Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Baibo imati payenela kukhala mboni zosacepela ziŵili zotsimikizila colakwa. (Num. 35:30; Deut. 17:6; 19:15; Mat. 18:16; 1 Tim. 5:19) Koma m’nthawi ya Cilamulo, mwamuna akagwilila mtsikana “kuthengo” amene analonjezedwa kukwatiwa ndipo mtsikanayo anakuwa, sanali kukhala na mlandu wa cigololo koma mwamunayo anali kukhala nawo. Popeza panalibe mboni zotsimikizila colakwaco, n’cifukwa ciani mtsikanayo sanali kukhala na mlandu koma mwamunayo?

Colinga cacikulu ca Deuteronomo 22:25-27 si kupeleka umboni wakuti mwamunayo anali wolakwa, cifukwa lembali likamba za mwamuna amene chimo lake latsimikizilika kale. Colinga ca lamulo limeneli ni kutsimikizila mfundo yakuti mtsikanayo sanali wolakwa. Onani zimene mavesi ena m’caputaci amakamba.

Mavesi a pambuyo akamba za mwamuna amene anagona na mtsikana “mumzinda,” amene ni wolonjezedwa kukwatiwa. Mwamunayo anali kukhala na mlandu wa cigololo, cifukwa mtsikana wotelo anali kuonedwa monga wokwatiwa. Nanga bwanji za mtsikanayo? Iye “sanakuwe mumzindawo.” Akanakuwa, sembe anthu anamvela na kubwela kudzamulanditsa. Koma popeza sanakuwe, nayenso anali kukhala na mlandu wa cigololo. Motelo, onse aŵili anali kuweluzidwa kuti anali olakwa.—Deut. 22:23, 24.

Mavesi otsatila m’lembali amafotokoza zocitika zosiyana na zimenezi. Amati: “Koma ngati mwamunayo wapeza mtsikana wolonjezedwa kukwatiwayo kuthengo ndipo wamugwila ndi kugona naye, mwamunayo afe yekha. Mtsikanayo musam’cite ciliconse. Iye sanachite chimo loyenela imfa, cifukwa mlanduwu ukufanana ndi wa munthu amene waukila mnzake ndi kumupha, kucotsa moyo wake. Popeza kuti anam’peza kuthengo, mtsikana wolonjezedwa kukwatiwayo anakuwa, koma panalibe womulanditsa.”—Deut. 22:25-27.

Zaconco zikacitika, oweluza anali kukhulupilila kuti mtsikanayo anakuwadi, “koma panalibe womulanditsa.” Ndiye cifukwa cake mtsikanayo analibe mlandu wa cigololo. Koma mwamunayo anali na mlandu wogwilila mkazi na kucita naye cigololo. Anali kupatsidwa mlandu cifukwa anacita kumugwila mwacikakamizo mtsikana wotomeledwayo “ndi kugona naye.”

Conco, colinga cacikulu ca lamulo limeneli ni kutsimikizila kuti mtsikanayo anali wosalakwa. Ndiye cifukwa cake lembali limangokamba kuti mwamunayo anali na mlandu wa cigololo komanso wogwilila mkazi. Sitikayikila kuti oweluza anali kufufuza mosamala kuti adziŵe zoona pa nkhaniyi, na kupeleka ciweluzo mogwilizana na malangizo osapita m’mbali amene Mulungu anawapatsa mobweleza-bweleza.—Deut. 13:14; 17:4; Eks. 20:14.