Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 49

Akufa Adzauka Ndithu—Sitikaika Konse!

Akufa Adzauka Ndithu—Sitikaika Konse!

“Ine ndili ndi ciyembekezo mwa Mulungu, . . . kuti kudzakhala kuuka.”—MAC. 24:15.

NYIMBO 151 Adzaitana

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Kodi atumiki a Yehova ali na ciyembekezo cabwino cotani?

KUKHALA na ciyembekezo n’kofunika kwambili. Anthu ena ciyembekezo cawo n’cokakhala na cikwati cabwino, kukalela ana athanzi, kapena kucila matenda aakulu. Nafenso Akhristu nthawi zina timayembekezela zimenezi. Koma ciyembekezo cathu cimene timaikilapo mtima kwambili cimaposa zimenezi. Timayembekezela kukhala na moyo kwamuyaya komanso kuti okondedwa athu amene anamwalila adzaukitsidwa.

2 Mtumwi Paulo anakamba kuti: “Ndili ndi ciyembekezo mwa Mulungu, . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Mac. 24:15) Paulo sanali woyamba kukamba za ciyembekezo ca kuuka kwa akufa. Yobu nayenso anakambapo. Iye anali na cidalilo cakuti Mulungu adzam’kumbukila ndipo adzamuukitsa n’kukhalanso na moyo.—Yobu 14:7-10, 12-15.

3. Kodi 1 Akorinto caputa 15 ingatithandize bwanji?

3 “Kuuka kwa akufa” ni mbali ya “maziko,” kapena kuti “ciphunzitso coyambilila,” pa ziphunzitso zonse zacikhristu. (Aheb. 6:1, 2) Paulo anafotokoza za kuuka kwa akufa mu 1 Akorinto caputa 15. Zimene analemba ziyenela kuti zinalimbikitsa Akhristu a m’nthawi ya atumwi. Ndipo caputa imeneyi ingatilimbikitse nafenso. Komanso ingalimbitse ciyembekezo cathu cimene mwina takhala naco kwa nthawi yaitali.

4. Kodi cofunika kwambili n’ciani pa ciyembekezo cakuti okondedwa athu amene anamwalila adzauka?

4 Kuukitsidwa kwa Yesu Khristu n’kofunika kwambili pa ciyembekezo cathu cakuti okondedwa athu amene anamwalila adzaukitsidwa. Imeneyi inali mbali ya “uthenga wabwino” umene Paulo analengeza kwa Akorinto. (1 Akor. 15:1, 2) Ndipo anakamba kuti ngati Mkhristu sanali kukhulupilila kuti akufa adzauka, ndiye kuti cikhulupililo cake cinali copanda pake. (1 Akor. 15:17) Conco, kukhulupilila kuti Yesu anaukitsidwa n’kofunika kwambili pa ciyembekezo cathu ca kuuka kwa akufa.

5-6. Kodi mawu a pa 1 Akorinto 15:3, 4 ali na tanthauzo lanji kwa ife?

5 Pamene Paulo anayamba kufotokoza za kuuka kwa akufa anafotokoza mfundo zitatu izi zosatsutsika: (1) “Khristu anafela macimo athu.” (2) “Anaikidwa m’manda.” (3) “Anaukitsidwa tsiku lacitatu, mogwilizana ndi Malemba.”—Ŵelengani 1 Akorinto 15:3, 4.

6 Kodi imfa ya Yesu, kuikidwa kwake m’manda, komanso kuukitsidwa kwake zili na tanthauzo lanji kwa ife? Mneneli Yesaya analosela kuti Mesiya anali ‘kudzadulidwa m’dziko la amoyo,’ ndipo “manda ake adzakhala limodzi ndi a anthu oipa.” Koma panali kudzacitikanso cinthu cina. Mneneliyo anakambanso kuti Mesiya anali ‘kudzanyamula chimo la anthu ambili.’ Yesu anacita zimenezi mwa kupeleka moyo wake monga dipo. (Yes. 53:8, 9, 12; Mat. 20:28; Aroma 5:8) Conco, imfa ya Yesu, kuikidwa kwake m’manda, na kuukitsidwa kwake, ni maziko olimba a ciyembekezo cathu cakuti tidzamasulidwa ku uchimo na imfa, komanso kuti tidzaonananso na okondedwa athu amene anamwalila.

