Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 51

Kodi Mumam’dziŵa Bwino Yehova?

Kodi Mumam’dziŵa Bwino Yehova?

“Anthu odziwa dzina lanu adzakukhulupililani, pakuti simudzasiya ndithu anthu okufunafunani, inu Yehova.”​—SAL. 9:10.

NYIMBO 56 Khulupilila Coonadi Iwe Mwini

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Malinga na citsanzo ca m’bale Angelito, kodi aliyense wa ife afunika kucita ciani?

KODI makolo anu ni Mboni za Yehova? Ngati n’telo, mufunika kukumbukila kuti simungakhale pa ubwenzi na Yehova cabe cifukwa cakuti iwo ni Mboni. Kaya makolo athu ni mboni kapena ayi, aliyense wa ife afunika kulimbitsa ubwenzi wake na Yehova.

2 Ganizilani citsanzo ca m’bale Angelito. Iye anakulila m’banja la Mboni. Koma pamene anali wacicepele, sanali pa ubwenzi wolimba na Mulungu. M’bale Angelito anati: “N’nali kutumikila Yehova cabe cifukwa n’nali kufuna kucita zimene banja lathu linali kucita.” Komabe, iye anayamba kupatula nthawi yaikulu yoŵelenga Mawu a Mulungu na kusinkhasinkha pa zimene anali kuŵelenga. Ndiponso anayamba kupemphela kwa Yehova kaŵili-kaŵili. Kodi panakhala zotulukapo zotani? Iye anati: “N’naphunzila kuti njila yokha yokhalila pa ubwenzi wolimba na Atate wathu wacikondi Yehova ni kum’dziŵa bwino ine mwini.” Citsanzo ca m’bale Angelito citipangitsa kuganizila mafunso ofunika awa: Kodi pali kusiyana kotani pakati pa kum’dziŵako Yehova na kum’dziŵa bwino? Nanga tingacite ciani kuti tim’dziŵe bwino?

3. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa kum’dziŵako Yehova na kum’dziŵa bwino?

3 Tingakambe kuti munthu amam’dziŵako Yehova ngati amadziŵa dzina lake kapena zinthu zina zimene anakamba kapenanso kucita. Koma kum’dziŵa bwino Yehova kumaphatikizapo zambili. Tifunika kupatula nthawi yophunzila za iye na makhalidwe ake abwino. Tikacita zimenezi, m’pamene tidzamvetsetsa cimene cimam’sonkhezela kukamba na kucita zinthu. Ndipo izi zidzatithandiza kuzindikila ngati iye amakondwela na zimene timaganiza na kucita. Tikadziŵa zimene Yehova afuna kuti ticite, tiyenela kucita zimenezo.

4. Kodi kukambilana zitsanzo za m’Baibo kudzatithandiza bwanji?

4 Anthu ena angayambe kutinyoza cifukwa cosankha kutumikila Yehova. Ndipo citsutso cingakule kwambili tikayamba kupita ku misonkhano. Koma ngati timadalila Yehova, iye sadzatisiya olo pang’ono. Tidzayala maziko a ubwenzi wolimba na Mulungu, umene udzakhala kwa moyo wathu wonse. Kodi n’zothekadi kum’dziŵa bwino Yehova? Inde, n’zotheka! Citsanzo ca Mose na Mfumu Davide, amene anali opanda ungwilo ngati ife, cionetsa kuti n’zotheka kum’dziŵa bwino Yehova. Pamene tikambilana zimene amuna aŵiliwa anacita, tidzayankha mafunso aŵili awa: N’ciani cinawathandiza kuti am’dziŵe bwino Yehova? Nanga tiphunzilapo ciani pa citsanzo cawo?

MOSE ANAONA “WOSAONEKAYO”

5. Kodi Mose anasankha kucita ciani?

5 Mose anasankha kutumikila Mulungu. Pamene Mose anali na zaka pafupi-fupi 40, anakana kuchedwa “mwana wa mwana wamkazi wa Farao,” koma anasankha kugwilizana ndi anthu a Mulungu, Aisiraeli. (Aheb. 11:24) Mose analolela kusiya umoyo wapamwamba. Iye atasankha kukhala ku mbali ya Aisiraeli, anadziŵa kuti Farao adzakwiya kwambili. Farao anali mfumu yamphamvu kwambili, ndipo Aiguputo anali kumuona monga mulungu. Ndithudi, Mose anali na cikhulupililo colimba kwambili! Iye anadalila Yehova. Kudalila Yehova n’kofunika kwambili kuti munthu akhale pa ubale wolimba na iye.—Miy. 3:5.

6. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Mose?

