Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tulilani Yehova Nkhawa Zanu Zonse

Tulilani Yehova Nkhawa Zanu Zonse

‘Tulilani Yehova nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.’—1 PET. 5:7.

NYIMBO: 38, 7

1, 2. (a) N’cifukwa ciani sitiyenela kudabwa tikakhala na nkhawa? (Onani pikica pamwambapa.) (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

TIKUKHALA m’nthawi yosautsa kwambili. Satana Mdyelekezi ni wokwiya ngako, ndipo “akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” (1 Pet. 5:8; Chiv. 12:17) Conco, n’zosadabwitsa kuti nthawi zina, ngakhale ise atumiki a Mulungu timakhala na nkhawa. Ngakhale atumiki a Yehova akale, monga Mfumu Davide, anakumana ndi “masautso.” (Sal. 13:2) Kumbukilaninso kuti mtumwi Paulo anali kudela ‘nkhawa mipingo yonse.’ (2 Akor. 11:28) Koma kodi tingacite ciani ngati nkhawa zatikulila msinkhu?

2 Kale, Atate wathu wacikondi wakumwamba anathandiza atumiki ake. Ndipo masiku anonso, amatithandiza kucepetsa nkhawa kapena kuvutika maganizo. Baibo imatilimbikitsa kuti: ‘Mutulileni nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.’ (1 Pet. 5:7) Koma kodi tingacite bwanji zimenezi? Tiyeni tikambilane njila zinayi zimene tingacitile zimenezi. Yoyamba ni pemphelo locokela pansi pamtima, ina ni kuŵelenga Mau a Mulungu na kuwasinkha-sinkha, inanso ni kupempha mzimu woyela wa Yehova, komanso ina ni kuuzako munthu amene mumam’dalila nkhawa zanu. Pamene tikambilana njila zinayi zimenezi, zindikilani masitepi amene mufunika kutenga kuti zitheke.

‘TULILANI YEHOVA NKHAWA ZANU’

3. Mungatulile bwanji Yehova nkhawa zanu kupitila m’pemphelo?

3 Sitepi yoyamba ni kum’fikila Yehova mwa pemphelo locokela pansi pamtima. Ngati pacitika zinthu zokuvutitsani maganizo, zokucititsani mantha kapena nkhawa, kambani naye Atate wanu wacikondi wakumwamba. Wamasalimo anacondelela Yehova kuti: “Inu Mulungu, mvetselani pemphelo langa.” Ndiyeno anawonjezelanso kuti: “Umutulile Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakucilikiza.” (Sal. 55:1, 22) Mukacita mbali yanu kuti muthetse vuto, pemphelo la mtima wonse limathandizani kucepetsa nkhawa. Koma kodi pemphelo lingakuthandizeni bwanji kucepetsako nkhawa?—Sal. 94:18, 19.

4. N’cifukwa ciani pemphelo n’lofunika tikakhala na nkhawa?

4 Ŵelengani Afilipi 4:6, 7Yehova amayankha mapemphelo na mapembedzelo athu ocokela pansi pamtima. Motani? Mwa kutipatsa mtendele wa maganizo umene ungatikhazike mtima pansi na kucepetsa nkhawa. Ambili angavomeleze kuti n’zimene zinacitikadi kwa iwo. M’malo mwa nkhawa yosautsa maganizo, Mulungu anawathandiza kukhala na mtendele waukulu umene umaposa kuganiza kwaumunthu. N’zimene zingacitikenso kwa imwe. Conco, “mtendele wa Mulungu” ungapambane vuto lililonse limene mungakumane nalo. Khalani na cidalilo conse pa lonjezo la Yehova lakuti: “Usacite mantha, . . . pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.”—Yes. 41:10.

MAU A MULUNGU AMATIPATSA MTENDELE WA MAGANIZO

5. Kodi Mau a Mulungu angatipatse bwanji mtendele wa maganizo?

5 Njila yaciŵili yopezela mtendele wa maganizo ni kuŵelenga Baibo na kusinkha-sinkha. Zimenezi n’zofunika cifukwa ciani? Cifukwa Baibo ili na malangizo othandiza kupewa nkhawa, kuzicepetsa, kapena kulimbana nazo. Mulungu ndiye anatilenga. Conco, Mau ake amatithandiza, kutitsitsimula, komanso kutipatsa nzelu. Posinkha-sinkha malingalilo a Mulungu, usana ndi usiku, ndi kuona mmene mfundo za m’Baibo zimathandizila, mudzalimbikitsidwa kwambili. Yehova amadziŵa kuti ngati tiŵelenga Mau ake, tidzakhala ‘olimba mtima ndi kucita zinthu mwamphamvu,’ m’malo ‘mocita mantha kapena kuopa.’—Yos. 1:7-9.

