Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Cocitika

Cocitika

Muzimvela Anthu Onse Cifundo

Tsiku lina mlongo wina wa ku New Zealand anaonelela vidiyo yakuti Khalani Omvelana Cifundo,” imene imafotokoza cifundo ca Yehova na mmene amacionetsela. (Yes. 63:​7-9) Iye anasankha kuseŵenzetsa zimene anaphunzila mwa kupeleka thandizo kwa ena. Tsiku limenelo pomwe anali kugula zinthu anakumana na mayi wina yemwe analibe pokhala. Iye anauza mayiyo kuti akufuna kumugulila cakudya. Mayiyo anavomela. Pamene mlongoyo anapeleka cakudya kwa mayiyo, iye anacita ulaliki wacidule poseŵenzetsa kathilakiti kakuti Kodi Mavuto Adzathadi?

Mayiyo anayamba kulila. Anafotokoza kuti anakulila m’banja la Mboni, koma anasankha kusiya coonadi zaka zambili m’mbuyomo. Koma caposacedwa anali kupemphela kwa Yehova kuti am’thandize kubwelelanso kwa iye. Mlongoyo anapatsa mayiyo Baibo, ndipo anapanga makonzedwe akuti ayambe kuphunzila naye. a

Tingaonetse ena cifundo mmene Yehova amacitila. Tingatelo kwa acibale athu, komanso abale na alongo athu mumpingo. Tingaonetsenso cifundo mwa kuyesetsa kupeza mipata yolalikila kwa ena.

a Kuti mudziŵe mmene mungathandizile ozilala, onani nkhani yakuti “Bwelelani Kwa Ine” mu Nsanja ya Mlonda ya June 2020.