Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 52

Mmene Tingagonjetsele Zolefula

Mmene Tingagonjetsele Zolefula

“Umutulile Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakucilikiza” —SAL. 55:22.

NYIMBO 33 Tulila Yehova Nkhawa Zako

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi zolefula zingatikhudze bwanji?

TSIKU lililonse timakumana na mavuto ndipo timayesetsa kuwapilila. Kodi simungavomeleze kuti zimakhala zovuta kulimbana na mavuto tikalefuka? Conco, tiyenela kukumbukila kuti zolefula zingatipangitse kudziona wopanda pake, komanso kutilanda cimwemwe. Ndipo Miyambo 24:10 imati: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zocepa.” Inde, zolefula zingatilande mphamvu zofunikila kuti tipilile mavuto paumoyo.

2. Kodi n’zotani zingatilefule, nanga m’nkhani ino tikambilana ciani?

2 Tingalefuke na zinthu zambili. Zina mwa zinthu zimenezi ni zofooka zathu, komanso matenda. Zingaphatikizeponso kusalandila utumiki umene timaulaka-laka m’gulu la Yehova kapena kulalikila m’gawo limene anthu ambili alibe cidwi. M’nkhani ino, tikambilana zina mwa zimene tingacite kuti tilimbane na zolefula.

POLIMBANA NA ZOFOOKA ZATHU

3. Kodi n’ciani cingatithandize kukhala na maganizo oyenela pa zofooka zathu?

3 N’cosavuta kuyamba kuona zofooka zathu mosayenela. Kukhala na kapenyedwe kameneka, kungatipangitse kuganiza kuti cifukwa ca zolakwa zathu, Yehova sangatilandile m’dziko lake latsopano. Kuganiza mwa njila imeneyi kungativulaze. Kodi zofooka zathu tiziziona motani? Baibo imakamba kuti kupatulapo Yesu Khristu, anthu “onse ndi ocimwa.” (Aroma 3:23) Koma Yehova sakhalila kutipeza zifukwa kapena kutiyembekezela kucita zinthu mwangwilo. M’malo mwake, ni Tate wacikondi amene amafuna kutithandiza. Kuwonjezela apo ni woleza mtima. Iye amadziŵa kuti ambili a ife zimativuta kucita zoyenela ndipo izi zimatipangitsa kudziona mosayenela. Koma iye ni wokonzeka kutithandiza.—Aroma 7:18, 19.

Yehova amadziŵa zabwino zimene tinacita kumbuyoku na zimene tikucita palipano (Onani ndime 5) *

4-5. Malinga na 1 Yohane 3:19, 20, kodi n’ciani cinathandiza alongo aŵili kugonjetsa zolefula?

4 Ganizilani citsanzo ca Mlongo Deborah na mlongo Maria. * Ali mwana, mlongo Deborah anali kucitilidwa zinthu zom’cititsa manyazi. Nthawi zambili sanali kuyamikilidwa. Izi zinapangitsa kuti azidziona mosayenela. Akalakwitsa zinthu zing’ono-zing’ono, anali kudziona kuti ni wolephelelatu. Mlongo Maria nayenso anali na vuto limeneli. Acibale ake anali kum’citila zinthu zom’cititsa manyazi. Izi zinapangitsa kuti azivutika na maganizo odziona kukhala wosafunika. Pambuyo pophunzila coonadi, iye anafika ngakhale podziona kukhala wosayenela kuchedwa na dzina la Mulungu.

5 Ngakhale n’telo, alongo aŵiliwa sanaleke kutumikila Yehova. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti anatulila nkhawa zawo Yehova mwa kupemphela mocokela pansi pamtima. (Sal. 55:22) Iwo anazindikila kuti Atate wathu wacikondi wakumwamba amadziŵa zimene tinapitamo mu umoyo wathu, komanso mmene maganizo athu olakwika amatikhudzila. Koma amaonanso zabwino mu mtima mwathu—makhalidwe amene ife eni sitingawaone.—Ŵelengani 1 Yohane 3:19, 20.

