NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA December 2019

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya February 3–March 1, 2020.

“Pali Nthawi” Yogwila Nchito na Nthawi Yopumula

M’nkhani ino, tidzakambilana za Sabata imene Aisiraeli anali kusunga wiki iliyonse. Izi zidzatithandiza kupendanso bwino mmene timaonela nchito na kupumula.

Yehova Wakonza Zakuti Akupatseni Ufulu

Caka ca Ufulu cimene Aisiraeli anali kukondwelela cimatikumbutsa makonzedwe amene Yehova anapanga n’colinga cakuti tikhale pa ufulu.

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

M’nthawi ya Cilamulo, mwamuna akagwilila mtsikana “kuthengo” amene analonjezedwa kukwatiwa ndipo mtsikanayo anakuwa, sanali kukhala na mlandu wa cigololo koma mwamunayo anali kukhala nawo. N’cifukwa ciani?

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Pamene Satana anauza Hava kuti sadzafa akadya cipatso ca mtengo wodziŵitsa cabwino na coipa, kodi anali kuyambitsa ciphunzitso cofala masiku ano cakuti munthu ali na mzimu wosafa?

Kodi Mumam’dziŵa Bwino Yehova?

Kodi kudziŵa Yehova kumatanthauza ciani? Nanga citsanzo ca Mose na Mfumu Davide citiphunzitsa ciani pa nkhani ya mmene tingakhalile pa ubale wolimba na Yehova?

Makolo—Phunzitsani Ana Anu Kukonda Yehova

Kodi makolo angaphunzitse bwanji ana awo kukonda Yehova na kum’tumikila?

“Muziyamika pa Ciliconse”

Pali zifukwa zingapo zoonetsa kuti kukhala na mzimu woyamikila kumatipindulitsa.

Kodi Mukumbukila?

Kodi munaŵelenga na kumvetsetsa mfundo za m’magazini aposacedwa a Nsanja ya Mlonda? Kodi mungakwanitse kuyankha mafunso angati?

Mlongoza Nkhani wa Magazini a 2019 a Nsanja Ya Mlonda na Galamuka!

Mlongoza nkhani wokhala na nkhani zonse za m’magazini a 2019 a Nsanja ya Mlonda na Galamuka! zondandalikidwa potengela mitu.