UMBONI WA ANTHU AMBILI

7-8. N’ciani cimathandiza Akhristu kukhulupilila kuti Yesu anaukitsidwa?

7 Pali kugwilizana pakati pa ciyembekezo cathu cakuti akufa adzauka na kuukitsidwa kwa Yesu. Conco, tiyenela kukhulupilila kuti Yesu anaukitsidwadi. Nanga tingatsimikize bwanji kuti Yehova anamuukitsadi Yesu?

8 Panali mboni zambili zoona na maso zimene zinatsimikizila kuti Yesu anaukitsidwadi. (1 Akor. 15:5-7) Mboni yoyamba imene Paulo anachula anali mtumwi Petulo (Kefa). Kagulu kena ka ophunzila kanatsimikizila kuti Petulo anaona Yesu ataukitsidwa. (Luka 24:33, 34) Kuwonjezela apo, atumwi nawonso anamuona Yesu ataukitsidwa. Ndiyeno Khristu “anaonekelanso kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi,” mwina ku msonkhano wosangalatsa wa ku Galileya wochulidwa pa Mateyu 28:16-20. Yesu ‘anaonekelanso kwa Yakobo,’ amene ayenela kuti anali m’bale wake wa Yesu, amene poyamba sanakhulupilile kuti Yesu anali Mesiya. (Yoh. 7:5) Yakobo ataona kuti Yesu waukitsidwa, anakhulupilila mwa iye. Ndipo cofunika kudziŵa n’cakuti ca m’ma 55 C.E. pamene Paulo anali kulemba kalatayi, mboni zambili zoona na maso zinali zikalipo. Conco, aliyense amene akanakaikila za nkhaniyi akanafunsa mwacindunji mboni zodalilika zimenezo.

9. Malinga na Machitidwe 9:3-5, n’cifukwa ciani tingakambe kuti Paulo anali na umboni wina wotsimikizila kuti Yesu anaukitsidwa?

9 Patapita nthawi, Yesu anaonekelanso kwa Paulo. (1 Akor. 15:8) Pamene Paulo (Saulo) anali paulendo wopita ku Damasiko, anamva mawu a Yesu woukitsidwayo na kumuona m’masomphenya ali mu ulemelelo wakumwamba. (Ŵelengani Machitidwe 9:3-5.) Masomphenya a Paulo amenewa anakhalansoumboni wina wotsimikizila kuti nkhani ya kuuka kwa Yesu ni yeni-yeni osati nthano cabe.—Mac. 26:12-15.

10. Kodi Paulo anacita ciani pambuyo pokhulupilila kuti Yesu anaukitsidwa?

10 Umboni wa Paulo unakhala wamphamvu kwambili kwa ena, cifukwa panthawi ina iye anali kuzunza Akhristu. Atakhulupililadi kuti Yesu anaukitsidwa, Paulo anatumikila molimbika kuti athandize ena kukhulupilila coonadi cimeneci. Iye anapilila zambili monga kumenyedwa, kuponyedwa m’ndende, komanso ngalawa inamuswekela pamene anali kufalitsa coonadi cakuti Yesu anafa koma anaukitsidwa. (1 Akor. 15:9-11; 2 Akor. 11:23-27) Paulo anali na cikhulupililo camphamvu cakuti Yesu anauka kwa akufa moti anali wokonzeka kufa poteteza cikhulupililo cake cimeneci. Kodi umboni wa m’nthawi ya atumwi umenewu, sutithandiza kukhulupilila kuti Yesu anaukadi kwa akufa? Kodi sulimbitsa cikhulupililo canu cakuti akufa adzauka?