6. Kodi munthu angacite ciani ngati wabwelezanso colakwa?

6 Munthu amene akuyesetsa kuthetsa cizolowezi coipa cozika mizu angabwelezenso colakwa cake, ndipo izi zingam’pangitse kudziimba mlandu kwambili. Mwacibadwa, anthufe timadziimba mlandu tikalakwitsa zina zake. (2 Akorinto 7:10) Komabe, sitiyenela kumadziimba mlandu mopitilila malile n’kumaganiza kuti: ‘Ine ndine wolephelelatu Yehova sanganikhululukile ngakhale pang’ono.’ Maganizo ofooketsa amenewa si ogwilizana na coonadi, ndipo angatipangitse kuleka kutumikila Yehova. Kumbukilani kuti Miyambo 24:10 imakamba kuti mphamvu zathu zimacepa tikafooka. Conco, ‘kambilanani’ na Yehova ‘kuti mukhalenso naye paubwenzi’ mwa kumufikila m’pemphelo na kum’pempha kuti akucitileni cifundo. (Yes. 1:18) Ndipo Yehova akaona kuti mwalapadi, adzakukhululukilani. Kuwonjezela apo, fikilani akulu. Iwo moleza mtima adzakuthandizani kucila mwauzimu.—Yak. 5:14, 15.

7. N’cifukwa ciani sitiyenela kulefuka ngati zimativuta kucita coyenela?

7 Ponena za amene akulimbana na cofooka cina cake, M’bale Jean-Luc mkulu ku France anati: “Munthu wolungama pamaso pa Yehova sikuti salakwitsa, koma ni munthu amene amavomeleza zolakwa zake ndipo nthawi zonse amalapa.” (Aroma. 7:21-25) Conco musamadziimbe mlandu mopitilila malile ngati mukulimbana na cofooka cina cake. Kumbukilani kuti palibe aliyense wa ife amene angakhale wolungama pamaso pa Mulungu cifukwa ca nchito zake. Tonsefe timafunikila cisomo ca Mulungu kupitila mu dipo la Yesu.—Aef. 1:7; 1 Yoh. 4:10.

8. Kodi ni kuti kumene tingapeze thandizo tikalefuka?

8 Tingapemphe abale na alongo athu amene ni banja lathu lauzimu kuti atilimbikitse! Iwo angatimvetsele tikafuna kufotokoza nkhawa zathu, ndipo angatilimbikitse. (Miy. 12:25; 1 Ates. 5:14) Mlongo Joy wa ku Nigeria amene anali kuvutika na maganizo olefula anati: “N’kanacita ciani popanda abale na alongo? Cilimbikitso ca abale na alongo anga ni umboni wakuti Yehova amayankha mapemphelo anga. Naphunzilanso kwa iwo mmene ningalimbikitsile ena amene ni olefuka.” Komabe, tiyenela kukumbukila kuti nthawi zina abale na alongo athu sangadziŵe kuti tikufunikila cilimbikitso. Conco, tingafunikile kuyamba ndife kufikila Mkhristu mnzathu wokhwima kuuzimu na kumuuza kuti tikufuna thandizo.

TIKADWALA

9. Kodi malemba a Salimo 41:3 na 94:19 angatilimbikitse bwanji?

9 Tembenukilani kwa Yehova kaamba ka thandizo. Ngati sitimvela bwino, maka-maka ngati tidwala matenda okhalitsa, cingakhale cosavuta kuyamba kuganizila zinthu zolefula. Ngakhale kuti Yehova saticilitsa mozizwitsa masiku ano, angatitonthoze na kutipatsa mphamvu zofunikila kuti tipilile. (Ŵelengani Salimo 41:3; 94:19.) Mwacitsanzo, angalimbikitse Akhristu anzathu kudzatithandizako nchito zina za pakhomo kapena kutigulilako zinthu. Angalimbikitsenso abale athu kupemphela nafe. Kapena angatithandize kukumbukila mfundo zolimbikitsa zopezeka m’Mawu ake. Mwacitsanzo, angatikumbutse za ciyembekezo cathu cabwino ca umoyo wangwilo wopanda matenda, komanso wopanda zowawa m’dziko latsopano.—Aroma 15:4.

