Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 50

“Udzakhala Ndi Ine m’Paradaiso”

“Udzakhala Ndi Ine m’Paradaiso”

“Ndithu ndikukuuza lelo, iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”—LUKA 23:43.

NYIMBO 145 Mulungu Analonjeza Paradaiso

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Yesu atatsala pang’ono kufa, kodi anamuuza ciyani munthu wocita zoipa amene anapacikidwa naye? (Luka 23:39-43)

 YESU na amuna aŵili ocita zoipa amene anapacikidwa naye anazunzika ali pafupi kufa. (Luka 23:32, 33) Amunawo anali kunyoza Yesu, zimene zionetsa kuti sanali ophunzila ake. (Mat. 27:44; Maliko 15:32) Koma mmodzi anasintha maganizo ake. Iye anati: “Yesu, mukandikumbukile mukakaloŵa mu Ufumu wanu.” Yesu anamuyankha kuti: “Ndithu ndikukuuza lelo, iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Ŵelengani Luka 23:39-43.) Palibe umboni woonetsa kuti munthu wocita zoipa ameneyu analandilapo uthenga wokamba za “Ufumu wakumwamba,” umene Yesu analalikila pa utumiki wake. Ndipo Yesu sanakambe kuti munthuyo adzaloŵa mu Ufumuwo kumwamba ayi. (Mat. 4:17) Apa iye anali kukamba za paradaiso wam’tsogolo padziko lapansi. N’cifukwa ciyani takamba conco?

Kodi tingati ciyani za munthu wocita zoipa uyu amene anakamba na Yesu, komanso zimene anali kudziŵako? (Onani ndime 2-3)

2. N’ciyani cionetsa kuti wocita zoipa wolapa uja anali Myuda?

2 Munthu wocita zoipa wolapayo ayenela kuti anali Myuda. Iye anauza mnzake kuti: “Kodi iwe suopa Mulungu eti, poona kuti nawenso ukulandila cilango cofanana ndi ca munthu ameneyu?” (Luka 23:40) Ayuda anali kulambila Mulungu mmodzi. Koma anthu a mitundu ina anali kukhulupilila milungu yambili. (Eks. 20:2, 3; 1 Akor. 8:5, 6) Ngati amuna ocita zoipawo anali a mitundu ina, mwina akanafunsa kuti, “Kodi iwe suopa milungu eti?” Cina, Yesu anatumidwa kwa “nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli,” osati kwa anthu a mitundu ina. (Mat. 15:24) Ndipo Mulungu kalelo anauza Aisiraeli kuti adzaukitsa akufa m’tsogolo. Wocita zoipa wolapayo ayenela kuti anali kudziŵa zimenezi, ndipo zimene anakamba zionetsa kuti Yehova adzaukitsa Yesu kuti akalamulile mu Ufumu wa Mulungu. Munthuyo ayenela kuti anali na ciyembekezo mwa Mulungu kuti adzamuukitsa.

3. N’ciyani ciyenela kuti cinabwela m’maganizo a munthu wocita zoipa wolapayo, Yesu atachula za Paradaiso? Fotokozani. (Genesis 2:15)

3 Pokhala Myuda, wocita zoipa wolapayo ayenela kuti anali kudziŵa mbili ya Adamu na Hava, komanso Paradaiso amene Yehova anawaikamo. Conco, iye ayenela kuti anazindikila kuti Paradaiso amene Yesu anachula adzakhala munda wokongola pano padziko lapansi.—Ŵelengani Genesis 2:15.

4. Kodi zimene Yesu anauza wocita zoipayo ziyenela kutilimbikitsa kuganizila za ciyani?

4 Zimene Yesu anauza wocita zoipayo ziyenela kutilimbikitsa kuganizila mmene umoyo udzakhalile m’Paradaiso. Ndipo pali zimene tingaphunzilepo zokhudza Paradaiso kucokela ku ulamulilo wamtendele wa Mfumu Solomo. Yesu pokhala Solomo wamkulu, adzagwila nchito pamodzi na olamulila anzake kuti adzasandutse dziko lapansi kukhala paradaiso. (Mat. 12:42) Conco, a “nkhosa zina” ayenela kuonetsetsa kuti akucita zinthu zowayeneleza kukakhala na moyo kwamuyaya m’Paradaiso.—Yoh. 10:16.

