Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Miyambo 24:16 imati : “Wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.” Kodi lembali limakamba za munthu amene amagwela m’chimo mobweleza-bweleza koma Mulungu n’kumamukhululukila?

Si zimene vesiyi imatanthauza. M’malomwake, imakamba za munthu amene wagwa m’lingalilo lakuti wakumana na mavuto mobweleza-bweleza, ndipo amadzukanso m’lingalilo lakuti wakwanitsa kuwapilila mavutowo.

Tiyeni tiŵelenge mavesi ena pa lembali. “Usamabisalile munthu wolungama pamalo ake okhala. Usamasakaze malo ake okhala, pakuti wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso. Koma anthu oipa, tsoka lidzawapunthwitsa. Mdani wako akagwa usamasangalale ndipo akapunthwa, mtima wako usamakondwele.”—Miy. 24:15-17.

Ena amaganiza kuti vesi 16 imakamba za munthu amene wacita chimo koma pambuyo pake n’kulapa. Akulu-akulu acipembedzo aŵili a ku Britain analemba kuti: “Aphunzitsi akale komanso a masiku ano amaseŵenzetsa vesiyi” mwa njila imeneyo. Iwo anawonjezelanso kuti “maganizo amenewo angatanthauze kuti munthu wabwino amacita macimo akulu-akulu, koma Mulungu n’kupitilizabe kum’konda, ndipo amadzukanso mwa kulapa akacimwa nthawi zonse.” Maganizo amenewa angaoneke okondweletsa kwa munthu amene amacita macimo koma safuna kuleka kucita macimowo. Iye angamaganize kuti ngakhale atamacita macimo mobweleza-bweleza, Mulungu adzam’khululukila nthawi zonse.

Koma izi si zimene vesi 16 imatanthauza.

Liwu la Cihebeli lotanthauza “kugwa” kapena kuti “akagwa” pa vesi 16 na 17 lingaseŵenzetsedwe m’njila zambili. Lingatanthauze kugwa kweni-kweni. Mwacitsanzo, nyama ingagwe pa msewu, munthu angagwe kucokela padenga, kapena mwala ungagwe pansi. (Deut. 22:4, 8; Amosi 9:9) Mawu amenewa angaseŵenzetsedwenso mophiphilitsa. Mwacitsanzo, Baibo imati: “Yehova walimbitsa mapazi a munthu wamphamvu zake, Ndipo Mulungu amakondwela ndi njila zake. Ngakhale atapunthwa, sadzagwelatu, pakuti Yehova wamugwila dzanja.”—Sal. 37:23, 24; Miy. 11:5; 13:17; 17:20.

Komabe, onani mfundo imene Pulofesa wina dzina lake Edward H. Plumptre anakamba: “Liwu la Cihebeli lomasulidwa kuti [“kugwa”] siligwilitsidwa nchito pokamba za kucita chimo.” Katswili wina wa Baibo anafotokoza vesi 16 mwa njila iyi: “N’kutaya nthawi komanso n’kudzivutitsa kuzunza anthu a Mulungu cifukwa iwo nthawi zonse amapambana, koma anthu oipa satelo.”

Inde, zimenezi zionetsa kuti Miyambo 24:16 siitanthauza kugwela m’chimo, komabe itanthauza kukumana na mavuto ngakhale mobweleza-bweleza. M’dziko loipali, munthu wolungama angadwale kapena kukumana na mavuto ena. Cina, iye angamazunzidwe kwambili na boma cifukwa ca cikhulupililo cake. Ngakhale n’telo, amakhulupilila kuti Mulungu adzam’cilikiza komanso kum’thandiza kupilila na kupambana. Dzifunseni kuti, ‘Kodi si zoona kuti zinthu nthawi zambili zimawayendela bwino atumiki a Mulungu?’ Cifukwa ciani? Cifukwa timakhulupilila kuti “Yehova amacilikiza amene ali pafupi kugwa, ndipo amawelamutsa onse amene awelama cifukwa ca masautso.”—Sal. 41:1-3; 145:14-19.

“Wolungama” sakondwela akaona kuti ena avutika. M’malomwake, amalimbikitsidwa kudziŵa kuti ‘anthu amene amaopa Mulungu woona zidzawayendela bwino, cifukwa cakuti amamuopa.’—Mlal. 8:11-13; Yobu 31:3-6; Sal. 27:5, 6.