Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 50

Yehova Wakonza Zakuti Akupatseni Ufulu

Yehova Wakonza Zakuti Akupatseni Ufulu

“Muzilengeza ufulu kwa anthu onse okhala m’dzikolo.”​—LEVITIKO 25:10.

NYIMBO 22 Ufumu Ulamulila—Ubwele!

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. (a) Kodi anthu ena amacita cikondwelelo cotani? (Onani kabokosi kakuti “ Kodi Caka ca Ufulu Cinali Caka Cotani?”) (b) Kodi Yesu anakamba za ciani pa Luka 4:16-18?

M’MAIKO ena, anthu amacita cikondwelelo capadela posangalala kuti mfumu yakwanitsa zaka 50 zolamulila. Maphwando amene amacita pa cikondweleloco, angatenge tsiku limodzi, wiki kapena kuposelapo. Koma m’kupita kwa nthawi maphwandowo amatha, ndipo cisangalalo cimene anthuwo anali naco mwamsanga cimaiŵalika.

2 Zaka 50 zikakwana, nawonso Aisiraeli anali kucita cikondwelelo capadela kwa caka conse. Nthawi ya cikondwelelo imeneyo inali kuchedwa Caka ca Ufulu. Caka ca Ufulu cimeneco cinali kuthandiza Aisiraeli kukhala pa ufulu. Koma kodi kukambilana zimenezi kuli na phindu lililonse masiku ano? Inde, cifukwa Caka ca Ufulu cimene Aisiraeli anali kukondwelela cimatikumbutsa za makonzedwe okondweletsa amene Yehova akupanga palipano, n’colinga cakuti tikakhale na ufulu wamuyaya—ufulu umene Yesu anakamba.—Ŵelengani Luka 4:16-18.

M’Caka ca Ufulu, Aisiraeli anali kukondwela cifukwa anthu amene anali akapolo anali kubwelela ku mabanja awo na ku malo awo (Onani ndime 3) *

3. Mogwilizana na Levitiko 25:8-12, kodi Aisiraeli anali kupindula bwanji na makonzedwe a Caka ca Ufulu?

3 Kuti timvetsetse zimene Yesu anatanthauza pokamba za ufulu, coyamba tifunika kukambilana za Caka ca Ufulu cimene Mulungu anauza anthu ake akale kuti azikondwelela. Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Caka ca 50 cizikhala copatulika, ndipo muzilengeza ufulu kwa anthu onse okhala m’dzikolo. Cizikhala Caka ca Ufulu kwa inu, ndipo aliyense wa inu azibwelela kumalo ake ndi kubanja lake.(Ŵelengani Levitiko 25:8-12.) M’nkhani yapita, tinakambilana mmene Aisiraeli anali kupindulila na Sabata ya wiki iliyonse. Nanga iwo anali kupindula bwanji na makonzedwe a Caka ca Ufulu? Tiyelekezele kuti Mwiisiraeli ali na nkhongole yaikulu, ndipo wakakamizika kugulitsa malo ake kuti abweze nkhongoleyo. Caka ca Ufulu cikafika, anali kumubwezela malo ake. Conco, iye anali ‘kubwelela kumalo ake’, ndipo m’kupita kwa nthawi ana ake anali kukhala na mwayi wolandila malowo monga coloŵa cawo. Tiyelekezelenso kuti Mwiisiraeli wina, cifukwa ca kukula kwa umphawi wafika pogulitsa ana ake monga akapolo, ngakhale kudzigulitsa kumene kuti abweze nkhongole. M’Caka ca Ufulu, kapolo aliyense anali kubwelela “kubanja lake.” Conco, palibe munthu amene anali kukhala kapolo kwa moyo wake wonse popanda ciyembekezo comasulidwa. Ndithudi, izi zionetsa kuti Yehova anali kuwaganizila kwambili anthu ake!

4-5. N’cifukwa ciani n’kofunika kwa ife kuphunzila za Caka ca Ufulu cimene Aisiraeli akale anali kukondwelela?

4 Kodi phindu lina la makonzedwe a Caka ca Ufulu linali lotani? Yehova anakamba kuti: “Pakati panu pasapezeke munthu wosauka, cifukwa Yehova adzakudalitsa ndithu m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti likhale colowa cako.” (Deut. 15:4) Izi n’zosiyana kwambili na zimene zikucitika masiku ano. Kaŵili-kaŵili timaona kuti olemela akulemelela-lemelela ndipo osauka akusaukila-saukila.

