NKHANI YOPHUNZILA 50
Cikhulupililo na Nchito ZakeZimapangitsa Munthu Kukhala Wolungama
“Amayenda moyenelela m’mapazi a cikhulupililo cimene bambo wathu Abulahamu anali naco.”—AROMA 4:12.
NYIMBO 119 Tikhale na Cikhulupililo
ZIMENE TIKAMBILANE a
1. Tikaganizila za cikhulupililo ca Abulahamu, tingadzifunse funso lanji?
NGAKHALE kuti anthu ambili anamvapo za Abulahamu, oculuka a iwo amadziŵa zocepa pa iye. Koma inu mumadziŵa zambili zokhudza Abulahamu. Mwacitsanzo, mudziŵa kuti Abulahamu amachedwa “tate wa onse okhala ndi cikhulupililo.” (Aroma 4:11) Koma nthawi zina mungadzifunse kuti, ‘Kodi n’zotheka nanenso kukhala na cikhulupililo colimba monga ca Abulahamu?’ Inde n’zotheka.
2. N’cifukwa ciyani n’kofunika kukambilana citsanzo ca Abulahamu? (Yakobo 2:22, 23)
2 Njila imodzi imene tingakhalile na cikhulupililo monga ca Abulahamu ni kuŵelenga citsanzo cake. Atalamulidwa na Mulungu, Abulahamu anacoka na kupita ku dziko lakutali, anakhala m’mahema kwa zaka zambili, ndipo anali wokonzeka kupeleka nsembe mwana wake wokondedwa Isaki. Zonsezi zionetsa kuti iye anali na cikhulupililo colimba. Cikhulupililo ca Abulahamu komanso nchito zake zinacititsa kuti ayanjidwe na Mulungu, komanso kuti akhale bwenzi lake. (Ŵelengani Yakobo 2:22, 23.) Yehova amafuna kuti tonsefe—kuphatikizapo inuyo—tisangalale na madalitso amenewa. Ndiye cifukwa cake iye anauzila Paulo komanso Yakobo kulemba za citsanzo ca Abulahamu. Tiyeni tikambilane za citsanzo cake malinga na zimene zinalembedwa mu Aroma caputala 4 komanso Yakobo caputala 2. Macaputala onse aŵiliwa amafotokoza mawu osangalatsa omwe ananenedwa onena za Abulahamu.
3. Kodi Paulo na Yakobo anagwila mawu lemba liti?
3 Onse aŵili Paulo na Yakobo anagwila mawu Genesis 15:6, imene imati: “Iye anakhulupilila mwa Yehova, ndipo Mulunguyo anamuona Abulamu ngati wolungama.” Kulungama kumatanthauza mmene Mulungu amaonela munthu kukhala wovomelezeka komanso wopanda colakwa. N’zosangalatsa kuti munthu wopanda ungwilo, komanso wocimwa, angaonedwe kukhala wosalakwa na Mulungu! Mwacionekele, nanunso mumafuna kuti Mulungu azikuonani kukhala wolungama, ndipo n’zotheka. Kuti zimenezi zitheke kwa ifenso, tiyenela kumvetsa cifukwa cake Abulahamu anaonedwa wolungama.
CIKHULUPILILO N’COFUNIKA KUTI MUNTHU ACHEDWE WOLUNGAMA
4. N’ciyani cimalepheletsa anthu kukhala olungama?
4 M’kalata yake yopita kwa Aroma, Paulo ananena kuti anthu onse ni ocimwa. (Aroma 3:23) Conco, zingatheke bwanji kuti Mulungu aone munthu kukhala wolungama komanso wopanda colakwa kuti amuyanje? Pofuna kuthandiza Akhristu oona mtima kuyankha funso limeneli, Paulo anaseŵenzetsa citsanzo ca Abulahamu.
5. N’ciyani cinapangitsa Yehova kuona Abulahamu kukhala wolungama? (Aroma 4:2-4)
5 Yehova anacha Abulahamu wolungama pomwe anali kukhala m’dziko la Kanani. N’ciyani cinapangitsa Yehova kuona Abulahamu kukhala wolungama? Kodi cinali cifukwa cakuti Abulahamu anali kusunga bwino-bwino malamulo onse a m’Cilamulo ca Mose? Ayi. (Aroma 4:13) Cilamuloco cinapatsidwa ku mtundu wa Isiraeli patapita zaka 400 kucokela pomwe Mulungu anacha Abulahamu kukhala wolungama. Ndiye, n’ciyani kwenikweni cinapangitsa Mulungu kuona Abulahamu kukhala wolungama? Mwa cisomo cake, Yehova anaona Abulahamu kukhala wolungama cifukwa ca kukhulupilika kwake.—Ŵelengani Aroma 4:2-4.
