Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 52

Makolo—Phunzitsani Ana Anu Kukonda Yehova

Makolo—Phunzitsani Ana Anu Kukonda Yehova

“Ana ndi colowa cocokela kwa Yehova.”​—SAL. 127:3.

NYIMBO 134 Ana ni Mphatso Zimene Mulungu Amaikiza kwa Makolo

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi Yehova anawapatsa udindo wotani makolo?

YEHOVA analenga mwamuna na mkazi oyambilila na mtima wofuna kubeleka ana. Mpake kuti Baibo imati: “Ana ndi colowa cocokela kwa Yehova.” (Sal. 127:3) Kodi mawu amenewa atanthauza ciani? Yelekezelani kuti mnzanu wapamtima wakupatsani ndalama zambili-mbili kuti mum’sungile. Kodi mungamvele bwanji? N’zodziŵikilatu kuti mungakondwele podziŵa kuti amakudalilani. Koma mungakhalenso na nkhawa kuti mudzasamalila bwanji ndalamazo kuti zikhale zotetezeka. Yehova, Bwenzi lathu lapamtima, anapatsa makolo udindo wosamalila cinthu cina camtengo wapatali kwambili kuposa ndalama. Anawapatsa udindo wosamalila bwino ana awo kuti azikhala mwacimwemwe.

2. Kodi tidzakambilana mafunso ati?

2 Kodi n’ndani afunika kusankha kuti anthu okwatilana akhale ndi ana kapena ayi, komanso nthawi imene ayenela kukhala nawo? Nanga makolo angacite ciani kuti athandize ana awo kukhala na umoyo wacimwemwe? Onani zina mwa mfundo za m’Baibo zimene zingathandize Akhristu okwatilana kupanga zosankha zanzelu pa nkhaniyi.

LEMEKEZANI COSANKHA CAWO

3. (a) N’ndani afunika kusankha kuti anthu amene aloŵa m’banja akhale ndi ana kapena ayi? (b) Ni mfundo ziti za m’Baibo zimene acibululu na mabwenzi a anthu amene aloŵa m’banja afunika kukumbukila?

3 M’zikhalidwe zina, mwamuna na mkazi akaloŵa m’banja, anthu amawayembekezela kukhala na mwana posapita nthawi. Acibululu ndi anthu ena akhoza kumawakakamiza kutsatila cikhalidwe cimeneci. M’bale wina wa ku Asia, dzina lake Jethro anati: “Mu mpingo mwathu, abale na alongo ena amene ali ndi ana amakakamiza Akhristu amene alibe ana kuti akhale nawo.” M’bale winanso wa ku Asia, dzina lake Jeffrey anati: “Ena amauza anthu amene alibe ana kuti akadzakalamba, adzasoŵa wowasamalila.” Komabe, mwamuna na mkazi afunika kusankha okha kubeleka ana kapena ayi. Ni udindo wawo kupanga cosankha pa nkhaniyi. (Agal. 6:5) N’zoona kuti acibululu na mabwenzi amafuna kuti oloŵa m’banjawo azikhala acimwemwe. Koma tonse tifunika kukumbukila kuti udindo wosankha kubeleka ana kapena ayi ni wa aŵiliwo.—1 Ates. 4:11.

4-5. Ni mafunso aŵili ati amene mwamuna na mkazi afunika kukambilana? Nanga nthawi yabwino yokambilana mafunso amenewo ni iti? Fotokozani.

4 Mwamuna na mkazi amene asankha kubeleka ana ayenela kukambilana mafunso aŵili awa ofunika kwambili: Loyamba, ni liti pamene afuna kudzakhala ndi ana? Laciŵili, afuna kudzakhala ndi ana angati? Kodi nthawi yabwino imene afunika kukambilana mafunso amenewa ni iti? Ndipo n’cifukwa ciani kukambilana mafunsowa n’kofunika kwambili?