10. N’cifukwa ciani m’bale Isang sanakhalebe wosweka mtima pambuyo pa ngozi?

10 M’bale Isang wa ku Nigeria, anapezeka pa ngozi imene inam’pangitsa kuti afe ziwalo. Dokotala anamuuza kuti sadzathanso kuyenda. M’bale Isang anati: “N’nasweka mtima ndipo n’nadzimvela cisoni.” Koma kodi anakhalabe wosweka mtima? Ayi ndithu! Kodi cinam’thandiza n’ciani? Iye anafotokoza kuti: “Ine na mkazi wanga sitinaleke kupemphela kwa Yehova na kuŵelenga Mawu ake. Tinatsimikizanso mtima kuyamikila madalitso athu, kuphatikizapo ciyembekezo cathu ca moyo m’dziko latsopano la Mulungu.”

Ngakhale amene thanzi lawo ni lofooka angatengeko mbali mokwanila mu ulaliki na kukhala na zotulukapo zabwino (Onani ndime 11-13)

11. Kodi mlongo Cindy anapeza bwanji cimwemwe pamene anali kudwala?

11 Mlongo Cindy wa ku Mexico, anam’peza na matenda owopsa. Kodi anapilila bwanji? Pamene anali kulandila cithandizo kucipatala, anadziikila colinga cakuti azilalikila tsiku lililonse. Iye analemba kuti: “Kucita zimenezi kunanithandiza kuika maganizo pa kuthandiza ena m’malo moganizila kwambili za opaleshoni yanga, komanso mmene n’nali kumvelela. Cimene n’nali kucita ni ici: Pokambilana na madokotala kapena manasi n’nali kuwafunsa za mabanja awo. N’nali kuwafunsa cifukwa cake anasankha nchito yovuta ngati imeneyo. Pambuyo pake, cinali kukhala cosavuta kwa ine kuona nkhani imene ingawafike pamtima. Ambili a iwo anakamba kuti si kambili kuti wodwala aziwafunsa kuti, ‘Kodi umoyo uli bwanji?’ Ndipo ambili ananiyamikila cifukwa cowadela nkhawa. Ena anafika ngakhale ponipatsa maadresi awo, komanso ena manambala awo afoni. Conco panthawi yovuta imeneyo mu umoyo wanga, Yehova ananipatsa cimwemwe cacikulu ca mumtima cakuti ngakhale ine n’nacita kudabwa!”—Miy. 15:15.

12-13. Kodi ena amene ni odwala kapena okalamba anakwanitsa bwanji kulalikila? Nanga panakhala zotulukapo zotani?

12 Odwala kapena okalamba angalefuke cifukwa colephela kucita zambili mu ulaliki. Komabe, ambili amakwanitsa kulalikila. Ku America, mlongo wina dzina lake Laurel anasungidwa m’makina omuthandiza kupuma kwa zaka 37! Anali na khansa, ndipo anacitidwa maopaleshoni akulu-akulu, komanso anali na matenda okhalitsa apakhungu. Koma ngakhale mavuto aakulu amenewa sanam’tseke pakamwa. Anali kulalikila manasi, na ena amene anali kubwela ku nyumba kwake. Cotulukapo? Anathandiza anthu 17 kudziŵa coonadi ca m’Baibo! *

13 M’bale Richard mkulu ku France, anapeleka malingalilo othandiza kwa amene sacoka panyumba kapena amene ali m’nyumba zosungila okalamba. Iye anati: “Niona zingakhale bwino kuti aziika zofalitsa zathu poonekela. Izi zimakopa cidwi ca anthu ndipo cimakhala cosavuta kuyambitsa makambilano. Zimenezi zingaŵalimbikitse abale na alongo athu amene sakwanitsanso kuyenda mu ulaliki wa nyumba na nyumba.” Awo amene sacoka panyumba nawonso angatengeko mbali mu ulaliki mwa kulemba makalata komanso kucita ulaliki wa pafoni.