KODI UMOYO M’PARADAISO UDZAKHALA WOTANI?

5. Kodi muyembekezela kudzacita ciyani m’Paradaiso?

5 N’ciyani cimabwela m’maganizo mwanu mukamaganizila mmene umoyo udzakhalile m’Paradaiso? N’kutheka kuti m’maganizo mwanu mumaona malo okongola, monga unalili munda wa Edeni. (Gen. 2:7-9) Mwina mumakumbukila ulosi umene Mika analemba wonena za anthu a Mulungu kuti, “aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu.” (Mika 4:3, 4) Mwinanso mumakumbukila malemba ena m’Baibo amene amakamba kuti kudzakhala cakudya camwana alilenji. (Sal. 72:16; Yes. 65:21, 22) Conco, mumayelekeza kuti muli m’munda wokongola, muli pathebulo ndipo mukusangalala na cakudya cokoma. Komanso, mumayelekeza kuti mukupuma kamphepo ka fungo labwino la zomela komanso maluŵa. Ndipo mwacionekele mukumva acibale anu na mabwenzi anu, kuphatikizapo oukitsidwa, akuseka pamene akuceza. Izi si maloto ayi. Sitikayikila kuti zinthu zimenezi zidzacitika pano padziko lapansi. Cina, m’Paradaiso tizikagwilanso nchito yokondweletsa.

Tizidzagwila nchito yofunika kwambili yophunzitsa anthu oukitsidwa (Onani ndime 6)

6. Kodi tizikacita ciyani m’Paradaiso? (Onani cithunzi.)

6 Yehova anatilenga m’njila yakuti tizipeza cimwemwe pogwila nchito. (Mlal. 2:24) Mu Ulamulilo wa Khristu wa Zaka Cikwi, tidzakhala na nchito yaikulu. Aja amene adzapulumuka Aramagedo, komanso anthu mamiliyoni amene adzaukitsidwe, adzafunikila zovala, cakudya, na malo okhala. Kuti zinthu zimenezi zikakhalepo, padzakhala nchito zambili zosangalatsa. Monga zinalili kwa Adamu na Hava, ifenso tidzakhala na mwayi wosandutsa dziko lapansi kukhala Paradaiso. Ganizilaninso mmene zidzakhalile zokondweletsa kuphunzitsa anthu mamiliyoni oukitsidwa amene sanali kudziŵa zambili za Yehova komanso colinga cake. Tizikaphunzitsanso anthu okhulupilika amene anakhalako Yesu asanabwele padziko lapansi.

7. Kodi ndife otsimikiza za ciyani? Nanga n’cifukwa ciyani?

7 Ndife otsimikiza kuti umoyo m’Paradaiso udzakhala wamtendele, wamwana alilenji, komanso tizikakhala mwadongosolo. Cifukwa ciyani tikutelo? Cifukwa Yehova anationetsa kale citsanzo ca mmene umoyo udzakhalile mu ulamulilo wa Mwana wake. Citsanzo cimeneco ni ulamulilo wa Mfumu Solomo.

ULAMULILO WA SOLOMO UNALI KADYONKHO CABE KA PARADAISO

8. Kodi mawu amene Mfumu Davide analemba pa Salimo 37:10, 11, 29 anakwanilitsidwa motani pambuyo pake? (Onani nkhani yakuti “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga,” m’magazini ino.