5 Nthawi zambili, cimakhala bwino kuti mwamuna na mkazi asanaloŵe m’banja akambilane nkhani ya kubeleka ana. N’cifukwa ciani iyi ndiyo nthawi yabwino? Cifukwa cimodzi n’cakuti kukhala na maganizo amodzi pa nkhani imeneyi n’kofunika kwambili. Cinanso, afunika kukambilana ngati ni okonzekadi kusamalila ana. Anthu ena akaloŵa m’banja, amasankha kuyembekezela kwa caka cimodzi kapena ziŵili asanabeleke mwana. Amacita izi cifukwa amadziŵa kuti akakhala ndi ana, adzayamba kutaila nthawi na mphamvu zoculuka posamalila anawo. Komanso amaona kuti kuyembekezako kwa kanthawi asanakhale ndi ana, kumawapatsa mwayi wojaila umoyo wa m’banja na kulimbitsa mgwilizano wawo.—Aef. 5:33.

6. Popeza tikukhala m’masiku otsiliza, kodi anthu ena amene ali pa banja asankha kucita ciani?

6 Akhristu ena asankha kutengela citsanzo ca ana atatu a Nowa na azikazi awo. Mabanja atatuwa anayamba kubeleka ana patapita nthawi yaitali kucokela pamene anakwatilana. (Gen. 6:18; 9:18, 19; 10:1; 2 Pet. 2:5) Yesu anayelekezela nthawi imene tikukhala na “masiku a Nowa.” Ndipo n’zosacita kufunsa kuti tikukhala mu “nthawi yapadela komanso yovuta.” (Mat. 24:37; 2 Tim. 3:1) Pa cifukwa ici, mabanja ena asankha kuyembekezela kuti papiteko nthawi asanakhale ndi ana, n’colinga cakuti acite zambili potumikila Yehova.

Pamene mwamuna na mkazi akambilana zakuti akhale ndi ana kapena ayi, komanso kuti adzakhale nawo angati, afunika kuŵelengela mtengo wake. Akatelo, amaonetsa kuti ni anzelu. (Onani ndime 7)) *

7. Kodi mfundo za pa Luka 14:28, 29 na pa Miyambo 21:5 zingathandize bwanji anthu amene afuna kuloŵa m’banja?

7 Pamene mwamuna na mkazi akambilana kuti akhale ndi ana kapena ayi, komanso kuti akhale nawo angati, afunika kuŵelengela mtengo wake. (Ŵelengani Luka 14:28, 29.) Makolo amene analelapo ana amadziŵa kuti kulela ana kumafuna ndalama zambili. Kumafunanso mphamvu na nthawi yoculuka. Pa cifukwa ici, mwamuna na mkazi amene afuna kuloŵa m’banja afunika kuganizila mafunso ofunika kwambili awa: ‘Kodi tonse aŵili tidzayamba kuseŵenza kuti tizipeza zofunikila za pa banja? Kodi tili na malingalilo ofanana pa zinthu zimene timaona kuti n’zofunika kwambili pa banja? Ngati tonse tidzayamba kuseŵenza, n’ndani azikasamalila ana? Kodi tifuna kuti anawo akatengele zocita na maganizo a ndani?’ Ngati mwamuna na mkazi akambilana mafunso amenewa mofatsa, ndiye kuti akuseŵenzetsa mfundo ya pa Miyambo 21:5.Ŵelengani.

Mwamuna wacikondi amacita zilizonse zimene angathe pothandiza mkazi wake (Onani ndime 8)

8. Ni zovuta zotani zimene makolo acikhristu ayenela kuyembekezela? Nanga mwamuna wacikondi amacita ciani?

8 Makolo onse aŵili amafunika kutaila nthawi na mphamvu zoculuka posamalila mwana. Conco, ngati iwo abeleka ana pafupi-pafupi, zingakhale zovuta kuti azipeleka cisamalilo cofunikila kwa mwana aliyense. Makolo ena amene anabeleka ana angapo m’nthawi yocepa, amacitila umboni kuti zimakhala zovuta kuwasamalila. Mayi angayambe kukhala wolema kwambili na wopanikizika maganizo. Izi zingapangitse kuti azilephela kucita phunzilo laumwini, kupemphela, na kulalikila mokhazikika. Zingakhalenso zovuta kwa iye kuti azimvetsela pa misonkhano na kupindula nayo. Mwamuna wacikondi ayenela kuyesetsa kuthandiza mkazi wake pamene ana awo afunika cisamalilo ku misonkhano na ku nyumba. Mwacitsanzo, iye angathandize mkazi wake kugwila nchito za pakhomo. Afunikanso kuonetsetsa kuti aliyense m’banjamo akupindula na pulogilamu ya Kulambila kwa Pabanja nthawi zonse. Komanso nthawi na nthawi, mutu wa banja lacikhristu ayenela kumayenda mu ulaliki pamodzi na banja lake.

