Kodi Mukukumbukila?
Kodi munaŵelenga mosamala magazini a caka cino a Nsanja ya Mlonda? Yesani kuyankha mafunso otsatilawa:
Kodi Yakobo 5:11, imatitsimikizila ciani ikamakamba kuti Yehova ni “wacikondi cacikulu” komanso “wacifundo”?
Tidziŵa kuti Yehova mwacifundo cake, amafunitsitsa kutikhululukila zolakwa zathu. Yakobo 5: 11 imatitsimikizila kuti iye amafunanso kutithandiza. Nafenso tiyenela kutengela citsanzo cake.—w21.01, tsa. 21.
N’cifukwa ciani Yehova anakhazikitsa dongosolo la umutu?
Anacita izi cifukwa ca cikondi cake. Umutu umapangitsa kuti zinthu zizicitika mwamtendele komanso mwadongosolo m’banja lake. Wa m’banja aliyense amene amacilikiza dongosolo limeneli, amadziŵa woyenela kupanga zigamulo, komanso amene ayenela kukhala patsogolo polabadila zigamulo zimenezo.—w21.02, tsa. 3.
N’cifukwa ciani Akhristu ayenela kukhala osamala poseŵenzetsa njila zotumizilana mauthenga pa intaneti?
Ngati munthu asankha kuseŵenzetsa njila zimenezi, ayenela kukhala wosamala posankha anthu oceza nawo. Kucita izi kungakhale kovuta m’gulu lalikulu lotumizilana mauthenga. (1 Tim. 5:13) Pamakhalanso ngozi yofalitsa nkhani zopanda maumboni, komanso poseŵenzetsa zinthu za gulu pa zamalonda.—w21.03, tsa. 31.
N’cifukwa ciani Mulungu analola Yesu kuvutika na kufa?
Coyamba n’cakuti mwa kupacikidwa pa mtengo, zinakhala zotheka kuti Ayuda amasuke ku tembelelo lawo. (Agal. 3:10, 13) Cifukwa caciŵili n’cakuti Yehova anali kuphunzitsa Yesu kuti akacite bwino udindo wake kutsogolo monga Mkulu wa Ansembe. Ndipo cifukwa cacitatu n’cakuti kukhululupilika kwa Yesu mpaka imfa zinaonetsa kuti n’zotheka anthu kukhalabe okhulupilika akakhala pa mayeso aakulu. (Yobu 1:9-11)—w21.04, mas. 16-17.
Kodi mungacite ciani ngati n’zovuta kupeza anthu mu ulaliki?
Muyenela kumapitako pa nthawi imene iwo angapezeke panyumba. Cina, mungayese kusintha malo olalikilako, kapena mungaseŵenzetse njila zosiyana-siyana zolalikilila, monga kucita ulaliki wa makalata.—w21.05, mas. 15-16.
Kodi mtumwi Paulo anatanthauza ciani pamene anakamba kuti: “Mwa cilamulo, ine ndinafa ku cilamulo”? (Agal. 2:19)
Cilamulo ca Mose cinaonetsa kuti anthu ni ocimwa, ndipo cinatsogolela Aisiraeli kwa Khristu. (Agal. 3:19, 24) Izi zinathandiza Paulo kulandila Khristu. Mwa kutelo, Paulo ‘anafa ku cilamulo’; ndipo sanalinso pansi pa cilamuloco.—w21.06, tsa. 31.
Kodi Yehova wapeleka citsanzo motani kwa ife pa kupilila?
Yehova wapilila kutonzedwa kwa dzina lake, kutsutsidwa kwa ulamulila wake, kupanduka kwa ena mwa ana ake, mabodza a Satana, kuvutika kwa atumiki ake okondeka, kutaikilidwa mabwenzi ake mu imfa, anthu oipa kupondeleza ena, kuwonjezeleka kwa makhalidwe oipa a anthu, komanso kuwonongedwa kwa cilengedwe cake.—w21.07, mas. 9-12.
Kodi Yosefe anapeleka citsanzo cotani pa nkhani yoleza mtima?
Iye anapilila zopanda cilungamo zimene abale anake anam’citila. Izi zinatsogolela kuti iye aimbidwe mlandu wabodza, na kum’ponya m’ndende ku Iguputo kwa zaka zambili.—w21.08, tsa. 12.
Kodi Hagai 2:6-9, 20-22, inalosela za kugwedeka kophiphilitsa kotani?
Mitundu ya anthu imakana uthenga wabwino wa Ufumu, koma anthu ambili aphunzila coonadi. Posacedwa, mitundu ya anthu idzagwedezedwa kothelatu mwa kuwonongedwa.—w21.09, mas. 15-19.
N’cifukwa ciani sitiyenela kuleka kulalikila?
Yehova amaona khama lathu, ndipo amakondwela. Ngati sitileka kulalikila, tidzalandila moyo wosatha.—w21.10, mas. 25-26.
Kodi Levitiko caputala 19, imatithandiza bwanji kutsatila malangizo akuti: “Khalani oyela m’makhalidwe anu onse”? (1 Pet. 1:15)
Vesi imeneyi iyenela kuti inagwila mawu apa Levitiko 19:2. Cuputala 19 imaonetsa mmene tingaseŵenzetsele lemba la 1 Petulo 1:15 mu umoyo wathu.—w21.12, mas. 3-4.