Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mukumbukila?

Kodi Mukumbukila?

Kodi munaŵelenga mosamala magazini a caka cino a Nsanja ya Mlonda? Yesani kuyankha mafunso otsatilawa:

Kodi Akhristu odzozedwa tiyenela kucita nawo zinthu motani?

Timayamikila kukhulupilika kwawo. Komabe, sitiyenela kuwalemekeza mopambanitsa. Timapewanso ‘kutamanda anthu ena.’ (Yuda 16) Tiyenela kupewa kuwafunsa mafunso amene ni aumwini okhudza ciyembekezo cawo.—w20.01, peji 29.

Kodi n’ciani cimakupangitsani kukhulupilila kuti Yehova amakuonani kuti ndinu wofunika?

Baibo imaonetsa kuti Yehova anakudziŵani ngakhale musanabadwe. Ndipo amamvetsela mapemphelo anu. Amadziŵa za mu mtima mwanu komanso zimene mumaganiza, ndipo zimene mumacita zimam’khudza Yehova. (1 Mbiri 28:9; Miy. 27:11) Yehova anakukokelani kwa iye.—w20.02, peji 12.

Kodi ni zitsanzo ziti zotithandiza kudziŵa nthawi yoyenela kukamba komanso nthawi yoyenela kukhala cete?

Timakondwela kukamba za Yehova. Timakamba na munthu amene wayamba kuyenda pa njila yolakwika. Akulu amakamba kuti apeleke uphungu pakafunikila kutelo. Sitiyenela kuulula mmene abale na alongo athu amagwilila nchito yolalikila m’maiko amene nchito yathu ni yoletsedwa. Timapewanso kuulula nkhani zacinsinsi.—w20.03, peji 20-21.

Kodi dzombe lofotokozedwa mu Yoweli caputa 2 limasiyana bwanji na lofotokozedwa mu Chivumbulutso caputa 9?

Yoweli 2:20-29 ikamba kuti Mulungu akucotsa dzombe kapena kuti kulithamangitsa ndipo akulonjeza kubwezela zimene dzombelo linawononga. Pambuyo pake, Mulungu atsanulila mzimu wake pa camoyo ciliconse. Mbali zimenezi zinakwanilitsidwa pamene asilikali a Babulo anaukila Aisiraeli komanso pambuyo pake. Chivumbulutso 9:1-11 ifotokoza za atumiki odzozedwa amene amalengeza uthenga waciweluzo wa Mulungu kwa anthu a m’dziko loipali, ndipo zotulukapo zake n’zakuti anthuwo amazunzika kwambili na uthengawo.—w20.04, peji 3-6.

Kodi mfumu ya kumpoto ndani masiku ano?

Russia na maiko ogwilizana naye. Zocita zawo zakhudza mwacindunji anthu a Mulungu. Analetsa nchito yolalikila, komanso amacita zinthu zoonetsa kuti amazonda Yehova ndi anthu ake. Maiko amenewa akhala akulimbana na mfumu ya kum’mwela.—w20.05, peji 13.

Kodi makhalidwe ochulidwa pa Agalatiya 5:22, 23 ndiwo okha “amene mzimu woyela umatulutsa”?

Ayi. Mzimu woyela umatithandiza kukulitsa makhalidwe ena abwino, monga cilungamo. (Aef. 5:8, 9)—w20.06, peji 17.

Kodi pali ngozi yotani ngati mumakonda kuika zinthu zokhudza inu pa intaneti?

Zimene mungatumize zingapangitse ena kuganiza kuti ndimwe wodzitama osati wodzicepetsa.—w20.07, peji 6-7.

Kodi Akhristu angaphunzile ciani kwa asodzi aluso?

Iwo amapita kukapha nsomba panthawi imene angazipeze komanso kumalo kumene angazipeze. Amadziŵanso moseŵenzetsela zida zoyenelela pogwila nchito yawo. Ndipo amalimba mtima kugwila nchito m’nyengo zosiyana-siyana. Nafenso tingacite cimodzi-modzi pa nchito yathu yolalikila.—w20.09, peji 5.

Kodi tingaŵathandize bwanji maphunzilo athu a Baibo kukulitsa cikondi cawo pa Yehova?

Tingawalimbikitse kumaŵelenga Baibo tsiku lililonse komanso kusinkha-sinkha pa zimene aŵelengazo. Tingawaphunzitsenso kupemphela.—w20.11, peji 4.

Kodi ochulidwa m’mawu awa akuti, “mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo” aphatikizapo ndani?—1 Akor. 15:22.

Paulo sanatanthauze kuti munthu aliyense adzaukitsidwa. Anali kukamba za Akhristu odzozedwa amene ‘anayeletsedwa mwa Khristu Yesu.’ (1 Akor. 1:2; 15:18)—w20.12, peji 5-6.

Kodi Akhristu odzozedwa adzacita ciani ‘akadzasandulika, m’kuphethila kwa diso, pa kulila kwa lipenga lomaliza’?—1 Akor. 15:51-53.

Iwo pamodzi na Khristu adzaŵeta anthu monga abusa ndi ndodo yacitsulo. (Chiv. 2:26, 27)—w20.12, peji 12-13.