Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Muziyamika pa Ciliconse”

“Muziyamika pa Ciliconse”

TONSE tingacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndine munthu woyamikila?’ Baibo inakambilatu kuti m’masiku ano otsiliza, anthu ambili adzakhala“osayamika.” (2 Tim. 3:2) Mwacionekele, munakumanapo ndi anthu amene amafuna kuti ena azingowapatsa kapena kuwacitila zinthu. Iwo saona kufunika koyamikila zimene ena amawapatsa. Mwina na imwe mungavomeleze kuti kukhala ndi anthu otelo sikusangalatsa.

Mosiyana na zimenezi, malemba amatilimbikitsa kuti: “Sonyezani kuti ndinu oyamikila.” Amatilimbikitsanso kukhala ‘oyamika pa ciliconse.’ (Akol. 3:15; 1 Ates. 5:18) Ndipo kukhala na mzimu woyamikila kumatipindulitsa. Motani? Tiyeni tione zifukwa zingapo.

KUKHALA OYAMIKILA KUMATITHANDIZA KUKHALA ACIMWEMWE

Cifukwa cacikulu cokhalila oyamikila nthawi zonse n’cakuti kumatithandiza kukhala acimwemwe. Munthu akakamba mawu oyamikila pa zimene wina wamucitila amakondwela, ndipo nayenso amene wayamikilidwa amasangalala. N’cifukwa ciani onse aŵili amakhala na cimwemwe? Cabwino, kodi mumamvela bwanji ngati munthu wayesetsa kukucitilani zinthu zinazake zabwino? Mwacionekele, mumadziŵa kuti amakukondani komanso amaona kuti ndinu ofunika. Mukazindikila zimenezi, mumakondwela. Mwacionekele, ni mmenenso Rute anamvelela pamene Boazi anam’thandiza moolowa manja. N’zosacita kufunsa kuti Rute anakondwela kwambili kudziŵa kuti Boazi anali kumuona kukhala wofunika.—Rute 2:10-13.

Kukhala woyamikila kwa Mulungu n’kofunika kwambili. Mosakayikila, mumaganizilako zinthu zambili zauzimu na zakuthupi zimene Mulungu anatipatsa komanso zimene akupitiliza kutipatsa. (Deut. 8:17, 18; Mac. 14:17) Koma bwanji osapatula nthawi yoganizila mozama madalitso amene Mulungu akukupatsani imwe na okondedwa anu? Kusinkha-sinkha za kuolowa manja kwa Mlengi wathu, kudzatithandiza kuti tizimuyamikila kwambili. Kudzatithandizanso kuzindikila kuti iye amatikonda kwambili na kutiona kukhala ofunika.—1 Yoh. 4:9.

Kuonjezela pa kuganizila mozama za kuolowa manja kwa Yehova, na madalitso amene watipatsa, tifunikanso kumuyamikila kaamba ka ubwino wake. (Sal. 100:4, 5) Ndipo ena amati: “Kuyamikila ena kumathandiza kwambili kuti munthu akhale wacimwemwe.”

KUKHALA OYAMIKILA KUMALIMBITSA UBWENZI

Cifukwa cina cokhalila oyamikila n’cakuti kumalimbitsa ubwenzi. Tonse timafuna kuti ena azitiyamikila. Mukayamikila wina mocokela pansi pa mtima kaamba ka zabwino zimene wakucitilani, ubwenzi wanu na munthuyo umalimbilako. (Aroma 16:3, 4) Kuonjezela apo, anthu oyamikila amakonda kuthandiza ena. Amaona zabwino zimene ena amawacitila, ndipo izi zimawasonkhezela kuti nawonso azicitila ena zabwino. Inde, kuthandiza ena kumabweletsa cimwemwe, monga mmene Yesu anakambila kuti: “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.”—Mac. 20:35.

Pa nthawi ina, yunivesiti ya California inacita kafuku-fuku pa nkhani ya kuyamikila. Mmodzi wa oyendetsa ameneyo, dzina lake Robert Emmons, anati: “Kuti tikhale oyamikila, tifunika kuzindikila kuti ife anthu timadalilana. Nthawi zina timafuna kuti ena atipatseko zinthu ndipo nthawi zina timafunikilanso kupatsako ena zinthu.” Apa mfundo yake ni yakuti, umoyo wathu umadalila pa ena m’njila zambili. Mwacitsanzo, ena angatipatseko zakudya kapena cithandizo camankhwala. (1 Akor. 12:21) Munthu woyamikila, amathokoza pa zimene ena amamucitila. Popeza zili conco, kodi imwe muli na cizolowezi coyamikila ena pa zimene amakucitilani?