5 Pokhala Akhristu, sitili pansi pa Cilamulo ca Mose. Izi zitanthauza kuti siticita zimene Aisiraeli akale anali kucita m’Caka ca Ufulu, monga kumasula anthu mu ukapolo, kukhululukila nkhongole, na kubweza malo a coloŵa. (Aroma 7:4; 10:4; Aef. 2:15) Ngakhale n’conco, kuphunzila za Caka ca Ufulu cimeneci n’kofunika kwambili kwa ife. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti makonzedwe amenewa amatikumbutsa zimene Yehova waticitila pofuna kutimasula ku ucimo.

YESU ANALENGEZA KUTI ANTHU ADZAMASULIDWA

6. Kodi ife anthu tifunika kumasulidwa ku ciani?

6 Ife tonse tifunika kumasulidwa ku ukapolo woŵaŵa kwambili wa ucimo. Pokhala anthu ocimwa, timakalamba, kudwala, na kufa. Anthu ambili amaona umboni wakuti ndife akapolo a ucimo, akadziyang’ana pa gilasi kapena akadwala. Ndipo tikacita chimo, timadzimvela cisoni kwambili. Mtumwi Paulo anakamba kuti “cilamulo ca ucimo cimene [cinali m’ziwalo zake]” cinamupanga kukhala kapolo. Anakambanso kuti: “Munthu wovutika ine! Ndani adzandipulumutse ku thupi limene likufa imfa imeneyi?”—Aroma 7:23, 24.

7. Kodi Yesaya analosela ciani za ufulu?

7 Koma cokondweletsa n’cakuti Mulungu anakonza njila yotimasulila ku ucimo kupitila mwa Yesu. M’zaka za m’ma 700 B.C.E, mneneli Yesaya analosela kuti anthu adzakhala pa ufulu waukulu kwambili kuposa ufulu umene Aisiraeli anali kusangalala nawo m’Caka ca Ufulu. Iye analemba kuti: “Mzimu wa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, uli pa ine, pakuti Yehova wandidzoza kuti ndikanene uthenga wabwino kwa anthu ofatsa. Wandituma kuti ndikamange zilonda za anthu osweka mtima, ndikalengeze za ufulu kwa anthu ogwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.” (Yes. 61:1) Kodi ulosi umenewu unali kukamba za ndani?

8. Kodi ulosi wa Yesaya wonena za ufulu na kumasulidwa umakamba za ndani?

8 Ulosi wofunika umenewu wokamba za ufulu unayamba kukwanilitsidwa Yesu atayamba utumiki wake. Tsiku lina Yesu atapita ku sunagoge m’tauni ya kwawo ku Nazareti, anaŵelenga mawu a Yesaya amenewa kwa Ayuda amene anasonkhana kumeneko. Iye anati: “Mzimu wa Yehova uli pa ine, cifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka. Anandituma kudzalalikila za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo, ndi zoti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula opondelezedwa kuti akhale mfulu, ndi kudzalalikila caka covomelezeka kwa Yehova.” Kenako, Yesu anaonetsa kuti mawu amenewa anali kukamba za iye. (Luka 4:16-19) Kodi Yesu anakwanilitsa bwanji ulosi umenewu?

ANTHU AMENE ANALI OYAMBA KUMASULIDWA

Yesu akulengeza za ufulu mu sunagoge ku Nazareti (Onani ndime 8-9)

9. Kodi anthu ambili m’nthawi ya Yesu anali kuyembekezela kumasulidwa ku ciani?

9 Kodi anthu anayamba liti kulandila ufulu wokambidwa mu ulosi wa Yesaya, umenenso Yesu anaŵelenga m’sunagoge? Anayamba kuulandila m’nthawi ya Yesu. Cimene cionetsa zimenezi ni mawu amene Yesu anakamba, akuti: “Lelo lemba ili, limene mwangolimva kumeneli lakwanilitsidwa.” (Luka 4:21) Mwina ambili mwa anthu amene anali kumvetsela pamene Yesu anali kuŵelenga ulosi umenewu, anali kulaka-laka kuti zinthu zisinthe pa ndale. Anali kuyembekezela kumasulidwa ku ulamulilo wa Aroma. N’kutheka kuti anali na maganizo ngati amene amuna aŵili aja anali nawo, akuti: “Tinali kuyembekezela kuti munthu ameneyu ndi amene adzapulumutse Isiraeli.” (Luka 24:13, 21) Koma monga tidziŵila, Yesu sanalimbikitse otsatila ake kupandukila ulamulilo wankhanza wa Aroma. M’malomwake, anawalangiza kuti azipeleka “zinthu za Kaisara kwa Kaisara.” (Mat. 22:21) Nanga Yesu anawamasula bwanji anthu pa nthawi imeneyo?

