Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 53

Inu Abale Acinyamata​—Khalani Amuna Okhwima Mwauzimu

Inu Abale Acinyamata​—Khalani Amuna Okhwima Mwauzimu

“Ucite zinthu mwamphamvu ndipo ukhale wolimba mtima.”—1 MAF. 2:2.

NYIMBO 135 Yehova Alangiza Mwacikondi Kuti: “Mwana Wanga, Khala Wanzelu”

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Kodi mwamuna wacikhristu ayenela kucita ciyani kuti akhale wopambana?

 MFUMU Davide inalangiza Solomo kuti: “Ucite zinthu mwamphamvu ndipo ukhale wolimba mtima.” (1 Maf. 2:​1-3) Amuna onse acikhristu masiku ano angacite bwino kutsatila ulangizi umenewu. Kuti athe kucita zimenezi, afunikila kumvela malamulo a Mulungu na kutsatila mfundo za m’Baibo m’mbali zonse za umoyo wawo. (Luka 2:52) N’cifukwa ciyani m’pofunika kwambili kuti abale acinyamata akhale amuna okhwima acikhristu?

2-3. N’cifukwa ciyani n’kofunika kuti m’bale wacinyamata akhale Mkhristu wokhwima?

2 Mwamuna wacikhristu amasenza maudindo ofunika m’banja komanso mu mpingo. Inu abale acinyamata, mosakayikila munagazilapo za maudindo ena amene mungasenze m’tsogolo. Mwina munadziikila colinga coyamba utumiki wa nthawi zonse, kukhala mtumiki wothandiza kapena mkulu mu mpingo. Mungafunenso kukwatila na kukhala na ana. (Aef. 6:4; 1 Tim. 3:1) Kuti mukwanilitse zolinga zimenezi na kukhala wopambana pa maudindo amenewa, muyenela kukhala Mkhristu wokhwima. b

3 N’ciyani cingakuthandizeni kukhala Mkhristu wokhwima? Muyenela kukulitsa maluso ena ofunika. Nanga n’ciyani cimene muyenela kucita pali pano kuti mukonzekele kukwanilitsa maudindo amene mungadzakhale nawo m’tsogolo?

KUKHALA MKHRISTU WOKHWIMA

Kutengela makhalidwe abwino a Yesu kungakuthandizeni kukhala mwamuna wokhwima wacikhristu (Onani ndime 4)

4. Mungapeze kuti zitsanzo zabwino zimene mungatengele? (Onaninso zithunzi.)

4 Sankhani zitsanzo zabwino zimene mungatengele. M’Baibo muli zitsanzo zambili zimene acinyamata angatengele. Amuna a m’nthawi zakale amenewo anali kumukonda Mulungu ndipo anasenza maudindo osiyana-siyana posamalila anthu ake. Mungapezenso zitsanzo zabwino za Akhristu okhwima m’banja mwanu komanso mu mpingo mwanu. (Aheb. 13:7) Ndipo mulinso na citsanzo cabwino kwambili ca Yesu Khristu. (1 Pet. 2:21) Pamene musinkhasinkha zitsanzo zimenezi mofatsa, ganizilani makhalidwe abwino amene mumasilila kwa iwo. (Aheb. 12:​1, 2) Ndiyeno onani mmene mungatengele citsanzo cawo.

5. Mungaphunzile bwanji kukhala woganiza bwino? Nanga n’cifukwa ciyani kucita zimenezi n’kofunika? (Salimo 119:9)

5 Kulitsani na kuteteza “kuganiza bwino.” (Miy 3:21) Mwamuna woganiza bwino amaganizila zosankha zake asanacitepo kanthu. Conco limbikilani kuti mukhale oganiza bwino. Cifukwa ciyani? Cifukwa dzikoli n’lodzala na acinyamata amene amatsogoleledwa na mfundo za iwo eni kapena amene amalola mmene akumvela kutsogolela kacitidwe kawo ka zinthu. (Miy. 7:7; 29:11) Mafilimu, intaneti komanso soshomidiya zingakhale na cisonkhezelo camphamvu pa inu. Koma kodi mungatani kuti mukhale oganiza bwino? Yambani mwa kuphunzila mfundo za m’Baibo na kuona cifukwa cake mfundozo n’zothandiza. Ndiyeno seŵenzetsani mfundozo kupanga zisankho zokondweletsa Yehova. (Ŵelengani Salimo 119:9.) Mukakulitsa luso lofunika limeneli, ndiye kuti mwatenga sitepe lalikulu lofunika kuti mukhale Mkhristu wokhwima. (Miy. 2:​11, 12; Aheb. 5:14) Onani mmene kuganiza bwino kungakuthandidzileni pa zocitika ziŵilizi: (1) pocita zinthu na alongo, komanso (2) popanga zisankho pa kavalidwe na kudzikongoletsa.

