Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Kodi mawu a mtumwi Paulo pa 1 Akorinto 15:29 atanthauza kuti Akhristu ena m’nthawi yakale anali kubatizika cifukwa ca akufa?

Ayi. Baibo komanso mbili sizionetsa kuti zimenezi zinali kucitika.

Mmene vesiyi inamasulidwila m’ma Baibo ambili, zapangitsa ena kuganiza kuti m’nthawi ya Paulo anthu anali kucita ubatizo wa m’madzi cifukwa ca akufa. Mwacitsanzo, m’Baibo ya Buku lopatulika vesiyi imati: “Ngati akufa saukitsidwa konse, adzacita ciyani iwo amene abatizidwa cifukwa ca akufa?”

Komabe, onani ndemanga za akatswili a Baibo aŵili. Katswili wina dzina lake Gregory Lockwood anakamba kuti Baibo komanso mbili sizipeleka umboni uliwonse woonetsa kuti anthu anali kubatizika “cifukwa ca ena amene anamwalila.” Mofananamo, katswili winanso dzina lake Gordon D. Fee analemba kuti: “Baibo kapena mbili sizionetsa kuti ubatizo umenewu unali kucitika. Ndipo Cipangano Catsopano sicikambapo ciliconse pankhani imeneyi. Komanso palibe umboni woonetsa kuti Akhristu oyambilila anali kucita ubatizo umenewu, kapena machalichi amene anakhazikitsidwa patapita nthawi yocepa atumwi onse atamwalila.”

Baibo imakamba kuti otsatila a Yesu anafunika ‘kuphunzitsa anthu amitundu yonse, kuwabatiza ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse’ zimene iye anawalamula. (Mat. 28:19, 20) Kuti munthu afike pokhala wophunzila wa Yesu wobatizika, anafunika kuphunzila za iye, kum’khulupilila, komanso kumvela Yehova na Mwana Wake. Conco munthu amene ni wakufa sakanacita zimenezo. Nayenso Mkhristu amene ali na moyo sakanacitila munthu wakufa zimenezo.—Mlal. 9:5, 10; Yoh. 4:1; 1 Akor. 1:14-16.

Kodi Paulo anali kutanthauza ciani pa lembali?

Anthu ena ku Korinto anali kutsutsa zakuti akufa adzauka. (1 Akor. 15:12) Ndipo Paulo anali kutsutsa maganizo amenewo. Anakamba kuti tsiku na tsiku anali kuyang’anizana na imfa. Koma iye anali akali moyo. Ngakhale kuti anakumana na zoopsa, anali na cidalilo cakuti pambuyo pa imfa yake adzaukitsidwa monga colengedwa camphamvu cauzimu, monga mmene Yesu analili.—1 Akor. 15:30-32, 42-44.

Akhristu a ku Korinto anafunika kuzindikila kuti pokhala Akhristu odzozedwa, adzakumana na mayeso tsiku na tsiku na kufa kenako n’kuukitsidwa. ‘Kubatizika mogwilizana ndi Khristu Yesu’ kunaphatikizapo ‘kubatizidwanso mu imfa yake.’ (Aroma 6:3) Ubatizo wawo wophiphilitsila unatanthauza kuti adzakumana na mayeso, komanso adzafa m’lingalilo leni-leni kuti akaukitsidwe kupita kumwamba.

Patapita zaka ziŵili kapena kuposapo kucokela pamene Yesu anabatizidwa m’madzi, anauza atumwi ake aŵili kuti: “Mudzabatizidwadi ndi ubatizo umene ine ndikubatizidwa nawo.” (Maliko 10:38, 39) Apa Yesu sanali kutanthauza kubatizika m’madzi. Iye anatanthauza kuti kukhulupilika kwake kwa Mulungu kudzamutsogolela ku imfa yeni-yeni. Paulo analemba kuti Akhristu odzozedwa ‘adzavutikila pamodzi kuti akalandile ulemelelo pamodzi.’ (Aroma 8:16, 17; 2 Akor. 4:17) Conco, nawonso anayenela kufa na kuukitsidwa kuti akakhale na moyo kumwamba.

Conco, kamasulidwe kolondola ka mawu a Paulo kangakhale kakuti: “Apo ayi, kodi amene akubatizidwa kuti akhale akufa adzatani? Ngati akufa sadzauka, n’cifukwa ciani anthuwo akubatizidwa kuti akhale akufa?”