KUWONGOLELA MAGANIZO OLAKWIKA

11. N’cifukwa ciani anthu ena ku Korinto anali na maganizo olakwika pa nkhani ya kuuka kwa akufa?

11 Anthu ena mu mzinda wa Korinto ku Girisi anali na maganizo olakwika pa nkhani ya kuuka kwa akufa. Ndipo ena anafika ngakhale pokamba kuti “akufa sadzaukitsidwa.” Cifukwa ciani? (1 Akor. 15:12) Akatswili a nzelu za anthu mu mzinda wa Atene ku Girisi anali kutsutsa mfundo yakuti Yesu anaukitsidwa. Ndipo maganizo amenewa ayenela kuti anakhudzanso Akhristu ena ku Korinto. (Mac. 17:18, 31, 32) Mwina ena anali kuganiza kuti nkhani ya kuuka kwa akufa inali yophiphilitsila cabe—kutanthauza kuti munthu anali ‘wakufa’ mu ucimo, koma n’kukhalanso “wamoyo” monga Mkhristu. Kaya zifukwa zawo zinali zotani, kutsutsa nkhani ya kuuka kwa akufa kunatanthauza kuti cikhulupililo cawo cinali copanda pake. Ngati Mulungu sanaukitse Yesu, ndiye kuti palibe dipo limene linapelekedwa, ndipo onse anakhalabe ocimwa. Conco awo amene anatsutsa za kuuka kwa akufa analibe ciyembekezo ceni-ceni.—1 Akor. 15:13-19; Aheb. 9:12, 14.

12. Mogwilizana na 1 Petulo 3:18, 22, kodi kuuka kwa Yesu kunasiyana bwanji na kuja kwa ena amene anaukitsidwa kumbuyoko?

12 Paulo anali kudziŵa bwino kuti “Khristu anaukitsidwa kwa akufa.” Kuuka kwa Yesu kunali kwapadela cifukwa kunasiyana na kuja kwa anthu ena amene anaukitsidwa kumbuyoko, koma pambuyo pake anamwalilanso. Paulo anati Yesu anali “cipatso coyambilila ca amene akugona mu imfa.” Kodi Yesu anali woyamba m’lingalilo lotani? Anali woyamba kuukitsidwa n’kukhala na moyo monga munthu wamzimu. Analinso munthu woyamba kupita kumwamba.—1 Akor. 15:20; Mac. 26:23; ŵelengani 1 Petulo 3:18, 22.

AMENE “ADZAPATSIDWA MOYO”

13. Kodi Paulo anafotokoza kusiyana kotani pakati pa Adamu na Yesu?

13 Kodi imfa ya munthu mmodzi ikanabweletsa bwanji moyo kwa anthu mamiliyoni? Paulo anapeleka yankho lomveka bwino pa funso limeneli. Anafotokoza kusiyana pakati pa mavuto amene Adamu anabweletsa na zimene zidzatheke cifukwa ca nsembe ya Khristu. Pokamba za Adamu, Paulo analemba kuti: “Imfa inafika kudzela mwa munthu mmodzi.” Adamu atacimwa, anabweletsa mavuto aakulu pa iyemwini komanso pa mbadwa zake. Mpaka pano timavutika na zotulukapo zoŵaŵa za kusamvela kwake. Koma cifukwa cakuti Mulungu anaukitsa Mwana wake, tili na ciyembekezo ca tsogolo labwino. “Kuuka kwa akufa kunafikanso kudzela mwa munthu mmodzi,” Yesu. Paulo anati: “Pakuti monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.”—1 Akor. 15:21, 22.

14. Kodi Adamu adzaukitsidwa? Fotokozani.

14 Kodi Paulo anatanthauzanji pamene anati “mwa Adamu onse akufa”? Paulo anali kukamba za mbadwa za Adamu, zimene zinatengela ucimo na kupanda ungwilo kucokela kwa Adamu, ndipo zimafa. (Aroma 5:12) Adamu sali pagulu la amene “adzapatsidwa moyo.” Dipo la Khristu siliphimbanso macimo a Adamu, cifukwa iye anali munthu wangwilo amene anasankha dala kusamvela Mulungu. Cilango ca Adamu n’cofanana na cimene adzalandila anthu amene “Mwana wa munthu” adzaŵaweluza kuti ni “mbuzi,” kutanthauza kuti ‘adzawonongedwa kothelatu.’—Mat. 25:31-33, 46; Aheb. 5:9.

