitsa na Atate wathu ndipo umabweletsa imfa. (Yes. 59:2) Ndiye cifukwa cake Satana, mngelo wopanduka uja amene anayambitsa mavuto onsewa, amakonda ucimo. Ndipo iye amalimbikitsa anthu kuti azicimwa masiku ano. N’kutheka kuti pamene Satana anacimwitsa Adamu na Hava m’munda wa Edeni, anaganiza kuti wakwanitsa kulepheletsa cifunilo ca Yehova. Koma iye sanadziŵe kuti Yehova ni Mulungu wacikondi cacikulu. Mulungu sanasinthe colinga cake cimene anali naco pa mbadwa za Adamu na Hava. Iye amakonda anthu. Conco Adamu na Hava atacimwa, nthawi yomweyo Mulungu anapeleka ciyembekezo kwa anthu onse. (Ŵelengani Aroma 8:​20, 21.) Yehova anadziŵa kuti padzakhala anthu ena amene adzasankha kumukonda komanso amene adzafuna thandizo lake polimbana na ucimo. Pokhala Atate wawo komanso Mlengi wawo, iye anali kudzawamasula ku ucimo na kuwathandiza kuti amuyandikile. Kodi Yehova anali kudzacita motani zimenezi?

5. Kodi ni liti pamene Yehova anapeleka ciyembekezo koyamba kwa anthu onse? Fotokozani. (Genesis 3:15)

5 Ŵelengani Genesis 3:15. Yehova anapeleka ciyembekezo nthawi yoyamba kwa anthu pomwe ananena zomwe zidzacitikile Satana. Mulungu anakamba kuti kudzabwela “mbadwa” imene idzapulumutse anthu. Mbadwa imeneyo inali kudzawononga Satana na kukonza zoipa zonse zimene zinayambila mu Edeni. (1 Yoh. 3:8) Komabe, mbadwa imeneyo inali kudzavutika pocita zimenezi. Satana anali kudzaivulaza mbewu imeneyi kapena kuti kuipha. Izi zinali kudzamupweteka kwambili Yehova. Koma iye analolela zimenezi kuti anthu ambili adzapulumutsidwe ku ucimo na imfa!

KODI ANTHU OCIMWA OCHULIDWA M’BAIBO ANACITA CIYANI KUTI AKONDWELETSE YEHOVA?

6. Kodi anthu acikhulupililo monga Abele na Nowa, anacita ciyani kuti ayandikile Yehova?

6 M’kupita kwa zaka, Yehova mwapang’ono-pang’ono anamveketsa bwino zimene anthu ocimwa angacite kuti amuyandikile. Munthu woyamba yemwe anaika cikhulupililo cake mwa Yehova pambuyo pa cipanduko ca mu Edeni anali Abele, mwana waciŵili wa Adamu na Hava. Popeza Abele anali kukonda Yehova, ndipo anali kufunitsitsa kumukondweletsa na kumuyandikila, anapeleka nsembe kwa iye. Abele anali m’busa, conco anatenga ena mwa ana a nkhosa zake na kuwapeleka nsembe kwa Yehova. Kodi Yehova anamva bwanji na nsembeyo? Iye “anasangalala ndi Abele komanso nsembe yake.” (Gen. 4:4) Yehova anakondwelanso na nsembe zimene anthu ena amene anali kumukonda komanso kumukhulupilila anapeleka. Mmodzi wa anthuwa anali Nowa. (Gen. 8:​20, 21) Mwa kulandila nsembe zawo, Yehova anaonetsa kuti anthu ocimwa angathe kumukondweletsa komanso kumuyandikila. b

7. Kodi tiphunzilapo ciyani pa kulolela kwa Abulahamu kupeleka mwana wake nsembe?

7 Abulahamu anali na cikhulupililo colimba mwa Yehova. Yehova anamupempha cina cake cimene cinali covuta kwa Abulahamu kucita. Anapempha Abulahamu kuti apeleke mwana wake Isaki nsembe. Izi ziyenela kuti zinamuvutitsa maganizo kwambili Abulahamu. Ngakhale n’telo, iye anali wofunitsitsa kumvela Yehova. Pamene Abulahamu anatsala pang’ono kupha mwana wake, Mulungu anamuletsa. Komabe citsanzoci cimaphunzitsa anthu onse okhulupilika zimene Yehova anali kudzacita m’tsogolo. Iye anali kudzalolela kupeleka nsembe Mwana wake wokondeka. Yehova anali kudzacita zimenezi cifukwa amakonda kwambili anthu.—Gen. 22:​1-18.

