Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 51

Ciyembekezo Cathu N’cosagwilitsa Mwala

Ciyembekezo Cathu N’cosagwilitsa Mwala

“Ciyembekezoco sicitikhumudwitsa.”—AROMA 5:5.

NYIMBO 142 Tigwilitsitse Ciyembekezo Cathu

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. N’cifukwa ciyani Abulahamu anayembekezelabe kuti adzakhala na mwana?

 YEHOVA analonjeza bwenzi lake Abulahamu kuti anthu a mitundu yonse adzadalitsidwa kupyolela mu mbewu yake. (Gen. 15:5; 22:18) Abulahamu anali wotsimikiza kuti lonjezo la Mulungu lidzakwanilitsidwa cifukwa anali na cikhulupililo colimba mwa iye. Ngakhale n’telo, pamene Abulahamu anali na zaka 100 komanso mkazi wake zaka 90, banja lokhulupilikali linali lisanakhalebe na mwana. (Gen. 21:​1-7) Komabe, Baibo imati: “[Abulahamu] anali ndi ciyembekezo ndiponso cikhulupililo cakuti adzakhala tate wa mitundu yambili, . . . mogwilizana ndi zimene zinanenedwa.” (Aroma 4:18) Mukudziŵa kuti lonjezoli linakwanilitsidwadi. Iye anakhala na mwana wa mwamuna amene anamuyembekezela kwa nthawi yaitali, ndipo anamucha Isaki. N’ciyani cinacititsa Abulahamu kulidalila kwambili lonjezo limeneli?

2. N’cifukwa ciyani Abulahamu anali wotsimikiza kuti lonjezo la Yehova lidzakwanilitsidwa?

2 Cifukwa cokhala pa ubale wolimba na Yehova, Abulahamu “anali wotsimikiza kuti zimene Mulungu analonjeza,” zidzakwanilitsidwa. (Aroma 4:21) Yehova anamuyanja Abulahamu na kumuona kukhala wolungama cifukwa ca cikhulupililo cake. (Yak. 2:23) Monga ionetsela Aroma 4:18 cikhulupililo ca Abulahamu cinali cogwilizana na ciyembekezo cake. Tiyeni tsopano tikambilane zimene Paulo ananena pa nkhani ya ciyembekezo, malinga na zimene zinalembedwa mu Aroma caputala 5.

3. Kodi Paulo anati ciyani za ciyembekezo?

3 Paulo anafotokoza cifukwa cake ciyembekezo cathu cili cosakhumudwitsa. (Aroma 5:5) Anatithandizanso kumvetsa mmene ciyembekezo cathu ca Cikhristu cimalimbila. Pamene tikambilana zimene Paulo anafotokoza pa Aroma 5:​1-5, ganizilani mmene zinalili kwa inu poyamba. Pocita zimenezi, mudzaona kuti ciyembekezo canu ca Cikhristu calimbilako. Nkhani ino ikuthandizaninso kuona mmene mungalimbikitsile ciyembekezo canu kuposa mmene cilili panopa. Coyamba tiyeni tikambilane ciyembekezo cosangalatsa cimene Paulo anati n’cosakhumudwitsa.

CIYEMBEKEZO CATHU COSANGALATSA

4. Kodi Aroma 5:​1, 2 ifotokoza ciyani?

4 Ŵelengani Aroma 5:​1, 2. Paulo analembela mawuwa mpingo wa ku Roma. Abale na alongo kumeneko anali ataphunzila za Yehova na Yesu, anaonetsa cikhulupililo cawo, ndipo anakhala Akhristu. Conco Mulungu anawayesa “olungama cifukwa cokhala ndi cikhulupililo,” ndipo anawadzoza na mzimu woyela. Inde, anakhala na ciyembekezo ceniceni komanso cokondweletsa.

5. Kodi odzozedwa ali na ciyembekezo canji?

5 Pambuyo pake, Paulo analembela Akhristu odzozedwa a ku Efeso pa ciyembekezo cimene anapatsidwa. Ciyembekezoco cinaphatikizapo kulandila zinthu zimene anasungila “oyela monga colowa.” (Aef. 1:18) Cina, anauza Akolose kumene adzalandilila mphoto yawo. Iye anati “ciyembekezo codzalandila zimene akusungilani kumwamba.” (Akol. 1:​4, 5) Ciyembekezo ca Akhristu odzozedwa n’cakuti adzaukitsidwa ku moyo wosatha kumwamba, kumene adzalamulila na Khristu.—1 Ates. 4:​13-17; Chiv. 20:6.

