Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mukukumbukila?

Kodi Mukukumbukila?

Kodi munaŵelenga mosamala magazini a caka cino a Nsanja ya Mlonda? Yesani kuyankha mafunso otsatilawa:

Kodi “kusintha maganizo anu” kumatanthauza ciyani? (Aroma 12:2)

Kumatanthauza zambili, osati kucita nchito zabwino cabe. Kumaphatikizapo kusanthula umunthu wathu wamkati, na kupanga masinthidwe alionse ofunikila kuti umoyo wathu ukhale wogwilizana na cifunilo ca Mulungu.—w23.01, mas. 8-9.

Timaonetsa bwanji kuti ndife osamala pamene tionelela zocitika za m’dzikoli?

Timacita cidwi kwambili na zocitika za m’dzikoli kuti tidziŵe mmene zingakwanilitsile maulosi. Timapewa kukamba zongoganizila cifukwa zingasokoneze mgwilizano mu mpingo. Makambilano athu amazikika m’zofalitsa za gulu la Yehova. (1 Akor. 1:10)—w23.02, tsa. 16.

Kodi ubatizo wa Yesu umasiyana bwanji na wa otsatila ake?

Yesu sanafunikile kudzipatulila kwa Yehova mmene zimakhalila kwa ife, cifukwa anabadwila mu mtundu wodzipatulila kale kwa Mulungu. Iye sanafunike kulapa macimo, cifukwa anali wangwilo, wopanda ucimo uliwonse.—w23.03, tsa. 5.

Tingatani kuti ambili azikhala na mpata wopelekapo ndemanga pa misonkhano?

Ndemanga zathu zizikhala zazifupi, kuti ena azikhalanso na mpata wopelekapo ndemanga. Tizipewanso kukamba mfundo zambili, moti ena n’kusoŵelatu ndemanga yopelekapo.—w23.04, tsa. 23.

Kodi “Msewu wa Ciyelo” wochulidwa pa Yesaya 35:8 umaimila ciyani?

Msewu umenewu poyamba unaimila njila imene Ayuda anadzela pobwelela kwawo pocoka ku Babulo. Nanga bwanji masiku ano? Zaka mahandiledi ambili cisanafike caka ca 1919, panagwilika nchito yokonza msewu umenewu—mwa zina panagwilika nchito yomasulila na kupulinta ma Baibo. Anthu a Mulungu akhala akuyenda pa “Msewu wa Ciyelo” umene umatsogolela ku madalitso a Ufumu.—w23.05, mas. 15-19.

Kodi Miyambo caputala 9 imapeleka malangizo otani poseŵenzetsa akazi aŵili ophiphilitsa?

Miyambo imakamba za “mkazi wopusa” amene ciitano cake cimatsogolela “ku Manda.” Imakambanso za “nzelu yeniyeni,” imene imafotokozedwa monga mkazi amene ciitano cake cimatsogolela “m’njila yomvetsa zinthu” komanso ku moyo. (Miy. 9:​1, 6, 13, 18)—w23.06, mas. 22-24.

Kodi kudzicepetsa kwa Mulungu na cifundo cake kunaonekela motani pamene anali kucita zinthu na Loti?

Yehova anauza Loti kuti athaŵile kumapili. Koma Loti atapempha kuti athaŵile ku Zowari, Mulungu anamva pempho lake.—w23.07, tsa. 21.

Kodi mkazi angatani ngati mwamuna wake amaonelela zamalisece?

Sayenela kudziimba mlandu. Ayenela kuika maganizo ake pa ubwenzi wake na Mulungu komanso kusinkhasinkha zitsanzo za akazi a m’Baibo amene anapeza citonthozo kwa Mulungu. Angathandize mwamuna wake kupewa zinthu zimene zingam’cititse kuonelela zamalisece.—w23.08, mas. 14-17.

Kodi kuzindikila kungatithandize bwanji kukhalabe odekha tikafunsidwa za cikhulupililo cathu?

Tidziona funso la munthu monga njila yotithandiza kudziŵa maganizo ake komanso zimene amakhulupilila. Izi zingatithandize kuyankha modekha.—w23.09, p. 17.

Tingaphunzile ciyani kwa Mariya pa nkhani yopeza mphamvu?

Mariya atadziŵa kuti adzakhala mayi wa Mesiya, anapeza mphamvu kucokela kwa. Mngelo Gabirieli na Elizabeti anapeleka cilimbikitso ca m’Malemba kwa Mariya. Nafenso tingapeze mphamvu kucokela kwa alambili anzathu.—w23.10, tsa. 15.

Kodi Yehova angayankhe bwanji mapemphelo athu?

Iye analonjeza kumvetsela ku mapemphelo athu na kuona mmene amagwilizanila na cifunilo cake. (Yer. 29:12) Angayankhe mapemphelo ofanana m’njila zosiyana, koma iye nthawi zonse amatithandiza.—w23.11, masa. 21-22.

Aroma 5:2 imachula za “ciyembekezo,” ndiye n’cifukwa ciyani cikuchulidwanso mu vesi 4?

Munthu akamvetsela uthenga wabwino, amakhala na ciyembekezo codzakhala m’paradaiso padziko lapansi. Koma pomwe akumana na masautso, kuwapilila, na kuona ciyanjo ca Mulungu, ciyembekezo cake cimalimbilako ndipo amacipanga kukhala cake-cake.—w23.12, mas. 12-13.