Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Yendelani Malangizo a Mulungu pa Nkhani ya Moŵa

Yendelani Malangizo a Mulungu pa Nkhani ya Moŵa

MOSAKAIKA mumayamikila mphatso zosiyana-siyana zocokela kwa Yehova, kuphatikizapo ufulu wanu wosankha mmene mungasangalalile na mphatso zimenezi. N’zocititsa cidwi kuti Baibo imanena kuti vinyo ni mphatso yocokela kwa Mulungu, ndipo imawonjezela kuti: “Cakudya cimacititsa anchito kuseka, ndipo vinyo amacititsa moyo kusangalala.” (Mlal. 10:19; Sal. 104:15) Ngakhale n’telo, mwina inu mwaonapo anthu ena akugwela m’mavuto cifukwa ca moŵa. Kuwonjezela apo, anthu pa dzikoli amayendela maganizo osiyana-siyana pa nkhani ya kamwedwe ka moŵa. Conco kodi ni njila iti yanzelu imene Akhristu angatsatile pankhani imeneyi?

Mosasamala kanthu za kumene tikhala kapena cikhalidwe cathu, tidzapeza mapindu okhalitsa ngati tilola maganizo a Mulungu kutsogolela kaganizidwe kathu na zisankho zathu.

Mwina inu munaonapo kuti anthu ambili padzikoli amamwa moŵa pafupi-pafupi ndipo amaumwa kwambili. Ena amamwa moŵa cifukwa umawacititsa kukhala omasuka kapena kuti aiŵaleko nkhawa zimene ali nazo ku mavuto awo. Ndipo kumalo ena anthu amamwa moŵa kwambili pofuna kuoneka kuti akhwima kapena kuti ni amuna enieni.

Koma Akhristufe tili na citsogozo canzelu cocokela kwa Mlengi wathu wacikondi. Mwacitsanzo, iye amaticenjeza za zoipa zimene zimatulukapo kaamba ka kumwa moŵa mopambanitsa. Mwina munaŵelengapo Miyambo 23:​29-35 pamene pafotokoza za munthu woledzela komanso mavuto amene amakumana nawo. a Daniel, mkulu mumpingo ku Europe, amakumbukila mmene umoyo wake unalili asanakhale Mkhristu weniweni. Anafotokoza kuti, “Kumwa moŵa mopambanitsa kunacititsa kuti nipange zitsankho zoipa, komanso kudzipeza m’zocitika zoipa zomwe zimaniŵaŵabe nikazikumbukila.”

Kodi Akhristu angaseŵenzetse bwanji ufulu wawo wodzisankhila zocita na kupewa mavuto amene amabwela cifukwa ca kumwa moŵa mopambanitsa? Mfundo yake yagona pa kulola mmene Mulungu amaonela zinthu kutsogolela kaganizidwe na zocita zathu.

Tiyeni tione zimene Baibo imakamba pa nkhani ya moŵa, komanso zifukwa zimene ena amamwela moŵa.

MIYESO YA M’BAIBO

Mawu a Mulungu saletsa kumwa moŵa pa mlingo woyenela. Ndi iko komwe, Baibo imavomeleza kuti vinyo amasangalatsa. Timaŵelenga kuti “Pita ukadye cakudya cako mokondwela ndi kumwa vinyo wako ndi mtima wosangalala.” (Mlal. 9:7) Nthawi zina Yesu anali kumwako vinyo, ndipo atumiki ena a Yehova okhulupilika anacitako cimodzi-modzi.—Mat. 26:​27-29; Luka 7:34; 1 Tim. 5:23.

Komabe, Mawu a Mulungu amaonetsa kusiyana pakati pa kumwa moŵa pamlingo woyenela na kuledzela nawo. Amanena momveka bwino kuti: “Musamaledzele naye vinyo.” (Aef. 5:18) Ndipo amanenanso kuti ‘zidakwa . . . sizidzaloŵa mu Ufumu wa Mulungu.’ (1 Akor. 6:10) Inde, Yehova amadzudzula mwamphamvu kumwa mopambanitsa komanso ucidakwa. M’malo motsatila mfundo zoumbidwa na zikhalidwe za anthu, timapanga zisankho motsatila miyeso ya Mulungu.