10. Kodi Yesu anamasula anthu ku ciani?

10 Mwana wa Mulungu anabwela kudzamasula anthu m’njila ziŵili. Yoyamba, Yesu anamasula anthu ku ukapolo wa ziphunzitso zabodza za atsogoleli a cipembedzo. Ayuda ambili pa nthawiyo anali akapolo a miyambo ya anthu na zikhulupililo zabodza. (Mat. 5:31-37; 15:1-11) Anthu amene anali kudziona monga aphunzitsi a Mawu a Mulungu, kweni-kweni anali anthu akhungu mwauzimu. Cifukwa cakuti anthu amenewo anakana Mesiya komanso coonadi cimene anali kuphunzitsa, anakhalabe mu mdima wauzimu, ndipo macimo awo sanakhululukidwe. (Yoh. 9:1, 14-16, 35-41) Koma Yesu anathandiza anthu ofatsa kumasuka ku ziphunzitso zabodza mwa kuwaphunzitsa coonadi na kuwapatsa citsanzo cabwino.—Maliko 1:22; 2:23–3:5.

11. Kodi njila yaciŵili imene Yesu anamasulila anthu ni iti?

11 Njila yaciŵili ni yakuti, Yesu anacititsa kuti zikhale zotheka anthu kumasulidwa ku ukapolo wa ucimo wobadwa nawo. Kupitila mu nsembe ya dipo la Yesu, Mulungu anali kukhululukila macimo anthu amene anakhulupilila dipo na kuonetsa cikhulupililoco mwa zocita zawo. (Aheb. 10:12-18) Yesu anati: “Ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka.” (Yoh. 8:36) Ufulu umenewu unali woposa umene Aisiraeli anali kulandila m’Caka ca Ufulu. Mwacitsanzo, kapolo akamasulidwa m’Caka ca Ufulu, zinali kutheka kudzakhalanso kapolo. Ndipo kaya adzakhalenso kapolo kapena ayi, m’kupita kwa nthawi anali kufa ndithu. Koma ufulu umene Yesu amapeleka sudzatha.

12. N’ndani amene anali oyamba kupindula na ufulu umene Yesu analengeza?

12 Pa Pentekosite wa mu 33 C.E, Yehova anadzoza atumwi na mzimu woyela komanso amuna na akazi ena okhulupilika. Anawasankha kukhala ana ake, n’colinga cakuti m’kupita kwa nthawi akawaukitse kuti akapite kumwamba kukalamulila pamodzi na Yesu. (Aroma 8:2, 15-17) Awa ndiwo anali oyamba kulandila ufulu umene Yesu anakamba m’sunagoge ku Nazareti. Anthu amenewo sanalinso akapolo a ziphunzitso zabodza na miyambo yosagwilizana na Malemba imene atsogoleli a cipembedzo ca Ciyuda anali kuphunzitsa. Komanso, Mulungu amawaona kuti ni omasuka ku ukapolo wa ucimo, umene umabweletsa imfa. Caka ca Ufulu cophiphilitsila cimene cinayamba pamene otsatila a Khristu anadzozedwa mu 33 C.E., cidzatha ku mapeto kwa Ulamulilo wa Yesu wa Zaka 1,000. Kodi ni zinthu ziti zokondweletsa zimene zidzakhala zitacitika podzafika nthawi imeneyo?

ANTHU ENANSO MAMILIYONI ADZAMASULIDWA

13-14. Kuwonjezela pa odzozedwa, n’ndani ena amene akupindula na ufulu umene Yesu anakamba?

13 Masiku ano, pali anthu a maganizo abwino ocokela m’mitundu yonse ofika m’mamiliyoni. Anthu amenewa ni a “nkhosa zina.” (Yoh. 10:16) Iwo sanaitanidwe na Mulungu kuti akalamulile na Yesu kumwamba. Koma Baibo imakamba kuti ali na ciyembekezo codzakhala na moyo wamuyaya pano pa dziko lapansi. Kodi ici ndico ciyembekezo cimene imwe muli naco?