6. Kodi mau a Yesu angakuthandizeni bwanji?

6 M’Baibo timapezamo mau a Yesu okhazika mtima pansi. Ndipo mau ake ndi ziphunzitso zake zinatsitsimula omvela ake. Yesu anali kutsitsimula anthu opanikizika, kulimbikitsa ofooka, ndi kutonthoza anthu ovutika maganizo. Pa cifukwa cimeneci, makamu a anthu anali kubwela kwa iye. (Ŵelengani Mateyu 11:28-30.) Mwacikondi, anali kuganizila zosoŵa za anthu zauzimu, zakuthupi, ndi mmene anali kumvelela. (Maliko 6:30-32) Lonjezo la Yesu lakuti adzaticilikiza likugwilabe nchito masiku ano. Inunso angakuthandizeni mmene anathandizila atumwi ake. Simufunika kucita kumuona Yesu kuti akuthandizeni. Monga Mfumu kumwamba, saleka kutionetsa cifundo cake. Conco mukakhala ndi nkhawa, mwacifundo iye ‘angakuthandizeni’ ‘pa nthawi imene mufunika thandizo.’ Ndithudi, Yesu angakuthandizeni kupilila nkhawa, ndi kukupatsani ciyembekezo na kukulimbikitsani.—Aheb. 2:17, 18; 4:16.

MZIMU WA MULUNGU UMABALA MAKHALIDWE AUMULUNGU

7. Kodi mudzapindula bwanji Mulungu akayankha pemphelo lanu lopempha mzimu woyela?

7 Yesu analonjeza kuti Atate wathu wakumwamba sadzalephela kupatsa mzimu woyela anthu omupempha. (Luka 11:10-13) Izi zitifikitsa pa njila yacitatu yocepetsela nkhawa zanu—cipatso ca mzimu. Makhalidwe abwinowo, amene ndiwo cipatso ca mzimu, amatipatsa cithunzi ca mmene alili Mulungu wamphamvuzonse. (Ŵelengani Agalatiya 5:22, 23; Akol. 3:10) Tikakulitsa makhalidwe a cipatso ca mzimu cimeneci, ubale wathu ndi anthu ena umakulanso. Mwa ici, tidzapewa zocitika zimene zingayambitse nkhawa. Ganizilani za mmene cipatso ca mzimu cingakuthandizileni.

8-12. Kodi makhalidwe a cipatso ca mzimu woyela angakuthandizeni bwanji kulimbana kapena kupewa zinthu zobweletsa nkhawa?

8 “Cikondi, cimwemwe, mtendele.” Ngati muyesetsa kucita zinthu mwaulemu ndi anthu, mwacionekele mudzakwanitsa kucepetsa nkhawa zanu. Motani? Eya, ngati muonetsa cikondi kwa abale na kuwalemekeza, mudzapewa zinthu zobweletsa nkhawa.—Aroma 12:10.

9 “Kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino.” Mumalimbitsa ubale mwa kutsatila malangizo akuti: “Khalani okomelana mtima, acifundo cacikulu, okhululukilana ndi mtima wonse.” (Aef. 4:32) Mwakutelo, mumapewa zocitika zobweletsa nkhawa. Komanso, mungadziŵe mocitila ndi mavuto obwela cifukwa ca kupanda ungwilo.

10 “Cikhulupililo.” Masiku ano, nkhawa imabwela maka-maka pofuna ndalama ndi zinthu zofunika paumoyo. (Miy. 18:11) Koma kukhala na cidalilo conse cakuti Yehova adzakusamalilani, kungakuthandizeni kupilila nkhawa, kapena kuzipewa. Zingatheke bwanji zimenezi? Mungapewe nkhawa zambili mwa kulabadila uphungu wa mtumwi Paulo, wakuti tizikhala ‘okhutila ndi zimene tili nazo pa nthawi ino.’ Paulo anawonjezela kuti: “Pakuti Mulungu anati: ‘Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.’ Conco, tifunika kukhala olimba mtima ndi kukamba kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandicite ciani?’”—Aheb. 13:5, 6.

