Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mukumbukila?

Kodi Mukumbukila?

Kodi mungayankhe mafunso aya ocokela m’makope a Nsanja ya Mlonda a 2019?

Kodi lonjezo la Mulungu lakuti: “Cida ciliconse cimene cidzapangidwe kuti cikuvulaze sicidzapambana” limatanthauza ciani? (Yes. 54:17)

Tili na cikhulupililo cakuti Mulungu adzatiteteza kwa “anthu ankhanza” amene amazunza anzawo. (Yes. 25:4,  5) Ndithudi, adani athu sadzakwanitsa kutiwononga kothelatu.—w19.01, peji 6-7.

Kodi mmene Mulungu anali kucitila zinthu na Akanani komanso Aisiraeli amene anasiya kum’lambila zimaonetsa bwanji cilungamo cake?

Mulungu anali kulanga anthu amene anali kucita khalidwe lonyansa laciwelewele kapena kuzunza akazi ndi ana. Koma anali kudalitsa anthu amene anali kumvela malamulo ake na kucitila ena cilungamo.—w19.02, peji 22-23.

Tiyenela kucita ciani ngati munthu amene akupeleka pemphelo ni wosakhulupilila?

Tiyenela kukhala cete komanso kuonetsa ulemu. Koma sitiyenela kukamba mawu akuti “ameni,” kapena kugwilana manja na ena pamene pemphelo likupelekedwa. Tingapeleke pemphelo lathu ca mumtima.—w19.03, peji 31.

Kodi kucitila mwana zolaula ni chimo lalikulu motani?

Kucitila mwana zolaula ni kucimwila mwanayo, mpingo, boma, na Mulungu. Ngati m’dziko muli malamulo ofuna kukanena kupolisi wina akacitila mwana zolaula, akulu amatsatila malamulo amenewo.—w19.05, peji 9-10.

Mungacite ciani kuti musinthe mphamvu yoyendetsa maganizo anu?

Mufunika kucita izi: Kambani na Yehova m’pemphelo. Sinkha-sinkhani na colinga cakuti mudzipende. Sankhani mabwenzi mwanzelu.—w19.06, peji 11.

N’ciani cimene tingacite pali pano kuti tikonzekele cizunzo?

Tifunika kulimbitsa ubwenzi wathu na Yehova. Tisakayikile olo pang’ono kuti amatikonda komanso kuti sadzatisiya. Tiziŵelenga Baibo tsiku lililonse na kupemphela nthawi zonse. Tisamakayikile kuti malonjezo a Ufumu adzakwanilitsidwa. Tiziloŵeza pa mtima malemba na nyimbo zotamanda Yehova zimene timakonda.—w19.07, peji 2-4.

Tingacite ciani kuti tithandize abululu athu kuti akapulumuke?

Tifunika kucita zinthu mowaganizila, kulola khalidwe lathu kuticitila umboni, na kukhala oleza mtima komanso okoma mtima.—w19.08, peji 15-17.

Malinga na lonjezo la Yesu pa Mateyu 11:28, kodi timatsitsimulidwa bwanji?

Tili na oyang’anila acikondi, mabwenzi abwino na nchito yabwino kwambili.—w19.09, peji 23.

Kodi Mulungu angalimbitse bwanji zolakalaka zathu na kutipatsa mphamvu kuti ticite cifunilo cake? (Afil. 2:13)

Pamene tiŵelenga mawu a Mulungu na kuwasinkha-sinkha, Mulungu angalimbitse zolakalaka zathu na kutipatsa mphamvu kuti ticite cifunilo cake. Ndipo mzimu wake ungatithandize kukulitsa maluso amene tili nawo.—w19.10, peji 21.

Ni mfundo ziti zothandiza zimene mungatsatile musanapange cosankha cacikulu?

Mungatsatile mfundo zisanu izi: Fufuzani mokwanila. Pemphani nzelu. Pendani zolinga zanu. Dziikileni zolinga zacindunji. Musadziikile zolinga zimene simungakwanitse.—w19.11, peji 27-29.

Kodi ciphunzitso cakuti munthu ali na mzimu umene sumafa cinacokela pa mawu amene Satana anauza Hava?

Mwacionekele iyai. Satana anauza Hava kuti sadzafa, osati kuti thupi lake lidzafa koma mzimu wake udzapitiliza kukhala na moyo kwinakwake. Panalibe munthu wokhulupilila ciphunzitso conama amene anapulumuka Cigumula. Cikhulupililo cakuti munthu ali na mzimu wosafa ciyenela kuti cinayamba Mulungu asanabalalitse anthu amene anali kumanga nsanja ya Babele.—w19.12, peji 15.