14 Ngati n’telo, na imwe mukupindula na ena mwa madalitso amene odzozedwa akulandila. Mwacitsanzo, cifukwa cokhulupilila nsembe ya magazi a Yesu, mungapemphe Yehova kuti akukhululukileni macimo. Pa cifukwa ici, muli na mwayi wokhala na cikumbumtima coyela komanso ubale wabwino na Mulungu. (Aef. 1:7; Chiv. 7:14, 15) Ganizilaninso za madalitso amene mwapeza cifukwa comasulidwa ku ziphunzitso zabodza zozika mizu. Yesu anati: “Mudzadziwa coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.” (Yoh. 8:32) Ndife okondwa kwambili kuti tili na ufulu umenewo.

15. Kodi ni ufulu na madalitso otani amene tikuyembekezela posacedwapa?

15 Posacedwapa, tidzakhala pa ufulu waukulu. Yesu adzawononga zipembedzo zonse zonama ndiponso ulamulilo woipa wa anthu. Pa nthawiyo, Mulungu adzapulumutsa “khamu lalikulu” la anthu amene amam’tumikila. Ndipo adzawapatsa mwayi wosangalala na madalitso m’paradaiso pano pa dziko lapansi. (Chiv. 7:9, 14) Cina, anthu ambili-mbili adzaukitsidwa, ndipo adzakhala na mwayi womasulidwa ku mavuto onse amene anayamba cifukwa ca ucimo wa Adamu.—Mac. 24:15.

16. Ni ufulu waukulu uti umene anthu adzakhala nawo?

16 Mu Ulamulilo wa Zaka 1,000, Yesu na olamulila anzake adzathandiza anthu kukhala angwilo komanso kukhala pa ubwenzi wabwino kwambili na Mulungu. Iyi idzakhala nthawi yobwezeletsa zinthu na kumasula anthu, monga mmene zinalili m’Caka ca Ufulu m’nthawi ya Aisiraeli. Izi zitanthauza kuti anthu onse amene amatumikila Yehova mokhulupilika adzakhala angwilo, opanda ucimo uliwonse.

M’dziko latsopano, tidzakhala na mwayi wogwila nchito yopindulitsa komanso yokondweletsa. (Onani ndime 17)

17. Malinga na Yesaya 65:21-23, kodi anthu a Mulungu adzakhala na umoyo wotani m’tsogolo? (Onani cithunzi pa cikuto.)

17 Lemba la Yesaya 65:21-23, imafotokoza mmene umoyo udzakhalila m’tsogolo pano pa dziko lapansi. (Ŵelengani.) Anthu ena amaganiza kuti m’paradaiso anthu azikangokhala osagwila nchito. Koma Baibo imaonetsa kuti pa nthawiyo, anthu a Mulungu azikagwila nchito zofunika ndiponso zokhutilitsa. Ulamulilo wa zaka 1,000 ukadzatha, cilengedwe “cidzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala ndi ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu.”—Aroma 8:21.

18. N’cifukwa ciani tili na cidalilo cakuti tidzakhala na umoyo wacimwemwe kutsogolo?

18 Yehova anakonza zakuti Aisiraeli azikhala na nthawi yogwila nchito na yopumula. Ni mmenenso zidzakhalila kwa anthu ake mu Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1,000. N’zodziŵikilatu kuti tidzakhala na nthawi yocita zinthu zauzimu. Kulambila Mulungu n’kofunika kwambili kuti tikhale na cimwemwe masiku ano, ndipo m’dziko latsopano tidzakhalanso na nthawi ya kulambila. Ndithudi, anthu onse okhulupilika adzasangalala na umoyo mu Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1,000, cifukwa tonse tizikatumikila Mulungu na kugwila nchito yokhutilitsa.

NYIMBO 142 Tigwilitsitse Ciyembekezo Cathu

^ ndime 5 Yehova anapanga makonzedwe apadela akuti Aisiraeli azilengeza ufulu m’dziko lawo. Anakonza zakuti iwo azikondwelela Caka ca Ufulu. Ife Akhristu sitili pansi pa Cilamulo ca Mose. Olo n’telo, kuphunzila za Caka ca Ufulu kungatipindulitse. M’nkhani ino, tidzaphunzila za Caka ca Ufulu cimene Aisiraeli anali kukondwelela. Tidzaona mmene cimatikumbutsila za makonzedwe amene Yehova anapanga n’colinga cakuti tikhale pa ufulu. Tidzaonanso mmene timapindulila na makonzedwe amenewo.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: M’Caka ca Ufulu, anthu amene anali ku ukapolo anali kumasulidwa, ndipo anali kubwelela ku mabanja awo na ku malo awo.