Yesu ndiye anali woyamba kuukitsidwa kwa akufa na kukakhala na moyo kumwamba (Onani ndime 15-16) *

15. Kodi “onse” amene “adzapatsidwa moyo” ndani?

15 Onani kuti Paulo anati “mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.” (1 Akor. 15:22) Paulo analemba kalata yake kwa Akhristu odzozedwa a ku Korinto, amene anali kudzaukitsidwa kukakhala na moyo kumwamba. Akhristu amenewo ‘anayeletsedwa mwa Khristu Yesu, ndipo anaitanidwa kuti akhale oyela.’ Paulo anakambanso za “anthu amene anagona mu imfa mwa Khristu.” (1 Akor. 1:2; 15:18; 2 Akor. 5:17) M’kalata ina youzilidwa, Paulo analemba kuti awo amene ‘agwilizana na Yesu pokhala ndi imfa yofanana ndi yake, adzagwilizananso naye poukitsidwa mofanana ndi iye.’ (Aroma 6:3-5) Yesu anaukitsidwa na thupi lamzimu ndipo anayenda kumwamba. Conco, zidzakhalanso cimodzi-modzi kwa onse amene ali “mwa Khristu,” kutanthauza Akhristu onse odzozedwa na mzimu.

16. Kodi Paulo anatanthauza ciani pamene anachula Yesu kuti “cipatso coyambilila”?

16 Paulo analemba kuti Khristu anaukitsidwa monga “cipatso coyambilila ca amene akugona mu imfa.” Kumbukilani kuti ena monga Lazaro, anaukitsidwa n’kukhalanso na moyo padziko lapansi. Koma Yesu yekha ndiye anali woyamba kuukitsidwa kwa akufa na thupi lamzimu na kulandila moyo wosatha. Anamuyelekezela na zipatso zoyambilila zimene Aisiraeli anali kupeleka nsembe kwa Mulungu. Kuwonjezela apo, pamene Paulo anachula Yesu kuti “cipatso coyambilila,” anatanthauza kuti ena adzaukitsidwa pambuyo pake kukakhala na moyo wa kumwamba. Atumwi na Akhristu ena odzozedwa anali kudzatsatila Yesu. Iwo anali kudzaukitsidwa mofanana na mmene Yesu anaukitsidwila.

17. Kodi awo amene ali “mwa Khristu” anali kudzalandila liti mphoto yawo kumwamba?

17 Kuuka kopita kumwamba kunali kusanayambe panthawi imene Paulo analembela kalata Akhristu a ku Korinto. Koma Paulo anaonetsa kuti izi zidzacitika kutsogolo. Iye anati: “Aliyense pamalo pake: Coyamba Khristu, amene ndi cipatso coyambilila, kenako ake a Khristu pa nthawi ya kukhalapo kwake.” (1 Akor. 15:23; 1 Ates. 4:15, 16) Masiku ano, tili m’nthawi ya “kukhalapo” kwa Khristu. Atumwi na Akhristu ena odzozedwa na mzimu amene anamwalila, anafunika kuyembekezela nthawi ya kukhalapo kwa Khristu imeneyi kuti akalandile mphoto yawo kumwamba na ‘kugwilizana na Yesu ataukitsidwa mofanana ndi iye.’

TILI NA CIYEMBEKEZO CAKUTI AKUFA ADZAUKA NDITHU!

18. (a) N’cifukwa ciani tingakambe kuti pambuyo pa kuuka kopita kumwamba padzakhalanso kuuka kwina? (b) Kodi 1 Akorinto 15:24-26 ionetsa kuti kumwamba kudzacitika zotani?