6. Kodi kuganiza bwino kungathandize m’bale wacinyamata kucita motani na alongo?

6 Kuganiza bwino kudzakuthandizani kulemekeza akazi. Si kulakwa m’bale wacinyamata kukopeka na mlongo wacikhristu na colinga coti akhale naye pa cibwenzi. Komabe, mnyamata woganiza bwino sangakambe, kulemba, kapena kucita ciliconse coonetsa kuti akukopeka na mlongo, pokhapo ngati ali na colinga codzamanga naye banja. (1 Tim. 5:​1, 2) Ngati m’bale wacinyamata ali pa cibwenzi, adzayesetsa kuteteza mbili yabwino ya mlongoyo mwa kupewa kukhala naye ali aŵili-ŵili popanda wowayang’anila.—1 Akor. 6:18.

7. Kodi kuganiza bwino kungam’thandize bwanji m’bale wacinyamata kupanga zisankho za nzelu pa nkhani ya kavalidwe na kudzikongoletsa?

7 Njila ina imene wacinyamata angaonetsele kuti ni woganiza bwino ni kupanga zisankho zanzelu pa nkhani ya kavalidwe na kudzikongoletsa. Nthawi zambili, masitayilo a zovala amapangidwa na anthu amene salemekeza Yehova komanso amene ali na umoyo wotayilila. Maganizo awo otayilila amaonekela m’masitayilo a zovala zimene n’zothina komanso zimene zimacititsa amuna kuoneka ngati akazi. Wacinyamata amene akukulitsa luso loganiza bwino, amatsogoleledwa na mfundo za m’Baibo komanso zitsanzo zabwino za mu mpingo pamene akusankha zovala. Angadzifunse kuti: ‘Kodi kavalidwe kanga kamaonetsa kuti ndine woganiza bwino komanso waulemu? Kodi mmene nimavalila zimapangitsa ena kukhulupilila mosavuta kuti ndine wodzipeleka potumikila Mulungu?’ (1 Akor. 10:​31-33; Tito 2:6) Mnyamata woganiza bwino amalemekezedwa na abale na alongo ndipo amakondweletsa Atate wake wakumwamba.

8. Kodi m’bale wacinyamata angaphunzile bwanji kukhala wodalilika?

8 Khalani wodalilika. Mnyamata wodalilika amasamalila bwino maudindo ake. (Luka 16:10) Ganizilani citsanzo cabwino ngako ca Yesu. Iye sanali kunyalanyaza maudindo ake. M’malo mwake, anakwanilitsa utumiki umene Yehova anam’patsa, ngakhale pamene zinali zovuta kucita zimenezo. Anali kukonda anthu—makamaka ophunzila ake—ndipo mofunitsitsa anapeleka moyo wake kamba ka iwo. (Yoh. 13:1) Potengela citsanzo ca Yesu, muzigwila nchito molimbika kuti mukwanilitse udindo uliwonse umene mwapatsidwa. Ngati simudziŵa mogwilila nchitoyo, dzicepetseni na kufunsila malangizo kwa abale okhwima . Muziikilapo mtima pokwanilitsa udindo wanu. (Aroma 12:11) Conco, muzigwila nchito ngati kuti “mukucitila Yehova, osati anthu.” (Akol. 3:23) N’zoona kuti ndinu opanda ungwilo, conco khalani odzicepetsa na kuvomeleza zimene mwalakwitsa pogwila nchito.—Miy. 11:2.

KULITSANI MALUSO OTHANDIZA

9. N’cifukwa ciyani m’bale wacinyamata ayenela kuphunzila maluso othandiza?

9 Kuti mukhale Mkhristu wokhwima, muyenela kukulitsa maluso othandiza. Izi zidzakuthandizani kusenza maudindo mu mpingo, kupeza nchito yokuthandizani inuyo na banja lanu, komanso kukhala pa ubwenzi wabwino na anthu ena. Onani ena mwa maluso ofunika amenewa.

Kuŵelenga na kulemba bwino kudzakupindulilani inuyo komanso mpingo (Onani ndime 10-11)

10-11. Kodi m’bale wacinyamata angapindule bwanji na kupindulila mpingo akaphunzila kuŵelenga na kulemba bwino? (Salimo 1:​1-3) (Onaninso zithunzi.)

10 Phunzilani kuŵelenga na kulemba bwino. Baibo imati mwamuna wacimwemwe komanso wopambana amaseŵenzetsa nthawi yake kuŵelenga mawu a Mulungu na kuwasinkhasinkha. (Ŵelengani Salimo 1:​1-3.) Kuŵelenga Baibo tsiku lililonse kumam’thandiza kudziŵa bwino kaganizidwe ka Yehova, zimene zimamuthandiza kukhala woganiza bwino. (Miy. 1:​3, 4) Amuna otelo ni ofunika mu mpingo. Cifukwa ciyani?