PHUNZITSANI ANA ANU KUKONDA YEHOVA

9-10. N’ciani cimene makolo afunika kucita kuti athandize ana awo?

9 N’zinthu zina ziti zimene makolo angacite kuti aphunzitse ana awo kukonda Yehova? Nanga angateteze bwanji anawo kuti asatengele makhalidwe oipa? Tiyeni lomba tikambilane zinthu zina zimene makolo angacite.

10 Pemphani thandizo kwa Yehova. Ganizilani citsanzo ca Manowa na mkazi wake, amene anali makolo a Samisoni. Manowa atadziŵa kuti mkazi wake ali na pakati, anacondelela Yehova kuti awapatse malangizo a mmene adzalelela mwana wodzabadwayo.

11. Mogwilizana na Oweruza 13:8, kodi makolo ena anatengela bwanji citsanzo ca Manowa?

11 M’bale Nihad na mkazi wake Alma, amene amakhala ku Bosnia ndi Herzegovina, anatengela citsanzo ca Manowa. Iwo anati: “Mofanana na Manowa, tinacondelela Yehova kuti atipatse malangizo a mmene tingalelele bwino ana athu. Ndipo Yehova anayankha mapemphelo athu m’njila zosiyana-siyana. Anatipatsa malangizo kupitila m’Baibo, m’zofalitsa zathu, m’misonkhano ya mpingo na yacigawo.”—Ŵelengani Oweruza 13:8.

12. Kodi Yosefe na Mariya anapeleka citsanzo cotani kwa ana awo?

12 Phunzitsani ana anu mwa kupeleka citsanzo. Zimene imwe makolo mumakamba pophunzitsa ana anu n’zofunika, koma cimene cimakhudza kwambili anawo ni zocita zanu. N’zosakayikitsa kuti Yosefe na Mariya anapeleka citsanzo cabwino kwambili kwa ana awo, kuphatikizapo Yesu. Yosefe anali kuseŵenza mwakhama kuti asamalile banja lake. Kuwonjezela apo, anali kulimbikitsa a m’banja lake kukonda zinthu zauzimu. (Deut. 4:9, 10) Mwacitsanzo, m’Cilamulo munali malangizo akuti “caka ndi caka” mwamuna aliyense waciisiraeli azipita ku Yerusalemu kukacita mwambo wa Pasika. Olo kuti Cilamulo cinangochula amuna, Yosefe anali kutenga banja lake lonse popita kumeneko. (Luka 2:41, 42) Pa nthawiyo, n’kutheka kuti amuna ena amene anali na mabanja anali kuona kuti kupita ku cikondweleloko na banja lonse kunali kotaitsa nthawi, kovuta, komanso kowonongetsa ndalama. Koma n’zodziŵikilatu kuti Yosefe anali munthu wokonda zinthu zauzimu ndipo anaphunzitsanso ana ake kukonda zinthu zauzimu. Cinanso, Mariya anali kuwadziŵa bwino Malemba. N’zoonekelatu kuti mwa zokamba na zocita zake, anali kuphunzitsa ana ake kukonda Mawu a Mulungu.

13. Kodi m’bale wina na mkazi wake anatengela bwanji citsanzo ca Yosefe na Mariya?

13 M’bale Nihad na mlongo Alma, amene tawachulapo kale m’nkhani ino, anatengelanso citsanzo ca Yosefe na Mariya. Kodi kucita zimenezi kunawathandiza bwanji kuphunzitsa mwana wawo kukonda Mulungu na kuyamba kum’tumikila? Iwo anati: “Mwa zocita zathu, tinayesetsa kuthandiza mwana wathu kuona ubwino wotsatila mfundo za Yehova.” M’bale Nihad anakambanso kuti: “Makolo ayenela kukhala na makhalidwe amene iwo afuna kuti mwana wawo atengele.”