NGATI SITIKULANDILA UTUMIKI UMENE TIMAUFUNA

14. Kodi ni citsanzo cabwino cotani cimene Mfumu Davide anapeleka?

14 Mwina cifukwa ca ukalamba, kufooka kwa thanzi, kapena zifukwa zina, sitingayenelele kupatsidwa utumiki wina wake m’gulu la Yehova. Zikakhala conco, tingaphunzilepo kanthu pa citsanzo ca Mfumu Davide. Iye anali kufunitsitsa kumanga kacisi wa Mulungu. Koma atauzidwa kuti sanasankhidwe kumanga kacisiyo sanakhumudwe, koma anacilikiza na mtima wonse munthu amene Mulungu anam’sankha kugwila nchitoyo. Davide anapeleka zinthu zake mowolowa manja pocilikiza nchitoyo. Iye ni citsanzo cabwino kwambili cimene tiyenela kutengela!—2 Sam. 7:12, 13; 1 Mbiri 29:1, 3-5.

15. Kodi m’bale Hugues anagonjetsa bwanji zolefula?

15 Cifukwa ca matenda m’bale Hugues wa ku France, analeka kutumikila monga mkulu, ndipo anali kulephela kugwila ngakhale nchito zing’ono-zing’ono za pakhomo. Iye analemba kuti: “Poyamba, n’nadziona wacabe-cabe ndipo n’nalefuka kwambili. Koma m’kupita kwa nthawi, n’naona kufunika kovomeleza kuti siningakwanitse kucita zinthu zina. Ndipo n’napeza cimwemwe mwa kutumikila Yehova mmene ningathele. Ndipo natsimikiza mtima kusabwelela m’mbuyo. Gidiyoni komanso amuna 300 amene anali naye anapitiliza kumenya nkhondo ngakhale kuti anali olema. Nanenso nidzapitilizabe kumenya nkhondo!”—Ower. 8:4.

16. Tingaphunzile ciani pa citsanzo ca angelo?

16 Angelo okhulupilika ni citsanzo cabwino kwa ife. Panthawi ya ulamulilo wa Mfumu Ahabu, Yehova anapempha angelo kuti apeleke malingalilo a mmene angapusitsile mfumu yoipa imeneyo. Angelo osiyana-siyana anapeleka malingalilo awo. Koma Mulungu anasankha cabe lingalilo la mngelo mmodzi na kumuuza kuti lingalilo lakelo lidzagwiladi nchito. (1 Maf. 22:19-22) Kodi angelo okhulupilika enawo analefuka, mwina n’kuganiza kuti, ‘N’cifukwa n’ciani n’nadzivutitsa kupelekapo malingalilo anga?’ Palibe cionetsa kuti iwo anacita zimenezi. Angelo ni odzicepetsa kwambili, ndipo amafuna kuti ulemelelo wonse upite kwa Yehova.—Ower. 13:16-18; Chiv. 19:10.

17. Kodi tiyenela kucita ciani tikalefuka cifukwa cakuti sitinapatsidwe mwayi wa utumiki wina wake?

17 Ikani maganizo anu pa mwayi umene tili nawo wochedwa na dzina la Mulungu na kulengeza Ufumu wake. Mwayi wa mautumiki umabwela na kupita, koma si ndiwo umatipangitsa kukhala ofunika kwambili kwa Mulungu. Koma tikakhala odzicepetsa m’pamene timakhala ofunika kwa Yehova komanso kwa abale na alongo athu. Conco, m’condeleleni Yehova kuti akuthandizeni kukhalabe wodzicepetsa. Muzisinkha-sinkha pa zitsanzo zabwino za anthu odzicepetsa ochulidwa m’Mawu ake. Khalani odzipeleka na mtima wonse kutumikila abale anu mulimonse mmene mungathele.—Sal. 138:6; 1 Pet. 5:5.

NGATI ANTHU AMBILI M’GAWO LANU ALIBE CIDWI

18-19. Kodi mungacite ciani kuti muzipeza cimwemwe mu ulaliki ngakhale kuti anthu m’gawo lanu alibe cidwi?