11 Abale na alongo athu amayang’ana kwa amuna oyenelela akafuna malangizo na upangili. (Tito 1:9) Ngati mumatha kuŵelenga na kulemba, mudzakwanitsa kukonzekela nkhani na ndemanga zogwila mtima komanso zolimbikitsa cikhulupililo. Mudzakwanitsanso kulemba manotsi atanthauzo pamene muŵelenga na kumvetsela nkhani pa msonkhano wa mpingo, wa dela komanso wa cigawo. Manotsi amenewa adzakuthandizani kulimbitsa cikhulupililo canu komanso kulimbikitsa ena.

12. N’ciyani cingakuthandizeni kumakambilana bwino na ena?

12 Kulitsani luso yokambilana bwino na ena. Mwamuna wacikhristu ayenela kuphunzila kukamba bwino na ena. Mwamuna amene amakamba bwino na ena amamvetsela zimene ena akunena ndipo amazindikila mmene akumvela. (Miy. 20:5) Amamvetsa mmene ena akumvela poona mmene akulankhulila, komanso magesica amene akupanga polankhula. Simungakwanitse kucita zimenezi ngati simupatula nthawi yoceza na anthu. Ngati nthawi zambili mumaceza na anthu pa mameseji, simungakulitse luso lanu lokambilana na anthu pamaso-m’pamaso. Conco, muzipeza mipata yokambilana na anthu pamaso-m’pamaso.—2 Yoh. 12.   

Cilibwino kuphunzila luso limene lingakuthandizeni kupeza nchito (Onani ndime 13)

13. N’ciyani cina cimene wacinyamata ayenela kuphunzila? (1 Timoteyo 5:8) (Onaninso zithunzi.)

13 Phunzilani kudzisamalila. Mkhristu wokhwima ayenela kudzisamalila komanso kusamalila a m’banja lake. (Ŵelengani 1 Timoteyo 5:8.) M’maiko ena, m’bale wacinyamata angaphunzile nchito kwa atate ake kapena kwa wacibale wina. Ndipo m’maiko ena, wacinyamata angaphunzile nchito kapena luso lina lake ku sukulu. Mulimonsemo, m’pofunikila kuphunzila luso lina lake limene lingakuthandizeni kupeza nchito. (Mac. 18:​2, 3; 20:34; Aef. 4:28) Muzidziŵika kuti ndinu munthu wakhama pa nchito, amene amayamba nchito na kuimalizitsa. Mukatelo, mudzapeza nchito na kukhalitsa pa nchitoyo. Makhalidwe komanso maluso amene takambilana ni ofunikanso kwa mwamuna wacikhristu kuti akakwanilitse maudindo a m’tsogolo. Tiyeni tikambilaneko ena mwa maudindo amenewa.

KONZEKELANI MAUDINDO A M’TSOGOLO

14. Kodi m’bale wacinyamata angakonzekele bwanji kudzakhala mtumiki wa nthawi zonse?

14 Kukhala mtumiki wa nthawi zonse. Amuna ambili okhwima acikhristu anayamba upainiya wa nthawi zonse ali acinyamata. Upainiya umathandiza wacinyamata kuphunzila kuseŵenza bwino na anthu osiyana-siyana. Umam’thandizanso kupanga bajeti yabwino na kuitsatila. (Afil. 4:​11-13) Ciyambi cabwino coyamba utumiki wa nthawi zonse ni kucita upainiya wothandiza. Ambili amacita upainiya wothandiza kwa kanthawi, zimene zimawathandiza kuti ayambe upainiya wa nthawi zonse. Upainiya wa nthawi zonse umatsegula mipata ku mautumiki ena a nthawi zonse osiyana-siyana, monga kutumikila m’dipatimenti ya zamamangidwe kapena pa Beteli.

15-16. Kodi m’bale wacinyamata angatani kuti ayenelele kutumikila mu mpingo?

15 Kukhala mtumiki wothandiza kapena mkulu. Amuna acikhristu ayenela kukhala na colinga cokwanilitsa ziyeneletso kuti atumikile abale na alongo awo mu mpingo monga akulu. Baibo imati amuna amene akuyesetsa kuti akhale oyang’anila “akufuna nchito yabwino.” (1 Tim. 3:1) Asanakhale mkulu, coyamba m’bale afunika kuyenelela kukhala mtumiki wothandiza. Atumiki othandiza amathandiza akulu m’njila zosiyana-siyana. Akulu na atumiki othandiza amatumikila abale na alongo awo modzicepetsa ndipo amalalikila mokangalika. Abale acinyamata angayenelele kukhala atumiki othandiza ngakhale pamene ali na zaka za m’ma 17. Ndipo mtumiki wothandiza woyenelela bwino angakhale mkulu ali na zaka za m’ma 20.