6 Kodi ife tiphunzilapo ciani? Mofanana na Mose, ni udindo wa munthu aliyense payekha kusankha kutumikila Mulungu na kuyamba kugwilizana ndi anthu ake. Nthawi zina, timafunika kudzimana zinthu zina kuti titumikile Mulungu, ndiponso tingatsutsidwe ndi anthu amene samudziŵa. Koma ngati tikhulupilila Atate wathu wakumwamba, Yehova, tingakhale na cidalilo cakuti iye adzaticilikiza.

7-8. Kodi Mose anapitiliza kuphunzila ciani?

7 Mose anapitiliza kuphunzila za makhalidwe a Yehova na kucita cifunilo cake. Mwacitsanzo, atauzidwa kuti akatulutse Aisiraeli mu ukapolo ku Iguputo, anadzikayikila ndipo anauza Yehova mobweleza-bweleza kuti anali kuona kuti sakanakwanitsa. Mulungu anamuyankha moonetsa kuti ni wacifundo. Anali kumvetsa mmene Mose anali kumvelela, moti anamuthandiza. (Eks. 4:10-16) Pa cifukwa cimeneci, iye anakwanitsa kupeleka uthenga wamphamvu waciweluzo kwa Farao. Ndiyeno, Mose anaona Yehova akuseŵenzetsa mphamvu zake populumutsa Aisiraeli na kuwononga Farao, pamodzi na asilikali ake pa Nyanja Yofiila.—Eks. 14:26-31; Sal. 136:15.

8 Mose atatulutsa Aisiraeli mu Iguputo, iwo anayamba kudandaula mobweleza-bweleza pa zinthu zosiyana-siyana. Olo zinali conco, Mose anaona kuleza mtima kwakukulu kumene Yehova anaonetsa kwa anthu ake amene anawatulutsa mu ukapolo. (Sal. 78:40-43) Mose anaonanso kudzicepetsa kwakukulu kumene Yehova anaonetsa, mwa kulolela kusintha maganizo pamene iye anamupempha kutelo.—Eks. 32:9-14.

9. Malinga na Aheberi 11:27, kodi ubale wa Mose na Yehova unali wolimba motani?

9 Aisiraeli atatuluka mu Iguputo, ubale wa Mose na Yehova unalimba kwambili, cakuti zinali monga kuti Mose anali kumuona Yehova, Atate wake wakumwamba. (Ŵelengani Aheberi 11:27.) Poonetsa ubale wolimba kwambili umene unali pakati pa Mose na Mulungu, Baibo imati: “Yehova anali kulankhula ndi Mose pamasom’pamaso, mmene munthu amalankhulila ndi munthu mnzake.”—Eks. 33:11.

10. Kodi tifunika kucita ciani kuti tim’dziŵe bwino Yehova?

10 Kodi ife tiphunzilapo ciani? Kuti timudziŵe bwino Yehova, tifunika kuphunzila za makhalidwe ake, komanso kucita cifunilo cake. Cifunilo ca Yehova masiku ano n’cakuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa coonadi molondola.” (1 Tim. 2:3, 4) Njila ina imene timacitila cifunilo ca Mulungu ni mwa kuphunzitsa ena za Yehova.

11. Kodi kuphunzitsa ena za Yehova kumatithandiza bwanji kum’dziŵa bwino iye?

11 Nthawi zambili, tikamaphunzitsa ena za Yehova, m’pamene timafika pom’dziŵa bwino iye. Mwacitsanzo, pamene tilalikila, Yehova amatitsogolela kwa anthu a maganizo abwino. Izi zimatithandiza kuona kuti iye ali na cifundo. (Yoh. 6:44; Mac. 13:48) Komanso, timaona mmene mphamvu ya Mawu a Mulungu imagwilila nchito, tikaona anthu amene timaphunzila nawo Baibo akuleka zizoloŵezi zoipa na kuyamba kuvala umunthu watsopano. (Akol. 3:9, 10) Timaonanso kuleza mtima kwa Mulungu tikaganizila mipata yambili imene wapeleka kwa anthu a m’gawo lathu kuti aphunzile za iye kuti akapulumuke.—Aroma 10:13-15.

12. Malinga na Ekisodo 33:13, kodi Mose anapempha ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

12 Mose sanali kuuona mopepuka ubale wake na Yehova. Mwacitsanzo, ngakhale pambuyo pocita nchito zamphamvu mothandizidwa na Mulungu, Mose anapempha Yehova mwaulemu kuti amuthandize kum’dziŵa bwino. (Ŵelengani Ekisodo 33:13.) Mose anali na zaka zoposa 80 pamene anapempha zimenezi. Koma anadziŵa kuti panali zambili zimene anafunika kuphunzila zokhudza Atate wake wacikondi wakumwamba.