8 Mfumu Davide anauzilidwa kulemba mmene umoyo udzakhalile, pamene mfumu yanzelu komanso yokhulupilika idzakhala pa mpando wacifumu. (Ŵelengani Salimo 37:10, 11, 29.) Nthawi zambili timaŵelengela anthu Salimo 37:11 tikamalalikila za Paradaiso amene akubwelayo. M’pake kutelo cifukwa Yesu anagwila mawu a lemba limeneli pa ulaliki wake wa pa Phili, kuonetsa kuti zidzakwanilitsidwa m’tsogolo. (Mat. 5:5) Koma mawu a Davide amenewo anaonetsanso mmene umoyo unali kudzakhalila m’masiku a Mfumu Solomo. Pamene Solomo anali kulamulila mu Isiraeli, anthu a Mulungu anali na mtendele woculuka komanso umoyo wabwino m’dziko “loyenda mkaka ndi uci.” Mulungu anati: “Mukapitiliza kutsatila malangizo anga . . . ndidzakupatsani mtendele m’dzikolo, moti mudzagona pansi popanda wokuopsani.” (Lev. 20:24; 26:3, 6) Malonjezo amenewo anakwanilitsidwa mu ulamulilo wa Solomo. (1 Mbiri 22:9; 29:26-28) Ndipo Mulungu anawalonjeza kuti anthu oipa “sadzakhalakonso.” (Sal. 37:10) Conco, mawu a pa Salimo 37:10, 11, 29 anakwanilitsidwa kalelo. Koma adzakwanilitsidwanso m’tsogolo.

9. Kodi mfumukazi ya ku Sheba inati ciyani za ulamulilo wa Mfumu Solomo?

9 Mfumukazi ya ku Sheba inamva za mtendele komanso umoyo wabwino umene Aisiraeli anali nawo mu ulamulilo wa Solomo. Mfumukazi imeneyo inayenda ulendo wautali kupita ku Yerusalemu kukadzionela na maso ake. (1 Maf. 10:1) Pambuyo poona ulemelelo wa Solomo, inati: “Ndinangouzidwa hafu cabe. . . . Odala anthu anu, odala atumiki anuwa amene amatumikila pamaso panu nthawi zonse, n’kumamva nzelu zanu.” (1 Maf. 10:6-8) Koma umoyo mu ulamulilo wa Solomo unali kadyonkho cabe ka zimene Yehova adzacitila mtundu wa anthu pansi pa ulamulilo wa Mwana wake, Yesu.

10. Kodi Yesu amapambana Solomo m’njila ziti?

10 Yesu amapambana Solomo m’njila zambili. Solomo anali wopanda ungwilo, ndipo anacita macimo aakulu amene pambuyo pake anabweletsa mavuto pa anthu a Mulungu. Koma Yesu ni Wolamulila wangwilo amene salakwa. (Luka 1:32; Aheb. 4:14, 15) Iye sanagonje ku mayeso ovuta amene Satana anabweletsa pa iye. Khristu anaonetsa kuti sangacimwe kapena kucita zinthu zimene zingavulaze nzika zokhulupilika za Ufumu wake. Ni mwayi waukulu zedi kukhala na Mfumu yotelo.

11. Kodi ndani adzathandiza Yesu kulamulila?

11 Yesu adzagwila nchito pamodzi na olamulila anzake a 144,000 yosamalila mtundu wa anthu, komanso kuti akwanilitse colinga ca Yehova cokhudza dziko lapansi. (Chiv. 14:1-3) Olamulila anzakewo anakumanapo na mayeso ambili pamene anali padziko lapansi. Conco, iwo adzakhala olamulila acifundo kwambili. Nanga kodi olamulila anzakewo azikagwila nchito yotani maka-maka?

KODI ODZOZEDWA AZIKAGWILA NCHITO YOTANI?

12. Ni mwayi wapadela uti umene Yehova anapatsa a 144,000?

12 Nchito imene Yesu na olamulila anzake anapatsidwa ni yaikulu kwambili kuposa imene Solomo anapatsidwa. Mfumu yaciisiraeli imeneyo inali kuyang’anila anthu mamiliyoni m’dziko limodzi cabe. Koma olamulila mu Ufumu wa Mulungu adzathandiza kusamalila anthu ofika m’mabiliyoni zungulile dziko lapansi. Ha, ni mwayi waukulu cotani nanga umene Yehova anapatsa a 144,000!