14. N’cifukwa ciani makolo afunika kudziŵa bwino mabwenzi a ana awo?

14 Thandizani ana anu kusankha mabwenzi abwino. Makolo onse aŵili afunika kudziŵa bwino mabwenzi a ana awo komanso zimene anawo amacita. Izi ziphatikizapo kudziŵa mabwenzi amene amaceza nawo pa malo ocezela a pa intaneti na pa foni. Mabwenzi amenewo angasokoneze maganizo a ana anu na khalidwe lawo.—1 Akor. 15:33.

15. Kodi makolo angaphunzilepo ciani pa citsanzo ca m’bale Jessie?

15 Kodi makolo angacite ciani ngati sadziŵa zambili zokhudza makompyuta na mafoni a m’manja? Tate wina, dzina lake Jessie, amene akhala ku Philippines, anati: “Sitinali kudziŵa zambili zokhudza zipangizo zamakono. Koma izi sizinatilepheletse kuthandiza ana athu kudziŵa ngozi imene ingakhalepo pamene aseŵenzetsa zipangizo zimenezi.” Olo kuti m’baleyu sanali kudziŵa moseŵenzetsela zipangizo zamakono, sanawaletse ana ake kuziseŵenzetsa. Iye anakamba kuti: “N’nalimbikitsa ana anga kuti aziseŵenzetsa zipangizo zamakono pophunzila cinenelo cina, kukonzekela misonkhano, na kuŵelenga Baibo tsiku lililonse.” Ngati ndimwe kholo, kodi munakambilanako ndi ana anu nkhani zokhudza kutumizilana mameseji na mapikica? Nkhani zimenezi zipezeka pa jw.org® ku Chichewa, pa mbali yakuti “Achinyamata.” Nanga kodi munatambako na kukambilana ndi ana anu vidiyo yakuti Muzisamala Poceza na Anthu pa Intaneti, na yakuti Kodi Zipangizo Zanu Zimakulamulilani? * Nkhani na mavidiyo amenewa zingakuthandizeni kwambili pamene muphunzitsa ana anu kuseŵenzetsa mwanzelu zipangizo zamakono.—Miy. 13:20.

16. Kodi makolo ambili amacita ciani? Ndipo zotulukapo zake zimakhala zotani?

16 Makolo ambili amayesetsa kupanga makonzedwe akuti ana awo aziceza na Akhristu amene ni zitsanzo zabwino potumikila Mulungu. Mwacitsanzo, m’bale N’Déni wa ku Côte d’Ivoire, na mkazi wake Bomine nthawi zambili anali kuitanila woyang’anila dela kuti akakhaleko nawo ku nyumba kwawo kwa kanthawi. M’baleyu anati: “Izi zinathandiza kwambili kuti mwana wathu apite patsogolo. Iye anayamba upainiya, ndipo pali pano akutumikila monga woyang’anila dela wogwilizila.” Kodi na imwe mungapangile ana anu makonzedwe ngati amenewa?

17-18. Ni liti pamene makolo afunika kuyamba kuphunzitsa ana awo?

17 Muziyamba kuphunzitsa ana akali aang’ono. Ana amakula bwino ngati makolo ayamba kuwaphunzitsa akali aang’ono. (Miy. 22:6) Ganizilani citsanzo ca Timoteyo, amene m’kupita kwa nthawi anayamba kuyenda na mtumwi Paulo. Amayi ake, a Yunike, na ambuye ake aakazi a Loisi anamuphunzitsa malemba oyela ‘kuyambila pamene anali wakhanda.’—2 Tim. 1:5; 3:15.

18 M’bale Jean-Claude na mkazi wake Peace, amene amakhala ku Côte d’Ivoire, anakwanitsa kuphunzitsa ana awo onse 6 kukonda Yehova na kuyamba kum’tumikila. Kodi n’ciani cinawathandiza? Anatengela citsanzo ca Yunike na Loisi. Iwo anati, “Tinali kuyesetsa kukhomeleza Mawu a Mulungu mwa ana athu kuyambila ali akhanda, akangobadwa.”—Deut. 6:6, 7.

19. Kodi kukhomeleza Mawu a Mulungu mwa ana kutanthauza ciani?

19 Kodi ‘kukhomeleza’ Mawu a Yehova mwa ana kutanthauza ciani? ‘Kukhomeleza’ kutanthauza “kuphunzitsa na kugogomeza zinthu mobweleza-bweleza.” Kuti makolo acite izi, amafunika kupatula nthawi yoceza ndi ana awo kaŵili-ŵili. Amafunikanso kupeleka malangizo mobweleza-bweleza kwa anawo, ndipo nthawi zina izi zingakhale zolefula. Koma makolo afunika kuona kuti umenewu ni mwayi wawo wothandiza anawo kumvetsetsa Mawu a Mulungu na kuwaseŵenzetsa.

