Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 52

Inu Alongo Acitsikana—Khalani Akazi Okhwima Mwauzimu

Inu Alongo Acitsikana—Khalani Akazi Okhwima Mwauzimu

“Nawonso amai akhale . . . ocita zinthu mosapitilila malile ndi okhulupilika m’zinthu zonse.”—1 TIM. 3:11.

NYIMBO 133 Lambila Yehova Ukali Wacicepele

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Kodi tingatani kuti tikhale Mkhristu wokhwima?

 TIMACITA cidwi kuona mmene mwana amakulila mwamsanga kukhala wamkulu. Kukula kumeneku kumacitika pakokha. Komabe, kukhala Mkhristu wokhwima sikucitika pakokha. b (1 Akor. 13:11; Aheb. 6:1) Kuti tikwanilitse colinga cimeneci, tiyenela kukhala paubwenzi wa thithithi na Yehova. Tifunikilanso mzimu wake woyela pokulitsa makhalidwe aumulungu, kukulitsa maluso othandiza komanso kukonzekela maudindo a m’tsogolo.—Miy. 1:5.

2. Tiphunzilapo ciyani pa Genesis 1:27? Ndipo tikambilane ciyani m’nkhani ino?

2 Yehova ndiye analenga amuna na akazi. (Ŵelengani Genesis 1:27) N’zoonekelatu kuti amuna na akazi amasiyana m’maonekedwe. Ndipo amasiyananso m’njila zina. Mwacitsanzo, Yehova analenga amuna na akazi kuti azigwila nchito zosiyana. Conco, onse ayenela kukhala na makhalidwe komanso maluso amene angawathandize kukwanilitsa maudindo awo. (Gen. 2:18) M’nkhani ino tikambilane zimene mlongo wacitsikana angacite kuti akhale Mkhristu wokhwima. Ndipo m’nkhani yotsatila tidzakambilana zimene abale acinyamata angacite.

KULITSANI MAKHALIDWE AUMULUNGU

Kutengela zitsanzo za akazi okhulupilika monga Rabeka, Esitere na Abigayeli, kungakuthandizeni kukhala Mkhristu wokhwima

(Onani ndime 3-4)

3-4. Kodi alongo acitsikana angapeze kuti zitsanzo zimene angatengele? (Onaninso cithunzi.)

3 Baibo imachula akazi ambili amene anali kum’konda Yehova na kum’tumikila. (Onani nkhani yakuti, “Kodi Tingaphunzile Ciyani kwa Akazi Ochulidwa m’Baibulo?” pa jw.org ku Chichewa.) Monga mmene lemba ya mfundo yaikulu yaonetsela, iwo anali “ocita zinthu mosapitilila malile” komanso “okhulupilika m’zinthu zonse.” Kuwonjezela apo, alongo acitsikana angapeze zitsanzo zabwino za alongo okhwima mwauzimu zimene angatengele mumpingo mwawo.

4 Inu alongo acitsikana, ganizilani zitsanzo za alongo okhwima mwauzimu amene mungatengeleko. Onani makhalidwe osililika amene ali nawo ndiyeno ganizilani mmene mungayaonetsele. M’ndime zotsatila, tikambilane makhalidwe aŵili ofunika kuti mukhale mlongo wokhwima.

5. N’cifukwa ciyani alongo okhwima mwauzimu ayenela kukhala odzicepetsa?

5 Kudzicepetsa ni khalidwe lofunika kuti munthu akhale Mkhristu wokhwima. Mkazi akakhala wodzicepetsa, amasangalala na ubwenzi wabwino na Yehova komanso na anthu ena. (Yak. 4:6) Mwacitsanzo, mkazi wokonda Yehova amasankha kucilikiza lamulo la umutu limene Atate wake wakumwamba anakhazikitsa. (1 Akor. 11:3) Mfundo imeneyi imagwila nchito mumpingo komanso m’banja. c