11 “Kufatsa ndi kudziletsa.” Ganizilani mmene mungapindulile ngati muonetsa makhalidwe amenewa. Mungapewe zinthu zimene zingabweletse nkhawa zosiyana-siyana. Mudzapindulanso mwa kupewa zinthu monga “kuwawidwa mtima konse kwa njilu, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mau acipongwe.”—Aef. 4:31.

12 Koma kudzicepetsa n’kofunika kuti mukhale pansi pa “dzanja lamphamvu la Mulungu,” ndi kuti ‘mumutulile nkhawa zanu zonse.’ (1 Pet. 5:6, 7) Kucita zinthu modzicepetsa, kudzakuthandizani kupeza ciyanjo ca Mulungu ndi thandizo lake. (Mika 6:8) Kusadalila kwambili nzelu zanu kapena maluso anu, kudzakuthandizani kucepetsako nkhawa cifukwa mudzayamba kudalila Mulungu.

“MUSAMADE NKHAWA”

13. Kodi Yesu anatanthauza ciani pamene anati: “Musamade nkhawa”?

13 Pa Mateyu 6:34 (ŵelengani), pali malangizo a Yesu othandiza akuti: “Musamade nkhawa.” Komabe, cingaoneke covuta kutsatila malangizo amenewa. Kodi Yesu anatanthauza ciani pamene anati: “Musamade nkhawa”? Mwacionekele, iye sanatanthauze kuti mtumiki wa Mulungu sadzakhala ndi nkhawa iliyonse. Taona kale mmene Davide na Paulo anakambilapo za nkhawa zawo. Apa Yesu anali kuthandiza ophunzila ake kuzindikila kuti nkhawa zosayenela kapena zopitilila malile sizithandiza. Tsiku lililonse limakhala kale na mavuto ake. Conco, Akhiristu sayenela kuwonjezelaponso nkhawa zina poganizila kwambili za mavuto akumbuyo kapena akutsogolo. Kodi mungatsatile bwanji malangizo a Yesu kuti mucepetse nkhawa zozizilitsa m’nkhongono?

14. Kodi mufunika kucita ciani na nkhawa zakumbuyo?

14 Nkhawa zina zingabwele cifukwa ca zolakwa zimene munthu anacita kumbuyoku. Angayambe kudziimba mlandu cifukwa ca zimene anacita m’mbuyomo, olo kuti papita zaka zambili. Nthawi zina, Mfumu Davide inaona kuti ‘zolakwa zake zinakwela kupitilila mutu wake.’ Anacita kuvomeleza kuti: “Ndikulila mofuula cifukwa ca kuvutika kwa mtima wanga.” (Sal. 38:3, 4, 8, 18) Kodi n’ciani cinali canzelu kwa Davide kucita? Kodi anacita ciani? Anadalila Yehova kuti am’citile cifundo na kum’khululukila. Mwacidalilo iye anati: “Wodala ndi munthu amene wakhululukidwa zolakwa zake.”—Ŵelengani Salimo 32:1-3, 5.

15. (a) N’cifukwa ciani simuyenela kuda nkhawa na zimene zikukucitikilani? (b) Mungacite ciani kuti mucepetseko nkhawa zanu? (Onani danga lakuti “ Njila Zina Zothandiza Kucepetsako Nkhawa.”)

15 Nthawi zina, mungade nkhawa na zimene zikukucitikilani. Mwacitsanzo, pamene Davide analemba Salimo 55, anali kudela nkhawa moyo wake. (Sal. 55:2-5) Koma sanalole nkhawa kumutayitsa cidalilo cake mwa Yehova. Davide anali kuchula mavuto ake m’pemphelo. Koma anadziŵanso kuti anafunika kucitapo kanthu kuti akwanitse kulimbana ndi nkhawa zake. (2 Sam. 15:30-34) Tengelani citsanzo ca Davide. M’malo molola nkhawa kukufooketsani, citani zimene mungathe kuti mulimbane ndi vutolo. Ndiyeno, siyani zonse m’manja mwa Yehova.