Makolo afunika kudziŵa mmene angaphunzitsile mwana aliyense payekha (Onani ndime 20)) *

20. Kodi mfundo ya pa Salimo 127:4 igwilizana bwanji na nkhani yolela ana?

20 Khalani ozindikila. Salimo 127 imakamba kuti ana ali ngati mivi. (Ŵelengani Salimo 127:4.) Mivi imakhala ya zitsulo zosiyana-siyana, komanso imasiyana-siyana kukula kwake. Ni mmenenso ana alili. Mwana aliyense ni wosiyana na mnzake. Telo, makolo afunika kudziŵa mmene angaphunzitsile mwana aliyense payekha. Mwamuna wina na mkazi wake m’dziko la Israel, amene anakwanitsa kuthandiza ana awo kuyamba kutumikila Yehova, anafotokoza cimene cinawathandiza. Iwo anati: “Tinali kuphunzila Baibo na mwana aliyense payekha.” Conco, mutu wa banja aliyense angaone ngati n’zofunika kapena n’zotheka kuphunzila ndi ana awo mwanjila imeneyi.

YEHOVA ADZAKUTHANDIZANI

21. Kodi Yehova amawathandiza bwanji makolo?

21 Nthawi zina makolo angalefuke maganizo cifukwa ca zovuta zimene amakumana nazo pophunzitsa ana awo. Koma ayenela kukumbukila kuti ana ni mphatso yocokela kwa Yehova. Ndipo iye ni wokonzeka nthawi zonse kuwathandiza. Komanso ni wofunitsitsa kumvetsela mapemphelo awo. Yehova amayankha mapemphelo amenewo kupitila m’Baibo na m’zofalitsa zathu. Amayankhanso kupitila m’zitsanzo na malangizo ocokela kwa makolo ena ofikapo mwauzimu mu mpingo.

22. Kodi zina mwa zinthu zabwino kwambili zimene makolo angacitile ana awo ni ziti?

22 Anthu ena amakamba kuti kulela ana ni nchito ya zaka 20. Koma zoona zake n’zakuti udindo wokhala kholo sumatha. Ndipo zina mwa zinthu zabwino kwambili zimene makolo angacitile ana awo ni kuwaonetsa cikondi, kuceza nawo, na kuwaphunzitsa mfundo za m’Baibo. Si ana onse amene angalabadile mukawaphunzitsa coonadi. Komabe, ambili amene aleledwa na makolo okonda Yehova, amamvela monga mmene mlongo Joanna Mae, wa ku Asia amamvelela. Iye anati: “Nikaganizila zimene makolo anga ananiphunzitsa, nimayamikila kwambili kuti anali kunilangiza, ndiponso ananiphunzitsa kukonda Yehova. Nimayamikila kuti ananibeleka. Koma koposa pamenepo, nimayamikila kuti ananithandiza kukhala na umoyo waphindu.” (Miy. 23:24, 25) Umu ni mmenenso abale na alongo athu ofika m’mamiliyoni amamvelela.

NYIMBO 59 Tamandani Yehova

^ ndime 5 Kodi anthu akaloŵa m’banja afunika kubeleka ana? Ngati asankha kutelo, kodi ayenela kubeleka ana angati? Nanga angawaphunzitse bwanji kukonda Yehova na kum’tumikila? M’nkhani ino, tidzakambilana zitsanzo zamakono zokhudza nkhaniyi komanso mfundo za m’Baibo zimene zidzatithandiza kuyankha mafunso amenewa.

^ ndime 15 Onaninso buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa—Buku Loyamba, mutu 36, na Buku Laciŵili, mutu 11.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale na mkazi wake akukambilana zakuti akhale ndi ana kapena ayi. Iwo akuganizila cimwemwe cimene angakhale naco ngati angakhale na mwana komanso udindo umene ungakhalepo.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale na mkazi wake akuphunzila ndi ana awo aliyense payekha-payekha, cifukwa cakuti ni osiyana zaka na luso logwila zinthu.