M’bale F. W Franz anafotokoza momveka bwino citsimikizo cimene Akhristu odzozedwa ali naco pa ciyembekezo cawo (Onani ndime 6)

6. Kodi m’bale wina wodzozedwa anati ciyani za ciyembekezo cake?

6 Akhristu odzozedwa amaona ciyembekezoci kukhala ca mtengo wapatali. Mmodzi wa iwo, M’bale Frederick Franz, anakamba kuti: “Ciyembekezo cathu n’cotsimikizika, ndipo cidzakwanilitsidwa kothelatu kwa aliyense wa a 144,000 a m’kagulu ka nkhosa kuposa mmene tikuganizila.” Pambuyo potumikila Mulungu mokhulupilika kwa zaka zambili, mu 1991 M’bale Franz anakamba motsimikiza kuti: “Sitinaleke kuona kufunika kwa ciyembekezo cimeneci. . . . Koma tikucigwilisitsabe zolimba, ndipo tikucimvesetsa mowonjezeleka kwa nthawi yonse imene tiyenela kuyembekezela. Ni cinthu coyenela kuciyembekezela ngakhale kwa zaka ma miliyoni. Nimakweza ciyembekezo cathu kuposa n’kale lonse.”

7-8. Kodi atumiki ambili a Yehova ali na ciyembekezo cotani? (Aroma 8:​20, 21)

7 Atumiki ambili a Yehova masiku ano, ali na ciyembekezo cosiyana na ca Akhristu odzozedwa. N’ciyembekezo cimene Abulahamu anali naco—codzakhala na moyo wosatha pa dziko lapansi, pansi pa Ufumu wa Mulungu. (Aheb. 11:​8-10, 13) Paulo analemba za ulemelelo umene awo amene ali na ciyembekezo cimeneci adzalandile. (Ŵelengani Aroma 8:​20, 21.) N’ciyani cinakusangalatsani nthawi yoyamba pamene munamvela lonjezo la m’Baibo lonena za tsogolo lathu? Kodi inali mfundo yakuti tsiku lina mudzakhala wangwilo, wopanda uchimo? Kapena kodi munakhudzika mtima podziŵa kuti okondedwa anu amene anamwalila adzakhalanso na moyo m’paradaiso padziko lapansi? Izi zinakupangitsani kuti muziyembekezela za kutsogolo mwacidwi “pa maziko a ciyembekezo.”

8 Kaya tili na ciyembekezo cokakhala na moyo wosatha kumwamba kapena pano pa dziko la pansi, tili na ciyembekezo cabwino cimene cimatipatsa cimwemwe. Ndipo ciyembekezo cosangalatsa cimeneci, tingacilimbitse. Cotsatila, Paulo anafotokoza mmene tingacitile zimenezi. Tiyeni tikambilane zimene analemba ponena za ciyembekezo cathu. Kucita izi kudzatithandiza kukhala otsimikiza kuti ciyembekezo cathu cidzapitiliza kulimba, ndiponso kuti cidzakwanilitsidwa.   

MMENE TINGALIMBIKITSILE CIYEMBEKEZO CATHU

Akhristu onse amayembekezela masautso ena ake (Onani ndime 9-10)

9-10. Malinga na citsanzo ca Paulo, kodi Akhristu amayembekezela ciyani? (Aroma 5:3)(Onaninso zithunzi.)

9 Ŵelengani Romans 5:3. Onani kuti masautso angatithandize kulimbikitsa ciyembekezo cathu. Izi zingamveke zodabwitsa. Koma mfundo yosatsutsika ni yakuti otsatila onse a Khristu amadziŵa kuti angazunzidwe. Ganizilani citsanzo ca Paulo. Iye analembela Atesalonika kuti: “Pamene tinali nanu limodzi, tinali kukuuzilanitu kuti tiyenela kudzakumana ndi masautso, ndipo mmene zacitikilamu ndi mmenenso inu mukudziŵila.” (1 Ates. 3:4) Analembelanso Akorinto kuti: “Abale, sitikufuna kuti mukhale osadziŵa za masautso amene tinakumana nawo . . . Tinalibenso ciyembekezo coti tikhala ndi moyo.”—2 Akor. 1:8; 11:​23-27.

10 Ngakhale masiku ano, Akhristu angayembekezele kuzunzidwa m’njila inayake. (2 Tim. 3:12) Kodi inunso munazunzidwapo cifukwa cokhulupilila Yesu na kuyamba kum’tsatila? Mwina munasekedwapo na mabwenzi komanso acibale anu. N’kutheka kuti anafika ngakhale pokucitilani nkhanza. Kodi munakumanapo na mavuto ku nchito cifukwa cocita zinthu moona mtima? (Aheb. 13:18) Kodi munazunzidwapo na boma cifukwa couzako ena ciyembekezo canu? Paulo anati tizisangalala mosasamala kanthu za mtundu wa masautso amene takumana nawo. Cifukwa ciyani?

