Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Pa Salimo 61:8, Davide analemba kuti iye adzatamanda dzina la Mulungu “mpaka muyaya.” Kodi izi zitanthauza kuti iye anali kuganiza kuti sadzamwalila?

Ayi. Komabe zimene Davide analemba zinali zoona.

Onani zimene anakamba pa lembali, komanso pa malemba ofanana nalo. Iye anati: “Ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu mpaka muyaya, kuti ndikwanilitse malonjezo anga tsiku ndi tsiku.” “Ndikukutamandani inu Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse, ndipo ndidzalemekeza dzina lanu mpaka kalekale.” “Ndidzatamanda dzina lanu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.”—Sal. 61:8; 86:12; 145:1, 2.

Polemba mawu awa, Davide sanali kuganiza kuti sadzamwalila. Iye anali kudziŵa kuti Yehova anali atakamba kuti ucimo udzabweletsa imfa, ndipo Davide anavomeleza kuti iye anali munthu wocimwa. (Gen. 3:3, 17-19; Sal. 51:4, 5) Anali kudziŵa kuti ngakhale anthu okhulupilika, monga Abulahamu, Isaki, na Yakobo, anamwalila. Conco, Davide anali kudziŵa kuti nayenso adzamwalila. (Sal. 37:25; 39:4) Koma mawu ake opezeka pa Salimo 61:8, amaonetsa kuti iye anali na cikhumbo cacikulu cotamanda Mulungu kwamuyaya, kutanthauza kwa moyo wake wonse.—2 Sam. 7:12.

Nthawi zina, Davide anali kulemba zimene anapitamo pa umoyo wake, malinga na tumawu twapamwamba pa Salimo 18, 51, na 52. Pa Salimo 23, Davide anafotokoza Yehova kuti ni m’busa amene anali kum’tsogolela, kumutsitsimutsa, komanso kum’teteza. Nayenso Davide anali m’busa wotelo. Ndipo anali kufuna kutumikila Mulungu ‘masiku onse a moyo wake.’—Sal. 23:6.

Cina, kumbukilani kuti Yehova ndiye anauzila Davide kulemba zonse zimene analemba. Zimene iye analemba zinaphatikizapo maulosi amene anali kudzakwanitsidwa m’tsogolo. Mwacitsanzo, pa Salimo 110 Davide analemba za nthawi pamene Mbuye wake ‘adzakhala kudzanja lamanja [la Mulungu]’ kumwamba, komanso pamene adzalandila mphamvu zoculuka. Kuti acite ciyani? Kuti agonjetse adani a Mulungu, komanso ‘kupeleka ciweluzo pakati pa anthu a mitundu ina’ padziko lapansi. Davide anali kholo la Mesiya. Mesiya ameneyo anali kudzalamulila ali kumwamba, komanso anali kudzakhala “wansembe mpaka kalekale.” (Sal. 110:1-6) Yesu anafotokoza kuti ulosi wa pa Salimo 110 unali kukamba za iye, komanso kuti unali kudzakwanilitsidwa m’tsogolo.—Mat. 22:41-45.

Inde, Davide anauzilidwa kulemba za nthawi yake, komanso nthawi yam’tsogolo pamene iye adzaukitsidwe kuti adzatamande Yehova kwamuyaya. Conco, Salimo 37:10, 11, 29 inakwanilitsidwa kwa Aisiraeli m’nthawi zakale. Komanso, idzakwanilitsidwa m’tsogolo padziko lonse lapansi Mulungu akadzakwanilitsa malonjezo ake.—Onani ndime 8 m’nkhani yakuti, “Udzakhala Ndi Ine m’Paradaiso,” m’magazini ino.

Conco, Salimo 61:8 na malemba ena ofanana nalo, imaonetsa kuti Davide anali kufuna kutamanda Yehova m’nthawi ya Aisiraeli mpaka imfa yake. Ndipo izi zionetselatu zimene iye adzacite m’tsogolo Yehova akadzamuukitsa.