13. Kodi nchito ya olamulila anzake a Yesu idzaphatikizapo udindo wapadela uti?

13 Mofanana na Yesu, a 144,000 adzakhala mafumu komanso ansembe. (Chiv. 5:10) Pansi pa Cilamulo ca Mose, udindo waukulu wa ansembe unali kusamalila thanzi la anthu kuthupi ndiponso kuuzimu. Cilamuloco cinali “mthunzi cabe wa zinthu zabwino.” Conco, m’pomveka kukamba kuti olamulila anzake a Yesu adzathandizila pa nchito yapadela yosamalila zosoŵa zakuthupi komanso zauzimu za anthu a Mulungu. (Aheb. 10:1) Tingofunika kuyembekezela kuti tikaone mmene mafumu komanso ansembe amenewo azikalankhulana na nzika za Ufumu wa Mulungu padziko lapansi. Mulimonse mmene Yehova adzakonzele, tingakhale na cidalilo conse kuti m’Paradaiso akubwelayo, anthu okhala padziko lapansi adzalandila citsogozo cofunikila.—Chiv. 21:3, 4.

KODI A “NKHOSA ZINA” AFUNIKA KUCITA CIYANI KUTI AYENELELE KUDZAKHALA M’PARADAISO?

14. Kodi pali ubale wotani pakati pa a “nkhosa zina” komanso abale a Khristu?

14 Yesu anacha aja amene adzalamulila naye kuti “kagulu ka nkhosa.” (Luka 12:32) Iye anakambanso za gulu lina laciŵili, limene analicha “nkhosa zina.” Magulu aŵili amenewa amapanga gulu limodzi la nkhosa logwilizana. (Yoh. 10:16) Magulu amenewa akuseŵenzela kale pamodzi, ndipo adzapitiliza kutelo ngakhale pamene dziko lapansi lidzakhala Paradaiso. Koma tidziŵa kuti pa nthawiyo, “kagulu ka nkhosa” kadzakhala kumwamba, ndipo a “nkhosa zina” adzakhala akuyembekezela moyo wamuyaya padziko lapansi. Koma pali zimene a “nkhosa zina” ayenela kucita palipano kuti ayenelele kudzakhala m’Paradaiso.

Tingaonetse ngakhale palipano kuti tikukonzekela kudzakhala m’Paradaiso amene akubwelayo (Onani ndime 15) b

15. (a) Kodi a “nkhosa zina” amaseŵenzela motani pamodzi na abale a Khristu? (b) Mungatengele bwanji citsanzo ca m’bale amene ali m’sitolo? (Onani cithunzi.)

15 Munthu wocita zoipa wolapa uja anafa asanakhale na mpata woonetsa mokulila ciyamikilo cake pa zimene Khristu anam’citila. Koma ife a “nkhosa zina” tili na mipata yambili palipano yoonetsa mmene timamuonela Yesu. Mwacitsanzo, mmene timacitila zinthu na abale ake odzozedwa zimaonetsa kuti timam’konda. Yesu anati adzaweluza nkhosa pamaziko amenewa. (Mat. 25:31-40) Tingawathandizile abale a Khristu pogwila kugwila nawo mokangalika nchito yolalikila na kupanga ophunzila. (Mat. 28:18-20) Ndipo kuti tiigwile bwino nchitoyi, tiyenela kuseŵenzetsa mwaluso zida zophunzitsila Baibo, monga buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Ngati mulibe phunzilo la Baibo, bwanji osakhala na colinga coyambitsa phunzilo la Baibo kwa anthu ambili mmene mungathele?

16. Kodi tingakonzekele motani kudzakhala nzika za Ufumu wa Mulungu?

16 Ino ndiyo nthawi yokhala mtundu wa munthu amene Yehova akufuna m’Paradaiso. Tiyenela kuyamba lelo kukhala oona mtima m’mawu na zocita zathu, komanso kucita mwacikatikati zimene timakonda. Tiyenelanso kukhala wokhulupilika kwa Yehova, kwa mnzathu wa mu ukwati, komanso kwa Akhristu anzathu. Ngati timatsatila kwambili malamulo a Mulungu palipano, cidzakhala cosavuta kukawatsatila tidzakhala m’Paradaiso. Cina, tikhoza kuphunzilako maluso othandiza poonetsa kuti tikukonzela kudzakhala m’Paradaiso. Onani nkhani yakuti, “Kodi Ndinu Okonzeka ‘Kudzalandila Dziko Lapansi’?” Nkhaniyi ili m’magazini ino.

