Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 51

Pezani Mtendele pa Nthawi ya Mavuto

Pezani Mtendele pa Nthawi ya Mavuto

“Mitima yanu isavutike kapena kucita mantha.” —YOH. 14:27.

NYIMBO 112 Yehova, Mulungu wa Mtendele

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Kodi “mtendele wa Mulungu” n’ciyani? Nanga timapindula bwanji tikakhala nawo? (Afilipi 4:6, 7)

 PALI mtendele wina wake umene anthu m‘dzikoli saudziŵa. Ni “mtendele wa Mulungu,” umene ndiwo bata limene timakhala nalo mu mtima (kapena kuti kudekha), cifukwa cokhala pa ubale wamtengo wapatali na Atate wathu wakumwamba. Tikakhala na mtendele wa Mulungu, timamva kukhala otetezeka. (Ŵelengani Afilipi 4:6, 7.) Cina, timapeza mabwenzi abwino okonda Mulungu. Komanso, timakhala pa ubale wabwino na “Mulungu wamtendele.” (1 Ates. 5:23) Tikafika pom’dziŵa bwino Atate wathu wakumwamba, kumukhulupilila, na kumumvela, mtendele wa Mulungu udzaika mtima wathu m’malo tikakumana na vuto lothetsa nzelu.

2. N’cifukwa ciyani tingakambe kuti n’zothekadi kukhala na mtendele wa Mulungu?

2 Kodi n’zothekadi kukhalabe na mtendele wa Mulungu pokumana na mavuto, monga mlili wa matenda, matsoka azacilengedwe, ziwawa, kapena tikamazunzidwa? Mavuto ngati amenewa angatipatse mantha. Komabe, Yesu analangiza otsatila ake kuti: “Mitima yanu isavutike kapena kucita mantha.” (Yoh. 14:27) N’zokondweletsa kuti abale na alongo akutsatila langizo la Yesu limeneli. Ndipo na thandizo la Yehova, iwo amapeza mtendele ngakhale atakhala pa mavuto aakulu.

MMENE TINGAPEZELE MTENDELE PANTHAWI YA MLILI

3. Kodi mlili ungatilande bwanji mtendele?

3 Mlili ungasinthe kwambili umoyo wathu. Tangoganizilani mmene COVID-19 yakhudzila anthu ambili. Pa kafukufuku wina, anati anthu opitilila hafu padziko lonse anali kuvutika kugona panthawi ya mliliwu. Ndipo mlili umenewu unawonjezela nkhawa kwa anthu ambili, komanso kupsinjika maganizo, kumwa moŵa mwaucidakwa, kuseŵenzetsa mankhwala osokoneza bongo, nkhanza m’mabanja, na kufuna kudzipha. Ngati m’dela limene mukhala munabuka matenda, kodi mungacite ciyani kuti mucepetse nkhawa zanu, komanso kuti mupeze mtendele wa Mulungu?

4. Kodi kudziŵa ulosi wa Yesu wokamba za masiku otsiliza kumatithandiza bwanji kukhala na mtendele?

4 Yesu analosela kuti m’masiku otsiliza, kudzakhala milili, kapena kuti kufalikila kwa matenda “m’malo osiyana-siyana.” (Luka 21:11) Kodi kudziŵa izi kumatithandiza bwanji kukhala na mtendele? Ife sitidabwa pakabuka matenda, cifukwa tikudziŵa kuti zikukwanilitsa mawu a Yesu. Conco, tili na cifukwa cabwino comvela langizo la Yesu kwa anthu okhala m’nthawi ya mapeto. Iye anati: “Izitu zisadzakucititseni mantha.”—Mat. 24:6.

Kumvetsela kuŵelengedwa kwa Baibo kungakuthandizeni kukhala na mtendele wa mumtima panthawi ya mlili (Onani ndime 5)

5. (a) Malinga na Afilipi 4:8, 9, kodi tiyenela kupemphelela ciyani pakabuka matenda? (b) Kodi kumvetsela kuŵelengedwa kwa Baibo kojambulidwa kungakupindulileni bwanji?