6. Kodi alongo acitsikana angaphunzile ciyani kwa Rabeka pa nkhani ya kudzicepetsa?

6 Ganizilani citsanzo ca Rabeka. Anali mkazi wanzelu, ndipo paumoyo wake wonse anapanga zisankho zimene zinali kufuna kulimba mtima. Anali kudziŵanso nthawi yabwino yocitapo kanthu. (Gen. 24:58; 27:​5-17) Ngakhale n’telo, iye anali waulemu komanso wogonjela. (Gen. 24:​17, 18, 65) Ngati mumagonjela makonzedwe a Yehova mmene Rabeka anacitila, mudzakhala citsanzo cabwino m’banja mwanu komanso mumpingo.

7. Kodi alongo acitsikana angatengele bwanji citsanzo ca Esitere pa nkhani ya kudzicepetsa?

7 Akhristu onse okhwima afunika kukhala odzicepetsa. Baibo imati “nzelu zimakhala ndi anthu odzicepetsa.” (Miy. 11:2) Esitere anali mtumiki wodzicepetsa wa Mulungu. Kudzicepetsa kwake kunam’thandiza kuti asakhale munthu wodzikuza. Anamvela upangili wa msuweni wake Moredekai na kuutsatila. (Esitere 2:​10, 20, 22) Mungaonetse kuti ndinu odzicepetsa mwa kupempha upangili na kuutsatila.—Tito 2:​3-5.

8. Malinga na 1 Timoteyo 2:​9, 10, kodi kudzicepetsa kungathandize bwanji alongo kupanga zisankho zanzelu pankhani ya kavalidwe na kudzikongoletsa?

8 Esitere anaonetsa kudzicepetsa m’njila inanso. Iye “anali wooneka bwino ndi wokongola kwambili” koma sanafune kutamandidwa cifukwa ca kukongola kwake. (Esitere 2:​7, 15) Kodi mungapindule bwanji na citsanzo ca Esitere? Njila imodzi yafotokozedwa pa 1 Timoteyo 2:​9, 10. (Ŵelengani.) Mtumwi Paulo analangiza alongo kuti ayenela kuvala mwaulemu komanso mwanzelu. Mawu Acigiriki omasulidwa kuti mwaulemu komanso mwanzelu, aonetsa kuti nthawi zonse alongo afunika kuvala zoyenela na kuganizila mmene anthu ena angamvele. Timawayamikila ngako alongo athu okhwima mwauzimu povala mwaulemu!

9. Tingaphunzile ciyani ku citsanzo ca Abigayeli?

9 Kuzindikila ni khalidwe lina limene alongo okhwima mwauzimu amaonetsa. Kodi kuzindikila n’kutani? Ni luntha lokwanitsa kusiyanitsa cabwino na coipa kenako n’kusankha coyenela. Ganizilani citsanzo ca Abigayeli. Mwamuna wake anapanga cisankho colakwika cimene cikanabweletsa mavuto ku banja lake lonse. Abigayeli anacitapo kanthu mwamsanga. Ndipo kucita kwake zinthu mozindikila kunapulumutsa miyoyo. (1 Sam. 25:​14-23, 32-35) Kuzindikila kumatithandizanso kudziŵa nthawi yolankhula komanso yokhala cete. Cina, kumatithandizanso kuonetsa cidwi kwa ena popanda kuwakhumudwitsa.—1 Ates. 4:11.

KULITSANI MALUSO OTHANDIZA

Kodi mwapindula motani cifukwa codziŵa kulemba na kuŵelenga? (Onani ndime 11)

10-11. Kodi kudziŵa kulemba na kuŵelenga kungakupindulileni motani inuyo komanso anthu ena? (Onaninso cithunzi.)

10 Mkazi wacikhristu ayenela kuphunzila maluso othandiza. Maluso amene mtsikana amaphunzila ali mwana, amakhalabe othandiza pa umoyo wake wonse. Ganizilani zitsanzo zocepa izi.