8. Kodi nsembe zimene Aisiraeli anali kupeleka zinali kuimila ciyani? (Levitiko 4:​27-29; 17:11)

8 Patapita zaka zambili, Yehova anapatsa Aisiraeli Cilamulo. Mu Cilamulo cimeneco, Yehova anawauza kuti azipeleka nsembe zanyama kuti macimo awo azikhululukidwa. (Ŵelengani Levitiko 4:​27-29; 17:11.) Nsembe zimenezi zinali kuimila makonzedwe a nsembe yaikulu imene Mulungu analinganiza, yomwe inali kudzapulumutsa anthu ku ucimo kothelatu. Mulungu anauzila aneneli kulemba za mbewu yolonjezedwa. Mbewu imeneyi ni Mwana wa Mulungu wapadela, ndipo anali kudzavutika komanso kuphedwa. Iye anali kudzaphedwa monga nkhosa yokapelekedwa nsembe. (Yes. 53:​1-12) Tangoganizani: Yehova anali kudzapeleka Mwana wake wokondeka nsembe kuti apulumutse anthu, kuphatikizapo inu, ku ucimo na imfa!

KODI YESU ANACITA CIYANI KUTI APULUMUTSE ANTHU?

9. Kodi Yohane M’batizi anati ciyani ponena za Yesu? (Aheberi 9:22; 10:​1-4, 12)

9 Mu 29 C.E., mtumiki wa Mulungu, Yohane M’batizi ananena mawu awa pofotokoza za Yesu wa ku Nazareti: “Taonani, Mwanawankhosa wa Mulungu amene akucotsa ucimo wa dziko!” (Yoh. 1:29) Mawu ouzilidwa amenewa anaonetsa kuti Yesu ndiye anali mbewu yapadela imene Mulungu anali atalonjeza. Yesu anali kudzapeleka nsembe imene inali italonjezedwa. Pamapeto pake, mbewu yolonjezedwayo ya Yehova inali itafika kuti ipulumutse anthu kothelatu ku ucimo.—Ŵelengani Aheberi 9:22; 10:​1-4, 12.

10. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anabwela “kudzaitana anthu ocimwa”‏?

10 Yesu anaika kwambili maganizo ake pa kuthandiza anthu amene anali kuvutika cifukwa ca ucimo. Ndipo anawapempha anthuwo kuti akhale otsatila ake. Iye anadziŵa kuti anthu anali kukumana na mavuto cifukwa ca ucimo. Yesu anathandiza ngako anthu amene anali kudziŵika kuti ni ocimwa kwambili. Mwa fanizo, iye anakamba kuti: “Anthu athanzi safunikila dokotala, koma odwala ndiwo amamufuna.” Anaonjezela kuti: “N’nabwela kudzaitana anthu ocimwa osati olungama.” (Mat. 9:​12, 13) Ndipo n’zimene Yesu anali kucita. Iye anacita zinthu mokoma mtima na mzimayi amene anatsuka mapazi ake na misozi, ndipo anamukhululukila macimo ake. (Luka 7:​37-50) Yesu anaphunzitsa mayi wacisamariya mfundo zofunika za coonadi ngakhale kuti anali kudziŵa kuti mayiyo anali kukhala na mwamuna yemwe sanali wake. (Yoh. 4:​7, 17-19, 25, 26) Mulungu anapatsanso Yesu mphamvu zogonjetsa imfa yomwe imabwela cifukwa ca ucimo. Yesu anaukitsapo amuna, akazi, ana, komanso acikulile amene anamwalila.—Mat. 11:5.

11. N’cifukwa ciyani anthu ocimwa anali kumumasukila Yesu?

11 Yesu anali kuwamvetsa anthu ocimwa kwambili ndipo anali kuwacitila cifundo. Conco n’zosadabwitsa kuti anthuwo anali kumasuka naye Yesu, ndipo sanali kuopa kukamba naye. (Luka 15:​1, 2) Iye anawayamikila kwambili anthu amene anaonetsa cikhulupililo mwa iye ndipo anawafupa. (Luka 19:​1-10) Yesu anaonetsa kuti anali wacifundo monga mmene Atate wake alili. (Yoh 14:9) Mwa mawu na zocita zake, Yesu anaonetsa kuti Atate wake wacifundo amakonda anthu, ndipo amafuna kuthandiza aliyense wa iwo kupambana polimbana na ucimo. Yesu anathandiza anthu ocimwa kukhala ofunitsitsa kusintha miyoyo yawo na kumutsatila.—Luka 5:​27, 28.