5 Pakabuka matenda, n’cosavuta kukhala na nkhawa yaikulu na kucita mantha. Izi n’zimene zinacitika kwa mlongo wina dzina lake Desi. b Amalume ake, msuweni wake, na dokotala wake atafa na COVID-19, anada nkhawa kuti nayenso angayambukidwe na kalombo kameneko n’kupatsila amayi ake okalamba. Cifukwa ca mliliwu, anadanso nkhawa kuti mwina nchito ingathe, ndiye n’kumavutika kugula cakudya na kulipila lendi. Nkhawa zimenezo zinayamba kum’culukila moti zinali kum’soŵetsa tulo. Koma mlongo Desi anaupezanso mtendele wa mumtima. Motani? Anali kupemphela kwa Yehova na kumuuza kuti am’thandize kukhala wodekha, komanso kuti aziona zinthu moyenela. (Ŵelengani Afilipi 4:8, 9.) Iye anali kumvetsela pamene Yehova anali “kukamba” naye kupitila m’kuŵelengedwa kwa Baibo kojambulidwa. Iye anati: “Mawu odekha a woŵelenga Baiboyo anakhazika pansi mtima wanga, ndipo ananikumbutsa kuti Yehova amasamala za ine.”—Sal. 94:19.

6. Kodi phunzilo la inu mwini na misonkhano ya mpingo ingakuthandizeni bwanji?

6 Panthawi ya mlili, cimakhala covuta kucita zinthu zimene tinali kucita kale. Koma musalole kuti mliliwo usokoneze phunzilo la inu mwini na kupezeka ku msonkhano. Zocitika zenizeni za anthu ena zopezeka m’zofalitsa zathu na mavidiyo, zidzakukumbutsani kuti abale na alongo auzimu akhalabe okhulupilika ngakhale kuti akukumana na mavuto. (1 Pet. 5:9) Nayonso misonkhano idzakuthandizani kudzaza maganizo anu na mfundo zolimbikitsa za m’Malemba. Cina, idzakupatsani mipata yakuti mulimbikitse ena, komanso kuti inunso mulimbikitsidwe. (Aroma 1:11, 12) Mukamaganizila mmene Yehova anathandizila atumiki ake pamene anali kudwala, kucita mantha, kapena kukhala osungulumwa, cikhulupililo canu cidzalimba, ndipo mudzakhala na cidalilo cakuti inunso adzakuthandizani.

7. Kodi muphunzilapo ciyani pa citsanzo ca mtumwi Yohane?

7 Yesetsani kuti muzikambilanako nawo abale na alongo. Matenda akabuka, mwina tingafunike kukhala motalikilana pamene tili na Akhristu anzathu. Pa nthawi ngati imeneyi, tingamve monga mmene mtumwi Yohane anamvela. Iye anali kufunitsitsa kuona mnzake Gayo pamaso-m’pamaso. (3 Yoh. 13, 14) Komabe, Yohane anadziŵa kuti panthawiyo kunali kosatheka kukamuona mnzakeyo. Conco, anacita zimene akanatha, anamulembela kalata Gayo. Ngati n’zosatheka palipano kukacezela abale na alongo, kambani nawo pafoni, pa vidiyo, kapena alembeleni uthenga. Mukamalankhula na Akhristu anzanu, simudzamva kuti muli nokha-nokha, komanso mudzakhala na mtendele. Mukakhala na nkhawa auzeni akulu, ndipo landilani cilimbikitso cawo.—Yes. 32:1, 2.

MMENE TINGAPEZELE MTENDELE PAKAGWA TSOKA LA ZACILENGEDWE

8. Kodi matsoka a zacilengedwe angasokoneze bwanji mtendele wanu?

8 Ngati munakhuzidwapo na kusefukila kwa madzi, civomezi, kapena moto, nkhawa yaikulu imene munali mwina inatenga nthawi yaitali kuti ithe. Ngati munafeledwa munthu amene m’makonda, kapena ngati munataikilidwa katundu, munali na cisoni, munasoŵa mtengo wogwila, kapena munakhumudwa. Izi sizitanthauza kuti mumakonda cuma kapena mulibe cikhulupililo ayi. Munakumana na mayeso aakulu, ndipo ena angayembekezele kuti mukhumudwa nawo mayesowo. (Yobu 1:11) Ngakhale kuti muli m’mikhalidwe yovuta, n’zotheka kuupeza mtendele. Motani?