Ena amaona kuti angamwe moŵa wambili popanda kuledzela. Koma kucita zimenezi n’koopsa kwambili. Malemba amanena momveka bwino kuti kukhala “akapolo a vinyo wambili” kungacititse munthu kuwononga makhalidwe ake abwino komanso uzimu wake. (Tito 2:3; Miy. 20:1) Ndipo Yesu anacenjeza kuti “kumwa kwambili” kungalepheletse munthu kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu. (Luka 21:​34-36) Cotelo, n’ciyani cingathandize Mkhristu kupewa kugwela m’mavuto amene angabwele cifukwa ca kumwa moŵa?

ONANI ZIFUKWA ZANU NA MMENE M’MAMWELA

Zimakhala zoopsa kwambili munthu akalola kuti cikhalidwe cawo cimutsogolele pamene akupanga cisankho ca mmene angamwele moŵa. Mwanzelu, Akhristu amasankha kucita zomwe zingakondweletse Yehova pa nkhani zokhudza cakudya na zakumwa. Baibo imatikumbutsa kuti: “Kaya mukudya kapena kumwa kapena mukucita cina ciliconse, citani zonse kuti zibweletse ulemelelo kwa Mulungu.” (1 Akor. 10:31) Onani mafunso na mfundo za m’Baibo zimene mungaganizilepo:

Kodi nimamwa moŵa na colinga cakuti ena anikonde? Ekisodo 23:2 imati: “Usatsatile khamu.” Pa lembali, Yehova anali kucenjeza Aisiraeli amene anali kutsatila anthu omwe sanali kum’kondweletsa. Mfundo imeneyi igwilanso nchito kwa Akhristu masiku ano. Ngati timalola anthu ena kusonkhezela kaganizidwe na zisankho zathu pa moŵa, tingatalikilane na Yehova komanso miyeso yake.—Aroma. 12:2.

Kodi nimamwa moŵa pofuna kuoneka wolimba? M’zikhalidwe zina, kumwa moŵa kwambili komanso pafupi-pafupi n’kololeka. (1 Pet. 4:3) Koma onani mfundo iyi yopezeka pa 1 Akorinto 16:13 pomwe pamati: “Khalani maso, limbani m’cikhulupililo, pitilizani kucita camuna, khalani amphamvu.” Kodi moŵa ungathandize munthu kupitiliza kucita camuna? Kutali-tali. Moŵa umafooketsa kaganizidwe ka munthu mosavuta, komanso luntha lake la kupanga zisankho. Conco, kumwa moŵa kwambili sikuonetsa kuti munthu ni wamphamvu, koma kumaonetsa kuti ni wofooka. Yesaya 28:7 imafotokoza za munthu yemwe wasocela cifukwa cakuti waledzela na moŵa komanso wapunthwa.

Mphamvu zenizeni zimacokela kwa Yehova, ndipo zimaphatikizapo ‘kukhala maso na kulimba m’cikhulupililo.’ (Sal. 18:32) Mkhristu woona angacite zimenezi mwa kukhala wogalamuka komanso kupanga zisankho zomwe zingamuteteze kuti asavulale mwauzimu. Yesu anaonetsa mphamvu zimenezo pomwe anali pa dziko lapansi, ndipo anthu ambili anamulemekeza cifukwa anali wolimba mtima komanso wotsimikiza kucita zoyenela.

Kodi nimamwa moŵa kuti niiŵaleko mavuto anga? Wolemba Salimo anauzilidwa kulemba kuti: “Malingalilo osautsa atandiculukila mumtima mwanga, mawu anu [Yehova] otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.” (Sal. 94:19) Ngati mwapanikizika na nkhawa za pa umoyo, dalilani Yehova kuti akuthandizeni, osati kumwa moŵa. Njila yothandiza kwambili imene mungacitile zimenezi ni kupemphela kaŵili-kaŵili kwa Yehova. Komanso, ena apindula kwambili mwakupempha thandizo kwa mnzawo amene ni wokhwima mwauzimu mu mpingo. Ndi iko komwe, kumwa moŵa kuti munthu athane na mavuto kungacititse munthuyo kuloŵelela m’makhalidwe oipa, ndipo zimakhala zovuta kuti acite zoyenela. (Hos. 4:11) Daniel, amene tam’chula m’nkhani ino, anavomeleza kuti: “N’nali kuvutika na nkhawa komanso kudziimba mlandu. Kuti nicepetseko mavutowa, n’nali kumwa moŵa, koma m’pamene mavutowa anali kukulilako. Pothela pake, ambili anasiya kukhala mabwenzi anga, ndipo n’nadzitaila ulemu.” Kodi n’ciyani cinam’thandiza Daniel? Iye anafotokoza kuti “N’nazindikila kuti n’nafunika kudalila Yehova m’malo modalila moŵa. N’tacita zimenezi pamapeto pake n’nakwanitsa kuthana na mavuto anga.” Zoona zake n’zakuti Yehova nthawi zonse amakhalapo kuti apeleke thandizo ngakhale ku mavuto amene angaoneke ngati ovuta kucita nawo.—Afil. 4:​6, 7; 1 Pet. 5:7.