12. Kodi Yesu anakamba ciyani za imfa yake?

12 Yesu anali kudziŵa zimene zinali kudzamucitikila. Kangapo konse, anauza otsatila ake kuti adzapelekedwa m’manja mwa anthu, ndipo adzakhomeledwa pamtengo. (Mat. 17:22; 20:​18, 19) Iye anadziŵa kuti nsembe yake idzacotsa ucimo wa dziko, monga mmene Yohane komanso aneneli ena anakambila. Yesu anakambanso kuti pambuyo pa imfa yake, ‘adzakokela anthu osiyanasiyana kwa iye.’ (Yoh. 12:32) Zinali zotheka tsopano kwa anthu ocimwa kukondweletsa Yehova mwa kuvomeleza kuti Yesu ni Ambuye, komanso kutengela citsanzo cake. Kucita izi kukanawathandiza kuti ‘amasulidwe ku ucimo.’ (Aroma 6:​14, 18, 22;Yoh. 8:32) Conco Yesu analimba mtima, ndipo anavomela kufa imfa yowawa kuti atipulumutse.—Yoh 10:​17, 18.

13. Kodi Yesu anafa imfa yotani? Nanga imfa yake imatiphunzitsa ciyani ponena za Yehova Mulungu? (Onaninso cithunzi.)

13 Yesu anapelekedwa m’manja mwa anthu, anamangidwa, ananyozedwa, anatonzedwa, anamenyedwa, ndipo pamapeto pake anagamulidwa kuti aphedwe. Asilikali anamutengela kumalo kumene anali kudzamupacikila, ndipo anamukhomelela pamtengo. Yesu anapilila zoŵaŵa komanso mavuto amenewa mokhulupilika. Komabe, Yehova anavutika koposelapo pomuona Mwana wakeyo akuvutika. Yehova ali na mphamvu zopanda malile. Conco akanafuna, akanaloŵelelapo kuti Mwana wake asafe imfa yowawa imeneyo. Koma sanatelo. Yehova amamukonda kwambili Mwana wake, conco n’cifukwa ciyani analolela kuti afe imfa yowawa imeneyi? Cikondi n’cimene cinamupangitsa kuti acite zimenezi. Yesu anakamba kuti: “Mulungu anakonda kwambili dziko moti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense womukhulupilila asawonongedwe koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yoh 3:16.

Zinamupweteka kwambili Yehova pamene analola Mwana wake kuphedwa kuti atimasule ku ucimo na imfa (Onani ndime 13)


14. Kodi nsembe ya Yesu imaonetsa ciyani za Yehova?

14 Nsembe ya Yesu ni umboni waukulu woonetsa kuti Yehova amakonda mbadwa zonse za Adamu na Hava. Imaonetsanso kukula kwa cikondi cimene Yehova ali naco pa imwe. Iye anapeleka Mwana wake na kupilila zambili kuti akupulumutseni ku ucimo na imfa. (1 Yoh 4:​9, 10) Iye amafuna kuthandiza aliyense wa ife kupambana polimbana na ucimo!

15. Kodi tiyenela kucita ciyani kuti tipindule na mphatso ya Mulungu ya nsembe ya dipo ya Yesu?

15 Mphatso ya Mulungu imene ni nsembe ya dipo ya Mwana wake wobadwa yekha, imatheketsa kuti macimo athu akhululukidwe. Koma kuti Mulungu atikhululukile tiyenela kucita cina cake. Kodi tiyenela kucita ciyani? Yohane M’batizi komanso Yesu Khristu iye mwini ananena kuti: “Lapani, cifukwa Ufumu wa kumwamba wayandikila.” (Mat. 3:​1, 2; 4:17) Conco tiyenela kulapa ngati tifuna kuti Yehova atikhululukile macimo athu komanso kuti timuyandikile. Koma kodi kulapa kutanthauza ciyani? Ndipo kumatithandiza bwanji kuti tikondweletse Yehova ngakhale kuti ndife ocimwa? Tidzakambilana zimenezi m’nkhani yotsatila.

NYIMBO 18 Tikuyamikani Cifukwa ca Dipo

a KUFOTOKOZELA MAWU ENA: M’Baibo, mawu akuti “ucimo” angatanthauze zinthu zoipa zimene munthu angacite, zomwe n’zosagwilizana na miyeso ya Yehova ya makhalidwe abwino. Koma nthawi zina mawu akuti “ucimo” angatanthauze kupanda ungwilo kumene tinatengela kwa Adamu. Ndipo tonsefe timafa cifukwa ca ucimo umenewu umene tinatengela kwa Adamu.

b Yehova anali kulandila nsembe za anthu okhulupilikawa cifukwa anali kudziŵa kuti m’tsogolo, nsembe ya Yesu idzamasula anthu ku ucimo na imfa kwamuyaya.—Aroma 3:25.