6. N’ciyani cingacititse Yehova kuona wocimwa kukhala wolungama?
6 Paulo anati munthu akaika cikhulupililo cake mwa Mulungu, “amayesedwa wolungama cifukwa ca cikhulupililo cake.” (Aroma 4:5) Iye anatinso: “Davide ananena kuti munthu amene Mulungu amamuyesa wolungama popanda munthuyo kucita nchito ndi wodala. Iye anati: ‘Odala ndi amene akhululukidwa zocita zawo zosamvela malamulo ndipo macimo awo aphimbidwa. Wodala ndi munthu amene Yehova sadzaŵelengela cimo lake.’” (Aroma 4:6-8; Sal. 32:1, 2) Mulungu amakhululuka, kapena kuti kuphimba macimo, a anthu oika cikhulupililo cawo mwa iye. Amawakhululukila kothelatu, ndipo sawapatsa cilango kaamba ka macimo amenewo. Amaona anthu amenewo kukhala osalakwa komanso olungama cifukwa ca cikhulupililo cawo.
7. Ni m’njila yotani imene alambili okhulupilika anaonedwa kukhala olungama?
7 Ngakhale kuti Abulahamu, Davide, komanso alambili ena a Mulungu okhulupilika anaonedwa olungama, iwo anali ocimwabe. Koma cifukwa ca cikhulupililo cawo, Mulungu anawaona kukhala osalakwa, maka-maka powayelekezela na anthu ena omwe sanali kumulambila. (Aef. 2:12) Paulo anafotokoza momveka bwino m’kalata yake kuti, cikhulupililo n’cofunika kuti munthu akhale paubwenzi na Mulungu. Umu ni mmene zinalili kwa Abulahamu na Davide, ndipo n’cimodzi-modzinso kwa ife.
KODI PALI MGWILIZANO WANJI PAKATI PA CIKHULUPILILO NA NCHITO?
8-9. Kodi anthu ena molakwika ananenapo ciyani pa zimene Paulo na Yakobo analemba? Nanga n’cifukwa ciyani?
8 Kwa zaka mahandiledi ambili, machalichi acikhristu akhala akutsutsana pa cimene cili cofunika kwambili pakati pa cikhulupililo na nchito. Atsogoleli acipembedzo ena amati, kuti munthu apulumuke angofunika kukhulupilila mwa Ambuye Yesu Khristu. Mwina munamvapo iwo akunena kuti, “Landila Yesu kuti upeze cipulumutso.” Atsogoleli ena acipembedzo amafika pogwila mawu a Paulo akuti: “Mulungu amamuyesa wolungama popanda munthuyo kucita nchito.” (Aroma 4:6) Komanso, ena amanena kuti “ungapeze cipulumutso” mwa kutenga ulendo wacipembedzo wokaona malo opatulika kapena kucita utumiki wopatulika wa chalichi. Potsindika mfundoyi, ena amagwila mawu a Yakobo 2:24 akuti: “Munthu amaonedwa ngati wolungama cifukwa ca nchito zake, osati cifukwa ca cikhulupililo cokha.”
9 Cifukwa ca kaonedwe kameneka, akatswili a Baibo ena amanena kuti Paulo na Yakobo anatsutsana pa nkhani ya cikhulupililo komanso nchito. Atsogoleli acipembedzo amanena kuti Paulo anali kukhulupilila kuti munthu amaonedwa wolungama cifukwa ca cikhulupililo, osati nchito. Amati Yakobo anaphunzitsa kuti nchito ndiye zofunika kuti munthu akhale wovomelezeka kwa Mulungu. Katswili wina wa zaumulungu anafotokoza motele: “Yakobo sanamvetse cifukwa cake Paulo anatsindika kuti cikhulupililo pacokha ndico cofunika kuti munthu akhale wolungama, osati nchito.” Koma ni Yehova anauzila onse aŵili Paulo na Yakobo kulemba zimenezi. (2 Tim. 3:16) Conco, payenela kukhala njila yosavuta yotithandiza kumvetsa zimene iwo analemba. Kuti timvetse zimene iwo anatanthauza tiyenela kuidziŵa bwino nkhani yonse imene aliyense analemba m’kalata yake.