18 Nanga bwanji za Akhristu onse okhulupilika amene alibe ciyembekezo cokakhala na Khristu kumwamba? Nawonso ali na ciyembekezo ca kuukitsidwa. Baibo imakamba kuti Paulo na ena amene amapita kumwamba ali “pa kuuka koyambilila kucokela kwa akufa.” (Afil. 3:11) Zimenezi zionetsa kuti padzakhalanso kuuka kwina kumene kudzatsatilapo. Ndipo n’zogwilizana na zimene Yobu anakamba ponena za tsogolo lake. (Yobu 14:15) “Ake a Khristu pa nthawi ya kukhalapo kwake” adzakhala kumwamba pamodzi na Yesu akadzacotsapo maboma onse, ulamulilo wonse komanso mphamvu. Ngakhale “imfa nayonso, monga mdani womalizila, idzawonongedwa.” Mosakaikila, onse amene adzaukitsidwa kukakhala na moyo kumwamba sadzafanso. Koma nanga bwanji za amene adzaukitsidwa kudzakhala na moyo padziko lapansi?—Ŵelengani 1 Akorinto 15:24-26.

19. Kodi awo amene ali na ciyembekezo codzakhala padziko lapansi angayembekezele ciani?

19 Kodi awo amene ali na ciyembekezo codzakhala padziko lapansi angayembekezele ciani? Iwo angakhale na ciyembekezo kucokela pa mawu a Paulo akuti: “Ndili ndi ciyembekezo . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Mac. 24:15) N’zodziŵikilatu kuti munthu wosalungama sangapite kumwamba. Conco mawu amenewa akamba za kuuka kwa akufa kutsogolo pano padziko lapansi.

Kukhulupilila kuti akufa adzauka kumatithandiza kuyang’ana kutsogolo mwacidalilo (Onani ndime 20) *

20. Kodi imwe pamwekha ciyembekezo canu calimbitsidwa motani?

20 Mosakaika konse, “kudzakhala kuuka”! Amene adzaukitsidwa n’kukhala padziko lapansi, adzakhala na ciyembekezo cokhala na moyo kwamuyaya. Muyenela kukhulupilila kuti lonjezo limeneli lidzakwanilitsidwadi. Ciyembekezo cimeneci cingakutonthozeni mukaganizila za okondedwa anu amene anamwalila. Iwo adzaukitsidwa kwa akufa pa nthawi imene Khristu ndi ena “adzalamulila monga mafumu . . . zaka 1,000.” (Chiv. 20:6) Na imwe mungakhale na ciyembekezo komanso cidalilo cakuti ngati mungamwalile zaka cikwi zimenezi zisanayambe, mudzaukitsidwa. “Ciyembekezoco [cimeneci] sicitikhumudwitsa.” (Aroma 5:5) Ciyembekezo cimeneci cingakulimbikitseni palipano komanso kukuwonjezelani cimwemwe potumikila Mulungu. Koma pali zambili zimene tingaphunzile mu 1 Akorinto caputa 15, monga mmene nkhani yotsatila idzafotokozela.

NYIMBO 147 Lonjezo la Moyo Wamuyaya

^ ndime 5 1 Akorinto caputa 15 imakamba za kuuka kwa akufa. N’cifukwa ciani ciphunzitso cimeneci n’cofunika kwa ife, ndipo tingakhale bwanji otsimikiza kuti Yesu anaukitsidwadi? Nkhani ino iyankha mafunso amenewa komanso ena ofunika kwambili okhudza kuuka kwa akufa.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yesu anali woyamba kupita kumwamba. (Mac. 1:9) Ena mwa ophunzila ake amene anali kudzam’tsatila anali Tomasi, Yakobo, Lidiya, Mariya, komanso Paulo.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale anataikilidwa mkazi wake wokondeka amene anatumikila naye kwa nthawi yaitali. Iye ali na cikhulupililo cakuti mkazi wake adzaukitsidwa, ndipo akupitiliza kutumikila Yehova mokhulupilika.