11. N’cifukwa ciyani tiyenela kukhala otsimikiza kupilila mayeso alionse?

11 Timakhala osangalala pozunzidwa cifukwa ca zimene zimatulukapo. Aroma 5:3 imati, “cisautso cimabala cipililo.” Akhristu onse adzakumana na masautso. Conco tonse tiyenela kukhala otsimikiza kupilila masautso alionse amene tingakumane nawo. Tikatelo, m’pamene tidzaona kukwanilitsidwa kwa ciyembekezo cathu. Sitifuna kukhala monga anthu amene Yesu anawayelekezela na mbewu zimene zinagwela pa miyala. Iwo poyamba analandila mawu na cimwemwe, koma “pamene cisautso kapena mazunzo” zinayamba, iwo anapunthwa. (Mat. 13:​5, 6, 20, 21) N’zoona kuti citsutso kapena mayeso n’zoŵaŵa. Koma kuzipilila kumabweletsa madalitso. Motani?

12. Timapindula motani tikakwanitsa kupilila mayeso?

12 Wophunzila Yakobo anafotokoza mapindu amene amabwela cifukwa copilila mayeso. Iye analemba kuti: “Mulole kuti kupilila kumalize kugwila nchito yake, kuti mukhale okwanila ndi opanda cilema m’mbali zonse, osapeleŵela kalikonse.” (Yak. 1:​2-4) Yakobo anafotokoza kuti kupilila kuli na nchito imene kuyenela kuigwila. Ni nchito yanji? Kumatithandiza kukulitsa kwambili makhalidwe monga kuleza mtima, cikhulupililo, komanso kudalila Mulungu. Koma pali phindu lina limene timapeza cifukwa ca kupilila.

13-14. Kodi kupilila kumabala ciyani? Nanga zimenezo zigwilizana bwanji na ciyembekezo? (Aroma 5:4)

13 Ŵelengani Aroma 5:4. Paulo anati kupilila kumacititsa “kuti tikhale ovomelezeka.” Kupilila kwanu kungacititse kuti mukhale ovomelezeka kwa Yehova. Izi sizitanthauza kuti Yehova amakondwela mukamakumana na mavuto ayi. M’malo mwake amakondwela kuti mwakwanitsa kupilila mokhulupilika. N’zolimbikitsa kwambili kudziŵa kuti tikapilila timakondweletsa Yehova!—Sal. 5:12.

14 Kumbukilani kuti Abulahamu anapilila mayeso, ndipo pothela pake anayanjidwa na Mulungu. Anakhala bwenzi la Yehova, ndipo anaonedwa wolungama. (Gen. 15:6; Aroma 4:​13, 22) Zingakhalenso cimodzi-modzi kwa ife. Mulungu satiyanja cifukwa ca kuculuka kwa nchito zimene timacita mu utumiki wake, kapena maudindo amene tili nawo. M’malo mwake, amatiyanja cifukwa ca kupilila kwathu mokhulupilika. Tonsefe tingakwanitse kupilila mosasamala kanthu za msinkhu wathu, mikhalidwe yathu, na maluso athu. Kodi mukupilila mokhulupilika mayeso ena ake pali pano? Ngati n’telo, pezani citonthozo podziŵa kuti Mulungu akusangalala nanu. Kudziŵa zimenezi kumalimbikitsa ciyembekezo cathu.

CIYEMBEKEZO COLIMBA

15. Ni mfundo ina iti imene Paulo anachula? Nanga n’cifukwa ciyani zimenezi zingakhale zosamveka kwa ena?

15 Monga anafotokozela Paulo, timapeza ciyanjo ca Yehova mwa kupilila mayeso mokhulupilika. Iye anapitiliza kuti: “Cipililo cimacititsa kuti tikhale ovomelezeka kwa Mulungu. Kukhala ovomelezeka kwa Mulungu kumabala ciyembekezo, ndipo ciyembekezoco sicitikhumudwitsa.” (Aroma 5:​4, 5) Izi zingakhale zosamveka kwa ena. Cifukwa ciyani? Cifukwa Paulo pa Aroma 5:​2, anali atafotokoza kale kuti Akhristu a ku Roma anali kale na ciyembekezo, “ciyembekezo ca ulemelelo wa Mulungu.” Wina angafunse kuti, ‘Ngati Akhristuwo anali kale na ciyembekezo, n’cifukwa ciyani Paulo anachulanso za ciyembekezo m’mavesi otsatila?’