17. Kodi tiyenela kudziimba mlandu pa macimo amene tinacita kumbuyoku? Fotokozani.

17 Kuwonjezela apo, tiyenela kupewa kudziimba mlandu pa macimo aakulu amene tinacita kumbuyoku. N’zoona kuti sitingapange nsembe ya dipo kukhala cifukwa ‘cocitila macimo mwadala.’ (Aheb. 10:26-31) Koma tingakhale otsimikiza kuti Yehova anatikhululukila na mtima wonse, ngati tinalapadi moona mtima pa chimo lalikulu limene tinacita, ndipo tinapempha thandizo limene Yehova amapeleka, komanso tinasintha khalidwe lathu. (Yes. 55:7; Mac. 3:19) Kumbukilani zimene Yesu anauza Afarisi kuti: “Sindinabwele kudzaitana anthu olungama, koma ocimwa.” (Mat. 9:13) Inde, nsembe ya dipo ili na mphamvu kwambili yophimba macimo athu onse.

MUNGATHE KUDZAKHALA NA MOYO KWAMUYAYA M’PARADAISO

18. Kodi mufuna mukakambilane zotani na wocita zoipa uja amene anafa pamodzi na Yesu?

18 Yelekezani kuti muli m’Paradaiso, ndipo mukulankhula na wocita zoipa uja amene anakamba na Yesu. Mosakayikila, nonsenu mudzaonetsa ciyamikilo canu pa nsembe ya Yesu. Ndipo mwina mungamufunse kuti akuuzeni zambili zimene zinacitika Yesu anali pafupi kufa, komanso mmene iye anamvela Yesu atayankha pempho lake. Kumbali ina, iye angakufunseni mmene zinalili kukhala m’masiku otsiliza m’dziko la Satana. Udzakhala mwayi waukulu kuphunzitsa Mawu a Mulungu anthu ngati wocita zoipa uja.—Aef. 4:22-24.

Mu ulamulilo wa zaka Cikwi, m’bale akunola luso lake limene anali kufunitsitsa mwacidwi kulikulitsa (Onani ndime 19)

19. N’cifukwa ciyani umoyo m’Paradaiso sudzakhala wogwetsa ulesi? (Onani cithunzi pacikuto.)

19 Umoyo m’Paradaiso sudzakhala wogwetsa ulesi. Tikutelo cifukwa nthawi zonse tizikaonana na anthu osiyana-siyana, komanso kugwila nchito yopindulitsa. Coposa zonse, tsiku lililonse tiziphunzila za Atate wathu wakumwamba kuti tim’dziŵe bwino, komanso tizisangalala na madalitso ake. Kuphunzila za iye sikudzatha, ndipo padzakhala zinthu zoculuka zacilengedwe zofunika kuziphunzila. Zaka zikamapita, cikondi cathu pa Yehova cizingokulila-kulila. Timuyamikila kwambili Yehova komanso Yesu potipatsa ciyembekezo codzakhala na moyo kwamuyaya m’Paradaiso!

NYIMBO 22 Ufumu Ulamulila—Ubwele!

a Kodi nthawi zambili mumaganizila mmene umoyo udzakhalile m’Paradaiso? Kucita zimenezi kumalimbikitsa. Tikamaganizila kwambili zimene Yehova watisungila m’tsogolo, tidzakhala ofunitsitsa kuuzako ena za dziko latsopano. Nkhani ino itithandiza kulimbitsa cikhulupililo cathu pa lonjezo la Yesu la paradaiso limene likubwelalo.

b MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale amene akuyembekezela mwacidwi kudzatengako mbali pa nchito yophunzitsa anthu oukitsidwa akuphunzitsa kale ena.