13. Ni njila ina iti imene timaonetsela kuti sitiuona mopepuka ubale wathu na Mulungu?

13 Kodi ife tiphunzilapo ciani? Olo kuti tatumikila Yehova kwa nthawi yaitali, sitiyenela kuuona mopepuka ubale wathu na iye. Njila ina imene tingaonetsele kuti sitiuona mopepuka ubale wathu na Mulungu ni mwa kupemphela kwa iye.

14. N’cifukwa ciani tingakambe kuti pemphelo n’lofunika kwambili kuti tim’dziŵe bwino Mulungu?

14 Kuti munthu apange ubwenzi wolimba na winawake, amafunika kukamba naye kaŵili-kaŵili. Mofananamo, kuti mulimbitse ubwenzi wanu na Mulungu, muyenela kupemphela kaŵili-kaŵili kwa iye. Musayope kum’khuthulila za mu mtima mwanu. (Aef. 6:18) Krista, amene akhala ku Turkey anati: “Nthawi zonse pamene nipemphela kwa Yehova na kuona kuti akunithandiza, cikondi na cikhulupililo canga pa iye zimakulila-kulila. Kuona mmene Yehova amayankhila mapemphelo anga kwanithandiza kuti nizimuona monga Atate wanga komanso Bwenzi langa.”

“MUNTHU WAPAMTIMA” KWA YEHOVA

15. Kodi Yehova anakamba kuti Mfumu Davide anali munthu wotani?

15 Mfumu Davide anabadwila mu mtundu umene unali wodzipatulila kwa Yehova Mulungu. Koma iye sanayambe kulambila Yehova cabe cifukwa cakuti anthu a m’banja lake anali kutelo. Davide anayesetsa pa iye yekha kupanga ubwenzi na Mulungu, ndipo Yehova anam’konda kwambili. Yehova anakamba kuti Davide anali “munthu wapamtima [pake].” (Mac. 13:22) Kodi n’ciani cinathandiza Davide kupanga ubale wolimba conco na Yehova?

16. Kodi Davide anaphunzila ciani za Yehova mwa kuyang’ana cilengedwe?

16 Davide anaphunzila za Yehova mwa kuona cilengedwe. Ali wacicepele, nthawi zambili Davide anali kukhala kusanga, kuŵeta nkhosa za atate wake. Mwina pa nthawiyi m’pamene anayamba kusinkha-sinkha pa zinthu zimene Yehova analenga. Mwacitsanzo, Davide akayang’ana kumwamba usiku, anali kuona nyenyezi zambili-mbili. Koma sanali kuona nyenyezi cabe. Anali kuonanso makhalidwe a Mulungu amene anazilenga. Iye analemba kuti: “Zakumwamba zikulengeza ulemelelo wa Mulungu. Ndipo m’mlengalenga mukufotokoza nchito ya manja ake.” (Sal. 19:1, 2) Pamene Davide anaganizila mmene anthu anapangidwila, anazindikila kuti Yehova ni wanzelu kwambili. (Sal. 139:14) Komanso, ataganizila mozama zinthu zimene Yehova analenga, anazindikila kuti iye ni wamng’ono kwambili poyelekezela na Mulungu.—Sal. 139:6.

17. Tidzaphunzila ciani ngati tiganizila zimene Mulungu analenga?

17 Kodi ife tiphunzilapo ciani? Tiyenela kucita cidwi na cilengedwe. Tizipatula nthawi yoganizila zinthu zokongola na zodabwitsa zimene Yehova analenga pa dzikoli. Pa zocita zathu za tsiku na tsiku, tiziganizila zinthu zacilengedwe zimene timaona, monga zomela, nyama, ndi anthu. Tiziganizila zimene tikuphunzilapo ponena za Atate wathu wacikondi, Yehova. Tikatelo, ndiye kuti tsiku lililonse tidzayamba kuphunzila zambili za iye. (Aroma 1:20) Ndipo tsiku na tsiku cikondi cathu pa iye cidzapitiliza kukula.

18. Mogwilizana na Salimo 18, kodi Davide anazindikila ciani?

18 Davide anadziŵa kuti Yehova anali kum’thandiza. Mwacitsanzo, pamene Davide anateteza nkhosa za atate wake kuti zisagwidwe na mkango komanso cimbalangondo, anadziŵa kuti Yehova ndiye anam’thandiza kugonjetsa zilombo zoopsa zimenezo. Pamene anagonjetsa Goliyati, Davide anazindikila kuti Yehova ndiye anali kum’tsogolela. (1 Sam. 17:37) Ndiponso pamene anakwanitsa kuthaŵa Mfumu yansanje Sauli, anazindikila kuti Yehova ndiye anam’pulumutsa. (Sal. 18, tumawu twa pamwamba) Davide akanakhala wodzikweza, sembe anaganiza kuti anakwanitsa yekha kucita zimenezi. Koma iye anali wodzicepetsa. Ndiye cifukwa cake anakwanitsa kuzindikila kuti Yehova anali kum’thandiza mu umoyo wake.—Sal. 138:6.

19. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Davide?

19 Kodi ife tiphunzilapo ciani? Tiphunzilapo kuti tikapempha thandizo kwa Yehova, tifunika kukhala chelu kuti tione ngati watiyankha. Tifunikanso kuzindikila mmene watiyankhila. Ngati ndife odzicepetsa, timadziŵa kuti pali zinthu zina zimene mwa ife tekha sitingakwanitse kucita, ndipo Yehova ndiye amatithandiza kucita zimenezo. Nthawi iliyonse imene taona kuti Yehova watithandiza, ubwenzi wathu na iye umalimbilako. M’bale Isaac wa ku Fiji, amene watumikila Yehova kwa zaka zambili anadzionela yekha kuti zimenezi n’zoona. Iye anati: “Nikaganizila za umoyo wanga, nimaona kuti Yehova wakhala akunithandiza kungocokela pamene n’nayamba kuphunzila Baibo mpaka lelo. Izi zapangitsa kuti nizimuona kukhala bwenzi langa leni-leni.”

20. N’ciani cinathandiza Davide kukhala pa ubwenzi na Yehova? Ndipo tingaphunzilepo ciani pa citsanzo cake?

20 Davide anatengela makhalidwe a Yehova. Yehova anatilenga m’njila yakuti tizikwanitsa kutengela makhalidwe ake. (Gen. 1:26) Tikadziŵa bwino makhalidwe a Yehova, sizikhala zovuta kutengela makhalidwe akewo. Davide anawadziŵa bwino kwambili Atate wake wakumwamba, moti anakwanitsa kutengela citsanzo cawo pocita zinthu ndi anthu. Mwacitsanzo, pa nthawi ina Davide anacimwila Yehova. Iye anacita cigololo na Bati-seba, ndipo pambuyo pake anaphetsa mwamuna wake. (2 Sam. 11:1-4, 15) Koma Yehova anam’citila cifundo, cifukwa nayenso anali kucitila cifundo ena. Popeza kuti Davide anali pa ubale wabwino kwambili na Yehova, Aisiraeli anali kumukonda kwambili, ndipo Yehova anamugwilitsila nchito monga citsanzo kwa mafumu ena a Isiraeli.—1 Maf. 15:11; 2 Maf. 14:1-3.

21. Malinga na Aefeso 4:24 na 5:1, n’ciani cimacitika ngati ‘titsanzila Mulungu’?

21 Kodi ife tiphunzilapo ciani? Tifunika ‘kutsanzila Mulungu.’ Kucita zimenezi kumatipindulitsa ndiponso kumatithandiza kum’dziŵa bwino. Tikamatengela makhalidwe a Mulungu, timaonetsa kuti ndifedi ana ake.—Ŵelengani Aefeso 4:24; 5:1.

YESETSANI KUM’DZIŴA BWINO YEHOVA

22-23. N’ciani cidzacitika ngati tiseŵenzetsa zimene timaphunzila ponena za Yehova?

22 Monga taonela, tingathe kum’dziŵa bwino Yehova mwa kuona cilengedwe komanso kuphunzila Mawu ake, Baibo. M’Baibo muli zitsanzo zambili za atumiki okhulupilika a Mulungu amene tingatengele, monga Mose na Davide. Yehova wacita mbali yake. Ndipo nafenso tifunika kucita mbali yathu mwa kuphunzila za iye mmene tingathele.

23 Kuphunzila za Yehova sikudzatha. (Mlal. 3:11) Cofunika kwambili si kuculuka kwa zimene taphunzila ponena za Mulungu, koma kuseŵenzetsa zimene taphunzilazo. Ngati timacita zimene timaphunzila na kuyesetsa kutengela Atate wathu wacikondi, iye adzapitiliza kutiyandikila. (Yak. 4:8) Kupitila m’Mawu ake, iye amatitsimikizila kuti sadzasiya aliyense amene amamufuna-funa.

NYIMBO 80 ‘Talaŵani, Muone Kuti Yehova ni Wabwino’

^ ndime 5 Anthu ambili amakhulupilila kuti Mulungu aliko, koma sam’dziŵa bwino. Kodi kudziŵa Yehova kumatanthauza ciani? Nanga citsanzo ca Mose na Mfumu Davide citiphunzitsa ciani pa nkhani ya mmene tingakhalile pa ubale wolimba na Yehova? Nkhani ino idzayankha mafunso amenewa.