10. Ni “nchito” zotani maka-maka zimene Paulo anali kukambapo? (Aroma 3:21, 28) (Onaninso cithunzi.)
10 Ni “nchito” ziti zimene Paulo anali kukambapo mu Aroma caputala 3 na 4? Iye anali kufotokoza za “nchito za cilamulo,” cilamulo ca Mose comwe cinapelekedwa pa Phili la Sinai. (Ŵelengani Aroma 3:21, 28.) Zioneka kuti m’nthawi ya Paulo, Akhristu aciyuda ena cinali cowavuta kuvomeleza kuti Cilamulo ca Mose, komanso nchito zochulidwa m’Cilamuloco zinali zitathetsedwa. Ndiye cifukwa cake, Paulo anaseŵenzetsa citsanzo ca Abulahamu kuti munthu samaonedwa kukhala wolungama kwa Mulungu cifukwa ca “nchito za cilamulo.” Zimatheka cifukwa ca cikhulupililo. Izi n’zolimbikitsa cifukwa zimatiphunzitsa kuti ngati tili na cikhulupililo mwa Mulungu komanso Khristu, n’zotheka kukhala wovomelezeka m’maso mwa Mulungu.
11. Kodi Yakobo anali kukamba “nchito” zotani?
11 Komabe, “nchito” zimene zinafotokozedwa mu Yakobo caputala 2 si “nchito za cilamulo” zimene Paulo anali kunena. Yakobo anali kufotokoza nchito, kapena kuti zinthu zimene Akhristu amacita pa umoyo wawo. Nchito zimenezo, ni zimene zimaonetsa ngati munthu ali na cikhulupililo ceniceni mwa Mulungu kapena ayi. Tiyeni tikambilane zitsanzo ziŵili zimene Yakobo anafotokoza.
12. Kodi Yakobo pali mgwilizano wotani pakati pa cikhulupililo na nchito zake? (Onaninso cithunzi.)
12 Mu citsanzo cake coyamba, Yakobo anafotokoza kuti Akhristu ayenela kukhala opanda tsankho pocita zinthu ni anthu ena. Anamveketsa mfundoyi poseŵenzetsa cocitika ca munthu yemwe anakondela munthu wolemela, koma sanakomele mtima munthu wosauka. Yakobo anafotokoza kuti munthu wotelo angakambe kuti ali na cikhulupililo. Koma kodi nchito zake zigwilizana na cikhulupililoco? (Yak. 2:1-5, 9) Mu citsanzo cake caciŵili, Yakobo anachula za munthu yemwe anaona “m’bale kapena mlongo ali waumphawi ndipo alibe cakudya cokwanila pa tsikulo,” koma sanapeleke thandizo lofunikila. Munthuyo angakambe kuti ali na cikhulupililo, koma cifukwa cakuti sanacionetse na zocita zake, cikhoza kukhala copanda pake. Ndiye cifukwa cake Yakobo analemba kuti, “momwemonso cikhulupililo pacokha, ngati cilibe nchito zake, ndi cakufa.”—Yak. 2:14-17.
13. Kodi Yakobo anaseŵenzetsa zitsanzo ziti poonetsa kuti cikhulupililo cifunika kukhala na nchito zake? (Yakobo 2:25, 26)
13 Yakobo anaseŵenzetsa Rahabi monga citsanzo ca munthu amene anaonetsa cikhulupililo mwa nchito zake. (Ŵelengani Yakobo 2:25, 26.) Iye anamva za Yehova, ndipo anadziŵa kuti anali kuthandizila Aisiraeli. (Yos. 2:9-11) Anaonetsa cikhulupililo mwa nchito zake—anateteza azondi aŵili aciisiraeli amene miyoyo yawo inali pa ciopsezo. Mwa izi, mkazi wopanda ungwilo ameneyu, komanso yemwe sanali Mwisiraeli n’komwe, anaonedwa kukhala wolungama monga zinalili kwa Abulahamu. Nkhani ya Rahabi itionetsa kufunika kokhala na cikhulupililo coonetsedwa na nchito zake.
14. Kodi zolemba za Paulo na Yakobo zigwilizana motani?
14 Olemba Baibo ameneŵa, Paulo na Yakobo, anali kufotokoza za nkhani ya cikhulupililo komanso nchito zake m’njila zosiyana. Paulo anali kuuza Akhristu aciyuda kuti Yehova sangawayanje cabe cifukwa cocita nchito za Cilamulo ca Mose. Koma Yakobo anali kufotokoza kufunika kwa Akhristu onse kuonetsa cikhulupililo cawo mwa kucitila ena zabwino.