9. Kodi Yesu anatikonzekeletsa motani ku matsoka a zacilengedwe?

9 Kumbukilani zimene Yesu analosela. Anthu ena m’dzikoli amaganiza kuti sadzakhudzidwapo na matsoka a zacilengedwe. Koma ife tidziŵa kuti m’nthawi yathu ino padzacitika matsoka ambili, ndipo ena a iwo akhoza kutikhudza. Yesu anauza otsatila ake kuti “zivomezi zamphamvu” komanso matsoka ena acilengedwe adzacitika mapeto asanafike. (Luka 21:11) Analoselanso kuti kudzakhala “kuwonjezeka kwa kusamvela malamulo,” ndipo upandu, ciwawa, komanso za ucigaŵenga ni umboni wa zimenezi. (Mat. 24:12) Yesu sanakambe kuti mavuto amenewa adzagwela anthu okhawo amene Yehova waakana. Atumiki ambili a Yehova okhulupilika akumanapo na matsoka. (Yes. 57:1; 2 Akor. 11:25) Yehova sangatiteteze mozizwitsa ku matsoka onse. Koma adzatipatsa zofunikila kuti tikhale na mtendele wa mumtima komanso bata.

10. N’cifukwa ciyani kukonzekela palipano matsoka a zacilengedwe sikutanthauza kuti tilibe cikhulupililo? (Miyambo 22:3)

10 Tikamakonzekela matsoka a zacilengedwe pasadakhale, tizitha kukhalabe osatekeseka matsokawo akacitika. Koma kodi tikakonzekela zitanthauza kuti tilibe cikhulupililo mwa Yehova? Ayi. Kukonzekela matsoka a zacilengedwe kumaonetsa kuti tili na cidalilo mwa iye cakuti adzatisamalila. Motani? Mawu a Mulungu amatilangiza kuti tizikonzekela matsoka. (Ŵelengani Miyambo 22:3.) Ndipo pogwilitsa nchito nkhani za m’magazini athu, za pa misonkhano ya mpingo, na zilengezo za panthawi yake, gulu la Mulungu limatilimbikitsa mobweleza-bweleza kukonzekela zakugwa mwadzidzidzi. c Kodi Yehova timam’khulupilila? Ngati n’telo, tidzatsatila malangizowo palipano, matsoka asanacitike.

Kukonzekela pasadakhale kungakuthandizeni kupulumuka tsoka (Onani ndime 11) d

11. Kodi muphunzilapo ciyani pa citsanzo ca mlongo Margaret?

11 Onani citsanzo ici ca mlongo wina dzina lake Margaret. Iye anauzidwa kuti acoke m’dela lakwawo cifukwa munabuka cimoto calupsa. Popeza anthu ambili anali kuthaŵa panthawi imodzi, kunali mpanipani wa mamotoka moti kunali kovuta kuyendetsa. Kunali ciutsi cakuda bii, moti mlongo Margaret sakanatha kuyendetsa motoka yake. Komabe, iye anapulumuka cifukwa cokonzekela pasadakhale. Iye anali na mapu m’kacikwama kake yoonetsa msewu wina umene akanatenga pothaŵa tsokalo. Msewu umenewo unali woti anadutsamo kale. Conco, unam’thandiza ngako pa zakugwa mwadzidzidzi. Cifukwa cokonzekela pasadakhale, mlongo Margaret anapulumuka tsokalo.