18 Kodi nthawi zina mumalefuka cifukwa cakuti ambili m’gawo lanu alibe cidwi, kapena cifukwa cakuti sapezeka pakhomo? Zikakhala conco, n’ciani cingatithandize kukhalabe acimwemwe kapena kuwonjezela cimwemwe cathu? Mungapeze malingalilo ena othandiza m’bokosi lakuti, “ Zimene Mungacite Kuti Utumiki Wanu Ukhale Wopindulitsa.” Koma tifunikanso kuona utumiki wathu moyenela. Kodi izi zitanthauza ciani?

19 Ikani maganizo anu pa kulengeza dzina la Mulungu na Ufumu wake. Yesu anakamba momveka bwino kuti si ambili amene adzapeza msewu wopita ku moyo. (Mat. 7:13, 14) Tikakhala mu ulaliki, timakhala na mwayi woseŵenza na Yehova, Yesu, komanso angelo. (Mat. 28:19, 20; 1 Akor. 3:9; Chiv. 14:6, 7) Yehova ndiye amakoka anthu kwa iye. (Yoh. 6:44) Conco, ngati munthu sanamvetsele uthenga wathu, mwina adzamvetsela tikadzam’fikila panthawi ina.

20. Kodi Yeremiya 20:8, 9 itiphunzitsa ciani pankhani yogonjetsa zolefula?

20 Tingaphunzile zambili kwa mneneli Yeremiya. Iye anapatsidwa gawo limene linali lovuta kwambili. Anthu anali kum’tukwana komanso kumunyodola “tsiku lonse.” (Ŵelengani Yeremiya 20:8, 9.) Panthawi ina, analefuka kwambili cakuti anafuna kuleka kulalikila. Koma sanatelo. Cifukwa ciani? “Mawu a Yehova” anali monga moto mu mtima mwa Yeremiya, ndipo sakanatha kuusunga! Ni mmenenso zimakhalila kwa ife tikadzadza mtima wathu na maganizo athu na Mawu a Mulungu. Izi zitilimbikitsa kuŵelenga Baibo tsiku lililonse na kusinkha-sinkha mfundo zake. Cotulukapo cake n’cakuti tidzapitilizabe kuwonjezela cimwemwe cathu, ndipo utumiki wathu ungakhale wopindulitsa kwambili.—Yer. 15:16.

21. N’ciani cingatithandize kugonjetsa zolefula mosasamala kaya zikhale zotani?

21 Mlongo Deborah amene tam’chula kumayambililo anati: “Satana amaseŵenzetsa zolefula monga cida camphamvu kuti atifooketse.” Koma Yehova Mulungu ni wamphamvu kuposa cida ciliconse cimene Satana angaseŵenzetse. Conco mukaona kuti mwalefuka pa cifukwa ciliconse, m’condeleleni Yehova kuti akuthandizeni. Iye adzakuthandizani kulimbana na zofooka zanu. Adzakucilikizani pamene mukudwala. Adzakuthandizaninso kukhala na maganizo oyenela pa utumiki umene mungapatsidwe. Cina, adzakuthandizani kuona nchito yolalikila moyenela. Koposa zonse, muzipemphela kwa Atate wanu wakumwamba na kumuuza mmene mumvelela. Na thandizo lake, mungapambane na kugonjetsa zolefula.

NYIMBO 41 Mvelani Pemphelo Langa Conde

^ ndime 5 Tonsefe timalefuka nthawi zina. M’nkhani ino, tikambilana zina mwa zimene tingacite tikalefuka. Monga tionele, na thandizo la Yehova tingakwanitse kugonjetsa zolefula.

^ ndime 4 Maina ena asinthidwa.

^ ndime 12 Ŵelengani zina zokhudza mbili ya mlongo Laurel Nisbet, mu Galamukani! ya October 8, 1993, peji 30 ndime 4, 5.

^ ndime 69 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo amene anali atalefuka kwakanthawi, akukumbukila za utumiki umene anacitapo kumbuyoku, ndipo akupemphela kwa Yehova. Iye akhulupililadi kuti Yehova amadziŵa zimene anacita kumbuyoku komanso zimene akucita palipano.