16. Kodi tanthauzo la dzina la Mulungu lingalimbitse bwanji cikhulupililo canu?

16 Ngati Mkhiristu amaganizila kwambili za mavuto a m’tsogolo, angakhale na nkhawa zosafunikila. Osada nkhawa na zinthu zimene mwina sizingacitike. Cifukwa ninji? Cifukwa nthawi zambili zinthu sizifika poipilatu mmene tinali kuganizila. Ndiponso, palibe vuto lingakulile Mulungu amene mumamutulila nkhawa zanu zonse. Dzina lake leni-lenilo limatanthauza kuti “Iye Amacititsa Kukhala.” (Eks. 3:14) Tanthauzo la dzina la Mulungu n’lakuti Iye akhoza kukwanilitsa cifunilo cake kwa atumiki ake. Khalani na cidalilo cakuti Mulungu amafupa anthu ake okhulupilika, ndi kuwathandiza kuthana ndi nkhawa zakumbuyo, za lelo, ndi za kutsogolo.

KUUZAKO ENA NKHAWA ZANU

17, 18. Kodi kuuzako munthu amene mumam’dalila nkhawa zanu kungakuthandizeni bwanji?

17 Njila yacinayi yokuthandizani kulimbana ndi nkhawa, ni kuuzako munthu amene mumam’dalila. Mnzanu wam’cikwati, bwenzi lanu lapamtima, kapena mkulu mumpingo angakuthandizeni pa nkhawa zanu. Baibo imati: “Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauwelamitsa, koma mau abwino ndi amene amausangalatsa.” (Miy. 12:25) Ngati muululila wina nkhawa zanu mosabisa kanthu angakuthandizeni kumvetsa zinthu ndi kudziŵa mmene mungacitile nazo. Baibo imatiuza kuti: “Zolingalila sizikwanilitsidwa ngati anthu sakambilana moona mtima, koma aphungu akaculuka zimakwanilitsidwa.”—Miy. 15:22.

18 Yehova naye amathandiza Akhiristu kulimbana ndi nkhawa pamisonkhano ya mpingo ya mlungu na mlungu. Kumeneko mumaceza ndi Akhiristu anzanu amene amakudelani nkhawa, ndipo amafuna kulimbikitsana wina na mnzake. (Aheb. 10:24, 25) ‘Kulimbikitsana’ kumeneku kudzakupatsani mphamvu mwauzimu, ndipo mudzakwanitsa kulimbana na nkhawa iliyonse.—Aroma 1:12.

UBALE WANU NA MULUNGU NDICO CITHANDIZO COPOSA ZONSE

19. N’cifukwa ciani mufunika kukhulupilila kuti ubale wanu na Mulungu udzakupatsani mphamvu?

19 Mvelani mmene mkulu wina mumpingo wa ku Canada anaphunzilila kufunika kotulila Yehova nkhawa zake. Iye amagwila nchito yopanikiza kwambili monga mphunzitsi komanso mlangizi. Komanso anali na vuto la maganizo. Kodi anakwanitsa bwanji? Iye anati: “Koposa zonse, naona kuti ubale wanga ndi Yehova umanipatsa mphamvu zolimbana na nkhawa zanga. Thandizo la mabwenzi anga apamtima ndi la abale auzimu, n’lofunika ngako pa nthawi zovuta. Mkazi wanga sinim’bisa nkhawa zanga. Akulu anzanga ndiponso woyang’anila wadela ananithandiza kwambili kuona zinthu moyenela. N’napezanso thandizo ku cipatala, kuyamba kuseŵenzetsa bwino nthawi yanga, ndi kupatula nthawi yopumula na kucita maseŵela olimbitsa thupi. Pang’ono ndi pang’ono nkhawa zanga zinayamba kucepa. Zimene siningakwanitse nimasiyila Yehova.”

20. (a) Tingam’tulile bwanji nkhawa zathu Mulungu? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

20 Mwacidule, taona kuti kutulila Mulungu nkhawa zathu m’pemphelo locokela pansi pa mtima, kuŵelenga Mau ake, ndi kusinkha-sinkha n’zothandiza kwambili. Taphunzilanso ubwino wokulitsa mikhalidwe ya cipatso ca mzimu wa Mulungu, kuuzako wina nkhawa zanu, na kupeza cilimbitso cauzimu ku mpingo. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mmene Yehova amatithandizila potipatsa ciyembekezo ca mphoto.—Aheb. 11:6.