12. N’cifukwa ciyani tiyenela kutsatila malangizo otithandiza kukhala otetezeka?

12 Pofuna kutiteteza, boma lingatipemphe kutsatila malangizo amene laika, monga kucoka m’dela lathu, kapena kucita zinthu zina zothandiza. Ena amacedwa kumvela malangizo otelo kapena amazengeleza kuwatsatila cifukwa safuna kusiya katundu wawo. Kodi Akhristu ayenela kucita motani? Baibo imatiuza kuti: “Cifukwa ca Ambuye, gonjelani dongosolo lililonse lopangidwa ndi anthu: kaya mfumu cifukwa ili ndi udindo waukulu, kapena nduna cifukwa n’zotumidwa ndi mfumuyo.” (1 Pet. 2:13, 14) Nalonso gulu la Mulungu limatipatsa malangizo kuti tikhale otetezeka. Timakumbutsidwa nthawi zonse kuti tizipatsa akulu manambala a foni amene tikuseŵenzetsa palipano, kuti akatitumile pakadzagwa za mwadzidzidzi. Kodi inu munacita zimenezi? Tingalandilenso malangizo okhudza kumene tingathaŵile, mopezela zinthu zofunikila, kapena mmene tingathandizile ena, na nthawi imene tingawathandizile. Tikapanda kumvela, tingaike moyo wathu komanso wa akulu pa ciwopsezo. Kumbukilani kuti amuna okhulupilika amenewa amayang’anila miyoyo yathu. (Aheb. 13:17) Mlongo Margaret anati: “Kukamba zoona, kutsatila malangizo a akulu komanso a gulu lathu n’kumene kunanipulumutsa.”

13. N’ciyani cathandiza Akhristu amene anasiya zinthu zawo kukhala na cimwemwe komanso mtendele?

13 Abale na alongo ambili amene anasiya zinthu zawo cifukwa ca matsoka a zacilengedwe, nkhondo, kapena ciwawa, ayesetsa kuzolowela umoyo watsopano, ndipo apitiliza kucita zauzimu kumalo awo atsopano. Mofanana na Akristu oyambilila amene anabalalika cifukwa ca cizunzo, iwo akupitiliza ‘kulengeza uthenga wabwino wa mawu opatulika.’ (Mac. 8:4) Kulalikila kumawathandiza kuika maganizo awo pa Ufumu wa Mulungu, osati pa mikhalidwe yawo yovuta. Zotulukapo n’zakuti iwo sanataye cimwemwe cawo ngakhale mtendele.

MMENE TINGAPEZELE MTENDELE POZUNZIDWA

14. Kodi cizunzo cingatilande motani mtendele wathu?

14 Cizunzo cingatilande zinthu zambili zimene zimatithandiza kukhala na mtendele. Timakondwela kukumana pamodzi, kulalikila mwaufulu, komanso kucita zinthu za masiku onse popanda kuopa kuti atimanga. Tikalandidwa ufulu umenewu, tingakhale na nkhawa posadziŵa kuti citicitikile n’ciyani. N’cibadwa kumva conco. Ngakhale n’telo, tiyenela kukhala osamala. Yesu anaonetsa kuti n’capafupi otsatila ake kupunthwa pa cikhulupililo akamazunzidwa. (Yoh. 16:1, 2) Conco, kodi tingacite ciyani kuti tikhalebe na mtendele pamene tikuzunzidwa?

15. N’cifukwa ciyani sitiyenela kuopa cizunzo? (Yohane 15:20; 16:33)

15 Mawu a Mulungu amati: “Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipeleka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.” (2 Tim. 3:12) M’bale wina dzina lake Andrei cinamuvuta kuvomeleza mfundoyi pamene nchito yathu inatsekedwa m’dziko lawo. Iye anali kuganiza motele: ‘Kuno kuli Mboni zoculuka. Boma silingacite kutimanga tonse.’ Maganizo amenewa sanam’bweletsele mtendele m’bale Andrei, m’malo mwake anangomuwonjezela nkhawa. Abale ena anangosiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova, ndipo sanayesepo kuganiza kuti sangamangidwe. Anadziŵa kuti akhoza kumangidwa, koma nkhawa yawo inali yocepa kuposa ya m’bale Andrei. Conco, iye anaganiza zotengela citsanzo ca abalewo, ndipo anaika cidalilo cake conse mwa Mulungu. Posakhalitsa, anaupeza mtendele, ndipo tsopano ni wacimwemwe ngakhale kuti amakumanabe na mavuto. Nafenso n’zotheka kuupeza mtendele. N’zoona kuti Yesu anatiuza kuti tidzazunzidwa. Koma anatitsimikizilanso kuti n’zotheka kukhalabe okhulupilika.—Ŵelengani Yohane 15:20; 16:33.