Ciyembekezo cacikhristu cimene cinakusangalatsani cazika mizu mwa inu, ndipo mwacipanga kukhala canu-canu (Onani ndime 16-17)

16. Kodi ciyembekezo cimayamba motani kulimba mwa munthu? (Onaninso zithunzi.)

16 Tingamvetse zimene Paulo anatanthauza tikazindikila mfundo yakuti ciyembekezo cimapitiliza kulimba. Tiyelekeze motele: Kodi mukumbukila mmene munamvela nthawi yoyamba pamene munamvela ciyembekezo ca m’mawu a Mulungu? Mwina pa nthawiyo munaona kuti nkhani yodzakhala na moyo wosatha pa dziko lapansi anali maloto cabe. Komabe, pamene munali kuphunzila zowonjezeleka zokhudza Yehova komanso malonjezo a m’Baibo, munakhala otsimikiza kuti ciyembekezo cimeneci n’ceniceni.

17. Kodi ciyembekezo canu cinalimbabe motani pambuyo pa kudzipatulila na kubatizika?

17 Ngakhale pambuyo podzipatulila na kubatizika, ciyembekezo canu cinapitlizabe kulimba pomwe munali kuphunzila zambili na kukhala wokhwima mwauzimu. Izi zinacititsa kuti ciyembekezo canu cipitilize kulimbilako. (Aheb. 5:13–6:1) Mwina munaona kukwanilitsidwa kwa Aroma 5:​2-4 pa inu. Munakumana na masautso osiyana-siyana, koma munawapilila. Ndipo munaona kuti Mulungu akukuyanjani. Podziŵa kuti ndinu oyanjidwa na Mulungu, ndinu otsimikiza kuti mudzalandila zonse zimene analonjeza. Ciyembekezo canu calimbilako kuposa mmene cinalili poyamba. Cakhala ceniceni kwa inu, ndipo mwacipanga kukhala canu-canu. Cimakhudza mbali zonse za umoyo wanu. Cakuthandizani kusintha mmene mumacitila zinthu na a m’banja lanu, mmene mumapangila zisankho, komanso mmene mumaseŵenzetsela nthawi yanu.

18. Kodi Yehova amapeleka citsimikizo cotani?

18 Mtumwi Paulo anawonjezela mfundo yofunika yokhudza ciyembekezo cimene munakhala naco mutayanjidwa na Mulungu. Iye anakutsimikizilani kuti ciyembekezo canu cidzakwanilitsidwa. N’cifukwa ciyani mungakhale otsimikiza? Paulo anapeleka citsimikizo couzilidwa kwa Akhristu pomwe anati: “Ciyembekezoco sicitikhumudwitsa cifukwa Mulungu wadzaza cikondi cake m’mitima yathu kudzela mwa mzimu woyela umene tinapatsidwa.” (Aroma 5:5) Muli na zifukwa zomveka zokhulupilila kuti ciyembekezo canu cidzakwanilitsidwa.

19. Kodi mungakhale otsimikiza za ciyani pa ciyembekezo canu?

19 Muzisinkhasinkha lonjezo la Yehova kwa Abulahamu komanso mmene anamuyanjila na kumuona kukhala bwenzi lake. Lonjezo limenelo linakwanilitsidwadi. Baibo imati: “Abulahamu ataonetsa kuleza mtima, analandila lonjezo limeneli.” (Aheb. 6:15; 11:​9, 18; Aroma. 4:​20-22) Ndipo sanagwilitsidwe mwala. Inunso mungakhale otsimikiza kuti mukakhalabe okhulupilika, mudzafupidwa pa ciyembekezo canu. Ciyembekezo canu n’ceniceni ndipo cimakucititsani kukhala osangalala, komanso sicidzakukhumudwitsani. (Aroma 12:12) Paulo analemba kuti: “Mulungu amene amapeleka ciyembekezo akudzazeni ndi cimwemwe conse ndi mtendele wonse cifukwa ca kukhulupilila kwanu, kuti mukhale ndi ciyembekezo cacikulu mwa mphamvu ya mzimu woyela.”—Aroma 15:13.

NYIMBO 139 Yelekeza Uli M’dziko Latsopano

a M’nkhani ino, tikambilane zimene ciyembekezo cacikhristu cimaphatikizapo, komanso cifukwa cake ndife otsimikiza kuti cidzakwanilitsidwa ndithu. Aroma caputala 5 itithandize kuona kusiyana kwa ciyembekezo cimene tili naco panopa, na cimene tinali naco titangoyamba kuphunzila coonadi.