Ngati nthawi zina mumamwako moŵa, bwanji osadzifufuza mmene mumamwela mwa kuyankha mafunso otsatilawa, ‘Kodi wacibale kapena mnzanga wa pamtima anadandaulapo pa kamwedwe kanga?’ Ngati n’conco, mwina ici cingakhale cizindikilo cakuti mwayamba cizoloŵezi kapena mwakhala na vuto limene simunalizindikile. ‘Kodi n’nayamba kumwa kuposa mmene n’nali kumwela kale?’ Izi zingacitike kwa munthu ngakhale kuti alibe cizoloŵezi ca kumwa moŵa, koma akhoza kuyamba kukhala na cizoloŵezi cimeneci. ‘Kodi zimanivuta kukhala osamwa moŵa kwa masiku angapo kapena kuposapo?’ Ngati n’telo, ndiye kuti moŵa wayamba kukuloŵelelani, kapena mwayamba kumwa mopitilila malile. Zikatelo, mungafunike thandizo la akatswili kuti muthane nalo vuto limeneli.

Akhristu ena asankha kulekelatu kumwa moŵa cifukwa ca mavuto amene umabweletsa. Ena samamwa moŵa cifukwa sakonda mmene umamvekela. Ngati mmodzi mwa anzanu anapanga cisankho cimeneci, mungaonetse kukoma mtima mwa kulemekeza cisankho cake popanda kumuimba mlandu.

Mwina munaona kuti n’kwanzelu kudziikila malile a kuculuka kwa moŵa umene mungamwe. Mwinanso angadziikile lamulo pamene angamamwe moŵa, mwina kamodzi pa mlungu, kapena mwa apa na apo pa zakudya zina. Ena angasankhe mtundu wa moŵa umene angamwe. Angasankhe kumwa vinyo kapena moŵa pamlingo waung’ono na kupewa umene uli na zoledzeletsa zambili ngakhale utasakanizidwa na zakumwa zina. Munthu akadziikila malile pa kamwedwe ka moŵa, cimakhala cosavuta kwa iye kutsatila zimene anasankhazo. Ndipo palibe cifukwa cakuti Mkhristu wokhwima azicita manyanzi ngati anaziikila cisankho cimeneci, ndipo niwotsimikiza mtima kutsatila zimene anasankhazo.

Tiyenelanso kuganizila ena pamene tikupanga zisankho zokhudza moŵa. Aroma 14:21 imati: “Ndi bwino kusadya nyama kapena kusamwa vinyo kapena kusacita kalikonse kamene kamakhumudwitsa m’bale wako.” Kodi mungatsatile bwanji uphungu umenewu? Mwa kuonetsa cikondi ca paubale. Ngati muona kuti kumwa moŵa kudzakhumudwitsa wina wake, cikondi cidzakusonkhezelani kuti musamwe pa nthawiyo. Mwakutelo, mudzaonetsa kuti mumaganizila ena komanso kuti mumalemekeza mmene ena amamvela mwa kuika patsogolo zofuna zawo osati zanu.—1 Akor. 10:24.

Kuwonjezela apo, boma lingakhale na malamulo amene angathandize Mkristu kupanga cisankho pa nkhani ya moŵa. Malamulo amenewa angakhale onena za ciŵelengelo ca zaka zakubadwa kuti munthu ayambe kumwa moŵa, komanso oletsa munthu kuyendetsa galimoto kapena kuseŵenzetsa makina ena ake akamwa moŵa.—Aroma. 13:​1-5.

Yehova watilemekeza potipatsa ufulu wosangalala na mphatso zambili zimene anatipatsa. Izi ziphatikizapo ufulu wathu wosankha zimene tidzadya kapena kumwa. Tiyeni tiziyesetsa kuonetsa kuti timayamikila ufulu umenewu mwa kuuseŵenzetsa kupanga zisankho zokondweletsa Atate wathu wakumwamba.

a Bungwe lina la ku America loona za umoyo linanena kuti kumwa moŵa mopambanitsa ngakhale kwa nthawi yocepa kumabweletsa mavuto monga kuphana, kudzipha, kugona munthu mwacikakamizo, nkhanza kwa mnzako wa mu ukwati, komanso kupita padela.