16 Kodi mungayenelele bwanji maudindo amenewa? Palibe njila yoikika. Komabe, ziyeneletso zofunikila n’zozikika m’Baibo, komanso cikondi canu pa Yehova, banja lanu, komanso mpingo. (1 Tim. 3:​1-13; Tito 1:​6-9; 1 Pet. 5:​2, 3) Yesetsani kumvetsa ciyeneletso ciliconse pacokha. Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kukwanilitsa ziyenelezo zimenezi. c

Yehova afuna kuti mwamuna azikonda mkazi wake na ana ake, komanso kuwasamalila mwakuthupi, koma koposa zonse mwauzimu (Onani ndime 17)

17. Kodi m’bale wacinyamata angakonzekele bwanji kudzakhala mwamuna m’banja komanso mutu wa banja? (Onaninso zithunzi.)

17 Kukhala mwamuna komanso mutu wa banja. Monga Yesu anakambila, amuna ena acikhristu amasankhabe kusakwatila. (Mat. 19:12) Komabe, ngati mwasankha kukwatila, mudzakhala na maudindo ena oonjezeleka okhala mwamuna m’banja komanso mutu wa banja. (1 Akor. 11:3) Yehova amayembekezela mwamuna kumukonda mkazi wake na kumusamalila kuthupi komanso kuuzimu. (Aef. 5:​28, 29) Makhalidwe na maluso amene takambilana kumayambililo kwa nkhani ino, monga kukhala oganiza bwino, kulemekeza akazi, komanso kukhala wodalilika, angakuthandizeni mukadzakwatila. Mudzakhala wokonzeka bwino kusamalila maudindo anu monga mwamuna m’banja komanso mutu wa banja.

18. Kodi m’bale wacinyamata angakonzekele bwanji kudzakhala tate?

18 Kukhala tate. Mukakwatila, mungakhale tate. Mungaphunzile ciyani kwa Yehova pa nkhani yokhala tate wabwino? Pali maphunzilo ambili. (Aef. 6:4) Yehova anauza mwana wake Yesu pa anthu kuti amamukonda komanso kuti amakondwela naye. (Mat. 3:17) Mukadzakhala tate muzikaonetsetsa kuti nthawi na nthawi mukuwatsimikizila ana anu kuti mumawakonda. Muzikawayamikila moona mtima pa zimene azikacita bwino. Atate amene amatengela citsanzo ca Yehova amathandiza ana awo kukhala Akhristu okhwima. Mungakonzekele pali pano udindo umenewu mwa kusamalila ena mwacikondi mu banja na mu mpingo komanso mwa kuwayamikila. (Yoh. 15:9) Izi zidzakuthandizani m’tsogolo kudzasamalila bwino udindo wanu monga mutu wa banja komanso tate. Koma pali pano khalanibe ciwiya codalilika kwa Yehova, m’banja lanu, komanso mu mpingo.

KODI MUFUNIKILA KUCITA CIYANI PALI PANO?

Acinyamata ambili amene anaphunzitsidwa kucokela m’Malemba na kugwilitsa nchito zimene anaphunzila akhala Akhristu okhwima (Onani ndime 19-​20)

19-20. N’ciyani cingathandize abale acinyamata kukhala amuna okhwima mwauzimu? (Onani cithunzi ca pacikuto.)

19 Inu abale acinyamata, kukhala Mkhristu wokhwima sikumacitika pakokha. Muyenela kukhala na zitsanzo zabwino zimene mungatengele, kukhala oganiza bwino, komanso odalilika. Muyenelanso kuphunzila maluso othandiza pa umoyo, komanso kukonzekela maudindo a m’tsogolo.

20 Nthawi zina mungade nkhawa mukamaganizila zinthu zimene muyenela kucita. Koma mungapambane. Kumbukilani kuti Yehova ni wofunitsitsa kukuthandizani. (Yes. 41:​10, 13) Nawonso abale na alongo anu mu mpingo adzakuthandizani. Mukakwanitsa kukhala mwamuna wokhwima wacikhristu, mudzakhala na umoyo wabwino komanso wokhutilitsa. Timakunyadilani ngako inu abale acinyamata! Yehova akudalitseni pamene muyesetsa kukhala Mkhristu wokhwima.—Miy. 22:4.

NYIMBO 65 Pita Patsogolo!

a Amuna okhwima ni ofunika mu mpingo wa Cikhristu. M’nkhani ino, tikambilane mmene inu abale acinyamata mungakhalile amuna okhwima acikhristu.

b Onani “Kufotokozela Mawu Ena” m’nkhani yapita.

c Onani buku lakuti Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova, mutu 5 na 6.