16. Ni citsogozo ca ndani cimene tiyenela kutsatila pamene tikuzunzidwa?

16 Nchito yathu ikatsekedwa kapena kuikilidwa ziletso, tingalandile malangizo kucokela ku ofesi ya nthambi komanso kwa akulu. Malangizowo colinga cake ni kutiteteza, kuonetsetsa kuti tikulandilabe cakudya cauzimu, komanso kutithandiza kupitiliza kulalikila mmene tingathele. Muziyesetsa kumvela malangizo amene mumalandila, ngakhale pamene simunamvetse cifukwa cake apelekedwa. (Yak. 3:17) Cina, conde osaulula nkhani zokhudza abale na alongo athu, kapena zokhudza mpingo kwa anthu amene safunikila kuzidziŵa.—Mlal. 3:7.

N’ciyani cingakuthandizeni kukhala na mtendele wa mumtima pa nthawi zovuta? (Onani ndime 17) e

17. Potengela atumwi a m’zaka za zana loyamba, kodi ndife ofunitsitsa kucita ciyani?

17 Cimodzi mwa zifukwa zazikulu zimene Satana amacitila nkhondo na anthu a Mulungu, n’cakuti iwo ali na “nchito yocitila umboni za Yesu.” (Chiv. 12:17) Musalole kuti Satana na dziko lake akuopseni. Kulalikila na kuphunzitsa ngakhale kuti tikuzunzidwa kumatibweletsela cimwemwe na mtendele. M’zaka za zana loyamba, pamene olamulila aciyuda analamula atumwi kuti aleke kulalikila, amuna okhulupilila amenewo anasankha kumvela Mulungu. Iwo sanaleke kulalikila, ndipo nchitoyo inawabweletsela cimwemwe. (Mac. 5:27-29, 41, 42) N’zoona kuti nchito yathu ikaikilidwa ziletso, tiyenela kulalikila mocenjela. (Mat. 10:16) Koma ngati ticita zonse zotheka, tidzakhala na mtendele umene umabwela cifukwa cokondweletsa Yehova, komanso cifukwa couzako ena uthenga wopulumutsa moyo.

“MULUNGU WAMTENDELE ADZAKHALA NANU”

18. Kodi tiyenela kukumbukila kuti ndani ali Gwelo la mtendele umene timaufuna?

18 Khalani na cidalilo kuti ngakhale panthawi zovuta kwambili, n’zotheka kukhala na mtendele wa mumtima. Pa nthawi zimenezo, tizikumbukila kuti mtendele umene timafunikila ni mtendele wa Mulungu, umene ni Yehova yekha angatipatse. Conco, mudalileni pamene kwabuka matenda, kwacitika matsoka a zacilengedwe, kapena pamene mukuzunzidwa. Mamatilani gulu lake. Ndipo pitilizani kuyembekezela mwacidwi tsogolo labwino limene wakusungilani. Mukatelo, “Mulungu wamtendele adzakhala nanu.” (Afil. 4:9) M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mmene tingathandizile Akhristu anzathu amene akuzunzidwa kupeza mtendele wa Mulungu.

NYIMBO 38 Adzakulimbitsa

a Yehova analonjeza kuti anthu amene amam’konda adzawapatsa mtendele. Kodi mtendele umene Mulungu amatipatsa n’ciyani? Nanga tingaupeze bwanji? Kodi kukhala na “mtendele wa Mulungu” kungatithandize bwanji pakabuka matenda, pakacitika matsoka azacilengedwe, kapena tikamazunzidwa? Nkhani ino iyankha mafunso menewa.

b Maina ena asinthidwa.

c Onani nkhani yakuti, “Zimene Tingachite Kuti Tipulumuke Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi.” Nkhaniyi ili mu Galamukani! ya Na. 5 2017.

d MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo anakonzekela pasadakhale kucoka m’dela lawo.

e MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale amene akukhala m’dziko limene nchito yathu inaikilidwa ziletso, akulalikila mocenjela.