11 Phunzilani kuŵelenga na kulemba. M’zikhalidwe zina, amaona kuti m’posafunika kuti akazi aphunzile kuŵelenga na kulemba. Komabe malusowa ni ofunika kwambili kwa Mkristu aliyense. d (1 Tim. 4:13) Conco, musalole ciliconse kukulepheletsani kukulitsa luso loŵelenga na kulemba bwino. Kodi mudzapindula motani? Maluso amenewa adzakuthandizani kupeza nchito na kukhalitsa pa nchitoyo. Cidzakhala cosavuta kwa inu kuŵelenga Mawu a Mulungu na kuphunzitsa ena. Koposa zonse, adzakuthandizani kumuyandikila kwambili Yehova pamene mukuŵelenga na kusinkhasinkha Mawu ake.—Yos. 1:8; 1 Tim. 4:15.

12. Kodi Miyambo 31:26 ingakuthandizeni bwanji kulankhula bwino na anthu ena?

12 Kulitsani luso lokamba bwino na anthu. Akhristu ayenela kumakambilana bwino na anthu ena. Pambali imeneyi, wophunzila Yakobo anatipatsa ulangizi wothandiza pamene anati: “Munthu aliyense akhale wofulumila kumva, wodekha polankhula.” (Yak. 1:19) Ngati timamvetsela ena akamalankhula, timaonetsa kuti timawamvela “cisoni.” (1 Pet. 3:8) Ngati simukumvetsa zimene munthu wina akulankhula kapena mmene akumvela, m’funseni mafunso oyenela. Ndipo ganizilam’poni musanalankhule. (Miy. 15:28) Dzifunseni kuti, ‘kodi zimene nifuna kulankhula n’zoona komanso n’zolimbikitsa? Kodi zidzaonetsa ulemu na kukoma mtima?’ Phunzilani kwa alongo okhwima amene amakamba mwaluso. (Ŵelengani Miyambo 31:26.) Onani mmene amakambila. Kukulitsa luso limeneli kudzakuthandizani kukhala paubale wabwino na anthu ena.

Mkazi yemwe waphunzila kusamalila nyumba amakhala citsanzo cabwino ku banja lake komanso mumpingo (Onani ndime 13)

13. Kodi mungaphunzile bwanji kusamalila nyumba? (Onaninso cithunzi.)

13 Phunzilani kusamalila nyumba. M’madela ambili, akazi ndiwo amagwila nchito zambili za pakhomo. Amayi anu kapena mlongo wina woyenela, angakuthandizeni kukulitsa maluso ofunikila. Mlongo wina dzina lake Cindy anati: “Imodzi mwa mphatso zofunika zimene amayi ananipatsa, ni kuniphunzitsa kupeza cimwemwe cifukwa cogwila nchito molimbika. Kuphunzila maluso monga kuphika, kuyeletsa, kusoka zovala, na kugula zinthu kunanipeputsila umoyo komanso kunitsegulila mwayi wocita zambili mu utumiki wa Yehova. Amayi ananiphunzitsanso kukhala woceleza. Izi zinanithandiza kukumana na abale na alongo ambili azitsanzo zabwino zimene ningatengele.” (Miy. 31:​15, 21, 22) Mkazi woceleza, amene anaphunzila kusamalila bwino nyumba, amakhala citsanzo cabwino m’banja komanso mumpingo.—Miy. 31:​13, 17, 27; Mac. 16:15.