15. Ni njila ziti zimene tingaonetsele cikhulupililo mwa nchito zathu? (Onaninso cithunzi.)
15 Yehova sananene kuti ngati tifuna kukhala wolungama tizicita ndendende zimene Abulahamu anacita. Ndi iko komwe, pali njila zambili zoonetsela cikhulupililo mwa nchito zathu. Tingatelo mwa kulandila acatsopano mu mpingo, kuthandiza abale na alongo omwe akukumana na mavuto, komanso kucitila zabwino a m’banja lathu. Ndipo nchito zonsezi Mulungu angaziyanje na kuzidalitsa. (Aroma 15:7; 1 Tim. 5:4, 8; 1 Yoh. 3:18) Nchito yabwino kwambili imene imaonetsa kuti tili na cikhulupililo ni kuuzako ena mwacangu uthenga wabwino. (1 Tim. 4:16) Tonsefe tingaonetse m’zocita zathu kuti timakhulupililadi zakuti malonjezo a Yehova adzakwanilitsidwa, komanso kuti njila zake ndizo zabwino kopambana. Tikatelo, tidzakhala otsimikiza kuti Mulungu adzationa kukhala olungama, ndipo adzaticha mabwenzi ake.
CIYEMBEKEZO CIMALIMBIKITSA CIKHULUPILILO
16. Kodi ciyembekezo ca Abulahamu cinathandiza bwanji cikhulupililo cake?
16 Aroma caputala 4 imafotokoza phunzilo limene tingatengepo kwa Abulahamu: kufunika kwa ciyembekezo. Yehova analonjeza kuti mwa Abulahamu “mitundu yambili” idzadalitsidwa. Ganizilani za ciyembekezo cosangalatsa cimene Abulahamu anali naco! (Gen. 12:3; 15:5; 17:4; Aroma 4:17) Komabe, ngakhale pamene Abulahamu anafika zaka 100 komanso Sara ali na zaka 90, mwana amene analonjezedwa anali asanabadwe. M’kaonedwe kaumunthu, zinali zosatheka kwa Abulahamu na Sara kukhala na mwana. Zimenezi zinayesa cikhulupililo ca Abulahamu pa mlingo waukulu. Komabe iye “anali ndi ciyembekezo ndiponso cikhulupililo cakuti adzakhala tate wa mitundu yambili.” (Aroma 4:18, 19) Ndipo patapita nthawi, lonjezo litakwanilitsidwa, iye anakhala tate wa Isaki, mwana yemwe anali atalonjezedwa kalelo.—Aroma 4:20-22.
17. Tidziŵa bwanji kuti n’zotheka kuonedwa bwenzi lolungama kwa Mulungu?
17 N’zotheka kuyanjidwa na Mulungu, komanso kuonedwa kukhala wolungama monga bwenzi lake monga zinalili kwa Abulahamu. Ndipo Paulo ananenapo za mfundo imeneyi pomwe anati: “Komabe, zonena kuti anayesedwa wolungama sizinalembedwele [Abulahamu] yekha, komanso ife amene tidzayesedwa otelo, cifukwa cakuti timakhulupilila iye amene anaukitsa Yesu.” (Aroma 4:23, 24) Monga Abulahamu, ifenso tifunikila cikhulupililo komanso nchito zake kuphatikizapo ciyembekezo. Paulo anapitiliza kufotokoza za ciyembekezo mu Aroma caputala 5, ndipo tidzakambilana zimenezi m’nkhani yotsatila.
NYIMBO 28 Kukhala Bwenzi la Yehova
a Timafuna kuti Mulungu atiyanje komanso kutiona olungama. Poseŵenzetsa zimene Paulo na Yakobo analemba, nkhani ino ifotokoza kuti cikhulupililo cathu komanso nchito zathu n’zofunika kuti tiyanjidwe na Yehova.
b MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Paulo analimbikitsa Akhristu aciyuda kuika maganizo awo maka-maka pa cikhulupililo, osati pa “nchito za cilamulo,” monga kusokelela ulusi wopota wa buluu ku covala, kukondwelela Pasika, komanso kusamba m’manja kwa mwambo.
c MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Yakobo analimbikitsa kuonetsa cikhulupililo mwa kucitila ena zabwino, monga kuthandiza osauka.