KUKHALA OYAMIKILA KUMAKHUDZA MMENE TIMAONELA ZINTHU MU UMOYO

Cifukwa cinanso cimene tiyenela kukhalila oyamikila n’cakuti kumatithandiza kuti tiziganizila kwambili pa zinthu zolimbikitsa osati pa zolefula. Maganizo athu ali ngati sefa. Nchito ya sefa ni kutithandiza kucotsa zinthu zosafunika ku zinthu zofunika. Mofananamo, maganizo athu amatilola kuika nzelu zathu pa zinthu zolimbikitsa. Pa nthawi imodzi-modziyo, amatithandiza kunyalanyaza zinthu zolefula. Munthu woyamikila amakonda kuganizila pa zabwino, osati pa mavuto. Ndipo ngati munthu ali na mzimu woyamikila kwambili, amakondanso kuganizila kwambili pa zabwino. Izi zimapangitsa kuti apitilize kukhala na mtima woyamikila. Kukhala woyamikila kumatithandiza kutsatila malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Nthawi zonse kondwelani mwa Ambuye.”—Afil. 4:4.

Kukhala woyamikila kumatithandiza kuti tisamakonde kuganizila zinthu zolefula. Mwina mungavomeleze kuti n’capatali munthu woyamikila kucita nsanje, kukhumudwa kapena kukalipa. Cina, kaŵili-kaŵili anthu oyamikila sakhala na mtima wokonda zinthu zakuthupi. Amakhutila na zimene ali nazo ndipo sawononga nthawi na mphamvu zawo zoculuka pofuna-funa zinthu zambili zakuthupi.—Afil. 4:12.

MUZIGANIZILA MADALITSO AMENE MWALANDILA

Ife Akhristu, timadziŵa kuti Satana amafuna kuti tizikhala okhumudwa komanso olefulidwa cifukwa ca mavuto amene timakumana nawo m’masiku otsiliza ano. Amafuna kuti tikhale na khalidwe loipa, lokonda kudandaula. Khalidwe laconco lingapangitse kuti tisakhale alaliki ogwila mtima a uthenga wabwino. Koma khalidwe loyamikila n’logwilizana kwambili na makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umabala. Mwacitsanzo, kukhala woyamikila pa zinthu zabwino zimene Yehova amatipatsa kumatithandiza kukhala acimwemwe komanso kukhala na cikhulupililo pa zimene iye watilonjeza.—Agal. 5:22, 23.

Popeza ndimwe mtumiki wa Yehova, mwina muvomeleza zimene zakambidwa m’nkhani ino ponena za kuyamikila. Ngakhale n’telo, si copepuka kukhala woyamikila na kuona zinthu moyenela nthawi zonse. Koma musalole zimenezi kukulefulani. N’zotheka kukulitsa khalidwe loyamikila. Motani? Muzipatula nthawi tsiku lililonse yoganizila zinthu zabwino mu umoyo wanu zimene mungayamikile. Pamene muyesetsa kucita zimenezi, m’pamenenso cidzakhala cosavuta kukhala woyamikila. Ndipo mudzakhala na cimwemwe coculuka kuposa anthu amene amakonda kuganizila za mavuto amene amakumana nawo. Muziganizila zinthu zabwino zimene Mulungu ndi anthu ena amakucitilani, zimene zimakulimbikitsani ndiponso kukukondweletsani. Mwina mungayambe kulemba zinthu zimenezo. Tsiku lililonse, mungalembe zinthu ziŵili kapena zitatu zimene mwayamikila.

Anthu ena amene acitapo kafuku-fuku pa nkhani ya kuyamikila amakamba kuti, “kukhala na cizoloŵezi coyamikila ena kungasinthe mmene ubongo wathu umagwilila nchito na kuticititsa kukhala acimwemwe.” Munthu woyamikila amakhala wacimwemwe kwambili kuposa wosayamikila. Conco, muziganizila zinthu zonse zabwino zimene mwalandila, muzikondwela na zinthu zabwino zimene zakucitikilani, ndipo khalani woyamikila nthawi zonse. M’malo motenga mopepuka zinthu zabwino zimene Yehova wakupatsani, “yamikani Yehova . . . , cifukwa iye ndi wabwino.” Inde, “muziyamika pa ciliconse.”—1 Mbiri 16:34; 1 Ates. 5:18.