14. Kodi mwaphunzila ciyani ku cocitika ca mlongo Crystal? Nanga muyenela kuika maganizo anu pa ciyani?

14 Phunzilani kudzisamalila nokha. Ici n’colinga cofunika cimene Akhristu onse okhwima ayenela kudziikila. (Afil. 4:11) Mlongo wina dzina lake Crystal anati: “Makolo anga anan’thandiza kusankha maphunzilo amene ningatenge ku sekondale amene anganithandize kukhala na maluso ofunikila. Atate ananilimbikitsa kutenga maphunzilo a mosamalila ndalama za pa kampani. Ndipo zimenezi zinakhala zothandiza kwa ine.” Kuwonjezela pa kuphunzila maluso amene angakuthandizeni kupeza nchito, yesani kuphunzila kupanga bajeti na kuitsatila. (Miy. 31:​16, 18) Muziika maganizo anu pa zolinga zauzimu na kupewa nkhongole zosafunikila mwa kukhala okhutila na umoyo wosalila zambili.—1 Tim. 6:8.

KONZEKELANI MAUDINDO A M’TSOGOLO

15-16. N’cifukwa ciyani alongo amene ni mbeta ni amtengo wapatali? (Maliko 10:​29, 30)

15 Mukakulitsa makhalidwe auzimu komanso maluso ofunikila, mudzakhala okonzeka kukwanilitsa maudindo anu a m’tsogolo. Ganizilani maudindo otsatilawa amene mungadzakhale nawo.

16 Mungakhalebe mbeta kwa kanthawi. Malinga na mawu a Yesu, akazi ena amasankha kukhalabe mbeta ngakhale kuti cikhalidwe cawo sicilimbikitsa zimenezi. (Mat. 19:​10-12) Ena amakhalabe mbeta cifukwa ca mmene zinthu zilili mu umoyo wawo. Dziŵani kuti Yehova na Yesu samaona Akhristu osakwatiwa kukhala osafunika. Kuzungulila dziko lonse, alongo osakwatiwa ni zitsanzo zabwino mumpingo. Kuonetsa ena cikondi komanso cidwi, kumalimbikitsa akazi acikhristu amenewa kukhala alongo auzimu komanso amayi kwa anthu ambili.—Ŵelengani Maliko 10:​29, 30; 1 Tim. 5:2.

17. Kodi mlongo angakonzekele bwanji kulowa mu utumiki wa nthawi zonse?

17 Mungakhale mtumiki wa nthawi zonse. Akazi acikhristu amacita zambili pa nchito yolalikila padziko lonse. (Sal. 68:11) Konzekelani pali pano kuyamba utumiki wa nthawi zonse. Mungatumikile monga mpainiya wa nthawi zonse, kudzipeleka pa nchito ya mamangidwe kapena kutumikila pa Beteli. Pemphelani za colinga canu. Funsilani kwa amene anakwanilitsa colingaco ndipo afunseni zimene mungacite kuti muyenelele. Ndiyeno onani zimene mungacite kuti mukwanilitse colingaco. Kukwanilitsa colinga canu kudzakutsegulilani mipata yosiyana-siyana mu utumiki wa Yehova.

Ngati mukuganizila zokwatiliwa, muyenela kusankha mosamala wokwatilana naye (Onani ndime 18)

18. N’cifukwa ciyani mlongo ayenela kusankha mwamuna wokwatilana naye mosamala kwambili? (Onaninso cithunzi.)

18 Mungasankhe kukwatiliwa. Makhalidwe komanso maluso amene takambilana angakuthandizeni kukhala mkazi wabwino m’banja. Komabe ngati mufuna kukwatiliwa, muyenela kusankha wokwatilana naye mosamala kwambili. Ici n’cimodzi mwa zisankho zofunika kwambili cimene mungapange. Kumbukilani kuti mudzakhala pansi pa ulamulilo wa mwamuna amene adzakukwatilani. (Aroma 7:2; Aef. 5:​23, 33) Conco dzifunseni kuti, ‘kodi ni Mkhristu wokhwima? Kodi amatsogoza zauzimu mu umoyo wake? Kodi amapanga zisankho zanzelu? Kodi amavomeleza akalakwitsa zina zake? Kodi amalemekeza akazi? Kodi anganisamalile mwauzimu, mwakuthupi komanso kukhala bwenzi leni-leni kwa ine? Kodi amasamalila bwino maudindo ake? Mwacitsanzo, kodi ali na maudindo anji mumpingo? Ndipo amawasamalila motani?’ (Luka 16:10; 1 Tim. 5:8) Inde, ngati mufuna kukapeza mwamuna wabwino, inunso muyenela kukonzekela kukakhala mkazi wabwino.

19. N’cifukwa ciyani udindo wa “mthandizi” ni wolemekezeka?

19 Baibo imati mkazi wabwino ni mthandizi wa mwamuna wake komanso womucilikiza. (Gen. 2:18) Kodi zitanthauza kuti mkazi ni wotsika kwa mwamuna? Ayi. Udindo wa mkazi monga mthandizi ni wolemekezeka. Ndi iko komwe Baibo imati Yehova ni “mthandizi”. (Sal. 54:4; Aheb. 13:6) Mkazi amakhala mthandizi weniweni ngati amacilikiza mwamuna wake pa zisankho zimene amapanga zokhudza banja lawo. Komanso, cifukwa cokonda Yehova, iye amayesetsa kuthandiza mwamuna wake kupanga mbili yabwino. (Miy. 31:​11, 12; 1 Tim. 3:11) Mungakonzekele udindo umenewu mwa kukulitsa cikondi canu pa Yehova komanso kuthandiza a m’banja lanu komanso mumpingo.

20. Kodi mayi amakhala na cisonkhezelo cotani ku banja lake?

20 Mungakhale nakubala. Mukakwatiliwa, inu na mwamuna wanu mungakhale na ana. (Sal. 127:3) Conco, zingakhale bwino kuganizila za m’tsogolo. Makhalidwe na maluso amene takambilana m’nkhani ino angakuthandizeni mukadzakwatiliwa komanso kukhala mayi. Makhalidwe monga cikondi, kukoma mtima, na kuleza mtima angakuthandizeni kudzakhala na banja labwino mmene ana anu angazimve otetezeka komanso acimwemwe.—Miy. 24:3.

Alongo ambili acitsikana amene anaphunzitsidwa kucokela m’Malemba komanso kutsatila zimene anaphunzitsidwa akhala Akhristu okhwima (Onani ndime 21)

21. Kodi alongo athu timawaona motani? Nanga n’cifukwa ciyani? (Onani cithunzi ca pacikuto.)

21 Timakukondani ngako inu alongo cifukwa ca zonse zimene mumacita potumikila Yehova na anthu ake. (Aheb. 6:10) Mumacita khama kuti mukulitse makhalidwe auzimu. Kuwonjezela apo, mumacitanso khama kukulitsa maluso amene angakuthandizeni inuyo na anthu okuzungulilani, komanso kukonzekela bwino maudindo a m’tsogolo. Ndinu a mtengo wapatali m’gulu la Yehova!

NYIMBO 137 Azimayi Okhulupilika, Alongo Athu

a Inu alongo okondedwa acitsikana ndinu a mtengo wapatali mumpingo. Mungafike pa ucikulile wauzimu mwa kukulitsa makhalidwe aumulungu, kuphunzila maluso ofunikila komanso kukonzekela maudindo a m’tsogolo. Mukatelo, mudzasangalala na mautumiki oculuka m’gulu la Yehova.

b KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Munthu amene wakhala Mkhristu wokhwima amatsogoleledwa na Mawu na Mulungu osati na nzelu za dziko. Iye amatengela citsanzo ca Yesu, komanso kucita khama kuti akhale paubale wolimba na Yehova, ndipo amaonetsanso cikondi codzimana kwa ena.

d Kuti mudziŵe zambili pa kufunika kophunzila kuŵelenga, onani nkhani yakuti “N’cifukwa Ciyani Kuŵelenga ndi Kofunika Kwambili kwa Ana?—Mbali Yoyamba: Kodi Zomwe Zingawathandize Ndi Zoŵelenga Kapena Zoonelela?” pa jw.org ku Chichewa.